New Testament in a Year
Kuwonongeka kwa Sitima
27 Pakati pa usiku wa tsiku la khumi ndi chinayi tikukankhidwabe ndi mphepo mʼnyanja ya Adriya, oyendetsa sitimayo anazindikira kuti timayandikira ku mtunda. 28 Iwo anatenga choyezera kuzama kwa nyanja ndi kupeza kuti kuzama kwake kunali mamita 36. Atayendanso pangʼono anatenganso choyezera chija napeza kuti kuzama kwake kunali 27. 29 Poopa kuti tingagunde miyala, iwo anatsitsira anangula anayi mʼmadzi kumbuyo kwa sitimayo ndipo tinapemphera kuti kuche. 30 Pofuna kuthawa mʼsitimayo, oyendetsa aja anatsitsira mʼnyanja bwato lopulumukiramo nʼkumachita ngati akufuna kutsitsira anangula mʼnyanjamo kutsogolo kwa sitimayo. 31 Pamenepo Paulo anawuza wolamulira asilikali uja ndi asilikaliwo kuti, “Ngati anthu awa sakhala mʼsitima muno, inu simungapulumuke.” 32 Pamenepo asilikaliwo anadula zingwe za bwatolo ndipo linagwera mʼmadzi.
33 Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anawawumiriza anthu onse kuti adye. Iye anati, “Kwa masiku khumi ndi anayi mwakhala mukuda nkhawa ndipo simumadya kanthu kalikonse. 34 Tsopano ine ndikukupemphani kuti mudye. Muyenera kudya kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe wa inu adzataye ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pake.” 35 Paulo atanena zimenezi, anatenga buledi nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo ananyema bulediyo nayamba kudya. 36 Onse analimba mtima nayamba kudyanso. 37 Tonse pamodzi mʼsitimamo tinalipo anthu 276. 38 Onse atadya, nakhuta anapeputsa sitimayo potaya tirigu mʼnyanja.
39 Kutacha, anthu sanazindikire dzikolo, koma anaona pomwe sitima zimayimapo pamodzi ndi mchenga wa pa gombe. Iwo anaganiza zokocheza sitimayo kumeneko ngati zikanatheka kutero. 40 Atadula anangula aja, nawasiya mʼnyanja, pa nthawi yomweyo anamasula zingwe zimene anamangira zowongolera sitimayo. Kenaka anayimika chinsalu chimene mphepo imakankha kuti sitima iyende, ndipo anayamba kupita ku gombe. 41 Koma sitimayo inagunda mchenga wobisika ndipo inayima. Mbali ya kutsogolo ya sitimayo inakanirira ndipo sinathe kuyendanso, ndipo mbali yakumbuyo inasweka ndi kuwomba kwa mafunde.
42 Asilikali anaganiza za kupha amʼndende onse, kuti angasambire kupita pa mtunda ndi kuthawa. 43 Koma wolamulira asilikali uja anafuna kupulumutsa Paulo ndipo anawaletsa kuchita zimene anakonza. Iye analamulira asilikali kuti amene amatha kusambira kuti adziponye mʼmadzi ndi kuyamba kukafika pa mtunda. 44 Otsalawo anayenera kugwira matabwa kapena tizidutswa ta sitimayo. Motero onse anapulumuka nakafika pa mtunda.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.