Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Old/New Testament

Each day includes a passage from both the Old Testament and New Testament.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 26-28

Kalembera Wachiwiri

26 Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni, “Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.” Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti, “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.”

Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa:

Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi:

kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki;

kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu;

kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi;

kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi.

Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730.

Mwana wa Palu anali Eliabu, ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova. 10 Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo. 11 Koma ana a Kora sanafe nawo.

12 Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele;

kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini;

kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini;

13 kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera;

kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli.

14 Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200.

15 Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi:

kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni;

kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi;

kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni;

16 kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini;

kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri;

17 kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi;

kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli.

18 Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500.

19 Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani.

20 Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Sela, fuko la Asera;

kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi;

kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera.

21 Zidzukulu za Perezi zinali izi:

kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi;

kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli.

22 Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500.

23 Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Tola, fuko la Atola;

kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa;

24 kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu.

Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi.

25 Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300.

26 Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi;

kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni;

kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli.

27 Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500.

28 Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi:

29 Zidzukulu za Manase:

kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi);

kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi.

30 Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi;

kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri;

kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki;

31 kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli;

kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu;

32 kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida;

kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi.

33 (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.)

34 Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700.

35 Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi;

kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela;

kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri;

kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani.

36 Zidzukulu za Sutela zinali izi:

kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani.

37 Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500.

Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo.

38 Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi:

kuchokera mwa Bela, fuko la Abela;

kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli;

kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu;

39 kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu;

kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu;

40 Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi:

kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi;

kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani;

41 Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600.

42 Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi:

kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu.

Izi zinali zidzukulu za Dani. 43 Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400.

44 Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna;

kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi;

kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya;

45 ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya:

kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi;

kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli;

46 (Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera)

47 Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400.

48 Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi:

kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli;

kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni;

49 kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri;

kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu.

50 Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400.

51 Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730.

52 Yehova anawuza Mose kuti, 53 “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo. 54 Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa. 55 Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo. 56 Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.”

57 Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa:

kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni;

kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati;

kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari.

58 Awanso anali mabanja a Alevi:

banja la Alibini,

banja la Ahebroni,

banja la Amali,

banja la Amusi, fuko la Kora

banja la Akohati,

(Kohati anali abambo a Amramu. 59 Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo. 60 Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo).

62 Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo.

63 Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko. 64 Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai; 65 Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Ana Aakazi a Zelofehadi

27 Kenaka ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wamwamuna wa Manase, a mʼmabanja a Manase, mwana wa Yosefe anabwera. Mayina a ana aakaziwo anali awa: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anakayima pa chipata cha tenti ya msonkhano pamaso pa Mose, wansembe Eliezara, atsogoleri ndi anthu onse, ndipo anati, “Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna. Nʼchifukwa chiyani dzina la abambo athu lasowa pakati pa fuko lawo, kodi popeza analibe mwana wamwamuna? Tipatseni cholowa chathu pakati pa abale a abambo athu.”

Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova ndipo Yehova anati kwa iye, “Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo.

“Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chakecho kwa abale ake. 10 Ngati alibe abale muzipereka cholowa chake kwa abale a abambo ake. 11 Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ”

Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose

12 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kwera phiri la Abarimu kuti ukaone dziko limene ndalipereka kwa Aisraeli. 13 Ukakaliona udzamwalira ngati Aaroni mʼbale wako, 14 chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini).

15 Mose anati kwa Yehova, 16 “Ngati nʼkotheka Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, sankhani munthu woti ayangʼanire gulu ili kuti 17 alitsogolere potuluka ndi polowa, kuti anthu a Yehova asakhale ngati nkhosa zopanda mʼbusa.”

18 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene ali ndi mzimu wa utsogoleri, ndipo umusanjike dzanja lako. 19 Umuyimiritse pamaso pa wansembe Eliezara ndi pamaso pa gulu lonse ndipo umupatse mphamvu zolamulira, anthuwo akuona. 20 Umupatse gawo lina la ulemerero wako kuti Aisraeli onse azimumvera. 21 Ayime pamaso pa wansembe Eliezara, amene adzamudziwitse zimene Yehova akufuna pogwiritsa ntchito Urimu. Iye akalamula, Aisraeli onse azituluka ndipo akalamulanso, Aisraeliwo azibwereranso.”

22 Mose anachita monga Yehova anamulamulira. Anatenga Yoswa ndi kumuyimiritsa pamaso pa Eliezara wansembe ndi pamaso pa gulu lonse. 23 Ndipo anamusanjika manja ndi kumupatsa mphamvu, monga Yehova ananenera kudzera mwa Mose.

Zopereka za Tsiku ndi Tsiku

28 Yehova anawuza Mose kuti, “Lamula Aisraeli kuti, ‘Onetsetsani kuti mukupereka kwa Ine pa nthawi yoyikika, chopereka cha chakudya chotentha pa moto monga fungo lokoma kwa Ine.’ Awuze kuti, ‘Nsembe ya chakudya imene muzipereka pa moto kwa Yehova tsiku ndi tsiku ndi iyi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri, wopanda chilema. Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. Muziperekanso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku imene analamula pa phiri la Sinai kuti ikhale fungo lokoma, nsembe yopsereza pa moto yopereka kwa Yehova. Chopereka chachakumwa chikhale lita imodzi yachakumwa chaukali pa nkhosa iliyonse. Muzithira pamalo opatulika, kupereka kwa Yehova. Muzipereka mwana wankhosa winayo madzulo, pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa. Ichi ndi chopereka chachakudya, fungo lokoma kwa Yehova.’ ”

Zopereka za pa Sabata

“ ‘Pa tsiku la Sabata, muzipereka nsembe ana ankhosa awiri a chaka chimodzi wopanda chilema, pamodzi ndi chopereka chachakumwa ndi chopereka chachakudya chokwana makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. 10 Iyi ndi nsembe yopsereza ya pa Sabata iliyonse, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake chachakumwa.’ ”

Zopereka za pa Mwezi

11 “Pa tsiku loyamba la mwezi uliwonse muzipereka kwa Yehova nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi, onse wopanda chilema. 12 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; ndi nkhosa yayimuna, chopereka cha chakudya cha makilogalamu awiri a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; 13 ndipo pa mwana wankhosa aliyense, chopereka cha ufa wa kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, izi ndi za nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yotentha pa moto ya kwa Yehova. 14 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pakhale chopereka cha chakumwa cha malita awiri a vinyo; ndipo pa nkhosa yayimuna, lita limodzi ndi theka, ndipo pa mwana wankhosa, lita limodzi. Iyi ndi nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi yoperekedwa pa mwezi watsopano mʼkati mwa chaka. 15 Powonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse ndi chopereka chake cha chakumwa, mbuzi yayimuna imodzi iperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopepesera machimo.

Paska

16 “ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita Paska wa Yehova. 17 Pa tsiku la 15 la mwezi womwewo pazikhala chikondwerero. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. 18 Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse. 19 Koma muzipereka kwa Yehova nsembe yotentha pa moto, nsembe yopsereza ya ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa yayimuna imodzi ndi ana ankhosa asanu ndi awiri aamuna a chaka chimodzi, onsewo wopanda chilema. 20 Pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, muzikonza chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta; makilogalamu awiri pa nkhosa yayimuna iliyonse. 21 Kilogalamu imodzi pa mwana wankhosa aliyense mwa ana ankhosa asanu ndi awiri aja. 22 Muziphatikizapo mbuzi yayimuna monga nsembe yopepesera machimo anu. 23 Muzikonza zimenezi nthawi zonse, powonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa. 24 Motere muzikonza chakudya cha nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku pa masiku asanu ndi awiri ngati fungo lokomera Yehova. Zimenezi ziziperekedwa kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya nthawi zonse pamodzi ndi nsembe yachakumwa. 25 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzichita msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito iliyonse.

Madyerero a Masabata

26 “ ‘Pa tsiku la zipatso zoyambirira kucha, pamene mukupereka chopereka cha chakudya chatsopano kwa Yehova, pa nthawi ya chikondwerero cha Masabata, muzichita msonkhano wopatulika ndipo musagwire ntchito zolemetsa. 27 Muzipereka nsembe zopsereza za ana angʼombe aamuna awiri, nkhosa imodzi yayimuna ndi ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri a chaka chimodzi monga fungo lokomera Yehova. 28 Pa ngʼombe yayimuna iliyonse pazikhala chopereka cha chakudya cha makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, pa nkhosa yayimuna iliyonse makilogalamu awiri. 29 Ndipo pa mwana wankhosa aliyense mwa asanu ndi awiri aja, kilogalamu imodzi. 30 Muziperekanso mbuzi yayimuna imodzi kuti izikhala nsembe yopepesera machimo anu. 31 Muzipereka zimenezi pamodzi ndi zopereka za zakumwa ndi nsembe yake ya chakudya. Onetsetsani kuti nyamazo zilibe chilema.

Marko 8

Yesu Adyetsa Anthu 4,000

Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali.”

Ophunzira ake anayankha nati, “Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?”

Yesu anafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”

Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo, 10 analowa mʼbwato pamodzi ndi ophunzira ake napita ku dera la Dalamanuta.

11 Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba. 12 Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.” 13 Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina.

Yisiti wa Afarisi ndi Herode

14 Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato. 15 Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.”

16 Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.”

17 Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa? 18 Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? 19 Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”

20 “Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”

21 Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?”

Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosaona ku Betisaida

22 Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. 23 Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”

24 Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.”

25 Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. 26 Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.”

Petro Avomereza Khristu

27 Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”

28 Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”

29 Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?”

Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”

30 Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.

Yesu Aneneratu za Imfa Yake

31 Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” 32 Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.

33 Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”

Njira ya Mtanda

34 Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. 35 Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. 36 Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? 37 Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? 38 Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.