New Testament in a Year
Yesu Ayenda pa Nyanja
22 Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo. 23 Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha. 24 Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.
25 Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja. 26 Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.
27 Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.”
28 Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”
29 Iye anati, “Bwera.”
Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu. 30 Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”
31 Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”
32 Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka. 33 Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”
34 Atawoloka, anafika ku Genesareti. 35 Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye. 36 Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.