Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 29

Kukonzanso Pangano

29 Awa ndiwo mawu a mʼpangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi Aisraeli ku Mowabu, powonjezera pa pangano limene anapangana nawo ku Horebu.

Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati kwa iwo:

Inu munaona zonse zimene Yehova anachita kwa Farao, nduna zake ndi dziko lake lonse ku Igupto. Ndi maso anu munaona mayesero onse aja, zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zazikulu zija. Koma mpaka lero Yehova sanakupatseni mtima wozindikira kapena maso openya kapena makutu akumva. Mʼzaka makumi anayi zimene ndinakutsogolerani mʼchipululu, zovala zanu ndiponso nsapato za ku mapazi anu sizinangʼambike. Inu simunadye buledi ndi kumwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa. Ndinachita izi kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Pamene munafika malo ano, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni ndi Ogi mfumu ya ku Basani anabwera kudzamenyana nafe koma tinawagonjetsa iwo. Tinatenga dziko lawo ndi kulipereka ngati cholowa cha fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase.

Tsatirani mosamalitsa mawu a mʼpangano ili kuti zinthu zizikuyenderani bwino pa zochitika zanu zonse. 10 Lero lino nonse mukuyima pamaso pa Yehova Mulungu wanu, atsogoleri a mafuko anu, akuluakulu ndi nduna zanu, ndi amuna ena onse a mu Israeli, 11 pamodzi ndi ana ndi akazi anu, kudzanso alendo amene akukhala pakati panu omwe amakuwazirani nkhuni ndi kukutungirani madzi. 12 Mukuyimirira pano kuti mulowe mʼpangano ndi Yehova Mulungu wanu, pangano limene Yehova akuchita ndi inu lero ndi kulisindikiza ndi malumbiro, 13 kukukhazikitsani lero lino ngati anthu ake, ndi kuti Iye akhale Mulungu wanu monga anakulonjezani inu ndiponso monga analumbira kwa makolo anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 14 Ndikupanga pangano ili ndi malumbiro ake osati kwa inu nokha, 15 amene muli pano pamaso pa Yehova Mulungu wathu, koma ndi iwonso amene sali pano lero.

16 Inu nomwe mukudziwa mmene tinkakhalira ku Igupto ndi mmene tinadutsira mayiko pa ulendo wobwera kuno. 17 Ife tinaona pakati pawo mafanizo ndi mafano awo onyansa, amtengo ndi amiyala, asiliva ndi agolide. 18 Onetsetsani kuti pasapezeke mwamuna kapena mkazi, banja kapena fuko pakati panu lero amene mtima wawo udzapandukira Yehova Mulungu wanu ndi kupita kukapembedza milungu ya mitundu iyo. Onetsetsani kuti pasapezeke muzu pakati panu wotulutsa mankhwala akupha otere.

19 Munthu wotere akamva mawu a lumbiro ili, asadzidalitse yekha mʼmaganizo mwake namati, “Ine ndidzapulumuka ngakhale nditapitiriza kuyenda njira yanga.” Zoterezi zidzadzetsa masautso pa nthaka ya chinyontho ndi yowuma yomwe. 20 Yehova sadzamukhululukira. Mkwiyo ndi nsanje ya Yehova zidzamuyakira munthuyo. Matemberero onse wolembedwa mʼbukuli adzamugwera iye ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pa dziko lapansi. 21 Yehova adzasankha pakati pa Aisraeli anthu oyenera masautso monga mwa matemberero onse a mʼpangano olembedwa Mʼbuku la Malamulo.

22 Ana anu a mibado yakutsogolo ndi alendo amene adzachokera kutali adzaona matsoka amene adzakugwerani mʼdziko muno ndiponso matenda amene Yehova adzabweretsa pa dzikoli. 23 Dziko lonse lidzasanduka nthaka ya mchere ndi ya sulufule. Simudzadzalamo kanthu, simudzakhala chomera chilichonse, ndi mbewu yomera mʼmenemo. Dziko lanu lidzakhala lowonongeka ngati Sodomu ndi Gomora, Adima ndi Zeboimu, mizinda imene Yehova anayiwononga ndi mkwiyo wake waukulu. 24 Mitundu yonse ya anthu idzafunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani Yehova anachita zotere mʼdziko lake? Kodi chifukwa chiyani anaonetsa mkwiyo woopsa wotere?”

25 Ndipo yankho la mafunso amenewa lidzakhala lakuti, “Chifukwa chakuti anthu awa aphwanya pangano la Yehova Mulungu wa makolo awo, pangano limene Iye anapangana nawo pamene anawatulutsa ku Igupto. 26 Iwo anachoka ndi kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, milungu imene sanayidziwe, milungu imene sanawapatse. 27 Choncho Yehova anakwiyira dziko lino, kotero anabweretsa matemberero onse amene analembedwa mʼbuku lino. 28 Ndi mkwiyo komanso ukali wake woopsa Yehova anawazula mʼdziko lawo ndi kuwaponyera mʼdziko lina, monga mmene zilili lero lino.”

29 Zinsinsi ndi za Yehova Mulungu wathu koma zinthu zimene zaululidwa ndi zathu ndi ana athu kwamuyaya, kuti titsatire mawu onse a mʼmalamulowa.

Masalimo 119:49-72

Zayini

49 Kumbukirani mawu anu kwa mtumiki wanu,
    popeza mwandipatsa chiyembekezo.
50 Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi:
    lonjezo lanu limasunga moyo wanga.
51 Odzikuza amandinyoza popanda chowaletsa,
    koma sindichoka pa malamulo anu.
52 Ndimakumbukira malamulo anu Yehova akalekale,
    ndipo mwa iwo ndimapeza chitonthozo.
53 Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa
    amene ataya malamulo anu.
54 Zophunzitsa zanu ndi mitu ya nyimbo yanga
    kulikonse kumene ndigonako.
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu Yehova,
    ndipo ndidzasunga malamulo anu.
56 Ichi ndicho ndakhala ndikuchita:
    ndimasunga malangizo anu.

Heti

57 Yehova, Inu ndiye gawo langa;
    ndalonjeza kumvera mawu anu.
58 Ndimafunafuna nkhope yanu ndi mtima wanga wonse;
    mundikomere mtima monga mwa lonjezo lanu.
59 Ndinalingalira za njira zanga
    ndipo ndatembenuza mayendedwe anga kutsatira umboni wanu.
60 Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza
    kumvera malamulo anu.
61 Ngakhale oyipa andimange ndi zingwe,
    sindidzayiwala lamulo lanu.
62 Ndimadzuka pakati pa usiku kuyamika Inu
    chifukwa cha malamulo anu olungama.
63 Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani,
    kwa onse amene amatsatira malangizo anu.
64 Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chanu chosasinthika,
    phunzitseni malamulo anu.

Teti

65 Inu Yehova, chitirani chabwino mtumiki wanu
    molingana ndi mawu anu.
66 Phunzitseni nzeru ndi chiweruzo chabwino,
    pakuti ndimakhulupirira malamulo anu.
67 Ndisanayambe kuzunzika ndinasochera,
    koma tsopano ndimamvera mawu anu.
68 Inu ndinu abwino ndipo zimene mumachita ndi zabwino;
    phunzitseni malamulo anu.
69 Ngakhale odzikuza andipaka mabodza,
    ine ndimasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.
70 Mitima yawo ndi yowuma ndi yosakhudzidwa,
    koma ine ndimakondwera ndi malamulo anu.
71 Ndi bwino kuti ndinasautsidwa
    kuti ndithe kuphunzira malamulo anu.
72 Lamulo lochokera mʼkamwa mwanu limandikomera kwambiri
    kuposa ndalama zambirimbiri za siliva ndi golide.

Yesaya 56

Chipulumutso kwa Anthu Ena Onse

56 Yehova akuti,

“Chitani chilungamo
    ndi zinthu zabwino,
chifukwa chipulumutso changa chili pafupi
    ndipo ndidzakuwombolani posachedwapa.
Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi,
    munthu amene amalimbika kuzichita,
amene amasunga Sabata osaliyipitsa,
    ndipo amadziletsa kuchita zoyipa.”

Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti,
    “Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake.”
Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti,
    “Ine ndine mtengo wowuma basi.”

Popeza Yehova akuti,

“Wofulidwa amene amasunga masabata anga,
    nachita zokomera Ine
    ndi kusunga pangano langa,
ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino
    mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake,
    kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi.
Ndidzawapatsa dzina labwino,
    losatha ndi losayiwalika.”
Yehova akuti, “Alendo amene amadziphatika kwa Yehova,
    motero kuti amamutumikira Iye,
amakonda dzina la Yehova,
    amamugwirira ntchito,
komanso kusunga Sabata osaliyipitsa
    ndi kusunga bwino pangano langa,
amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika,
    ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero.
Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo
    ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe.
Paja nyumba yanga idzatchedwa
    nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse.”
Ambuye Yehova, amene amasonkhanitsa
    Aisraeli onse ali ku ukapolo akunena kuti,
“Ndidzasonkhanitsano anthu ena
    kuwonjezera amene anasonkhana kale.”

Mulungu Adzazula Anthu Oyipa

Bwerani, inu zirombo zonse zakuthengo,
    inu nonse zirombo zamʼnkhalango bwerani mudzadye!
10 Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu,
    onse ndi opanda nzeru;
onse ndi agalu opanda mawu,
    samatha kuwuwa:
amagona pansi nʼkumalota
    amakonda kugona tulo.
11 Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu;
    sakhuta konse.
Abusa nawonso samvetsa zinthu;
    onse amachita monga akufunira,
    aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.
12 Aliyense amafuwulira mnzake kuti, “Bwera, tiye timwe vinyo!
    Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta!
Mawa lidzakhala ngati leroli,
    kapena kuposa lero lino.”

Mateyu 4

Yesu Ayesedwa Mʼchipululu

Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala. Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”

Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”

Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa:

“ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe,
    ndipo adzakunyamula ndi manja awo
    kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”

Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”

Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo. Ndipo anati kwa Iye, “Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine.”

10 Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”

11 Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.

Yesu Ayamba Kulalikira

12 Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya. 13 Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali; 14 pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,

15 “Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,
    njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani,
    Galileya wa anthu a mitundu ina,
16 anthu okhala mu mdima
    awona kuwala kwakukulu;
ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa
    kuwunika kwawafikira.”

17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”

Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba

18 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi. 19 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.

21 Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana. 22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.

Yesu Achiritsa Odwala

23 Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu. 24 Mbiri yake yonse inawanda ku Siriya konse ndipo anthu anabweretsa kwa Iye onse amene anali odwala nthenda zosiyanasiyana, womva maululu aakulu, ogwidwa ndi ziwanda, odwala matenda akugwa ndi olumala ndipo Iye anawachiritsa. 25 Magulu ambiri a anthu anachokera ku Galileya, Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya ndi ku madera a kutsidya la mtsinje wa Yorodani namutsata Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.