M’Cheyne Bible Reading Plan
24 Ngati mwamuna wakwatira mkazi amene sakukondwera naye chifukwa wapeza vuto pa mkaziyo, namulembera mkaziyo kalata ya chisudzulo, namupatsa ndi kumutulutsa mʼnyumba mwake, 2 mkaziyo ndi kukakwatiwa ndi mwamuna wina, 3 ndipo mwamuna wachiwiriyo nʼkuyipidwa nayenso ndi kumulemberanso kalata ya chisudzulo nʼkumutulutsa mʼnyumba mwake, kapena ngati mwamunayo amwalira, 4 mwamuna wake woyamba uja, amene anamuleka saloledwanso kumukwatira kachiwiri popeza mkaziyo wadetsedwa. Chimenechi ndi chonyansa pamaso pa Yehova. Musalowetse tchimo mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu.
5 Mwamuna akangokwatira kumene asamatumizidwe ku nkhondo kapena kupatsidwa ntchito ina iliyonse. Kwa chaka chathunthu akhale ndi ufulu wokhala pa khomo pake kumasangalatsa mkazi wakeyo.
6 Munthu akakhala nanu ndi ngongole musamutengere mwala wake wa mphero ngati chikole, chifukwa kutero nʼkumutengera moyo kukhala chikole cha ngongole.
7 Ngati munthu agwidwa akuba mʼbale wake wa Chiisraeli namamuzunza ngati kapolo kapena kumugulitsa, wogulitsa mnzakeyo ayenera kuphedwa. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
8 Pakagwa matenda a khate, samalitsani kuchita zonse zimene ansembe, amene ndi Alevi, anakulangizani. Mutsatire mosamalitsa zimene ndinawalamula. 9 Kumbukirani zimene Yehova Mulungu wanu anachita kwa Miriamu muli paulendo mutatuluka mu Igupto.
10 Ukabwereketsa mnzako kanthu kena kalikonse, usalowe mʼnyumba mwake kukatenga chimene wachipereka ngati chikole. 11 Uziyima kunja kwa nyumba kuti munthu amene wamubwereketsa kanthuyo akubweretsere kunja komweko. 12 Ngati munthuyo ndi wosauka, usamutengere chikolecho mpaka kukagona nacho kwanu. 13 Pomalowa dzuwa ukhale utamubwezera mkanjo wakewo kuti akafunde. Pamenepo adzakuthokoza, ndipo amenewa adzawerengedwa ngati machitidwe olungama kwa iweyo pamaso pa Yehova Mulungu wako.
14 Osamapezera mwayi pa anthu aganyu osauka ndi aumphawi, kaya ndi Mwisraeli kapena mlendo wokhala mu umodzi mwa mizinda yanu. 15 Mumulipire malipiro ake a tsiku dzuwa lisanalowe chifukwa ndi wosauka ndipo akudalira malipirowo. Kupanda kutero adzakudandaulirani kwa Yehova ndipo mudzapezeka ochimwa.
16 Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.
17 Musachitire mlendo kapena mwana wamasiye zoyipa, kapena kulanda mkazi wamasiye chovala ngati chikole cha ngongole. 18 Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani kumeneko. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.
19 Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse. 20 Mukathyola zipatso mu mtengo wa olivi, musamabwererenso kachiwiri ku mtengo womwewo. Zotsalazo zilekereni alendo, ana ndi akazi amasiye. 21 Mukakolola mphesa mʼmunda mwanu musamabwereremonso kachiwiri. Zotsalazo muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye. 22 Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.
114 Pamene Israeli anatuluka mu Igupto,
nyumba ya Yakobo kuchoka ku mtundu wa anthu a chiyankhulo chachilendo,
2 Yuda anasanduka malo opatulika a Mulungu,
Israeli anasanduka ufumu wake.
3 Nyanja inaona ndi kuthawa,
mtsinje wa Yorodani unabwerera mʼmbuyo;
4 mapiri analumphalumpha ngati nkhosa zazimuna,
timapiri ngati ana ankhosa.
5 Nʼchifukwa chiyani iwe unathawa?
iwe mtsinje wa Yorodani unabwereranji mʼmbuyo?
6 inu mapiri, munalumphalumphiranji ngati nkhosa zazimuna,
inu timapiri, ngati ana ankhosa?
7 Njenjemera pamaso pa Ambuye iwe dziko lapansi,
pamaso pa Mulungu wa Yakobo,
8 amene anasandutsa thanthwe kukhala chitsime,
thanthwe lolimba kukhala akasupe a madzi.
115 Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi
koma ulemerero ukhale pa dzina lanu,
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
2 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,
“Mulungu wawo ali kuti?”
3 Mulungu wathu ali kumwamba;
Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
4 Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
5 Pakamwa ali napo koma sayankhula,
maso ali nawo koma sapenya;
6 makutu ali nawo koma samva,
mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
7 manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;
mapazi ali nawo koma sayenda;
kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
8 Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,
chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
9 Inu Aisraeli, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
10 Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;
Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
11 Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
12 Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:
adzadalitsa nyumba ya Israeli,
adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
13 adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;
aangʼono ndi aakulu omwe.
14 Yehova akuwonjezereni madalitso;
inuyo pamodzi ndi ana anu.
15 Mudalitsidwe ndi Yehova,
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Kumwamba ndi kwa Yehova,
koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
17 Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,
amene amatsikira kuli chete;
18 ndi ife amene timatamanda Yehova,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Tamandani Yehova.
Chipulumutso Chamuyaya cha Ziyoni
51 “Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso
ndiponso amene mumafunafuna Yehova:
Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa
ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
2 taganizani za Abrahamu, kholo lanu,
ndi Sara, amene anakubalani.
Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana,
koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
3 Yehova adzatonthozadi Ziyoni,
ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse;
Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni,
malo ake owuma ngati munda wa Yehova.
Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda
ndi kundiyamika.
4 “Mverani Ine, anthu anga:
tcherani khutu, inu mtundu wanga:
malangizo adzachokera kwa Ine;
cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse.
5 Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga.
Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga;
ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse.
Mayiko akutali akundiyembekezera.
Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.
6 Kwezani maso anu mlengalenga,
yangʼanani pansi pa dziko;
mlengalenga udzazimirira ngati utsi,
dziko lapansi lidzatha ngati chovala
ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe.
Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,
chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.
7 “Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi,
anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu;
musaope kudzudzulidwa ndi anthu
kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
8 Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala;
mbozi idzawadya ngati thonje.
Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya,
chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”
9 Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe,
Inu Yehova;
dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana,
monga nthawi ya mibado yakale.
Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe,
amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija?
10 Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu,
madzi ozama kwambiri aja?
Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama,
kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma?
11 Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera
nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa;
chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo.
Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe,
chisoni ndi kubuwula zidzathawa.
12 Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima.
Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa?
Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.
13 Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu,
amene anayala za mlengalenga
ndi kuyika maziko a dziko lapansi.
Inu nthawi zonse mumaopsezedwa
chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani
amene angofuna kukuwonongani.
Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?
14 Amʼndende adzamasulidwa posachedwa;
sadzalowa mʼmanda awo,
kapena kusowa chakudya.
15 Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma.
Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
16 Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanu
ndipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa.
Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga,
ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi,
ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
Kutha kwa Mavuto A Yerusalemu
17 Dzambatuka, dzambatuka!
Imirira iwe Yerusalemu.
Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo
chimene Yehova anakupatsa.
Iwe amene unagugudiza
chikho chochititsa chizwezwe.
18 Mwa ana onse amene anabereka,
panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera;
mwa ana onse amene analera,
panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja.
19 Mavuto awiriwa akugwera iwe.
Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga.
Ndani angakumvere chisoni?
Ndani angakutonthoze?
20 Ana ako akomoka;
ali lambalamba pa msewu,
ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde.
Ukali wa Yehova
ndi chidzudzulo chake zidzawagwera.
21 Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika,
iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.
22 Ambuye Yehova wanu,
Mulungu amene amateteza anthu ake akuti,
“Taona, ndachotsa mʼdzanja lako
chikho chimene chimakuchititsa kudzandira;
sudzamwanso chikho
cha ukali wanga.
23 Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza,
amene ankakuwuza kuti,
‘gona pansi tikuyende pa msana.’
Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo,
ngati msewu woti ayendepo.”
Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zatsopano
21 Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. 2 Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. 3 Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. 4 ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”
5 Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.”
6 Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo. 7 Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga. 8 Koma amantha, osakhulupirira, okonda zonyansa, opha anthu, achiwerewere, amatsenga, opembedza mafano ndi abodza, malo awo adzakhala nyanja yamoto ya sulufule wotentha. Iyi ndi imfa yachiwiri.”
Mzinda wa Yerusalemu Watsopano
9 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja, anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi miliri yotsiriza isanu ndi iwiri anandiwuza kuti, “Bwera, ine ndidzakuonetsa mkwatibwi wa Mwana Wankhosa.” 10 Ndipo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku phiri lalikulu ndi lalitali nandionetsa mzinda wopatulika, Yerusalemu ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu. 11 Unawala ndi ulemerero wa Mulungu, ndipo kuthwanima kwake kunali ngati mwala wamtengowapatali, ngati jasipa; woyera ngati krustalo. 12 Mzindawo unali ndi mpanda waukulu ndi wautali, unali ndi zipata khumi ndi ziwiri, ndipo panali angelo khumi ndi awiri. Pa chipata chilichonse panayima mngelo. Pa chipata chilichonse panalembedwa dzina la fuko la Israeli. 13 Kummawa kunali zipata zitatu, kumpoto zitatu, kummwera zitatu ndi kumadzulo zitatu. 14 Mpanda wa mzindawu unali ndi maziko khumi ndi awiri ndipo pa mazikopo panali mayina khumi ndi awiri a atumwi a Mwana Wankhosa.
15 Mngelo amene ankayankhula nane uja anali ndi ndodo yagolide yoyezera mzindawo, zipata zake ndi mpanda wake. 16 Mzindawo unamangidwa mofanana kutalika kwake, mulitali ndi mulifupi munali mofanana. Anayeza mzindawo ndi ndodo ija ndipo anapeza kuti mulitali, mulifupi ndi msinkhu wake kutalika kwake kunali makilomita 2,200. 17 Anayesa mpanda uja ndipo kuchindikala kwake kunali kopitirirapo mamita 65 monga mwa muyeso wa anthu umene mngelo anagwiritsa ntchito. 18 Mpandawo unapangidwa ndi yasipa, ndipo mzindawo unali wagolide oyengeka owala ngati galasi. 19 Maziko a mpanda wa mzindawo anali okongoletsedwa ndi miyala yamtengowapatali ya mtundu uliwonse. Maziko oyamba anali yasipa, achiwiri anali safiro, achitatu ndi kalikedo, achinayi ndi simaragido, 20 achisanu ndi sardiyo, achisanu ndi chiwiri ndi krusolito, achisanu ndi chitatu ndi berulo, achisanu ndi chinayi ndi topaziyo, a khumi ndi krusoprazo, a khumi ndi chimodzi ndi huakito, a khumi ndi chiwiri ndi emetusto. 21 Zipata khumi ndi ziwiri zija zinapangidwa ndi ngale, chipata chilichonse chinapangidwa ndi ngale imodzi. Misewu ya mzindawo inali yopangidwa ndi golide oyengeka, owala ngati galasi.
22 Ine sindinaone Nyumba ya Mulungu iliyonse mu mzindawo chifukwa Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse ndi Mwana Wankhosa ndiwo Nyumba yake. 23 Palibe chifukwa choti dzuwa kapena mwezi ziwale popeza mu mzindawo ulemerero wa Mulungu ndiwo umawalamo ndipo nyale yake ndi Mwana Wankhosa uja. 24 Mitundu ya anthu idzayenda mʼkuwala kwake ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mu mzindamo. 25 Zipata zake sizidzatsekedwa ngakhale tsiku limodzi lomwe pakuti sikudzakhala usiku kumeneko. 26 Ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu adzapita nazo kumeneko. 27 Kanthu kosayeretsedwa sikadzalowamo, kuphatikizanso aliyense wochita zinthu zochititsa manyazi ndi zachinyengo, koma okhawo amene mayina awo alembedwa mʼbuku lamoyo la Mwana Wankhosa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.