Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Machitidwe a Atumwi 5:1-21

Hananiya ndi Safira

Koma munthu wina dzina lake Hananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, anagulitsanso munda wawo. Mogwirizana ndi mkazi wakeyo anapatulapo pa ndalamazo nazisunga, ndipo anatenga zotsalazo ndi kukapereka kwa atumwi.

Koma Petro anamufunsa kuti, “Hananiya, chifukwa chiyani Satana anadzaza chotere mu mtima wako kuti unamize Mzimu Woyera ndipo wapatula ndi kusunga ndalama? Kodi sunali wako usanagulitse? Ndipo utagulitsa ndalamazo sizinali mʼmanja mwako kodi? Nʼchiyani chinakuchititsa zimenezi? Iwe sunanamize anthu koma Mulungu.”

Hananiya atamva mawu amenewa anagwa pansi namwalira. Onse amene anamva zimene zinachitikazi anachita mantha kwambiri. Kenaka anyamata anafika, nakulunga thupi lake, ndipo anamunyamula ndi kukamuyika mʼmanda.

Patapita maora atatu mkazi wake analowa, wosadziwa zimene zinachitika. Petro anamufunsa iye kuti, “Tandiwuza, kodi izi ndi ndalama zonse zimene iwe ndi Hananiya munalandira mutagulitsa munda?”

Mkaziyo anati, “Inde ndi zimenezo.”

Petro anati kwa iye, “Bwanji inu munapangana kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona! Anthu amene anakayika mwamuna wako mʼmanda ali pa khomo, ndipo adzakunyamula iwenso.”

10 Nthawi yomweyo anagwa pansi pa mapazi a Petro ndipo anamwalira. Ndipo anyamata aja analowa, napeza kuti wafa kale, anamunyamula ndi kukamuyika pafupi ndi mwamuna wake. 11 Mpingo wonse ndi anthu onse amene anamva zimenezi anachita mantha kwambiri.

Atumwi Achiritsa Anthu Ambiri

12 Atumwi anachita zizindikiro zodabwitsa ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Ndipo onse okhulupirira ankasonkhana pamodzi mu Khonde la Solomoni. 13 Palibe ndi mmodzi yemwe analimba mtima kuphatikana nawo, ngakhale kuti anthu onse amawalemekeza kwambiri. 14 Ngakhale zinali chotere, anthu ambiri anakhulupirira Ambuye ndipo amawonjezeredwa ku chiwerengero chawo. 15 Chifukwa cha zimenezi, anthu anabweretsa odwala mʼmisewu ya mu mzinda nawagoneka pa mabedi ndi pa mphasa kuti chithunzi chokha cha Petro chikhudze ena mwa iwo iye akamadutsa. 16 Anthu ochuluka ochokera ku mizinda yayingʼono ozungulira Yerusalemu amasonkhananso atatenga odwala awo ndi iwo amene amasautsidwa ndi mizimu yoyipa ndipo onsewo amachiritsidwa.

Atumwi Azunzidwa

17 Koma mkulu wa ansembe pamodzi ndi onse omuthandiza, amene anali a gulu la Asaduki, anachita nsanje. 18 Iwo anagwira atumwi ndi kuwatsekera mʼndende ya anthu wamba. 19 Koma usiku mngelo wa Ambuye anatsekula zitseko za ndende ndi kuwatulutsa 20 Mngeloyo anati, “Pitani, ku mabwalo a Nyumba ya Mulungu ndipo mukawuze anthu uthenga onse wamoyo watsopanowu.”

21 Kutacha mmawa, atumwi analowa mʼbwalo la mʼNyumba ya Mulungu, monga anawuzidwa ndipo anayamba kuphunzitsa anthu.

Mkulu wa ansembe pamodzi ndi omuthandiza ake amene anali naye anafika, anayitanitsa msonkhano wa Bwalo Lalikulu, ndilo bwalo la akulu onse a Israeli. Anatuma alonda kuti akatenge atumwi aja kundende.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.