Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 18

Zopereka za kwa Ansembe ndi Alevi

18 Ansembe Achilevi amene ndi fuko lonse la Alevi, asapatsidwe malo kapena cholowa pakati pa Aisraeli. Iwowa azidzadya zoperekedwa kwa Yehova ngati nsembe, popeza zimenezo ndiye cholowa chawo. Iwowa sadzakhala ndi cholowa pakati pa abale awo pakuti Yehova ndiye cholowa chawo monga anawalonjezera.

Anthu amene abwera kudzapereka nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe gawo lake motere: mwendo wakutsogolo, nyama yamʼmasaya ndi zamʼkati. Muziwapatsa zamasika zoyamba za tirigu wanu, vinyo watsopano ndi mafuta, ndi ubweya woyamba pometa nkhosa zanu, pakuti Yehova Mulungu wanu wawasankha iwowa ndi ana awo pakati pa mafuko anu onse kuti aziyimirira ndi kutumikira mʼdzina la Yehova nthawi zonse.

Ngati Mlevi asuntha achoka ku mzinda wake ndi kupita kumalo kwina kumene Yehova wasankha mu Israeli momwemo ndi mtima wake wonse, kumeneko akhoza kukatumikirako mʼdzina la Yehova Mulungu wake monga Alevi anzake onse amene akutumikira pamaso pa Yehova. Iye ayenera kulandira zogawana zawo mofanana ndi anzakewo ngakhale kuti iye anagulitsa kale cholowa cha pa banja pawo.

Makhalidwe Oletsedwa

Mukafika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musakaphunzire makhalidwe onyansa a anthu a mʼdzikolo. 10 Pasapezeke pakati panu munthu wootcha pa moto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi ngati nsembe. Asapezekenso pakati panu munthu wowombeza kapena wochita mawula, wolosera, wochita za ufiti, 11 wolodza, kapena woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndi kumafunsira nzeru kwa anthu akufawo. 12 Aliyense wochita zinthu zotere ndi wonyansa pamaso pa Yehova, ndipo chifukwa cha zonyansa zimenezi Yehova adzakupirikitsirani mitundu ya anthu imeneyi. 13 Muzikhala angwiro pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Aneneri

14 Mitundu ya anthu imene mudzayipirikitseyo imamvera anyanga kapena owombeza mawula. Koma inu Yehova Mulungu wanu sanakuvomerezeni kutero. 15 Yehova Mulungu wanu adzawutsa pakati pa abale anu mneneri ngati ine. Muyenera kumumvera ameneyo. 16 Pakuti izi ndi zimene munapempha kwa Yehova Mulungu wanu ku Horebu pa tsiku la msonkhano lija pamene munati, “Ife tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu kapena kuona moto woopsawu, kuopa kuti tingafe.”

17 Yehova anati kwa ine, “Zimene akunenazi ndi zabwino. 18 Ndidzawawutsira mneneri ngati iwe pakati pa abale awo ndipo ndidzayika mawu anga mʼkamwa mwake ndipo adzawawuza chilichonse chimene ndidzamulamula. 19 Ine mwini ndidzaweruza aliyense amene sadzamvera mawu anga amene mneneriyo adzayankhula mʼdzina langa. 20 Koma mneneri wonena zinthu mʼdzina langa ndisanamulamulire kutero, kapena mneneri wonenera mʼdzina la milungu ina, ayenera kuphedwa.”

21 Mwina mukhoza kumadzifunsa kuti, “Kodi tingadziwe bwanji kuti uthengawu sanayankhule ndi Yehova?” 22 Ngati zimene mneneriyo wanenera mʼdzina la Yehova sizinachitike kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti umenewo si uthenga umene Yehova wayankhula. Mneneri ameneyo amangoyankhula za mʼmutu mwake ndiye musadzidzimuke naye.

Masalimo 105

105 Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikirani pakati pa anthu a mitundu ina zimene Iye wachita.
Imbirani Iye, imbani matamando kwa Iyeyo;
    fotokozani za machitidwe ake onse odabwitsa.
Munyadire dzina lake loyera;
    mitima ya iwo amene amafunafuna Yehova ikondwere.
Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi yonse.

Kumbukirani zodabwitsa zimene Iye anazichita,
    zozizwitsa zake ndi maweruzo amene anapereka,
inu zidzukulu za Abrahamu mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhika ake.
Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
    maweruzo ake ali pa dziko lonse lapansi.

Iyeyo amakumbukira pangano lake kwamuyaya,
    mawu amene analamula kwa mibado yonse,
pangano limene Iye anapanga ndi Abrahamu,
    lumbiro limene analumbira kwa Isake.
10 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga zophunzitsa,
    kwa Israeli monga pangano lamuyaya:
11 “Ndidzapereka kwa iwe dziko la Kanaani
    ngati gawo la cholowa chako.”

12 Pamene iwo anali ngati anthu ochepa mʼchiwerengero,
    ochepa ndithu, ndiponso alendo mʼdzikolo,
13 ankayendayenda kuchoka ku mtundu wina wa anthu ndi kupita ku mtundu wina,
    kuchoka mu ufumu wina kupita ku wina.
14 Iye sanalole wina aliyense kuwapondereza;
    anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo:
15 “Musakhudze odzozedwa anga;
    musachitire choyipa aneneri anga.”

16 Iye anabweretsa njala pa dziko
    ndipo anawononga chakudya chonse;
17 Iyeyo anatumiza munthu patsogolo pawo,
    Yosefe anagulitsidwa ngati kapolo.
18 Iwo anavulaza mapazi ake ndi matangadza,
    khosi lake analiyika mʼzitsulo,
19 mpaka zimene Iye ananeneratu zitakwaniritsidwa,
    mpaka mawu a Yehova ataonetsa kuti Iye ananena zoona.
20 Mfumu inatuma munthu kukamumasula,
    wolamulira wa mitundu ya anthu anamasula iyeyo.
21 Anamuyika kukhala wolamulira nyumba yake,
    wolamulira zonse zimene iye anali nazo,
22 kulangiza ana a mfumu monga ankafunira
    ndi kuphunzitsa nzeru akuluakulu.

23 Tsono Israeli analowa mu Igupto;
    Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.
24 Yehova anachulukitsa anthu ake;
    ndipo anachititsa kuti akhale ochuluka kwambiri kuposa adani awo;
25 amene mitima yawo anayitembenuza kuti idane ndi anthu ake,
    kukonzera chiwembu atumiki ake.
26 Yehova anatuma Mose mtumiki wake,
    ndi Aaroni amene Iye anamusankha.
27 Iwo anachita zizindikiro zozizwitsa pakati pawo,
    zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.
28 Yehova anatumiza mdima nasandutsa dziko kuti likhale la mdima.
    Koma anthuwo anakaniratu mawu a Yehova.
29 Yehova anasandutsa madzi awo kukhala magazi,
    kuchititsa kuti nsomba zawo zife.
30 Dziko lawo linadzaza ndi achule
    amene analowa mʼzipinda zogona za olamulira awo.
31 Iye anayankhula, ndipo kunabwera ntchentche zochuluka
    ndi nsabwe mʼdziko lawo lonse.
32 Iyeyo anatembenuza mvula yawo kukhala matalala,
    ndi zingʼaningʼani mʼdziko lawo lonse;
33 Anagwetsa mitengo yawo ya mpesa ndi mitengo yawo ya mkuyu,
    nawononganso mitengo ina ya mʼdziko lawolo.
34 Iye anayankhula, ndipo dzombe linabwera,
    ziwala zosawerengeka;
35 zinadya chilichonse chobiriwira cha mʼdziko lawo,
    zinadya zonse zotuluka mʼnthaka yawo.
36 Kenaka anakantha ana onse oyamba kubadwa a mʼdziko lawo,
    zipatso zoyamba za umunthu wawo wonse.

37 Yehova anatulutsa Israeli, atatenga siliva ndi golide wambiri,
    ndipo pakati pa mafuko awo palibe mmodzi amene anafowoka.
38 Dziko la Igupto linakondwa pamene iwo anachoka,
    pakuti kuopsa kwa Israeli kunawagwera iwo.
39 Iye anatambasula mitambo ngati chofunda chawo,
    ndi moto owawunikira usiku.
40 Iwo anapempha, ndipo Iye anawabweretsera zinziri
    ndipo anawakhutitsa ndi chakudya chochokera kumwamba.
41 Iye anatsekula thanthwe, ndipo madzi anatuluka;
    ngati mtsinje anayenda mʼchipululu.

42 Pakuti anakumbukira lonjezo lake loyera limene
    linaperekedwa kwa Abrahamu mtumiki wake.
43 Iye anatulutsa anthu ake akukondwera,
    osankhika ake akufuwula mwachimwemwe;
44 Iye anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina
    ndipo anakhala olowamʼmalo a zimene ena anazivutikira,
45 kuti iwo asunge malangizo ake
    ndi kutsatira malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Yesaya 45

45 Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake
    Koresi amene anamugwira dzanja lamanja
kuti agonjetse mitundu ya anthu
    ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,
ndi kutsekula zitseko
    kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
Ine ndidzayenda patsogolo pako,
    ndi kusalaza mapiri;
ndidzaphwanya zitseko za mkuwa
    ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,
    katundu wa pamalo obisika,
kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova
    Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,
    chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,
Ine ndakuyitana pokutchula dzina
    ndipo ndakupatsa dzina laulemu
    ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;
    kupatula Ine palibenso Mulungu wina.
Ndidzakupatsa mphamvu,
    ngakhale sukundidziwa Ine,
kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo
    anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.
Ine ndine Yehova,
    ndipo palibenso wina.
Ndimalenga kuwala ndi mdima,
    ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;
    ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.

“Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba;
    mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo.
Dziko lapansi litsekuke,
    ndipo chipulumutso chiphuke kuti
chilungamo chimereponso;
    Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.

“Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,
    ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.
Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,
    ‘Kodi ukuwumba chiyani?’
Kodi ntchito yako inganene kuti,
    ‘Ulibe luso?’
10 Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti,
    ‘Kodi munabereka chiyani?’
Kapena amayi ake kuti,
    ‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’

11 “Yehova
    Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,
zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:
    Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,
    kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
12 Ndine amene ndinapanga dziko lapansi
    ndikulenga munthu kuti akhalemo.
Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;
    ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
13 Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:
    ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.
Iye adzamanganso mzinda wanga
    ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,
wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,
    akutero Yehova Wamphamvuzonse.”

14 Yehova akuti,

“Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.
    Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba
adzabwera kwa inu
    ndipo adzakhala anthu anu;
iwo adzidzakutsatani pambuyo panu
    ali mʼmaunyolo.
Adzakugwadirani
    ndi kukupemphani, ponena kuti,
‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;
    palibenso mulungu wina.’ ”

15 Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika
    amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
16 Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.
    Adzakhala osokonezeka maganizo.
17 Koma Yehova adzapulumutsa Israeli
    ndi chipulumutso chamuyaya;
simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka
    mpaka kalekale.

18 Yehova
analenga zinthu zakumwamba,
    Iye ndiye Mulungu;
amene akulenga dziko lapansi,
    ndi kulikhazikitsa,
sanalipange kuti likhale lopanda kanthu,
    koma analipanga kuti anthu akhalemo.
Iyeyu akunena kuti:
Ine ndine Yehova,
    ndipo palibenso wina.
19 Ine sindinayankhule mwachinsinsi,
    pamalo ena a mdima;
Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,
    “Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”
Ine Yehova, ndimayankhula zoona;
    ndikunena zolungama.

20 Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;
    yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.
Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,
    amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
21 Fotokozani mlandu wanu,
    mupatsane nzeru nonse pamodzi.
Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?
    Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?
Kodi si Ineyo Yehova?
    Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,
Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,
    palibenso wina kupatula Ine.

22 “Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,
    inu anthu onse a pa dziko lapansi,
    pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
23 Ndalumbira ndekha,
    pakamwa panga patulutsa mawu owona,
    mawu amene sadzasinthika konse akuti,
bondo lililonse lidzagwada pamaso panga;
    anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
24 Iwo adzanene kwa Ine kuti,
    ‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”
Onse amene anamuwukira Iye
    adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
25 Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli
    zidzapambana ndi kupeza ulemerero.

Chivumbulutso 15

Angelo Asanu ndi Awiri Okhala ndi Miliri Isanu ndi Iwiri

15 Kumwamba ndinaona chizindikiro china chachikulu ndi chodabwitsa: angelo asanu ndi awiri ali ndi miliri isanu ndi iwiri yomaliza chifukwa Mulungu anakwiya kotheratu. Ndipo ndinaona chimene chinaoneka ngati nyanja yonyezimira yosakaniza ndi moto, ndipo pambali pa nyanjayo panayima amene anagonjetsa chirombo chija ndi fano lake, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo ananyamula azeze amene Mulungu anawapatsa. Iwo ankayimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwana Wankhosa. Nyimbo yake inkati,

“Zochita zanu ndi zazikulu ndi zodabwitsa,
    Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse
Njira zanu ndi zachilungamo ndi zoona,
    Mfumu ya mitundu yonse.
Inu Ambuye, ndani angapande kukuopani,
    ndi kulemekeza dzina lanu?
Pakuti Inu nokha ndiye woyera.
Anthu a mitundu yonse adzabwera
    kudzapembedza pamaso panu,
pakuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”

Zitatha izi, ndinaona kumwamba Nyumba ya Mulungu imene ndi Tenti ya Umboni, atatsekula. Mʼnyumbamo munatuluka angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri. Angelowo anavala nsalu zoyera bwino zonyezimira ndi malamba agolide pa zifuwa zawo. Ndipo kenaka chimodzi cha zamoyo zinayi zija chinapereka kwa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zodzaza ndi ukali wa Mulungu amene ali ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo Nyumba ya Mulungu inadzaza ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu zake, ndipo panalibe yemwe akanalowa mʼNyumbayo mpaka miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri aja itatha.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.