Old/New Testament
Chilango cha Israeli
9 Iwe Israeli, usakondwere;
monga imachitira mitundu ina.
Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako;
umakonda malipiro a chiwerewere
pa malo aliwonse opunthira tirigu.
2 Malo opunthira tirigu ndi malo opsinyira mphesa sadzadyetsa anthu;
adzasowa vinyo watsopano.
3 Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova.
Efereimu adzabwerera ku Igupto
ndipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.
4 Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova,
kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo.
Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa;
onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa.
Chakudya ichi chidzakhala chodya okha,
sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.
5 Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika;
pa masiku a zikondwerero za Yehova?
6 Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko,
Igupto adzawasonkhanitsa,
ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda.
Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva,
ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
7 Masiku achilango akubwera,
masiku obwezera ali pafupi.
Israeli adziwe zimenezi.
Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri
ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri.
Mneneri amamuyesa chitsiru,
munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
8 Mneneri pamodzi ndi Mulungu wanga
ndiwo alonda a Efereimu,
koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse,
ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
9 Iwo azama mu zachinyengo
monga masiku a Gibeya.
Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo
ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.
10 “Pamene ndinamupeza Israeli
zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu.
Nditaona makolo anu,
zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa.
Koma atafika ku Baala Peori,
anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi
ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho.
11 Ulemerero wa Efereimu udzawuluka ngati mbalame.
Sipadzakhalanso kubereka ana, kuyembekezera kapena kutenga pathupi.
12 Ngakhale atalera ana
ndidzachititsa kuti mwana aliyense amwalire.
Tsoka kwa anthuwo
pamene Ine ndidzawafulatira!
13 Ndaona Efereimu ngati Turo,
atadzalidwa pa nthaka ya chonde.
Koma Efereimu adzatsogolera
ana ake kuti akaphedwe.”
14 Inu Yehova, muwapatse.
Kodi mudzawapatsa chiyani?
Apatseni mimba yomangopita padera
ndi mawere owuma.
15 “Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala,
Ine ndinawada kumeneko.
Chifukwa cha machitidwe awo auchimo,
ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga.
Sindidzawakondanso;
atsogoleri awo onse ndi owukira.
16 Efereimu wathedwa,
mizu yake yauma
sakubalanso zipatso.
Ngakhale atabereka ana,
Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”
17 Mulungu wanga adzawakana
chifukwa sanamumvere Iye;
adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.
10 Israeli anali mpesa wotambalala;
anabereka zipatso zambiri.
Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka,
anawonjezera kumanga maguwa ansembe.
Pamene dziko lake linkatukuka,
anakongoletsa miyala yake yopatulika.
2 Mtima wawo ndi wonyenga
ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo.
Yehova adzagumula maguwa awo ansembe
ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.
3 Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu
chifukwa sitinaope Yehova.
Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu,
kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
4 Mafumu amalonjeza zambiri,
amalumbira zabodza
pochita mapangano.
Kotero maweruzo amaphuka
ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.
5 Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha
chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni.
Anthu ake adzalirira fanolo,
chimodzimodzinso ansembe ake adamawo,
amene anakondwera ndi kukongola kwake,
chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
6 Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya
ngati mphatso kwa mfumu yayikulu.
Efereimu adzachititsidwa manyazi
chifukwa cha mafano ake amitengo.
7 Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali
ngati kanthambi koyenda pa madzi.
8 Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa.
Ili ndiye tchimo la Israeli.
Minga ndi mitungwi zidzamera
ndi kuphimba maguwa awo ansembe.
Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!”
ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
9 “Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya,
ndipo wakhala uli pomwepo.
Kodi nkhondo sinagonjetse anthu
ochita zoyipa ku Gibeya?
10 Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo;
mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo,
kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
11 Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa
amene amakonda kupuntha tirigu,
choncho Ine ndidzayika goli
mʼkhosi lake lokongolalo.
Ndidzasenzetsa Efereimu goli,
Yuda ayenera kulima,
ndipo Yakobo ayenera kutipula.
12 Mufese nokha chilungamo
ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika.
Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo;
pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova,
mpaka Iye atabwera
kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
13 Koma inu munadzala zolakwa,
mwakolola zoyipa;
mwadya chipatso cha chinyengo.
Chifukwa mumadalira mphamvu zanu
ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
14 phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga
kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka,
monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo;
pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
15 Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli
chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu.
Tsiku limeneli likadzafika,
mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.
Chikondi cha Mulungu pa Israeli
11 “Israeli ali mwana, ndinamukonda,
ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.
2 Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana
iwo amandithawa kupita kutali.
Ankapereka nsembe kwa Abaala
ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.
3 Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda,
ndipo ndinawagwira pa mkono;
koma iwo sanazindikire
kuti ndine amene ndinawachiritsa.
4 Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu
ndi zomangira za chikondi;
ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo
ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa.
5 “Sadzabwerera ku Igupto,
koma Asiriya ndiye adzakhala mfumu yawo
pakuti akana kutembenuka.
6 Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo,
ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo
nadzathetseratu malingaliro awo.
7 Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine.
Ngakhale atayitana Wammwambamwamba,
sizidzatheka kuti Iye awakwezenso.
8 “Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu?
Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli?
Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima?
Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu?
Mtima wanga wakana kutero;
chifundo changa chonse chikusefukira.
9 Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa,
kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu.
Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu,
Woyerayo pakati panu.
Sindidzabwera mwaukali.
10 Iwo adzatsatira Yehova;
Iye adzabangula ngati mkango.
Akadzabangula,
ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.
11 Adzabwera akunjenjemera
ngati mbalame kuchokera ku Igupto,
ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya.
Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,”
akutero Yehova.
Tchimo la Israeli
12 Efereimu wandizungulira ndi mabodza,
nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo.
Ndipo Yuda wawukira Mulungu,
wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Sarde
3 “Lembera mngelo wampingo wa ku Sarde kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene amasunga mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri. Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zako; umadziwika kuti ndiwe wamoyo koma ndiwe wakufa. 2 Dzuka! Limbitsa zimene zatsalira zomwe zatsala pangʼono kufa, pakuti ndaona kuti ntchito zako nʼzosakwanira pamaso pa Mulungu. 3 Choncho, kumbukira zimene unalandira ndi kumva; uzisunge ndipo ulape. Koma ngati sudzuka, ndidzabwera ngati mbala ndipo sudzadziwa nthawi imene ndidzabwere kwanu.
4 Komabe uli ndi anthu angapo mu Sarde amene sanadetse zovala zawo. Amenewa adzayenda ndi Ine atavala zoyera popeza ndi oyenera kutero. 5 Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake. 6 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Filadefiya
7 “Lembera mngelo wampingo wa ku Filadefiya kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi woyera ndi woonadi, amene ali ndi kiyi ya Davide. Iye akatsekula palibe amene angatseke; ndipo akatseka palibe amene angatsekule. 8 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa ntchito zako. Taona, ndakutsekulira pa khomo ndipo palibe wina amene angatseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa komabe wasunga mawu anga ndipo sunandikane. 9 Amene ndi mpingo wa Satana, amene amadzitcha kuti ndi Ayuda pamene sali choncho, koma ndi onama, ndidzawabweretsa kwa inu ndi kuwagwetsa pansi pa mapazi anu kuti adzazindikire kuti ndimakukondani. 10 Popeza mwasunga mawu anga woti mupirire ndipo mwawugwira mtima, Inenso ndidzakupulumutsani nthawi ya mayesero imene idzabwera pa dziko lonse lapansi kuyesa onse okhala pa dziko lapansi.
11 Ine ndikubwera msanga. Gwiritsitsa chimene uli nacho kuti wina angakulande chipewa chako chaufumu. 12 Iye amene adzapambane ndidzamusandutsa mzati wa mʼNyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso. Pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano, umene ukubwera pansi kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga; ndipo pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano. 13 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.’ ”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Laodikaya
14 “Lembera mngelo wampingo wa ku Laodikaya kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa Ameni, mboni yokhulupirika ndi yoona, gwero la zolengedwa zonse za Mulungu. 15 Ine ndimadziwa ntchito zako, kuti sindiwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha! 16 Tsono popeza ndiwe wofunda chabe, sindiwe wotentha kapena wozizira, ndatsala pangʼono kuti ndikulavule mʼkamwa mwanga. 17 Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche. 18 Ndikukulangiza kuti ugule kwa Ine golide woyengedwa ndi moto kuti ukhale wolemera. Ugule zovala zoyera kuti uvale ndi kuphimba umaliseche wako wochititsa manyaziwo. Ndiponso ugule kwa Ine mankhwala a mʼmaso kuti uwone.
19 Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa. 20 Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.
21 Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu. 22 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.