Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yoswa 1

Yehova Asankha Yoswa Kukhala Mtsogoleri

Atamwalira Mose mtumiki wa Mulungu, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mthandizi wa Mose: “Mose mtumiki wanga wamwalira. Ndipo iwe ndi anthu onsewa, tsopano konzekani kuwoloka mtsinje wa Yorodani kupita ku dziko limene ndiwapatse Aisraeli onse. Paliponse pamene phazi lanu liponde, ndikupatsani monga momwe ndinalonjezera Mose. Dziko lanu lidzayambira ku chipululu kummwera mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kummawa, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yayikulu ya kumadzulo. Palibe munthu amene adzatha kukugonjetsa masiku onse a moyo wako. Monga Ine ndinakhalira ndi Mose, chomwechonso ndidzakhala nawe. Sindidzakusiya kapena kukataya.

“Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima, chifukwa iwe udzatsogolera anthu awa kukalandira dziko limene Ine ndinalonjeza makolo awo kuti ndidzawapatsa. Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti umvere malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakupatsa. Usachoke pa malamulo anga ndipo kulikonse kumene udzapite udzapambana. Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana. Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

10 Tsono Yoswa analamula atsogoleri a Aisraeli nawawuza kuti, 11 “Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’ ”

12 Koma Yoswa anawuza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti, 13 “Kumbukirani zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani kuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndi dziko ili kuti likhale lanu.’ 14 Tsono akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu zitsale mʼdziko lino limene Mose anakupatsani kummawa kwa Yorodani. Koma ankhondo anu okha ndiwo awoloke atatenga zida zawo ndi kupita patsogolo pa abale anu kukawathandiza. 15 Abale anuwo akadzalandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa monga inu mwachitira, inu mudzabwerera kudzakhazikika mʼdziko lanu limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya la kummawa kwa Yorodani.”

16 Kenaka iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife tidzachita chilichonse chimene mwatilamula, ndipo kulikonse kumene mudzatitume tidzapita. 17 Monga momwe tinamvera Mose kwathunthu, chomwechonso tidzakumvera iwe. Yehova Mulungu wanu akhale nanu monga momwe anachitira ndi Mose. 18 Aliyense wotsutsana ndi inu kapena wosamvera zimene mutilamula adzaphedwa. Inu mukhale wamphamvu ndi wolimba mtima!”

Masalimo 120-122

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

120 Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga,
    ndipo Iye amandiyankha.
Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza,
    ndi kwa anthu achinyengo.

Kodi adzakuchitani chiyani,
    ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?
Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo,
    ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.

Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki,
    kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!
Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati
    pa iwo amene amadana ndi mtendere.
Ine ndine munthu wamtendere;
    koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

121 Ndikweza maso anga ku mapiri;
    kodi thandizo langa limachokera kuti?
Thandizo langa limachokera kwa Yehova,
    wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Sadzalola kuti phazi lako literereke;
    Iye amene amakusunga sadzawodzera.
Taonani, Iye amene amasunga Israeli
    sadzawodzera kapena kugona.

Yehova ndiye amene amakusunga;
    Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja.
Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana,
    kapena mwezi nthawi ya usiku.

Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse;
    adzasunga moyo wako.
Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako;
    kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

122 Ndinakondwera atandiwuza kuti,
    “Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”
Mapazi athu akuyima mʼzipata
    zako, Iwe Yerusalemu.

Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda
    umene uli wothithikana pamodzi.
Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko,
    mafuko a Yehova,
umboni wa kwa Israeli,
    kuti atamande dzina la Yehova.
Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo,
    mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.

Pemphererani mtendere wa Yerusalemu:
    “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.
Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako,
    ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.”
Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga
    ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.”
Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu,
    ndidzakufunira zabwino.

Yesaya 61

Uthenga Wabwino wa Yehova

61 Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,
    chifukwa Yehova wandidzoza
    kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.
Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,
    ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu
    ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;
    za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.
Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
    Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,
nkhata ya maluwa yokongola
    mʼmalo mwa phulusa,
ndiwapatse mafuta achikondwerero
    mʼmalo mwa kulira.
Ndiwapatse chovala cha matamando
    mʼmalo mwa mtima wopsinjika.
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,
    yoyidzala Yehova
    kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.

Adzamanganso mabwinja akale a mzinda
    ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso.
Adzakonzanso mizinda imene inapasuka,
    imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.
Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu;
    iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.
Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova,
    adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu.
Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu,
    ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.

Chifukwa manyazi awo anali owirikiza;
    ndi kuti munalandira
chitonzo ndi kutukwana,
    adzakondwera ndi cholowa chawo,
tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza,
    ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.

“Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo;
    ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa.
Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika
    ndikupangana nawo pangano losatha.
Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu
    ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina.
Aliyense wowaona adzazindikira
    kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”

10 Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;
    moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.
Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,
    ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.
Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,
    ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.
11 Monga momwe nthaka imameretsa mbewu
    ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala,
momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando
    pamaso pa mitundu yonse ya anthu.

Mateyu 9

Munthu Wakufa Ziwalo wa ku Kaperenawo

Yesu analowa mʼbwato nawoloka, ndipo anabwera ku mudzi wa kwawo. Amuna ena anabwera ndi munthu wakufa ziwalo kwa Iye atamugoneka pa mphasa. Yesu ataona chikhulupiriro chawo anati kwa wakufa ziwaloyo, “Limba mtima mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”

Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.”

Ndipo podziwa maganizo awo Yesu anati, “Bwanji mukuganiza zoyipa mʼmitima mwanu? Chapafupi ndi chiti kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa’ kapena kunena kuti, ‘Imirira ndipo yenda?’ Tsono kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko wokhululuka machimo, pamenepo anati kwa wakufa ziwaloyo, ‘Imirira, tenga mphasa yako kazipita kwanu.’ ” Ndipo munthuyo anayimirira napita kwawo. Gulu la anthu litaona izi, linadzazidwa ndi mantha ndipo linalemekeza Mulungu amene anapereka ulamuliro kwa anthu.

Kuyitanidwa kwa Mateyu

Ndipo Yesu atachoka kumeneko, anaona munthu wina dzina lake Mateyu, atakhala mʼnyumba ya msonkho. Anati kwa iye, “Nditsate Ine.” Ndipo iye ananyamuka namutsata.

10 Ndipo pamene Iye ankadya mʼnyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anabwera nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11 Ndipo Afarisi poona izi, anati kwa ophunzira ake, “Nʼchifukwa chiyani Aphunzitsi anu akudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”

12 Yesu atamva, anati, “Munthu wamoyo safuna singʼanga ayi, koma wodwala. 13 Koma pitani kaphunzireni tanthauzo la mawu awa: ‘Ndimafuna chifundo osati nsembe ayi.’ Pakuti sindinabwere kudzayitana olungama koma ochimwa.”

Za Kusala Kudya

14 Ndipo ophunzira a Yohane anabwera namufunsa Iye kuti, “Bwanji ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”

15 Yesu anayankha kuti, “Kodi oyitanidwa ku ukwati angamalire bwanji pamene mkwati ali naye pamodzi? Nthawi idzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa ndi pamene adzasala kudya.”

16 Ndipo palibe munthu amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale chifukwa chigambacho chidzachoka ndipo chibowocho chidzakula kuposa kale. 17 Kapena sathira vinyo watsopano mʼmatumba akale; akatero, matumba akalewo adzaphulika ndipo vinyoyo adzatayika, matumbawo adzawonongeka; satero ayi. Amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso ndipo zonse zimasungika.

Za Mwana Wamkazi wa Yairo ndi Mayi Wokhudza Chovala cha Yesu

18 Pamene ankanena zimenezi, mkulu wa sunagoge anabwera namugwadira Iye nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira posachedwapa koma tiyeni mukasanjike dzanja lanu pa iye ndipo adzakhala ndi moyo.” 19 Yesu ndi ophunzira ake ananyamuka napita naye pamodzi.

20 Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake. 21 Iyeyo anati mwa iye yekha, “Nditangokhudza kasonga ka mkanjo wake, ine ndidzachiritsidwa.”

22 Ndipo Yesu anatembenuka namuona mayiyo nati, “Limbani mtima mayi iwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthawi yomweyo mayiyo anachiritsidwa.

23 Yesu atalowa mʼnyumba ya mkulu wa sunagoge ndi kuona oyimba zitoliro ndi gulu la anthu ochita phokoso, 24 anati, “Tulukani, mtsikanayu sanafe koma ali mtulo.” Koma anamuseka Iye. 25 Atangowatulutsa anthuwo, analowa mʼnyumba ndipo anagwira dzanja la mtsikanayo ndipo anauka. 26 Mbiriyi inamveka mʼdera lonse.

Yesu Achiritsa Osaona ndi Osayankhula

27 Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!”

28 Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?”

Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.”

29 Pomwepo anakhudza maso awo nati, “Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.” 30 Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, “Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi.” 31 Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse.

32 Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula. 33 Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, “Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli.”

34 Koma Afarisi anati, “Akutulutsa mizimu yoyipa ndi mphamvu ya mkulu wa ziwanda.”

Antchito ndi Ochepa

35 Yesu anayendayenda mʼmizinda yonse ndi mʼmidzi, kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa nthenda zawo zonse ndi zofowoka za mʼmatupi mwawo. 36 Ataona maguluwo, anagwidwa ndi chisoni chifukwa anali ozunzika ndi osowa chithandizo ngati nkhosa zopanda mʼbusa. 37 Pamenepo anati kwa ophunzira ake, “Zokolola ndi zambiri koma antchito ndi ochepa. 38 Nʼchifukwa chake, pemphani Ambuye mwini zokolola kuti atumize antchito ku munda wake.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.