New Testament in a Year
45 Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine. 46 Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate. 47 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha. 48 Ine ndine chakudya chamoyo. 49 Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa. 50 Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe. 51 Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”
52 Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?”
53 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. 54 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 55 Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye. 57 Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58 Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.” 59 Iye ankanena izi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge mu Kaperenawo.
Ophunzira Ambiri Aleka Kutsata Yesu
60 Pakumva izi ambiri a ophunzira ake anati, “Ichi ndi chiphunzitso chovuta. Angachilandire ndani?”
61 Pozindikira kuti ophunzira ake ankangʼungʼudza, Yesu anawafunsa kuti, “Kodi izi zikukukhumudwitsani? 62 Nanga mutaona Mwana wa Munthu akukwera kupita kumene Iye anali poyamba! 63 Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo. 64 Komabe alipo ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti Yesu ankadziwa kuyambira pachiyambi ena mwa iwo amene samakhulupirira ndi amene adzamupereka Iye. 65 Iye anapitiriza kunena kuti, “Ichi ndi chifukwa chake ndinakuwuzani kuti palibe wina angabwere kwa Ine pokhapokha Atate atamuthandiza.”
66 Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye.
67 Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, “Kodi inu mukufuna kuchokanso?”
68 Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha. 69 Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu.”
70 Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi Ine sindinakusankheni inu khumi ndi awiri? Komabe mmodzi wa inu ndi mdierekezi.” 71 (Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka).
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.