Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 17

17 Musapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena cholakwika chilichonse, pakuti zimenezi zimamunyansa.

Ngati mwamuna kapena mkazi pakati panu, mʼmizinda imene Yehova akukupatsani apezeka akuchita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu pophwanya pangano lake, ndipo ngati motsutsana ndi lamulo langa wapembedza milungu ina, kuyigwadira milunguyo, kaya ndi dzuwa kapena mwezi kapena nyenyezi zakumwamba, ndipo inu nʼkuwuzidwa zimenezi, mufufuze bwinobwino. Ngati ndi zoona, ndipo ngati zatsimikizika kuti chonyansa choterechi chachitikadi mu Israeli, mumutengere mwamuna kapena mkazi amene wachita chonyansa choterechi ku chipata cha mzinda wanu ndi kumupha pomugenda miyala. Munthu aziphedwa pakakhala mboni ziwiri kapena zitatu koma osati mboni imodzi yokha ayi. Wochitira umboniwo ndiwo aziyamba kumupha munthuyo, ndipo kenaka anthu onse. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.

Mabwalo a Milandu

Ngati akubweretserani milandu mʼmabwalo anu imene ili yovuta kuweruza kaya ndi yokhetsa magazi, kaya ndi yophwanyirana ufulu, kaya ndi yovulazana, muyitengere kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Mudzapite kwa ansembe Alevi ndi kwa woweruza wa pa nthawi imeneyo. Kawafunseni ndipo iwowo adzakuwuzani zoyenera kuchita. 10 Kachiteni zimene adzakuwuzenizo kuchokera ku malo amene Yehova adzasankhe. Kaonetsetseni kuti mukutsatira zonse zimene akuwuzanizo. 11 Kachiteni motsatira malamulo ndi malangizo amene adzakuwuzeni; osawanyoza, potembenukira kumanja kapena kumanzere. 12 Munthu aliyense amene adzanyoza woweruza kapena wansembe amene akutumikira kumeneko mʼmalo mwa Yehova Mulungu wanu, aphedwe ndithu. Muzichotsa choyipa pakati pa Israeli. 13 Anthu onse adzamva zimenezi ndipo adzachita mantha, choncho sadzadzikuzanso.

Mfumu

14 Mukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge, ndipo mukakakhazikika mʼmenemo nimunena kuti, “Tiyeni tisankhe mfumu yoti izitilamulira monga imachitira mitundu yonse yotizungulirayi,” 15 mudzakhazikitse mfumu yoti izikakulamulirani, mfumu imene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati panu. Mudzasankhe mfumuyo kuchokera pakati pa abale anu. Osasankha mlendo, munthu amene sachokera pakati pa abale anu Aisraeli. 16 Komatu mfumuyo isadzikundikire akavalo, kapena kutuma anthu kupita ku Igupto kukayipezera akavalo ena, pakuti Ambuye akuti, “Simuyenera kubweranso ku Igupto mʼnjira yomweyo.” 17 Asadziwunjikire akazi kuopa kuti mtima wake ungamusocheretse. Asadziwunjikirenso golide ndi siliva wambiri.

18 Akakhala pa mpando waufumuwo, ayenera kulemba za iye mwini mʼbuku la malamuloli, kuchokera kwa ansembe Alevi. 19 Asunge zimene walembazo ndipo ayenera kumaziwerenga masiku onse a moyo wake, kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake posunga mosamalitsa malamulo ndi malangizowa. 20 Asadzione kuti iyeyo ndi wopambana kuposa abale ake, nalekeratu kutsatira malamulo. Akasamala zimenezi iye ndi ana ake adzalamulira ufumu wa Israeli kwa nthawi yayitali.

Masalimo 104

104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.

Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
    mwavala ulemerero ndi ufumu.
Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
    watambasula miyamba ngati tenti
    ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
    ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
    malawi amoto kukhala atumiki ake.

Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
    silingasunthike.
Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
    madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
    pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
Inu munamiza mapiri,
    iwo anatsikira ku zigwa
    kumalo kumene munawakonzera.
Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
    iwo sadzamizanso dziko lapansi.

10 Iye achititsa akasupe kutulutsa madzi kupita ku zigwa;
    madziwo amayenda pakati pa mapiri.
11 Iwo amapereka madzi kwa zirombo zonse zakuthengo;
    abulu akuthengo amapha ludzu lawo.
12 Mbalame zamlengalenga zimayika zisa mʼmbali mwa madzi;
    zimayimba pakati pa thambo.
13 Iye amathirira mapiri kuchokera ku zipinda zake zapamwamba;
    dziko lapansi limakhutitsidwa ndi chipatso cha ntchito yake.
14 Amameretsa udzu kuti ngʼombe zidye,
    ndi zomera, kuti munthu azilima
    kubweretsa chakudya kuchokera mʼdziko lapansi:
15 vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,
    mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala,
    ndi buledi amene amapereka mphamvu.
16 Mitengo ya Yehova ndi yothiriridwa bwino,
    mikungudza ya ku Lebanoni imene Iye anadzala.
17 Mbalame zimamanga zisa zawo;
    kakowa ali ndi malo ake mʼmikungudzamo.
18 Mapiri ataliatali ndi a mbalale;
    mʼmingʼalu ya miyala ndi mobisalamo mbira.

19 Mwezi umasiyanitsa nyengo
    ndipo dzuwa limadziwa nthawi yake yolowera.
20 Inu mumabweretsa mdima nukhala usiku,
    ndipo zirombo zonse za ku nkhalango zimatuluka.
21 Mikango imabangula kufuna nyama,
    ndi kufunafuna chakudya chawo kuchokera kwa Mulungu.
22 Dzuwa limatuluka ndipo iyo imapita kukabisala;
    imabwerera kukagona pansi mʼmapanga awo.
23 Pamenepo munthu amapita ku ntchito yake,
    kukagwira ntchito yake mpaka madzulo.

24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
    Munazipanga zonse mwanzeru,
    dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
25 Kuli nyanja yayikulu ndi yotambalala,
    yodzaza ndi zolengedwa zosawerengeka,
    zamoyo zanu zazikulu ndi zazingʼono zomwe.
26 Kumeneko sitima zapamadzi zimayenda uku ndi uku,
    ndiponso Leviyatani amene munamulenga kuti asewere kumeneko.

27 Zonsezi zimayangʼana kwa Inu
    kuti muzipatse chakudya chawo pa nthawi yake yoyenera.
28 Mukazipatsa,
    zimachisonkhanitsa pamodzi;
mukatsekula dzanja lanu,
    izo zimakhutitsidwa ndi zinthu zabwino.
29 Mukabisa nkhope yanu,
    izo zimachita mantha aakulu;
mukachotsa mpweya wawo,
    zimafa ndi kubwerera ku fumbi.
30 Mukatumiza mzimu wanu,
    izo zimalengedwa
    ndipo mumakozanso maonekedwe a dziko lapansi.

31 Ulemerero wa Yehova ukhalebe mpaka muyaya;
    Yehova akondwere ndi ntchito ya manja ake;
32 Iye amene amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera,
    amene amakhudza mapiri ndipo amatuluka utsi.

33 Ine ndidzayimbira Yehova moyo wanga wonse;
    ndidzayimbira matamando Mulungu wanga nthawi yonse imene ndili ndi moyo.
34 Zolingalira zanga zikhale zomukomera Iye,
    pamene ndikusangalala mwa Yehova.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
    ndipo anthu oyipa asapezekenso.

Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.

Tamandani Yehova.

Yesaya 44

Israeli Wosankhidwa wa Yehova

44 Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
    Israeli, amene ndinakusankha.
Yehova
    amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,
    ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,
Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
    Yesuruni, amene ndinakusankha.
Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,
    ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;
ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,
    ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino
    ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’
    wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;
winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’
    ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.

Yehova, Osati Mafano

“Yehova Mfumu
    ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:
Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;
    palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule.
    Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe
zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale,
    ndi ziti zimene zidzachitike;
    inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
Musanjenjemere, musachite mantha.
    Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe?
Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?
    Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”

Onse amene amapanga mafano ngachabe,
    ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu.
Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona;
    ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi.
10 Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano,
    limene silingamupindulire?
11 Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi;
    amisiri a mafano ndi anthu chabe.
Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu;
    onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.

12 Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo
    ndipo amachiyika pa makala amoto;
ndi dzanja lake lamphamvu
    amachisula pochimenya ndi nyundo.
Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu;
    iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
13 Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe
    ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera;
amasema bwinobwino ndi chipangizo chake
    ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake.
Amachipanga ngati munthu,
    munthu wake wokongola
    kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
14 Amagwetsa mitengo ya mkungudza,
    mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu
nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango,
    ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
15 Mitengoyo munthu amachitako nkhuni;
    nthambi zina amasonkhera moto wowotha,
    amakolezera moto wophikira buledi
ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza;
    iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
16 Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto
    wowotcherapo nyama imene
    amadya, nakhuta.
Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti,
    “Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
17 Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo;
    amaligwadira ndi kulipembedza.
Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti,
    “Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
18 Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse;
    maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona,
    ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
19 Palibe amene amayima nʼkulingalira.
    Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti,
chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto;
    pa makala ake ndinaphikira buledi,
    ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya.
Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi.
    Kodi ndidzagwadira mtengo?
20 Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa;
    motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti,
    “Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”

21 Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi
    popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli.
Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga;
    iwe Israeli, sindidzakuyiwala.
22 Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo,
    ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa.
Bwerera kwa Ine,
    popeza ndakupulumutsa.”

23 Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi;
    fuwula, iwe dziko lapansi.
Imbani nyimbo, inu mapiri,
    inu nkhalango ndi mitengo yonse,
chifukwa Yehova wawombola Yakobo,
    waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.

Anthu Adzakhalanso mu Yerusalemu

24 Yehova Mpulumutsi wanu, amene
    anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti:

“Ine ndine Yehova,
amene anapanga zinthu zonse,
ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo,
ndinayala ndekha dziko lapansi.
25 Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga,
    ndipo ndimapusitsa owombeza mawula.
Ndimasokoneza anthu a nzeru,
    ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.
26 Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake
    ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake.

“Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu.
    Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso.
    Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.
27 Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’
    ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako.
28 Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’
    ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna;
    iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’
    ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ”

Chivumbulutso 14

Mwana Wankhosa ndi Anthu 144,000

14 Kenaka ndinaona patsogolo panga panali Mwana Wankhosa, atayimirira pa Phiri la Ziyoni, ndipo Iye anali pamodzi ndi anthu 144,000 amene pa mphumi pawo panalembedwa dzina la Mwana Wankhosayo ndi la Atate ake. Ndipo ndinamva liwu lochokera kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndinamvalo linali ngati a anthu akuyimba azeze awo. Anthuwo ankayimba nyimbo yatsopano patsogolo pa mpando waufumu ndi zamoyo zinayi zija ndi akuluakulu aja. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatula anthu 144,000 aja amene anawomboledwa pa dziko lapansi. Awa ndiwo amene sanadzidetse koma anadzisunga ndipo sanadziyipitse ndi akazi. Anthu amenewa ndiwo ankatsatira Mwana Wankhosa kulikonse kumene ankapita. Ndiwo amene anagulidwa pakati pa anthu a dziko lapansi kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwana Wankhosa. Iwo sananenepo bodza ndipo alibe cholakwa.

Angelo Atatu

Kenaka ndinaona mngelo wina akuwuluka mu mlengalenga ndipo anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalikire kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, a chiyankhulo chilichonse ndi kwa anthu onse. Mngeloyo anayankhula mokweza mawu kuti, “Wopani Mulungu ndi kumutamanda, chifukwa nthawi yoweruza anthu yafika. Mumupembedze Iye amene analenga thambo, dziko lapansi, nyanja ndi akasupe amadzi.”

Mngelo wachiwiri anatsatana naye ndipo anati, “Wagwa! Wagwa Babuloni womveka uja, amene anachititsa anthu a mitundu yonse kumwa vinyo wa zilakolako zake zachigololo.”

Mngelo wachitatu anatsatana nawo ndi mawu ofuwula anati, “Ngati wina apembedza chirombo chija ndi fano lake ndi kulembedwa chizindikiro pa mphumi kapena pa dzanja, 10 nayenso adzamwa vinyo waukali wa Mulungu, umene wathiridwa popanda kuchepetsa mphamvu zake mʼchikho cha ukali wa Mulungu. Munthuyo adzazunzidwa ndi moto wamiyala yasulufure pamaso pa angelo oyera ndi pa Mwana Wankhosa. 11 Ndipo utsi wa moto wowazunzawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya. Sikudzakhala kupumula usana ndi usiku kwa amene anapembedza chirombo chija ndi fano lake kapena kwa aliyense amene analembedwa chizindikiro cha dzina lake lija.” 12 Pamenepa ndi pofunika kupirira kwa anthu oyera mtima amene amasunga malamulo a Mulungu ndi kukhalabe okhulupirika kwa Yesu.

13 Kenaka ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti, Odala anthu amene akufa ali mwa Ambuye kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo.”

“Inde,” akutero Mzimu, “akapumule ntchito zawo zotopetsa pakuti ntchito zawo zidzawatsata.”

Zokolola za Dziko la Pansi

14 Ndinayangʼana patsogolo panga ndinaona mtambo woyera patakhalapo wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chipewa chaufumu chagolide ndipo mʼdzanja mwake munali chikwakwa chakunthwa. 15 Tsono mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu nafuwula mwamphamvu kwa uja wokhala pa mtamboyu. Mngeloyo anati, “Tenga chikwakwa chako ndipo kolola, pakuti nthawi yokolola ya dziko la pansi yakwana” 16 Choncho wokhala pa mtambo uja anayamba kukolola dzinthu pa dziko lapansi ndi chikwakwa chakecho.

17 Mngelo wina anatuluka mʼNyumba ya Mulungu kumwamba ndipo nayenso anali ndi chikwakwa chakunthwa. 18 Kenaka mngelo winanso amene amalamulira moto, anatuluka kuchokera ku guwa lansembe nayitana mwamphamvu mngelo uja amene anali ndi chikwakwa chakunthwa chija, nati, “Tenga chikwakwa chako chakunthwacho yamba kudula mphesa za mʼmunda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesa zapsa kale.” 19 Pamenepo mngeloyo anayambadi kugwiritsa ntchito chikwakwa chake nadula mphesa za dziko lapansi, naziponya mʼchopondera mphesa chachikulu cha ukali woopsa wa Mulungu. 20 Mphesazo zinapondedwa mʼchopondera mphesa kunja kwa mzinda. Mʼchopondera mphesamo munatuluka magazi amene anayenderera ngati mtsinje, kuzama kwake mita ndi theka ndipo kutalika kwake makilomita 300.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.