Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yohane 4:31-54

31 Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, “Rabi idyani.”

32 Koma Iye anawawuza kuti, “Ine ndili ndi chakudya choti ndidye chimene inu simukuchidziwa.”

33 Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?”

34 Yesu anati, “Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake. 35 Kodi inu simunena kuti, ‘Kwatsala miyezi inayi ndipo kenaka kukolola?’ Ine ndikukuwuzani kuti, tsekulani maso anu ndipo muyangʼane mʼminda! Mbewu zacha kale kuti zikololedwe. 36 Ngakhale tsopano amene akukolola akulandira malipiro ake, ndipo akututa mbewu ku moyo wosatha kuti wofesa ndi wokolola asangalale pamodzi. 37 Nʼchifukwa chake mawu akuti, ‘Wina amafesa ndipo wina amakolola’ ndi woona. 38 Ine ndinakutumani kukakolola zimene simunagwirire ntchito. Ena anagwira ntchito yolemetsa ndipo inu mwatuta phindu la ntchito yawo.”

Asamariya Ambiri Akhulupirira

39 Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.” 40 Choncho Asamariya atabwera kwa Iye, anamuwumiriza Iye kuti akhale nawo, ndipo Iye anakhala nawo masiku awiri. 41 Ndipo chifukwa cha mawu ake, ena ambiri anakhulupirira.

42 Iwo anati kwa mayiyo, “Ife sitikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha, koma tsopano ife tadzimvera tokha, ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndithu ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi.”

Yesu Achiritsa Mwana wa Nduna ya Mfumu

43 Patatha masiku awiri Iye anachoka napita ku Galileya. 44 (Tsopano Yesu mwini ananena kale kuti mneneri salandira ulemu mʼdziko lake). 45 Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.

46 Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo. 47 Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.

48 Yesu anawawuza iwo kuti, “Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira.”

49 Nduna ya mfumuyo inati, “Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe.”

50 Yesu anayankha kuti, “Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo.”

Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka. 51 Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira. 52 Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, “Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri.”

53 Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye, “Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira.

54 Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.