Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 26

Zipatso Zoyamba ndi Chakhumi

26 Mukalowa ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, mutengeko zina mwa zipatso zoyamba pa zonse zimene mudzakola mʼnthaka ya dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndi kuziyika mʼdengu. Mukatero mupite kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzakhazikitsako dzina lake ndipo mudzamuwuze wansembe amene ali pa ntchito pa nthawiyo kuti, “Ndikunenetsa lero kwa Yehova Mulungu wanu kuti ndabwera ku dziko limene Yehova analumbirira makolo athu kuti adzatipatsa ife.” Wansembe adzatenga dengulo mʼmanja mwanu ndi kuliyika pansi patsogolo pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. Ndipo mudzanenetsa pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, “Abambo anga anali Mwaramu woyendayenda, anapita ku Igupto ndi anthu ochepa nakhala kumeneko. Pambuyo pake anakhala mtundu waukulu, wamphamvu ndi wochuluka. Koma Aigupto anatisautsa natizunza, kumatigwiritsa ntchito yakalavulagaga. Kenaka tinafuwulira Yehova, Mulungu wa makolo athu ndipo Yehova anamva mawu athu ndi kuona kusauka, kuvutika ndi kuponderezedwa kwathu. Kotero Yehova anatitulutsa ku Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndi mkono wotambasuka ndi zoopsa zazikulu ndi zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa. Iye anatibweretsa ku malo ano natipatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi lino. 10 Ndipo tsopano ndikubweretsa zipatso zoyamba zimene inu Yehova mwandipatsa.” Ikani dengulo pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kuwerama mopereka ulemu pamaso pake. 11 Ndipo inu ndi Alevi pamodzi ndi alendo okhala pakati panu mudzakondwera mʼzinthu zonse zabwino zimene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, inu ndi a pa banja panu.

12 Mukatha kupatula chakhumi pa zonse zimene mwakolola mʼchaka chachitatu chimene ndi chaka chakhumi, muzichipereka kwa wansembe, mlendo, ana ndi akazi amasiye, kuti pamenepo adye mʼmizinda yanu nakhuta. 13 Kenaka munene kwa Yehova Mulungu wanu kuti “Ndatulutsamo mʼnyumba mwanga gawo lopatulika ndipo ndalipereka kwa Mlevi, mlendo, ana ndi akazi amasiye, monga mwa zonse zimene munalamula. Sindinapatuke pa zimene munalamula kapena kuyiwala ndi chimodzi chomwe. 14 Sindinadye kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndimalira maliro kapena kuchotsapo kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndinali wodetsedwa, kapena kuperekako nsembe kwa akufa kalikonse ka gawoli. Ine ndamvera Yehova Mulungu wanga, ndachita chilichonse chimene inu munandilamula. 15 Yangʼanani pa dziko kuchokera kumwamba, ku malo anu wopatulika, ndi kudalitsa anthu anu Aisraeli ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi limene mwatipatsa ife monga momwe munalonjezera pa malumbiro anu kwa makolo athu.”

Tsatirani Malamulo a Yehova

16 Yehova Mulungu wanu akukulamulani lero lino kuti mutsate malangizo ndi malamulo ake ndipo muwasunge mosamalitsa ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 17 Mwanena motsimikiza lero lino kuti Yehova ndiye Mulungu wanu ndi kuti mudzayenda mʼnjira zake, kusunga malangizo, malamulo ndi zonse akukulamulani ndi kutinso mudzamumvera. 18 Ndipo Yehova wanenetsa lero lino kuti inu ndinu anthu ake, chuma chake chamtengowapatali monga momwe analonjezera, ndipo mukuyenera kusunga malamulo ake onse. 19 Iye wanenetsa kuti adzakuyikani kukhala oyamikika, otchuka ndi olemekezeka koposa mitundu yonse imene anayilenga. Komanso mudzakhala anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu monga momwe analonjezera.

Masalimo 117-118

117 Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse;
    mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu.
Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu,
    ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha.

Tamandani Yehova.
118 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Israeli anene kuti:
    “Chikondi chake ndi chosatha.”
Banja la Aaroni linene kuti,
    “Chikondi chake ndi chosatha.”
Iwo amene amaopa Yehova anene kuti:
    “Chikondi chake ndi chosatha.”

Ndili mʼmasautso anga ndinalirira Yehova,
    ndipo Iye anayankha pondichotsa mʼmasautsowo.
Yehova ali nane; sindidzachita mantha.
    Munthu angandichite chiyani?
Yehova ali nane; Iye ndiye thandizo langa.
    Ndidzayangʼana adani anga mwachipambano.

Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
    kusiyana ndi kudalira munthu.
Nʼkwabwino kuthawira kwa Yehova
    kusiyana ndi kudalira mafumu.

10 Anthu a mitundu yonse anandizinga,
    koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
11 Anandizinga mbali zonse,
    koma mʼdzina la Yehova ndinawawononga.
12 Anandizinga ngati njuchi,
    koma anatha msanga ngati moto wapaminga;
    mʼdzina la Yehova ndinawawononga.

13 Anandikankha uku ndi uko ndipo ndinali pafupi kugwa,
    koma Yehova anandithandiza.
14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
    Iye wakhala chipulumutso changa.

15 Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano
    ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti:
“Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
16     Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba
    Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”

17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo
    ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
18 Yehova wandilanga koopsa,
    koma sanandipereke ku imfa.

19 Tsekulireni zipata zachilungamo,
    kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova
    chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
    mwakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
    wasanduka wapangodya;
23 Yehova ndiye wachita zimenezi
    ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
    tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.

25 Inu Yehova, tipulumutseni;
    Yehova, tipambanitseni.
26 Wodala amene akubwera mʼdzina la Yehova.
    Tikukudalitsani kuchokera ku nyumba ya Yehova.
27 Yehova ndi Mulungu,
    ndipo kuwala kwake kwatiwunikira Ife.
Lowani nawo pa mʼdipiti wa ku chikondwerero mutanyamula nthambi mʼdzanja lanu,
    mpaka ku nyanga za guwa.

28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;
    Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakukwezani.

29 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.

Yesaya 53

53 Ndani wakhulupirira zimene tanenazi;
    kapena ndani amene Yehova wamuzindikiritsa mphamvu zake?
Iye anakula ngati mphukira pamaso pake,
    ndiponso ngati muzu mʼnthaka yowuma.
Iye analibe thupi labwino kapena nkhope yokongola yoti ife nʼkumamuchewukira,
    analibe maonekedwe woti ife nʼkumamukhumbira.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu,
    munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa,
ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona.
    Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.

Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife;
    ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu.
Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga,
    kumukantha ndi kumusautsa.
Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,
    ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;
iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,
    ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.
Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera,
    aliyense mwa ife akungodziyendera;
ndipo Yehova wamusenzetsa
    zoyipa zathu zonse.

Anthu anamuzunza ndi kumusautsa,
    koma sanayankhule kanthu.
Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,
    kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,
    momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha.
    Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake,
poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?
    Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga?
Anamukonzera manda ake pamodzi ndi anthu oyipa
    ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi anthu achuma,
ngakhale kuti iye sanachite za chiwawa,
    kapena kuyankhula za chinyengo.

10 Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa.
    Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa.
Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali,
    ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye.
11 Atatha mazunzo a moyo wake,
    adzaona kuwala, ndipo adzakhutira.
Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri,
    popeza adzasenza zolakwa zawo.
12 Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu,
    adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu,
popeza anapereka moyo wake mpaka kufa,
    ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe.
Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri,
    ndipo anawapempherera anthu olakwa.

Mateyu 1

Makolo a Yesu Khristu Monga mwa Thupi

Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:

Abrahamu anabereka Isake,

Isake anabereka Yakobo,

Yakobo anabereka Yuda ndi abale ake.

Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara.

Perezi anabereka Hezironi,

Hezironi anabereka Aramu.

Aramu anabereka Aminadabu,

Aminadabu anabereka Naasoni,

Naasoni anabereka Salimoni.

Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe,

Bowazi anabereka Obedi amene amayi ake anali Rute,

Obedi anabereka Yese.

Yese anabereka Mfumu Davide.

Ndipo Davide anabereka Solomoni, amene amayi ake anali mkazi wa Uriya.

Solomoni anabereka Rehabiamu,

Rehabiamu anabereka Abiya,

Abiya anabereka Asa,

Asa anabereka Yehosafati,

Yehosafati anabereka Yoramu,

Yoramu anabereka Uziya.

Uziya anabereka Yotamu,

Yotamu anabereka Ahazi,

Ahazi anabereka Hezekiya.

10 Hezekiya anabereka Manase,

Manase anabereka Amoni,

Amoni anabereka Yosiya.

11 Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni.

12 Ali ku ukapolo ku Babuloni,

Yekoniya anabereka Salatieli,

Salatieli anabereka Zerubabeli.

13 Zerubabeli anabereka Abiudi,

Abiudi anabereka Eliakimu,

Eliakimu anabereka Azoro.

14 Azoro anabereka Zadoki,

Zadoki anabereka Akimu,

Akimu anabereka Eliudi.

15 Eliudi anabereka Eliezara,

Eliezara anabereka Matani,

Matani anabereka Yakobo.

16 Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu.

17 Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.

Kubadwa kwa Yesu Khristu

18 Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. 19 Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.

20 Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. 21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”

22 Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, 23 “Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”

24 Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake. 25 Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.