M’Cheyne Bible Reading Plan
Mizinda Yothawirako
19 Yehova Mulungu wanu akadzawononga anthu amene dziko lawo akukupatsani, ndipo inu mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼmizinda ndi mʼnyumba zawo, 2 mukapatule mizinda itatu imene ili pakati pa dziko lomwe Yehova Mulungu akukupatsani kukhala lanu. 3 Mudzakonze misewu ndi kuligawa patatu dzikolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, kuti aliyense wopha munthu akhoza kuthawirako.
4 Ili ndi lamulo lokhudza munthu amene wapha mnzake mosazindikira osati mwadala, nathawira kumeneko kupulumutsa moyo wake. Ndi munthu amene wapha mnzake mosazindikira, popanda maganizo oyipa. 5 Mwachitsanzo, munthu atapita ku nkhalango ndi mnzake kukadula mitengo, ndiye posamula nkhwangwa kuti adule mtengo, nkhwangwa ikhoza kuguluka nʼkukagwera mnzake uja nʼkumupha. Munthu ameneyo akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizindayo napulumutsa moyo wake. 6 Kupanda kutero ndiye kuti wolipsira akhoza kumuthamangitsa mwaukali ndi kumugwira ngati mtunda utalika, ndipo akhoza kumupha ngakhale kuti sanayenera kufa popeza sanaphe mnzake mwadala. 7 Ichi ndi chifukwa chake ndikukulamulani kuti mudzipatulire nokha mizinda itatu.
8 Ngati Yehova Mulungu wanu akulitsa malire anu monga analonjezera pa malumbiro ndi makolo anu, nakupatsani dziko lonse monga analonjezera, 9 chifukwa chotsatira bwino malamulo onse amene ndikukuwuzani lero, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse, ndiye kuti mukuyenera kupatula mizinda itatu yowonjezera. 10 Muchite zimenezi kuti musakhetse magazi wosalakwa mʼdziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa, ndipo kuti musapezeke ndi mlandu wokhetsa magazi.
11 Koma ngati munthu adana ndi mnzake namubisalira panjira nʼkumuvulaza mpaka kumupha, nathawira ku umodzi mwa mizindayi, 12 akuluakulu a mu mzinda wake akamugwire ndi kumubwezera ku mzinda wake namupereka kwa wolipsira kuti aphedwe. 13 Osamumvera chisoni. Muyenera kuchotsa tchimo lokhetsa magazi wosalakwa mu Israeli kuti zinthu zizikuyenderani bwino.
14 Musamasunthe mwala wa malire anu ndi mnzanu amene anayikidwa ndi makolo anu pa cholowa chimene mulandire mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Mboni
15 Mboni imodzi siyokwanira kupeza munthu kuti ndi wolakwa pa mlandu uliwonse umene wapalamula. Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.
16 Ngati mboni yonama ifuna kunamizira munthu mlandu, 17 anthu awiri okhudzidwa ndi mlanduwo ayenera kuyima pamaso pa Yehova pali ansembe ndi oweruza amene ali pa ntchito pa nthawiyo. 18 Oweruza afufuze bwinobwino, ndipo ngati zatsimikizika kuti mboniyo ndi yabodza, yopereka umboni wonama pa mʼbale wake, 19 ndiye kuti amuchitire iyeyo zimene anafuna kuchitira mʼbale wakezo. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu. 20 Anthu ena onse adzamva zimenezi nachita mantha, ndipo choyipa choterechi sichidzachitikanso pakati panu. 21 Osachita chisoni, moyo uzilipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja ndi phazi kulipira phazi.
106 Tamandani Yehova.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2 Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
kapena kumutamanda mokwanira?
3 Odala ndi amene amasunga chilungamo,
amene amachita zolungama nthawi zonse.
4 Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
5 kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.
6 Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
7 Pamene makolo athu anali mu Igupto,
sanalingalire za zozizwitsa zanu;
iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka,
ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
8 Komabe Iye anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake,
kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
9 Anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inawuma;
anawatsogolera mʼnyanja yakuya ngati akuyenda mʼchipululu.
10 Anawapulumutsa mʼdzanja la amaliwongo;
anawawombola mʼdzanja la mdani.
11 Madzi anamiza adani awo,
palibe mmodzi wa iwo anapulumuka.
12 Kenaka iwo anakhulupirira malonjezo ake
ndi kuyimba nyimbo zamatamando.
13 Koma posachedwa anayiwala zimene Iye anachita,
ndipo sanayembekezere uphungu wake.
14 Mʼchipululu, anadzipereka ku zilakolako zawo;
mʼdziko lopanda kanthu anayesa Mulungu.
15 Choncho Iye anawapatsa chimene anapempha,
koma anatumiza nthenda yowondetsa.
16 Mʼmisasa, anachitira nsanje Mose ndi Aaroni,
amene Yehova anadzipatulira.
17 Nthaka inatsekuka ndipo inameza Datani;
inakwirira gulu la Abiramu.
18 Moto unayaka pakati pa otsatira awo;
lawi lamoto linapsereza anthu oyipa.
19 Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu
ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
20 Anasinthanitsa ulemerero wawo
ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
21 Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa,
amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
22 zozizwitsa mʼdziko la Hamu
ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
23 Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga,
pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa,
kuyima pamaso pake,
ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.
24 Motero iwo ananyoza dziko lokoma;
sanakhulupirire malonjezo ake.
25 Anangʼungʼudza mʼmatenti mwawo
ndipo sanamvere Yehova.
26 Kotero Iye analumbira atakweza dzanja lake,
kuti adzachititsa kuti iwowo afere mʼchipululu,
27 kuchititsa kuti zidzukulu zawo zifere pakati pa anthu a mitundu ina
ndi kuwabalalitsa mʼdziko lonse.
28 Iwo anayamba kupembedza Baala-Peori
ndi kudya nsembe zoperekedwa kwa milungu yopanda moyo;
29 anaputa mkwiyo wa Yehova pa machitidwe awo oyipa,
ndipo mliri unabuka pakati pawo.
30 Koma Finehasi anayimirira ndi kulowererapo,
ndipo mliri unaleka.
31 Chimenechi ndicho chinayesedwa chilungamo chake,
kwa mibado yosatha imene ikubwera.
32 Pa madzi a ku Meriba iwo anakwiyitsa Yehova
ndipo mavuto anabwera kwa Mose chifukwa cha anthuwo,
33 pakuti iwowo anawukira mzimu wa Mulungu,
ndipo pa milomo ya Mose panatuluka mawu osayenera.
34 Aisraeliwo sanawononge mitundu ya anthu
monga momwe Yehova anawalamulira.
35 Koma anasakanizana ndi anthu a mitundu inayo
ndi kuphunzira miyambo yawo.
36 Ndipo anapembedza mafano awo,
amene anakhala msampha kwa iwowo.
37 Anapereka nsembe ana awo aamuna
ndi ana awo aakazi kwa ziwanda.
38 Anakhetsa magazi a anthu osalakwa,
magazi a ana awo aamuna ndi a ana awo aakazi,
amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanaani,
ndipo dziko linayipitsidwa ndi magazi awo.
39 Iwo anadzidetsa okha ndi zimene anachita;
ndi machitidwe awo amakhala ngati munthu wachigololo.
40 Tsono Yehova anakwiya ndi anthu ake
ndipo ananyansidwa ndi cholowa chake.
41 Iye anawapereka kwa anthu a mitundu ina,
ndipo adani awo anawalamulira.
42 Adani awo anawazunza
ndi kuwakhazika pansi pa mphamvu yawo.
43 Iye ankawapulumutsa nthawi zambiri,
koma iwo ankatsimikiza za kuwukira
ndipo anawonongeka mʼmachimo awo.
44 Koma Iye anaona kuzunzika kwawo
pamene anamva kulira kwawo;
45 Chifukwa cha iwo Iye anakumbukira pangano lake
ndipo anawalezera mtima chifukwa cha kukula kwa chikondi chake.
46 Iye anachititsa kuti amene anawagwira iwo ukapolo
awamvere chisoni.
47 Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu,
ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina
kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera
ndi kunyadira mʼmatamando anu.
48 Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli,
Kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Anthu onse anene kuti, “Ameni!”
Tamandani Yehova.
Za Kupasuka kwa Babuloni ndi Mafano Ake
46 Beli wagwada pansi, Nebo wawerama;
nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo.
Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe.
Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
2 Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo;
sizikutha kupulumutsa katunduyo,
izo zomwe zikupita ku ukapolo.
3 Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,
inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,
Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,
ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
4 Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi
ndidzakusamalirani ndithu.
Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,
ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
5 “Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani?
Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?
6 Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo
ndipo amayeza siliva pa masikelo;
amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu,
kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
7 Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo;
amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo.
Singathe kusuntha pamalo pakepo.
Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha;
kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
8 “Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi,
Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.
9 Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana;
chifukwa Ine ndine Mulungu
ndipo palibe wina ofanana nane.
10 Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe.
Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike.
Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi.
Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
11 Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa.
Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa.
Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi;
zimene ndafuna ndidzazichitadi.
12 Ndimvereni, inu anthu owuma mtima,
inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
13 Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa;
sichili kutali.
Tsikulo layandikira
ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani
ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.
Mbale Zisanu ndi Ziwiri za Mkwiyo wa Mulungu
16 Kenaka ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Nyumba ya Mulungu ija kuwuza angelo asanu ndi awiri kuti, “Pitani, katsanulireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu umene uli mʼmbale zisanu ndi ziwirizi!”
2 Mngelo woyamba anapita natsanula mbale yake pa dziko lapansi ndipo zilonda zoyipa ndi zowawa zinabuka pa anthu amene anali ndi chizindikiro cha chirombo chija, napembedza fano lake.
3 Mngelo wachiwiri anapita natsanula mbale yake pa nyanja ndipo madzi ake anasanduka magazi, magazi ake ngati a munthu wakufa. Chamoyo chilichonse cha mʼnyanjamo chinafa.
4 Mngelo wachitatu anapita natsanula mbale yake pa mitsinje ndi akasupe amadzi ndipo zinasanduka magazi. 5 Kenaka ndinamva mngelo wolamulira madzi uja akuti,
“Inu mwachita chilungamo, Inu Woyerayo,
amene mulipo ndipo munalipo;
6 pakuti iwo anakhetsa magazi a oyera anu ndi aneneri anu,
nʼchifukwa chake mwawapatsa magazi kuti amwe, zomwe zikuwayenera.”
7 Kenaka ndinamva mawu ochokera ku guwa lansembe akuti,
“Inde, Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,
chiweruzo chanu ndi choona ndi cholungama.”
8 Mngelo wachinayi anapita natsanula mbale yake pa dzuwa ndipo dzuwa linapatsidwa mphamvu yopsereza anthu ndi moto. 9 Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.
10 Mngelo wachisanu anapita natsanula mbale yake pa mpando waufumu wa chirombo chija ndipo mdima unagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu analuma malilime awo chifukwa cha ululu. 11 Ndipo anatukwana Mulungu wakumwamba chifukwa cha maululu awo ndi zilonda zawo koma anakana kulapa pa zimene anachita.
12 Mngelo wachisanu ndi chimodzi anapita natsanula mbale yake pa mtsinje waukulu wa Yufurate, ndipo madzi ake anaphwa kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kummawa. 13 Kenaka ndinaona mizimu yoyipa itatu imene inkaoneka ngati achule; inatuluka mʼkamwa mwa chinjoka chija, mʼkamwa mwa chirombo chija ndi mʼkamwa mwa mneneri wonyenga uja. 14 Imeneyi ndiyo mizimu ya ziwanda imene imachita zizindikiro zodabwitsa ndipo imatuluka kupita kwa mafumu a dziko lonse, kukawasonkhanitsa ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuzonse.
15 “Taonani, ndikubwera ngati mbala! Wodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuti asayende maliseche kuti angaonetse maliseche ake.”
16 Kenaka mizimu ija inasonkhanitsa pamodzi mafumu ku malo amene mʼChihebri amatchedwa Armagedo.
17 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anatsanulira mbale yake mu mlengalenga ndipo ku Nyumba ya Mulungu kunamveka mawu ofuwula kuchokera ku mpando waufumu kuti, “Kwatha!” 18 Kenaka kunachitika mphenzi, phokoso, mabingu ndi chivomerezi choopsa. Chivomerezi ngati ichi sichinachitikepo chikhalire cha munthu pa dziko lapansi. Chinali chivomerezi choopsa kwambiri. 19 Mzinda waukuluwo unagawika magawo atatu ndipo mizinda ya mitundu ya anthu inagwa. Mulungu anakumbukira Babuloni Wamkulu namupatsa chikho chake chodzaza ndi vinyo wa ukali wa mkwiyo wake. 20 Chilumba chilichonse chinathawa ndipo mapiri sanaonekenso. 21 Matalala akuluakulu olemera pafupifupi makilogalamu makumi asanu anagwa kuchokera kumwamba kugwera pa anthu. Ndipo anthu anatukwana Mulungu chifukwa cha mliri wa matalala popeza unali mliri woopsa kwambiri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.