M’Cheyne Bible Reading Plan
Wosayenera mu Msonkhano
23 Mwamuna aliyense wofulidwa kapena woduka chiwalo chachimuna asalowe nawo mu msonkhano wa Yehova.
2 Aliyense wobadwa mʼbanja losavomerezeka, kapena mdzukulu wake wina aliyense, ngakhale mibado khumi pambuyo pake, asalowe mu msonkhano wa Yehova.
3 Mwamoni kapena Mmowabu asalowe mu msonkhano wa anthu a Yehova ngakhale mibado khumi yobwera pambuyo pake. 4 Pakuti iwowa sanabwere kudzakulonjerani ndi chakudya kapena madzi pamene mumadutsa pochokera ku Igupto, mʼmalo mwake anakalemba ganyu Balaamu mwana wa Beori wochokera ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni. 5 Komabe Yehova Mulungu wanu sanamvere Balaamu koma anatembenuza temberero kukhala dalitso kwa inu chifukwa Yehova Mulungu wanu amakukondani. 6 Musachite nawo mgwirizano uliwonse wa mtendere pa moyo wanu wonse.
7 Musapeputse Mwedomu pakuti ndi mʼbale wanu ndithu. Musapeputse Mwigupto chifukwa munali alendo mʼdziko lake. 8 Mʼbado wachitatu wa ana awo akhoza kulowa mu msonkhano wa anthu a Yehova.
Masamalidwe a Msasa
9 Mukamakhala pa msasa pokonzekera adani anu, musayandikane ndi china chilichonse chodetsedwa. 10 Wina mwa asilikali anu akadziwonongera ndi umuna usiku, ayenera kuchoka pa msasapo ndipo akhale kunja kwa msasa. 11 Koma dzuwa likapendeka ayenera kusamba ndipo polowa dzuwa akhoza kubwerera ku msasa.
12 Mukonze malo kunja kwa msasa kumene mukhoza kukadzithandizirako. 13 Pakati pa zida zanu muzikhala ndi china chokumbira, ndipo pokadzithandiza muzikumba kadzenje ndi kukwirira chimbudzi chanu. 14 Pakuti Yehova Mulungu wanu amayendayenda ku msasa wanu kukutchinjirizani ndi kupereka adani anu kwa inu. Nʼchifukwa chake msasa wanu uzikhala wopatulika kuti mwina angaone china chonyansa nabwerera osakuyandikirani.
Malamulo Osiyanasiyana
15 Ngati kapolo wathawa mbuye wake nakabisala kwanu, musamuperekenso kwa mbuye wakeyo. 16 Mumulole akhale pakati panu, paliponse pamene angakonde, mʼmudzi umene angasankhe ndipo musamupondereze.
17 Pasapezeke Mwisraeli wamwamuna kapena wamkazi wochita chiwerewere ku Nyumba ya Mulungu. 18 Musabweretse malipiro a wachiwerewere wamkazi kapena wamwamuna Mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kudzapereka za malumbiro aliwonse, chifukwa Yehova Mulungu wanu amadana ndi zimenezi.
19 Musamalipitse mʼbale wanu chiwongoladzanja, kaya pa ndalama, kapena pa chakudya, kapena pa china chilichonse choti nʼkupereketsa chiwongoladzanja. 20 Mlendo mukhoza kumulipitsa chiwongoladzanja koma osati mʼbale wanu Mwisraeli, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochitika zanu zonse mʼdziko mukulowamoli.
21 Mukalumbira kupereka kanthu kwa Yehova Mulungu wanu, musamachedwetse kupereka, chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakufunsanibe kanthuko ndipo mudzapezeka wochimwa. 22 Koma ngati mupewa kupanga mapangano simudzapezeka ochimwa. 23 Zilizonse zimene mulumbira ndi pakamwa panu muzitsimikiza kuzichita, chifukwa mwalumbira mwaufulu pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi pakamwa panu.
24 Mukalowa mʼmunda wamphesa wa mnzanu mukhoza kudya mphesa mmene mungafunire koma musayike zina mʼdengu mwanu. 25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mʼbale wanu, mukhoza kutengako ngala mʼmanja mwanu, koma osasenga tirigu ndi chikwakwa.
112 Tamandani Yehova.
Wodala munthu amene amaopa Yehova,
amene amakondwera kwambiri ndi malamulo ake.
2 Ana ake adzakhala amphamvu mʼdziko;
mʼbado wa olungama mtima udzadalitsidwa.
3 Kulemera ndi chuma zili mʼnyumba yake,
ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4 Ngakhale mu mdima kuwala kumatulukira olungama mtima;
wokoma mtima, wachifundo ndi wowongoka mtima.
5 Zinthu zabwino zidzabwera kwa iye amene amapereka mowolowamanja ndi wokongoletsa mwaufulu,
amene amachita ntchito yake mwachilungamo.
6 Ndithu sadzagwedezeka;
munthu wolungama sadzayiwalika mpaka muyaya.
7 Saopa akamva zoyipa zimene zachitika;
mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.
8 Mtima wake ndi wotetezedwa, sadzakhala ndi mantha;
potsiriza pake adzayangʼana adani ake mwachipambano.
9 Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
chilungamo chake chimanka mpaka muyaya;
nyanga yake idzakwezedwa mwaulemu.
10 Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima;
adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka.
Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.
113 Tamandani Yehova.
Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
tamandani dzina la Yehova.
2 Yehova atamandidwe,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
3 Kuyambira ku matulukiro a dzuwa mpaka ku malowero ake,
dzina la Yehova liyenera kutamandidwa.
4 Yehova wakwezeka pa anthu a mitundu yonse,
ulemerero wake ndi woposa mayiko akumwamba.
5 Ndani wofanana ndi Yehova Mulungu wathu,
Iye amene amakhala mwaufumu mmwamba?
6 amene amawerama pansi kuyangʼana
miyamba ndi dziko lapansi?
7 Iye amakweza munthu wosauka kuchoka pa fumbi
ndi kutukula munthu wosowa kuchoka pa dzala;
8 amawakhazika pamodzi ndi mafumu,
pamodzi ndi mafumu a anthu ake.
9 Amakhazikitsa mayi wosabereka mʼnyumba yake
monga mayi wa ana wosangalala.
Tamandani Yehova.
Tchimo la Israeli, Kumvera kwa Mtumiki
50 Yehova akuti,
“Kalata imene ndinasudzulira amayi
anu ili kuti?
Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole,
ndinakugulitsani kwa ati?
Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu;
amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
2 Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu?
Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha?
Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani?
Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani?
Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu,
mitsinje ndinayisandutsa chipululu;
nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi;
ndipo zinafa ndi ludzu.
3 Ndinaphimba thambo ndi mdima
ndipo chiguduli chinakhala chofunda chake.”
4 Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula
kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka.
Mmawa mulimonse amandidzutsa,
amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.
5 Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga,
ndipo sindinakhale munthu wowukira
ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.
6 Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya
masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu;
sindinawabisire nkhope yanga
anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
7 Popeza Ambuye Yehova amandithandiza,
sindidzachita manyazi.
Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi,
chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
8 Wondikhalira kumbuyo ali pafupi,
ndaninso amene adzandiyimba mlandu?
Abwere kuti tionane maso ndi maso!
Mdani wanga ndi ndani?
Abweretu kuti tilimbane!
9 Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza.
Ndaninso amene adzanditsutsa?
Onse adzatha ngati chovala
chodyedwa ndi njenjete.
10 Ndani mwa inu amaopa Yehova
ndi kumvera mawu a mtumiki wake?
Aliyense woyenda mu mdima,
popanda chomuwunikira,
iye akhulupirire dzina la Yehova
ndi kudalira Mulungu wake.
11 Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto
ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu,
lowani mʼmoto wanu womwewo.
Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa.
Ndipo ine Yehova
ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.
Zaka 1,000
20 Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya ku chidzenje chakuya chija atanyamula mʼdzanja lake unyolo waukulu. 2 Iye anachigwira chinjokacho, chinjoka chakalekale chija, amene ndi Mdierekezi kapena kuti Satana, ndipo anamumanga zaka 1,000. 3 Anamuponya ku chidzenje chakuya chija namutsekera ndi kiyi ndi kumatirira pa khomopo kuti asatulukenso kukanyenga mitundu ya anthu mpaka patapita zaka 1,000. Zikadzatha zakazo, adzamumasula kwa kanthawi pangʼono chabe.
4 Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000. 5 (Akufa ena onse sanaukenso mpaka zitatha zaka 1,000). Uku ndiko kuuka kwa akufa koyamba. 6 Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.
Kugonjetsedwa kwa Satana
7 Zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa ku ndende yake 8 ndipo adzapita kukanyenga mitundu ya anthu kumbali zonse zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa kuti akachite nkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 9 Iwo anayenda ponseponse pa dziko lapansi nazinga msasa wa anthu a Mulungu, mzinda umene Iye amawukonda. Koma moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa. 10 Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya.
Chiweruzo Chotsiriza
11 Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo. 12 Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku. 13 Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. 14 Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. 15 Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.