Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Mateyu 5:27-48

Zokhudza Chigololo

27 “Munamva kuti kunanenedwa kuti, ‘Usachite chigololo.’ 28 Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake. 29 Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. 30 Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.

Zokhudza Kusudzula Mkazi

31 “Ananena kuti, ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenera amupatse kalata ya chisudzulo.’ 32 Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.

Malonjezo

33 “Munamvanso kuti kunanenedwa kwa anthu akale kuti, ‘Musaphwanye lonjezo; koma sungani malonjezo anu amene mwachita kwa Yehova.’ 34 Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu. 35 Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu. 36 Ndipo musalumbire ndi mutu wanu chifukwa simungathe kuyeretsa ngakhale kudetsa tsitsi limodzi. 37 Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.

Za Kubwezera Choyipa

38 “Munamva kuti, ‘Diso kulipira diso ndi dzino kulipira dzino.’ 39 Koma ndikuwuzani kuti musamukanize munthu woyipa, akakumenya patsaya mupatseni tsaya linalo. 40 Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako. 41 Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri. 42 Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.

Kukonda Adani

43 “Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’ 44 Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani 45 kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’ 46 Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi? 47 Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi? 48 Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.