Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 28:20-68

20 Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi minyozo pa chilichonse chimene mudzachichita mpaka mudzawonongedwa ndi kukhala bwinja mofulumira chifukwa cha zoyipa zimene mwazichita pa kumutaya Yehova. 21 Yehova adzakugwetserani mliri wa matenda mpaka atakuwonongani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali. 22 Yehova adzakukanthani ndi nthenda yowondetsa, ya malungo ndi ya zotupatupa, ndi kutentha kwakukulu ndi chilala, ndi chinsikwi ndi chiwawu zimene zidzakusautsani mpaka mutawonongeka. 23 Mitambo ya pamutu panu idzawuma ngati mkuwa ndipo sidzagwetsa mvula mpaka nthaka yanu idzawuma gwaa ngati chitsulo. 24 Mʼmalo mwa mvula Yehova adzakupatsani fumbi ndi dothi ndipo lidzakugwerani kuchokera kumwamba mpaka mutawonongeka.

25 Yehova adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Mudzadzera njira imodzi pokalimbana ndi adani anu koma pothawa mudzabalalika mbali zisanu ndi ziwiri. Mudzakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. 26 Mitembo yanu idzadyedwa ndi mbalame zamumlengalenga ndi nyama zakutchire, ndipo palibe amene adzaziyingitse. 27 Yehova adzakusautsani ndi zithupsa za ku Igupto ndi zotupatupa, zipere, ndi mphere zimene simudzachiritsika nazo. 28 Yehova adzakusautsani inu ndi misala, khungu ndi chisokonekero cha maganizo. 29 Masanasana mudzayenda ngati muli mu mdima, kumafufuzira njira ngati wosaona. Mudzakhala olephera pa chilichonse mungachite. Tsiku ndi tsiku mudzaponderezedwa ndi kuberedwa wopanda wokupulumutsani.

30 Mudzachita chinkhoswe ndi mkazi, koma wina adzakulandani ndi kumukwatira. Mudzamanga nyumba koma simudzagonamo. Mudzalima munda wamphesa koma simudzadyako zipatso zake. 31 Ngʼombe yanu yamtheno idzaphedwa inu muli pomwepo koma simudzadyako. Bulu wanu adzalandidwa kwa inu mwamakani osabwera nayenso. Nkhosa zanu zidzapatsidwa kwa adani anu, ndipo palibe amene adzazipulumutsa. 32 Ana anu aamuna ndi aakazi adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina ndipo inu mudzafika potopa ndi kulefuka nʼkudikirira tsiku ndi tsiku kuti mwina anawo abwerako. 33 Anthu amene simukuwadziwa adzakudyerani zokolola zanu, ndipo mudzakhala mukuponderezedwa mwankhanza masiku onse. 34 Zimene muzidzaziona zidzakusokonezani mitu. 35 Yehova adzakusautsani ndi zithupsa zaululu ndi zosachiritsika za mʼmawondo ndi mʼmiyendo ndipo zidzafalikira kuchoka kuphazi mpaka kumutu.

36 Yehova adzakuthamangitsirani, inu ndi mafumu anu amene muwayika, ku dziko losadziwika kwa inu ndi kwa makolo anu. Kumeneko mudzakapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi miyala. 37 Inu mudzakhala chinthu chochititsa mantha kuchisunga ndiponso chinthu chotukwanidwa ndi chonyozeka kwa anthu a mitundu yonse kumene Yehova adzakuthamangitsirani.

38 Mudzadzala mbewu zambiri ku munda koma mudzakolola pangʼono, chifukwa dzombe lidzaziwononga. 39 Mudzadzala mpesa ndi kulimirira koma vinyo wake simudzamumwa kapena kukolola mphesazo, chifukwa mphutsi zidzadya mphesazo. 40 Mudzakhala ndi mitengo ya olivi mʼdziko lanu lonse koma simudzagwiritsa ntchito mafuta ake, chifukwa zipatso zake zidzayoyoka. 41 Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi koma sadzakhala anu, chifukwa adzapita ku ukapolo. 42 Magulumagulu a dzombe adzawononga mitengo yanu ndi mbewu za mʼdziko lanu.

43 Mlendo wokhala pakati panu adzatukuka kuposa inu, koma inuyo mudzaloweralowera pansi. 44 Iye adzakubwereketsani, koma inu simudzatha kubwereketsa. Iye adzakhala mutu ndipo inu mudzakhala mchira.

45 Matemberero onsewa adzabwera pa inu. Adzakulondolani ndi kukugonjetsani mpaka mutawonongeka, chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo ndi malangizo amene anakupatsani. 46 Matemberero amenewa adzakhala chizindikiro ndi chozizwitsa kwa inu ndi zidzukulu zanu mpaka kalekale. 47 Pakuti inu simunatumikire Yehova Mulungu wanu pa nthawi imene zinthu zinkakuyenderani bwino, 48 chomwecho pa nthawi ya njala ndi ludzu, ya maliseche ndi umphawi woopsa, mudzatumikira adani amene Yehova adzakutumizirani. Iye adzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwanu kufikira atakuwonongani.

49 Yehova adzakutumizirani mtundu wa anthu kuchokera kutali kumapeto kwa dziko lapansi nudzachita ngati mphungu yowulukira pansi, mtundu wa anthu umene chiyankhulo chawo simudzachimva, 50 mtundu wooneka wochititsa mantha, wopanda ulemu kwa okalamba kapena chisoni kwa ana. 51 Iwo adzagwira ana a ziweto zanu, natenga zokolola za mʼdziko lanu kufikira mutawonongeka. Iwo sadzakusiyirani tirigu, vinyo watsopano kapena mafuta a olivi, kapena mwana wangʼombe aliyense kapena mwana wankhosa mpaka mutasanduka bwinja. 52 Iwo adzathira nkhondo mizinda yonse mʼdziko lanu lonse mpaka malinga anu ataliatali omwe mumadalira aja atagwa. Adzathira nkhondo mizinda yonse ya mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.

53 Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani. 54 Ngakhale munthu woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu sadzakhala ndi chifundo pa mʼbale wake weniweni kapena mkazi wake amene iye amamukonda kapena ana ake otsalawo, 55 ndipo sadzagawirako aliyense wa iwo mnofu wa ana ake amene akudyawo. Kadzakhala kali komweko basi kamene kamutsalira chifukwa cha msautso umene mdani wanu adzagwetsa pa nthawi yothira nkhondo mizinda yanu yonse. 56 Mayi woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu, uja woti sangayerekeze kuponda pansi, adzabisira mwamuna wake amene amamukonda ndi ana ake omwe aamuna ndi aakazi 57 zotsalira za uchembere zochoka mʼmimba mwake ndi ana amene wabereka. Pakuti adzafuna kuti adye zimenezi yekha mobisa pa nthawi yothiridwa nkhondo chifukwa cha masautso amene mdani wanu adzagwetsa pa inu mʼmizinda yanu.

58 Ngati simutsata mosamalitsa mawu onse a malamulo awa amene alembedwa mʼbuku lino, komanso ngati simuopa dzina la ulemerero ndi loopsa, dzina la Yehova Mulungu wanu, 59 Yehova adzatumiza pa inu ndi zidzukulu zanu miliri yoopsa, zosautsa zowawa ndi zokhalitsa, ndi matenda aakulu ndi ovuta kuchiritsika. 60 Adzakubweretserani matenda onse a ku Igupto aja mumawaopawa ndipo adzakukanirirani. 61 Yehova adzakubweretseraninso mtundu uliwonse wa matenda ndi zosautsa zimene sizinalembedwe mʼbuku la malamulo lino, mpaka mutawonongeka. 62 Inu aja munali ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba mudzatsala ochepa chabe chifukwa simunamvere Yehova Mulungu wanu. 63 Monga kunamukomera Yehova kukulemeretsani ndi kukuchulukitsani, momwemonso kudzamukondweretsa kukunthani ndi kukuwonongani. Inu mudzazulidwa kukuchotsani mʼdziko limene mukulowa kukalitengali.

64 Kenaka Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu yonse, kuchokera ku mapeto a dziko kufika ku mapeto ena. Kumeneko mudzapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi ya miyala, imene inu eni kapena makolo anu sanayidziwepo. 65 Pakati pa mitundu ya anthu imeneyi simudzapeza mpata, popanda malo woti nʼkuyikapo phazi. Kumeneko Yehova adzakupatsani moyo wa nkhawa, maso otopa ndi chiyembekezo, ndi mtima wosakhazikika. 66 Inu mudzakhala osakhazikika mopitirira, odzazidwa ndi mantha usiku ndi usana womwe, osowa chitsimikizo cha pa moyo wanu. 67 Mmawa muzidzati, “Chikhala anali madzulo!” ndipo madzulo mudzati, “Chikhala unali mmawa!” Mudzanena zimenezi chifukwa cha mantha amene adzakhale mu mtima mwanu ndi chifukwa cha zomwe muzidzaziona. 68 Yehova adzakubwezani ku Igupto pa sitima zapamadzi paulendo umene Ine ndinati musawuyendenso. Kumeneko mudzadzitsatsa nokha kwa adani anu monga akapolo aamuna ndi aakazi, koma palibe amene adzakuguleni.

Masalimo 119:25-48

Daleti

25 Moyo wanga wakangamira fumbi;
    tsitsimutseni molingana ndi mawu anu.
26 Ndinafotokoza njira zanga ndipo Inu munandiyankha;
    phunzitseni malamulo anu.
27 Mundidziwitse chiphunzitso cha malangizo anu;
    pamenepo ndidzalingalira zodabwitsa zanu.
28 Moyo wanga wafowoka ndi chisoni;
    limbikitseni monga mwa mawu anu.
29 Mundichotse mʼnjira zachinyengo;
    mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.
30 Ndasankha njira ya choonadi;
    ndayika malamulo anu pa mtima panga.
31 Ndagwiritsitsa umboni wanu, Inu Yehova;
    musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
32 Ndimathamanga mʼnjira ya malamulo anu,
    pakuti Inu mwamasula mtima wanga.

He

33 Yehova, phunzitseni kutsatira zophunzitsa zanu;
    ndipo ndidzazisunga mpaka kumapeto.
34 Mundipatse mtima womvetsa zinthu ndipo ndidzasunga malamulo anu
    ndi kuwamvera ndi mtima wanga wonse.
35 Munditsogolere mʼnjira ya malamulo anu,
    pakuti mʼmenemo ndimapezamo chikondwerero changa.
36 Tembenuzani mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu,
    osati chuma.
37 Tembenuzani maso anga kuchoka ku zinthu zachabechabe;
    sungani moyo wanga monga mwa mawu anu.
38 Kwaniritsani lonjezo lanu kwa mtumiki wanu,
    kuti Inu muopedwe.
39 Mundichotsere chipongwe chimene ndikuchiopa,
    pakuti malamulo anu ndi abwino.
40 Taonani, ndimalakalakatu malangizo anu!
    Sungani moyo wanga mʼchilungamo chanu.

Wawi

41 Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova,
    chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;
42 ndipo ndidzayankha amene amandinyoza,
    popeza ndimadalira mawu anu.
43 Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga,
    pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.
44 Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse,
    ku nthawi za nthawi.
45 Ndidzayendayenda mwaufulu,
    chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.
46 Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu
    ndipo sindidzachititsidwa manyazi,
47 popeza ndimakondwera ndi malamulo anu
    chifukwa ndimawakonda.
48 Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda,
    ndipo ndimalingalira malangizo anu.

Yesaya 55

Kuyitanidwa kwa Womva Ludzu

55 “Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu,
    bwerani madzi alipo;
ndipo inu amene mulibe ndalama
    bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye!
Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka
    osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya,
    ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa?
Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino;
    ndipo mudzisangalatse.
Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine;
    mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo.
Ndidzachita nanu pangano losatha,
    chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.
Taonani, ine ndamusankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu,
    kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira mitundu ya anthu.
Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa,
    ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu.
Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu,
    Woyerayo wa Israeli,
    wakuvekani ulemerero.”

Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka.
    Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.
Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa,
    ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa.
Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo,
    ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.

“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu,
    ngakhale njira zanu si njira zanga,”
            akutero Yehova.
“Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi,
    momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu,
    ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
10 Monga mvula ndi chisanu chowundana
    zimatsika kuchokera kumwamba,
ndipo sizibwerera komweko
    koma zimathirira dziko lapansi.
Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera
    kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.
11 Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga.
    Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake,
koma adzachita zonse zimene ndifuna,
    ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.
12 Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe
    ndipo adzakutsogolerani mwamtendere;
mapiri ndi zitunda
    zidzakuyimbirani nyimbo,
ndipo mitengo yonse yamʼthengo
    idzakuwombereni mʼmanja.
13 Mʼmalo mʼmene tsopano muli mitengo ya minga mudzamera mitengo ya payini,
    ndipo kumene kuli mkandankhuku kudzamera mchisu.
Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Yehova,
    ngati chizindikiro chamuyaya,
    chimene sichidzafafanizika konse.”

Mateyu 3

Yohane Mʼbatizi

Mʼmasiku amenewo, Yohane Mʼbatizi anadza nalalikira mʼchipululu cha Yudeya kuti, “Tembenukani mtima chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.” Uyu ndi amene mneneri Yesaya ananena za iye kuti,

“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
    wongolani njira zake.’ ”

Zovala za Yohane zinali zopangidwa ndi ubweya wa ngamira, ndipo amamangira lamba wachikopa mʼchiwuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wa kuthengo. Anthu ankapita kwa iye kuchokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndi ku madera onse a Yorodani. Ndipo akavomereza machimo awo ankabatizidwa mu mtsinje wa Yorodani.

Koma iye ataona Afarisi ndi Asaduki ambiri akubwera kumene ankabatiza, anawawuza kuti, “Ana a njoka inu! Ndani anakuchenjezani kuthawa mkwiyo umene ukubwera? Onetsani chipatso cha kutembenuka mtima. Ndipo musaganize ndi kunena mwa inu nokha kuti, ‘Tili nawo abambo athu Abrahamu.’ Ndinena kwa inu kuti Mulungu akhoza kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abrahamu. 10 Tikukamba pano nkhwangwa yayikidwa kale pa mizu ya mitengo, ndipo mtengo umene subala chipatso chabwino udulidwa ndi kuponyedwa pa moto.

11 “Ine ndikubatizani ndi madzi kusonyeza kutembenuka mtima. Koma pambuyo panga akubwera wina amene ali ndi mphamvu kuposa ine, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani ndi Mzimu Woyera ndi moto. 12 Mʼdzanja lake muli chopetera ndipo adzayeretsa popunthirapo pake nadzathira tirigu wake mʼnkhokwe ndi kutentha zotsalira zonse ndi moto wosazima.”

Kubatizidwa kwa Yesu

13 Pamenepo Yesu anabwera kuchokera ku Galileya kudzabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 14 Koma Yohane anayesetsa kumukanira nati, “Ndiyenera kubatizidwa ndi Inu, bwanji Inu mubwera kwa ine?”

15 Yesu anayankha kuti, “Zibatero tsopano, ndi koyenera kwa ife kuchita zimenezi kukwaniritsa chilungamo chonse.” Ndipo Yohane anavomera.

16 Yesu atangobatizidwa, nthawi yomweyo potuluka mʼmadzi, kumwamba kunatsekuka ndipo taonani, Mzimu wa Mulungu anatsika ngati nkhunda natera pa Iye. 17 Ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba kuti, “Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa amene ndikondwera naye.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.