Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 25

25 Anthu akasemphana mawu, ayenera kupita ku bwalo la milandu ndipo woweruza adzaweruza mlanduwo. Adzamasula wosalakwa nalanga wolakwa. Munthu akapezeka wolakwa ayenera kukwapulidwa, woweruza amugoneke pansi wolakwayo ndipo akwapulidwe pamaso pake zikoti zochuluka molingana ndi mlandu wake, koma asamukwapule zikoti zopitirira makumi anayi. Akakwapulidwa kupitirira apo ndiye kuti mʼbale wanuyo anyozeka pamaso panu.

Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.

Ngati abale akukhala pamodzi ndipo wina mwa iwo akamwalira wosasiya mwana wamwamuna, mkazi wamasiyeyo asakakwatiwe ndi mlendo. Mʼbale wake wa mwamuna wakeyo amukwatire kukwaniritsa chimene akuyenera kuchita kwa mlamu wakeyo. Mwana wamwamuna woyamba amene mayiyo angabereke ayenera kutenga dzina la mwamuna wake womwalirayo kuti dzina lake lisafafanizike mu Israeli.

Komabe, ngati munthu sakufuna kukwatira mkazi wa mʼbale wakeyo, mkaziyo ayenera kupita kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda ndi kukanena kuti, “Mʼbale wake wa mwamuna wanga akukana kupitiriza dzina la mʼbale wake mu Israeli. Iye akukana kulowa chokolo.” Pamenepo akuluakulu a mu mzinda wawowo adzamuyitanitsa nakamba naye. Ngati alimbikirabe kunena kuti, “Ine sindikufuna kumukwatira mkaziyu,” mkazi wamasiye wa mʼbale wakeyo adzapita kwa iye pamaso pa akuluakuluwo namuvula nsapato imodzi, adzamulavulire kumaso nʼkunena kuti, “Izi ndi zimene amachitira munthu amene safuna kupitiriza mbiri ya banja la mʼbale wake.” 10 Mbiri ya banja la munthu ameneyo idzadziwika mu Israeli kuti ndi Banja la Wovulidwa nsapato.

11 Ngati anthu awiri akuchita ndewu ndipo mkazi wa mmodzi wa iwo abwera kudzaleretsa mwamuna wake kwa mnzakeyo natambasula dzanja lake kugwira ku maliseche kwa winayo, 12 muyenera kumudula dzanja, osamumvera chisoni.

13 Musamakhale ndi miyeso iwiri yosiyana mʼthumba mwanu, wolemera ndi wopepuka. 14 Musamakhale ndi milingo iwiri yosiyana mʼnyumba mwanu, waukulu ndi waungʼono. 15 Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 16 Pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita za chinyengo zoterezi.

17 Kumbukirani zimene Aamaleki anakuchitirani pamene munali pa ulendo wochokera ku Igupto. 18 Pamene munali otopa ndi ofowoka, iwo anakumana nanu pa ulendo wanu ndi kukantha onse otsalira mʼmbuyo ndipo iwo sanaope Mulungu. 19 Pamene Yehova Mulungu wanu akupumulitsani kwa adani onse okuzungulirani mʼdziko limene akupatsani inu ngati cholowa chanu, mudzawafafanize Aamaleki, asadzawakumbukirenso pa dziko lapansi. Musadzayiwale chimenechi!

Masalimo 116

116 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;
    Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
Pakuti ananditchera khutu,
    ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.

Zingwe za imfa zinandizinga,
    zoopsa za ku dziko la anthu akufa zinandigwera;
    ndinapeza mavuto ndi chisoni.
Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova:
    “Inu Yehova, pulumutseni!”

Yehova ndi wokoma mtima ndi wolungama
    Mulungu wathu ndi wodzaza ndi chifundo.
Yehova amateteza munthu wodzichepetsa mtima;
    pamene ndinali ndi chosowa chachikulu, Iye anandipulumutsa.

Pumula iwe moyo wanga,
    pakuti Yehova wakuchitira zokoma.

Pakuti Inu Yehova mwapulumutsa moyo wanga ku imfa,
    maso anga ku misozi,
    mapazi anga kuti angapunthwe,
kuti ine ndiyende pamaso pa Yehova
    mʼdziko la anthu amoyo.
10 Ine ndinakhulupirira; choncho ndinati,
    “Ndasautsidwa kwambiri.”
11 Ndipo ndili mʼnkhawa yanga ndinati,
    “Anthu onse ndi abodza.”

12 Ndingamubwezere chiyani Yehova,
    chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso
    ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse.

15 Imfa ya anthu oyera mtima
    ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:
    ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
    Inu mwamasula maunyolo anga.

17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu
    ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
    pamaso pa anthu ake onse,
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,
    mʼkati mwako iwe Yerusalemu.

Tamandani Yehova.

Yesaya 52

52 Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni,
    vala zilimbe.
Vala zovala zako zokongola,
    iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika.
Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwa
    sadzalowanso pa zipata zako.
Sasa fumbi lako;
    imirira nukhale pa mpando waufumu, iwe Yerusalemu.
Inu omangidwa a ku Ziyoni,
    masulani maunyolo amene ali mʼkhosi mwanumo.

Pakuti Yehova akuti,

“Sindinalandirepo kanthu pamene ndinakugulitsani,
    choncho mudzawomboledwa wopanda ndalama.”

Pakuti Ambuye Yehova akuti,

“Poyamba paja anthu anga anapita kukakhala ku Igupto;
    nawonso Asiriya awapondereza popanda chifukwa.”

Tsopano Ine Yehova ndikuti,

“Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu,
    amene amawalamulira amawanyoza,”
            akutero Yehova.
“Ndipo tsiku lonse, akungokhalira
    kuchita chipongwe dzina langa.
Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa;
    kotero adzadziwa
kuti ndi Ine amene ndikuyankhula,
    Indedi, ndine.”

Ngokongoladi mapazi a
    amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri.
Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere,
    chisangalalo ndi chipulumutso.
    Iwo akubwera kudzawuza anthu
a ku Ziyoni kuti,
    “Mulungu wako ndi mfumu!”
Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo;
    akuyimba pamodzi mwachimwemwe.
Popeza akuona chamaso
    kubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.
Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe,
    inu mabwinja a Yerusalemu,
pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,
    wapulumutsa Yerusalemu.
10 Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika
    pamaso pa anthu a mitundu yonse,
ndipo anthu onse a dziko lapansi
    adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

11 Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko!
    Musakhudze kanthu kodetsedwa!
Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehova
    tulukanimo ndipo mudziyeretse.
12 Koma simudzachoka mofulumira
    kapena kuchita chothawa;
pakuti Yehova adzayenda patsogolo panu,
    Mulungu wa Israeli adzakutetezani kumbuyo kwanu.

Kuzunzika ndi Ulemerero wa Mtumiki

13 Taonani, mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake
    adzakwezedwa ndi kulemekezedwa ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.
14 Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka,
    chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu.
    Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.
15 Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye,
    ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye.
Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona,
    ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.

Chivumbulutso 22

Mtsinje Wamoyo

22 Ndipo mngeloyo anandionetsa mtsinje wamadzi amoyo, oyera ngati mwala wa krustalo ukutuluka ku mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa, Ukuyenda pakati pa msewu waukulu wa mu mzindawo. Mbali iliyonse ya mtsinjewo kunali mtengo wamoyo, utabala zipatso khumi ndi ziwiri. Kubereka zipatso mwezi uliwonse. Ndipo masamba a mtengowo ndi mankhwala wochiritsa anthu a mitundu ina. Sipadzakhalanso temberero lililonse. Mpando waufumu wa Mulungu ndi wa Mwana Wankhosa udzakhala mu mzindawo, ndipo atumiki ake adzamutumikira. Iwo adzaona nkhope yake ndipo dzina lake lidzalembedwa pa mphumi zawo. Sipadzakhalanso usiku. Sadzafuna kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa pakuti Ambuye Mulungu adzakhala kuwala kwawo. Ndipo adzalamulira kwamuyaya.

Mngeloyo anandiwuza kuti, “Mawu awa ndi okhulupirika ndi owona. Ambuye Mulungu wa mizimu ya aneneri anatumiza mngelo wake kudzaonetsa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”

Yesu Akubweranso

“Taonani, ndikubwera posachedwa! Wodala ndi amene asunga mawu oneneratu za kutsogolo a mʼbuku ili.”

Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi. Koma mngeloyo anandiwuza kuti, “Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu.”

10 Kenaka anandiwuza kuti, “Usabise mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili chifukwa nthawi yayandikira. 11 Wochita zoyipa apitirire kuchita zoyipazo; wochita zonyansa apitirire kuchita zonyansazo; wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo; ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”

Mawu Otsiriza: Kuyitanidwa ndi Chenjezo

12 “Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita. 13 Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimaliziro ndine.

14 “Odala amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wopita ku mtengo wamoyo ndi kuti akalowe mʼzipata za mu mzindawo. 15 Kunja kuli agalu, amatsenga, achiwerewere, akupha anthu, opembedza mafano ndi aliyense amene amakonda bodza ndi kulichita.

16 “Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”

17 Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.

18 Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. 19 Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”

20 Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, “Inde, Ine ndikubwera posachedwa.”

Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.

21 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi anthu onse. Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.