New Testament in a Year
Za Kuuka kwa Khristu
15 Tsono abale, ndikufuna ndikukumbutseni za Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani. Munawulandira ndipo munawukhulupirira kolimba. 2 Inu munapulumutsidwa ndi Uthenga Wabwinowu, ngati mwasunga mawu amene ndinakulalikirani. Kupanda kutero, mwangokhulupirira pachabe.
3 Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika kuposa zonse, kuti Khristu anafera zoyipa zathu monga mwa Malemba, 4 kuti anayikidwa mʼmanda, kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu monga mwa Malemba; 5 ndipo kuti anaonekera kwa Petro, ndipo kenaka kwa Atumwi khumi ndi awiriwo. 6 Pambuyo pake, Iye anaonekera kwa anthu oposa 500 mwa abale pa nthawi imodzi, ndipo ambiri mwa iwo akanali ndi moyo ngakhale kuti ena anagona tulo. 7 Kenaka anaonekeranso kwa Yakobo, kenaka kwa atumwi onse. 8 Potsiriza pa onse anaonekeranso kwa ine, monga mwana wobadwa nthawi isanakwane.
9 Pakuti ine ndine wamngʼono kwa atumwi ndipo sindiyenera nʼkomwe kutchedwa mtumwi chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu. 10 Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine. 11 Tsono kaya ndi ineyo kapena iwowo, izi ndi zomwe timalalikira, ndipo izi ndi zimene munakhulupirira.
Kuuka kwa Oyera Mtima
12 Koma ngati timalalikira kuti Khristu anaukitsidwa kwa akufa, zikutheka bwanji kuti ena mwa inu azinena kuti kulibe kuuka kwa akufa? 13 Ngati kulibe kuuka kwa akufa, ndiye kuti ngakhale Khristu sanaukenso. 14 Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, ndiye kuti kulalikira kwathu nʼkopanda ntchito, ndipo chikhulupiriro chanu nʼchopandanso ntchito. 15 Kuwonjezera pamenepa, ndiye kuti ndife mboni zabodza pa za Mulungu, pakuti tikuchita umboni kuti Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa. Ngati nʼzoona kuti akufa saukitsidwa, ndiye kuti Mulungu sanaukitsenso Khristu. 16 Pakuti ngati akufa saukitsidwa, ndiye kuti nayenso Khristu sanaukitsidwe. 17 Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu nʼchopanda ntchito; mukanali mu machimo anu. 18 Ndiye kuti nawonso amene agona tulo mwa Ambuye ndi otayika. 19 Ngati kukanakhala kuti tili ndi chiyembekezo mwa Khristu mʼmoyo uno wokha, tikanakhala omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.
20 Koma nʼzoonadi kuti Khristu anaukitsidwa kwa kufa, chipatso choyamba cha onse ogona tulo. 21 Pakuti monga imfa inadza kudzera mwa munthu, kuuka kwa akufa kwabweranso kudzera mwa munthu. 22 Pakuti monga mwa Adamu onse amafa, chomwechonso mwa Khristu onse adzakhala ndi amoyo. 23 Koma aliyense adzauka pa nthawi yake. Khristu ndiye woyambirira, pambuyo pake, pamene Khristu adzabwera, iwo amene ali ake adzauka. 24 Pamenepo chimaliziro chidzafika, pamene Iye adzapereka ufumu kwa Mulungu Atate, atathetsa ufumu wonse, ulamuliro wonse ndi mphamvu zonse. 25 Pakuti Iye ayenera kulamulira mpaka Mulungu atayika pansi pa mapazi ake adani ake onse. 26 Mdani wotsiriza kuwonongedwa ndi imfa. 27 Pakuti Mulungu “wayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Ponena kuti wayika “zinthu zonse pansi pa mapazi ake,” nʼchodziwikiratu kuti sakuphatikizapo ndi Mulungu yemwe, amene anayika zinthu zonse pansi pa Khristu. 28 Pamene adzatsiriza kuchita zimenezi, Mwana weniweniyo adzakhala pansi pa ulamuliro wa Iye amene anayika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.