M’Cheyne Bible Reading Plan
Konda Yehova Mulungu Wako
6 Awa ndi malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene Yehova Mulungu wanu anandilamula kuti ndikuphunzitseni kuti mukawatsatire mʼdziko limene mukuwolokera Yorodani kuti mukalitenge, 2 kuti inuyo, ana anu, ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo mudzaope Yehova Mulungu wanu moyo wanu wonse posunga malangizo ndi malamulo ake onse amene ndinakupatsani inu kuti musangalale ndi moyo wautali. 3 Mvera Israeli ndipo usamalitse kuchita malamulowa kuti zinthu zikuyendere bwino mʼdziko ndi kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.
4 Tamvani inu Aisraeli, Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi. 5 Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse. 6 Malamulo amene ndakupatsani lero ayenera kukhala mu mtima mwanu. 7 Muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu. Muzikamba za malamulowa pamene muli mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mukugona ndi pamene mukudzuka. 8 Muwamange ngati zizindikiro pa manja anu ndi kuwamangirira pa zipumi zanu. 9 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.
10 Pamene Yehova Mulungu wanu akukulowetsani ndi kukupatsani dziko limene analumbirira makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo, dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu imene inu simunamange, 11 nyumba zodzaza ndi zinthu za mitundu yonse zimene inu simunayikemo, zitsime zimene inu simunakumbe, minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi zimene inuyo simunadzale, tsono mukadya ndi kukhuta, 12 samalani kuti mungayiwale Yehova amene anakutulutsani ku Igupto, kukuchotsani mu ukapolo.
13 Muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iye yekha, ndipo muzilumbira pa dzina lake. 14 Musamatsatire milungu ina, milungu ya anthu ena okuzungulirani, 15 pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu, ndi Mulungu wansanje ndipo adzakukwiyirani kwambiri ndi kukuwonongani, kukufafanizani mʼdziko. 16 Musamuyese Yehova Mulungu wanu monga munachitira ku Masa. 17 Onetsetsani kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, malangizo ake ndi zikhazikitso zake zimene anakulamulirani. 18 Chitani zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova, kuti zikuyendereni bwino ndi kuti mukhoza kukalowa ndi kulanda dziko labwinolo limene Yehova analonjeza molumbira kwa makolo anu, 19 kupirikitsiratu adani anu onse, monga Yehova wanenera.
20 Mʼtsogolo muno, ana anu akadzakufunsani kuti, “Kodi tanthauzo la ndondomeko, malangizo, zikhazikitso ndi malamulo amene Yehova Mulungu wathu anakulamulani nʼchiyani?” 21 Inu mudzawawuze kuti, “Ife tinali akapolo a Farao ku Igupto, koma Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lamphamvu. 22 Ifeyo tikuona Yehova anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa, zazikulu ndi zoopsa, pa Aigupto ndi Farao pamodzi ndi banja lake lonse. 23 Koma anatitulutsa kumeneko ndi kutilowetsa kuno natipatsa dziko limene analonjeza mwa lumbiro kwa makolo athu. 24 Yehova anatilamula kuti tizimvera malamulo onsewa, kuti tizimuopa kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu monga momwe zilili leromu. 25 Ndipo ngati tisamala kumvera malamulo onsewa pamaso pa Yehova Mulungu wathu monga momwe anatilamulira ife, chimenecho chidzakhala chilungamo chathu.”
Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara.
89 Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya;
ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.
2 Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya,
kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.
3 Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga,
ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
4 ‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya.
Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ”
Sela.
5 Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova,
kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.
6 Pakuti ndani mu mlengalenga angalingane ndi Yehova?
Ndani wofanana ndi Yehova pakati pa zolengedwa zakumwamba?
7 Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri;
Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.
8 Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu?
Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.
9 Mumalamula nyanja ya mafunde awukali;
pamene mafunde ake awundana Inu mumawakhalitsa bata.
10 Munaphwanya Rahabe monga munthu wophedwa;
ndi dzanja lanu lamphamvu munabalalitsa adani anu.
11 Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu;
munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.
12 Munalenga Kumpoto ndi Kummwera;
Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.
13 Mkono wanu ndi wamphamvu;
dzanja lanu ndi lamphamvu, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
14 Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu;
chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.
15 Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu,
amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova.
16 Amakondwera mʼdzina lanu tsiku lonse lathunthu;
amasangalala koposa mʼchilungamo chanu.
17 Pakuti Inu ndiye ulemerero wawo ndi mphamvu yawo
ndipo mwa kukoma mtima kwanu Inu mumakweza nyanga yathu.
18 Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova,
Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.
19 Kale munayankhula mʼmasomphenya,
kwa anthu anu okhulupirika munati,
“Ndapatsa mphamvu wankhondo;
ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.
20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’
27 Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa;
wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.
28 Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya,
ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.
29 Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya,
mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.
30 “Ngati ana ake adzataya lamulo langa
ndi kusatsatira malangizo anga,
31 ngati adzaswa malamulo anga
ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,
32 Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo,
mphulupulu zawo powakwapula.
33 Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye,
kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.
34 Sindidzaswa pangano langa
kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.
35 Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga
ndipo sindidzanama kwa Davide,
36 kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya
ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;
37 udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi,
mboni yokhulupirika mʼmitambo.
Sela
38 “Koma tsopano Inu mwamukana, mwamutaya,
mwamukwiyira kwambiri wodzozedwa wanu.
39 Mwakana pangano ndi mtumiki wanu
ndipo mwadetsa mʼfumbi chipewa chake chaufumu.
40 Inu mwagumula makoma ake onse
ndipo mwasandutsa bwinja malinga ake.
41 Onse amene amadutsa amalanda zinthu zake;
iye wakhala chotonzedwa cha anansi ake.
42 Mwakweza dzanja lamanja la adani ake;
mwachititsa kuti adani ake akondwere.
43 Mwabunthitsa lupanga lake,
simunamuthandize pa nkhondo.
44 Inu mwathetsa kukongola kwa ulemerero wake
ndipo mwagwetsa pansi mpando wake waufumu.
45 Mwachepetsa masiku a unyamata wake;
mwamuphimba ndi chofunda chochititsa manyazi.
Sela
46 “Mpaka liti Yehova? Kodi mudzadzibisa mpaka kalekale?
Mpaka liti ukali wanu udzayaka ngati moto?
47 Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa
pakuti munalenga kwachabe anthu onse!
48 Kodi ndi munthu uti angakhale ndi moyo ndi kusaona imfa?
Kapena kudzipulumutsa yekha ku mphamvu ya manda?
Sela
49 Inu Ambuye kodi chili kuti chikondi chanu chachikulu choyamba chija,
chimene mwa kukhulupirika kwanu munalumbira kwa Davide?
50 Kumbukirani, Ambuye momwe mtumiki wanu wanyozedwera,
momwe ndakhalira ndi kusunga mu mtima mwanga mawu a pangano a anthu a mitundu yonse,
51 mawu achipongwe amene adani anu akhala akunyoza, Inu Yehova,
ndi mawu amene akhala akunyoza mayendedwe onse a wodzozedwa wanu.
52 “Matamando akhale kwa Yehova mpaka muyaya!”
Ameni ndi Ameni.
Chiweruzo cha Anthu a Mitundu Yonse
34 Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve:
tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse:
Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!
2 Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse;
wapsera mtima magulu awo onse ankhondo.
Iye adzawawononga kotheratu,
nawapereka kuti aphedwe.
3 Anthu awo ophedwa adzatayidwa kunja,
mitembo yawo idzawola ndi kununkha;
mapiri adzafiira ndi magazi awo.
4 Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka
ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala;
nyenyezi zonse zidzayoyoka
ngati masamba ofota a mphesa,
ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.
5 Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba;
taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu,
anthu amene ndawawononga kotheratu.”
6 Lupanga la Yehova lakhuta magazi,
lakutidwa ndi mafuta;
magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi,
mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna.
Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira
ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.
7 Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati,
ngʼombe zazimuna zazingʼono ndi zazikulu zomwe.
Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha,
ndipo nthaka idzakutidwa ndi mafuta.
8 Iyi ndi nthawi imene Yehova adzalipsira
ndi kulanga adani a Ziyoni.
9 Madzi a mʼmitsinje ya Edomu adzasanduka phula,
ndipo fumbi lake lidzasanduka sulufule;
dziko lake lidzasanduka phula lamoto!
10 Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana;
utsi wake udzafuka kosalekeza.
Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado;
palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.
11 Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu;
amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo.
Mulungu adzatambalitsa pa Edomu
chingwe choyezera cha chisokonezo
ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.
12 Anthu olemekezeka ake sadzatchedwanso mfumu kumeneko;
akalonga ake onse adzachotsedwa.
13 Minga idzamera mʼnyumba zake zankhondo zotetezedwa,
khwisa ndi mitungwi zidzamera mʼmalinga ake.
Ankhandwe azidzadya mʼmenemo;
malo okhalamo akadzidzi.
14 Avumbwe adzakumana ndi afisi,
ndipo zirombo za mʼchipululu zizidzayitanizana.
Kumeneko kudzafikanso mizimu yoyipa
ndi kupeza malo opumulirako.
15 Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira,
adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake;
akamtema adzasonkhananso kumeneko,
awiriawiri.
16 Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga:
mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa;
sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake.
Pakuti Yehova walamula kuti zitero,
ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.
17 Yehova wagawa dziko lawo;
wapatsa chilichonse chigawo chake.
Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya
ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.
Mapembedzedwe a Kumpando Waufumu Kumwamba
4 Kenaka, nditayangʼana patsogolo panga ndinaona khomo lotsekuka la kumwamba. Ndipo liwu lija ndinalimva poyamba lokhala ngati lipenga linati, “Bwera kuno, ndipo ndidzakuonetsa zimene zichitike zikatha izi.” 2 Nthawi yomweyo ndinatengedwa ndi Mzimu Woyera, ndipo patsogolo panga ndinaona mpando waufumu wina atakhalapo. 3 Ndipo amene anakhalapoyo anali wa maonekedwe ngati miyala ya jasipa ndi sardiyo. Utawaleza wooneka ngati simaragido unazinga mpando waufumuwo. 4 Kuzungulira mpando waufumuwu panalinso mipando ina yaufumu yokwana 24 ndipo panakhala akuluakulu 24 atavala zoyera ndipo anavala zipewa zaufumu zagolide pamutu. 5 Kumpando waufumuwo kunkatuluka mphenzi, phokoso ndi mabingu. Patsogolo pake pa mpando waufumuwo panali nyale zisanu ndi ziwiri zoyaka. Iyi ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu. 6 Patsogolo pa mpando waufumu pomwepo panalinso ngati nyanja yagalasi yonyezimira ngati mwala wa krustalo.
Pakatinʼpakati, kuzungulira mpando waufumuwo panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ponseponse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. 7 Chamoyo choyamba chinali ngati mkango, chachiwiri chinali ngati mwana wangʼombe, chachitatu chinali ndi nkhope ngati munthu, chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chowuluka. 8 Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo chinali ndi maso ponseponse ndi mʼkati mwa mapiko momwe. Usana ndi usiku zimanena mosalekeza kuti,
“Woyera, woyera, woyera
ndi Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,
amene munali, amene muli ndi amene mukubwera.”
9 Nthawi zonse zamoyozo zimapereka ulemerero, ulemu ndi mayamiko kwa uja wokhala pa mpando waufumu, amene ali ndi moyo wamuyaya. 10 Izi zikamachitika akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pansi pamaso pa wokhala pa mpando waufumuyo, namupembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Iwo amaponya pansi zipewa zawo zaufumu patsogolo pa mpando waufumu nati:
11 “Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu,
Ambuye ndi Mulungu wathu,
pakuti munalenga zinthu zonse,
ndipo mwakufuna kwanu
zinalengedwa monga zilili.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.