M’Cheyne Bible Reading Plan
22 Ngati uwona ngʼombe kapena nkhosa ya mʼbale wako ikusochera, usayilekerere koma uyesetse kuyibwezera kwa iye. 2 Ngati mʼbale wakoyo sakhala pafupi kapena sukudziwa kuti ndi yandani, uyitengere ku nyumba kwako ndi kuyisamala mpaka mwini wake atayilondola ndipo umubwezere. 3 Uzitero ndithu ngati upeza bulu kapena mkanjo kapena chilichonse chimene chatayika. Osachilekerera.
4 Ngati wapeza bulu kapena ngʼombe ya mʼbale wako itagwa panjira, usayilekerere. Ithandize kuti idzuke.
5 Akazi asavale zovala za amuna, kapena mwamuna kuvala zovala za akazi, pakuti Yehova Mulungu wanu amanyansidwa ndi aliyense wochita izi.
6 Ukapeza chisa cha mbalame mʼmphepete mwa msewu, kaya ndi mu mtengo kapena pansi, mbalame yayikazi itafungatira ana kapena mazira, usatenge mbalameyo pamodzi ndi ana ake omwe. 7 Anawo mukhoza kutenga koma onetsetsani kuti mayi wawo mwamutaya kuti apite, kuti zinthu zizikuyenderani bwino ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali.
8 Mukamanga nyumba yatsopano, mutchingire khonde lake la pa denga kuti inu musapezeke ndi mlandu wopha munthu ngati wina agwa kuchokera pa khonde la pa dengalo.
9 Musadzale mbewu zamitundu iwiri mʼmunda wanu wa mpesa, ngati mutero, si mbewu zanu zokha zimene zidzakhale zodetsedwa, komanso zipatso za mʼmunda wamphesawo.
10 Musatipule pogwiritsa ntchito ngʼombe ndi bulu pa goli limodzi.
11 Musamavale chovala chopangidwa mophatikiza ubweya ndi thonje.
12 Muzipanga mphonje mʼngodya za mkanjo umene mumavala.
Malamulo a Ukwati
13 Ngati munthu akwatira mkazi, ndipo atagona naye nʼkusamufunanso 14 namunyoza ndi kumuyipitsira dzina nʼkumati, “Ine ndinakwatira mkazi uyu, koma pamene ndinakhala naye, sindinachione chizindikiro cha unamwali wake,” 15 zikatero abambo ndi amayi ake ayenera kubweretsa chitsimikizo chakuti anali namwali kwa akuluakulu a mzinda ku chipata. 16 Abambo ake a mtsikanayo adzanene kwa akuluakuluwo kuti, “Ine ndinamupatsa munthu uyu mwana wanga wamkazi kuti amukwatire, koma sakumufunanso. 17 Tsopano wamunyoza ndipo wanena kuti, ‘Ine sindinapeze kuti mwana wanu wamkaziyu ndi namwali.’ Koma tsopano onani chitsimikizo ichi cha unamwali wa mwana wanga wamkazi.” Kenaka makolo a mtsikanayo adzaonetse kansalu kwa akuluakulu aja, 18 ndipo akuluakuluwo adzamugwire munthuyo namupatsa chilango. 19 Iwo adzamulipitse ndalama zasiliva zokwana 100 nazipereka kwa abambo a mtsikana, chifukwa munthu uyu wayipitsa dzina la mtsikana wa Chiisraeli. Ayenera kukhalabe mkazi wake ndipo asadzamuleke moyo wake wonse.
20 Koma ngati zomunenerazo ndi zoona, ndipo kuti chitsimikizo cha unamwali wa mtsikanayo sichinapezeke, 21 iyeyu ayenera kumutengera pa khomo pa abambo ake pamene anthu a mu mzinda wake akamuphere ndi miyala. Iyeyo wachita chinthu chochititsa manyazi mu Israeli pochita chiwerewere akanali pa khomo pa abambo ake. Muyenera kuchotsa zoyipa pakati panu.
22 Ngati munthu apezeka akugona ndi mkazi wa mwini wake, ayenera kuphedwa munthuyo pamodzi ndi mkazi yemwe wagona nayeyo. Muyenera kuchotsa zoyipa mu Israeli.
23 Ngati munthu mu mzinda akumana ndi mkazi yemwe anachita kale chinkhoswe nagona naye, 24 muwatengere awiriwo ku chipata cha mzinda ndi kuwapha ndi miyala. Aphedwe chifukwa mtsikanayo anali pafupi ndi anthu ndipo sanakuwe kuti ena amuthandize ndipo mwamunayo chifukwa anayipitsa mkazi wa mwini. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
25 Koma ngati munthu akumana ndi mkazi kutchire yemwe anachita kale chinkhoswe namugwiririra, mwamuna yekhayo ndiye woyenera kuphedwa. 26 Mtsikanayo musamuchite chilichonse, palibe tchimo limene wachita loti ayenera kuphedwa. Mlandu uwu ufanana ndi wa munthu amene alimbana ndi kupha mnzake woyandikana naye, 27 pakuti mwamunayo anamupeza mtsikanayo kutchire, ndipo ngakhale mtsikana wachinkhosweyo anakuwa, panalibe anamulanditsa.
28 Ngati munthu apezana ndi namwali woti sanachite chinkhoswe, namugwiririra, munthuyo nʼkupezeka, 29 ayenera kuwalipira abambo ake a namwaliyo ndalama za siliva makumi asanu. Iye ayenera kumukwatira mkaziyo chifukwa wamuyipitsa, ndipo sadzamulekanso moyo wake wonse.
30 Munthu asakwatire mkazi wa abambo ake pakuti ayenera kuchitira ulemu pogona pa abambo ake.
Salimo la Davide.
110 Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,
“Khala ku dzanja langa lamanja
mpaka nditasandutsa adani ako
kukhala chopondapo mapazi ako.”
2 Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;
udzalamulira pakati pa adani ako.
3 Ankhondo ako adzakhala odzipereka
pa tsiku lako la nkhondo.
Atavala chiyero chaulemerero,
kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,
udzalandira mame a unyamata wako.
4 Yehova walumbira
ndipo sadzasintha maganizo ake:
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya
monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”
5 Ambuye ali kudzanja lako lamanja;
Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake.
6 Adzaweruza anthu a mitundu ina,
adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi.
7 Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira;
choncho adzaweramutsa mutu wake.
111 Tamandani Yehova.
Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse
mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.
2 Ntchito za Yehova nʼzazikulu;
onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
3 Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,
ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
4 Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;
Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.
5 Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;
amakumbukira pangano lake kwamuyaya.
6 Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,
kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
7 Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;
malangizo ake onse ndi odalirika.
8 Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,
ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.
9 Iyeyo amawombola anthu ake;
anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya
dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;
onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.
Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.
Mtumiki wa Yehova
49 Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba
tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali:
Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe,
ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
2 Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa,
anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake;
Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa
ndipo anandibisa mʼchimake.
3 Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli.
Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
4 Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito
ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe,
koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova,
ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”
5 Yehova anandiwumba ine
mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake
kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye
ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye,
choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova,
ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
6 Yehovayo tsono akuti,
“Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga,
kuti udzutse mafuko a Yakobo
ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka.
Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira,
udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”
7 Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula,
Woyerayo wa Israeli akunena,
amene mitundu ya anthu inamuda,
amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti,
“Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira.
Akalonga nawonso adzagwada pansi.
Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika
ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
8 Yehova akuti,
“Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha,
ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza;
ndinakusunga ndi kukusandutsa
kuti ukhale pangano kwa anthu,
kuti dziko libwerere mwakale
ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
9 Ndidzawuza a mʼndende kuti atuluke
ndi a mu mdima kuti aonekere poyera.
“Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira
ndi msipu pa mʼmalo owuma.
10 Iwo sadzamva njala kapena ludzu,
kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza;
chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolera
ndi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.
11 Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo,
ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza.
12 Taonani, anthu anga adzachokera kutali,
ena kumpoto, ena kumadzulo,
enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”
13 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga;
kondwera, iwe dziko lapansi;
imbani nyimbo inu mapiri!
Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,
ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.
14 Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya,
Ambuye wandiyiwala.”
15 “Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere
ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?
Ngakhale iye angathe kuyiwala,
Ine sindidzakuyiwala iwe!
16 Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;
makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
17 Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira,
ndipo amene anakupasula akuchokapo.
18 Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane
ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe.
Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo,
anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa
chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’
19 “Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa
ndipo dziko lako ndi kusakazidwa,
chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera
ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
20 Ana obadwa nthawi yako yachisoni
adzanena kuti,
‘Malo ano atichepera,
tipatse malo ena woti tikhalemo.’
21 Tsono iwe udzadzifunsa kuti,
‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa?
Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena;
ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa.
Ndani anawalera ana amenewa?
Ndinatsala ndekha,
nanga awa, achokera kuti?’ ”
22 Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi,
“Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere.
Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere.
Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo
ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
23 Mafumu adzakhala abambo wongokulera
ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera.
Iwo adzagwetsa nkhope
zawo pansi.
Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova;
iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”
24 Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo,
kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza?
25 Koma zimene Yehova akunena ndi izi,
“Ankhondo adzawalanda amʼndende awo,
ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo;
ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu,
ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
26 Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe;
adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo.
Zikadzatero anthu onse adzadziwa
kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu,
Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”
Babuloni Wagwa, Haleluya!
19 Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti,
“Haleluya!
Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,
2 pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo.
Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja
amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake.
Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”
3 Ndipo anafuwulanso kuti,
“Haleluya!
Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”
4 Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti,
“Ameni, Haleluya!”
5 Kenaka mawu anachoka ku mpando waufumu kuti,
“Lemekezani Mulungu wathu
inu nonse atumiki ake,
inu amene mumamuopa,
nonse angʼono ndi akulu!”
6 Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati,
“Haleluya!
Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.
7 Tiyeni tisangalale ndi kukondwera
ndi kumutamanda!
Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika,
ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu.
8 Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosada
kuti avale.”
(Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima).
9 Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”
10 Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.”
Wokwera pa Kavalo Woyera
11 Ndinaona kumwamba kutatsekuka ndipo patsogolo panga panali kavalo woyera, amene anakwerapo dzina lake linali Wokhulupirika ndiponso Woona. Poweruza ndi kuchita nkhondo, amachita molungama. 12 Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense. 13 Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu. 14 Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada. 15 Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse. 16 Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili:
MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.
17 Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu. 18 Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.”
19 Kenaka ndinaona chirombo chija ndi mafumu a dziko lapansi ndi magulu ankhondo atasonkhana pamodzi kuti achite nkhondo ndi wokwera pa kavalo ndi ankhondo ake. 20 Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha. 21 Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.