M’Cheyne Bible Reading Plan
Paska
16 Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto. 2 Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake. 3 Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto. 4 Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.
5 Musamangopereka nsembe ya Paska mu mzinda wina uliwonse umene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, 6 koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto. 7 Muyiwotche ndi kuyidya pa malo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Kenaka mmawa mubwerere ku matenti anu. 8 Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
Chikondwerero cha Masabata
9 Muziwerenga masabata asanu ndi awiri kuyambira pamene mwatenga chikwakwa ndi kuyamba kumweta tirigu wachilili. 10 Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani 11 Ndipo inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi a mʼmizinda mwanu, alendo, ana ndi akazi amasiye okhala pakati panu, mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku malo amene adzawasankhe kukhazikitsako dzina lake. 12 Kumbukirani kuti inunso munali akapolo ku Igupto, ndiye muzitsatira malangizo awa mosamalitsa.
Chikondwerero cha Misasa
13 Mukatha kukolola tirigu wanu ndi kupsinya vinyo wanu, muzikhala ndi Chikondwerero cha Misasa kwa masiku asanu ndi awiri. 14 Musangalale pa chikondwerero chanu, inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi, alendo, ana ndi akazi amasiye amene ali mʼmizinda yanu. 15 Kwa masiku asanu ndi awiri muzichita chikondwererochi kwa Yehova Mulungu wanu kumalo kumene Yehova adzasankhe. Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani inu pa zokolola zanu ndi pa ntchito za manja anu, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
16 Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake. 17 Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.
Oweruza
18 Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo. 19 Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. 20 Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Kupembedza Milungu Ina
21 Musazike mtengo wina uliwonse wa mafano a Asera pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, 22 ndipo musayimike mwala wachipembedzo pakuti Yehova Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.
Salimo la Davide.
103 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga;
ndi zonse zamʼkati mwanga zitamande dzina lake loyera.
2 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga,
ndipo usayiwale zabwino zake zonse.
3 Amene amakhululuka machimo ako onse
ndi kuchiritsa nthenda zako zonse,
4 amene awombola moyo wako ku dzenje
ndi kukuveka chikondi ndi chifundo chake ngati chipewa chaufumu,
5 amene akwaniritsa zokhumba zako ndi zinthu zabwino,
kotero kuti umakhala wamphamvu zatsopano ngati mphungu.
6 Yehova amachita chilungamo
ndipo amaweruza molungama onse opsinjika.
7 Iye anadziwitsa Mose njira zake,
ntchito zake kwa Aisraeli.
8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga ndi wachikondi chochuluka.
9 Iye sadzatsutsa nthawi zonse,
kapena kusunga mkwiyo wake kwamuyaya;
10 satichitira molingana ndi machimo athu,
kapena kutibwezera molingana ndi mphulupulu zathu.
11 Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi,
koteronso chikondi chake nʼchachikulu kwa iwo amene amamuopa;
12 monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo,
koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale kutali nafe.
13 Monga bambo amachitira chifundo ana ake,
choncho Yehova ali ndi chifundo ndi iwo amene amamuopa;
14 pakuti Iye amadziwa momwe tinawumbidwira,
amakumbukira kuti ndife fumbi.
15 Kunena za munthu, masiku ake ali ngati udzu,
amaphuka ngati duwa la mʼmunda;
16 koma mphepo imawombapo ndipo silionekanso
ndipo malo ake sakumbukirikanso.
17 Koma kuchokera muyaya mpaka muyaya
chikondi cha Yehova chili ndi iwo amene amamuopa,
ndi chilungamo chake chili ndi ana a ana awo;
18 iwo amene amasunga pangano lake
ndi kukumbukira kumvera malangizo ake.
19 Yehova wakhazikitsa mpando wake waufumu mmwamba
ndipo ufumu wake umalamulira onse.
20 Tamandani Yehova, inu angelo ake,
amphamvu inu amene mumachita zimene amalamula,
amene mumamvera mawu ake.
21 Tamandani Yehova, zolengedwa zonse zakumwamba,
inu atumiki ake amene mumachita chifuniro chake.
22 Tamandani Yehova, ntchito yake yonse
kulikonse mu ulamuliro wake.
Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Yehova Yekha Mpulumutsi wa Israeli
43 Koma tsopano, Yehova
amene anakulenga, iwe Yakobo,
amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,
“Usaope, pakuti ndakuwombola;
Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
2 Pamene ukuwoloka nyanja,
ndidzakhala nawe;
ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,
sidzakukokolola.
Pamene ukudutsa pa moto,
sudzapsa;
lawi la moto silidzakutentha.
3 Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,
Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.
Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,
ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
4 Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,
ndipo chifukwa ndimakukonda,
ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,
ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
5 Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;
ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,
ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
6 Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’
ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’
Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali,
ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
7 onsewo amadziwika ndi dzina langa;
ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga,
ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
8 Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya,
anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.
9 Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi,
anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu.
Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi?
Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale?
Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona,
kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
10 Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga,
ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha,
kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha.
Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina,
ngakhale pambuyo panga
sipadzakhalaponso wina.”
11 Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova,
ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.
12 Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa;
ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu.
Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
13 “Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse.
Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga,
ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”
Chifundo cha Mulungu ndi Kusakhulupirika kwa Israeli
14 Yehova akuti,
Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti,
“Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni
ndi kukupulumutsani.
Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja,
Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”
16 Yehova
anapanga njira pa nyanja,
anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.
17 Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo,
gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu,
ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso
anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
18 “Iwalani zinthu zakale;
ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.
19 Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano!
Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona?
Ine ndikulambula msewu mʼchipululu
ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
20 Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi
zinandilemekeza.
Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma
kuti ndiwapatse madzi anthu anga
osankhidwa.
21 Anthu amene ndinadziwumbira ndekha
kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.
22 “Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo,
munatopa nane, Inu Aisraeli.
23 Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza,
kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu.
Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya
kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.
24 Simunandigulire bango lonunkhira
kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu.
Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu
ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
25 “Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza
zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini,
ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
26 Mundikumbutse zakale,
ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi;
fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.
27 Kholo lanu loyamba linachimwa;
ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.
28 Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero,
ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe
ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”
Chirombo Chotuluka Mʼnyanja
13 Ndipo ndinaona chirombo chikutuluka mʼnyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri. Pa nyanga iliyonse chinavala chipewa chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu. 2 Chirombo chimene ndinachionacho chinali ngati kambuku, mapazi ake ngati chimbalangondo, kukamwa kwake ngati kwa mkango. Chinjoka chija chinapatsa chirombocho mphamvu zake, mpando wake waufumu ndiponso ulamuliro waukulu. 3 Umodzi wa mitu wa chirombocho unkaoneka ngati uli ndi bala losati nʼkupola, koma nʼkuti balalo litapola. Dziko lonse linadabwa ndipo linatsatira chirombocho. 4 Anthu anapembedza chinjoka chija chifukwa chinapereka ulamuliro wake kwa chirombocho. Nachonso chirombo chija anachipembedza nʼkumafunsa kuti, “Ndani angafanane ndi chirombochi? Ndani angachite nacho nkhondo?”
5 Chirombo chija chinaloledwa kuyankhula mawu onyada ndi achipongwe kwa Mulungu. Chinapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42. 6 Ndipo chinayamba kuyankhula mawu achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo okhalamo ndi onse amene amakhala kumwamba. 7 Chinaloledwa kuchita nkhondo ndi oyera mtima ndi kuwagonjetsa. Ndipo chinapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse. 8 Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja.
9 Iye amene ali ndi makutu, amve.
10 “Woyenera kupita ku ukapolo,
adzapita ku ukapolo.
Woyenera kufa ndi lupanga,
adzafa ndi lupanga.”
Pamenepa kwa anthu a Mulungu pakufunika kupirira ndi kukhulupirika.
Chirombo Chotuluka Mʼnthaka
11 Kenaka ndinaona chirombo china chikutuluka mʼnthaka. Chinali ndi nyanga ziwiri ngati mwana wankhosa koma kuyankhula kwake ngati chinjoka. 12 Chinalamulira ndi mphamvu zonse za chirombo choyamba chija, ndipo chinachititsa kuti dziko lapansi ndi anthu okhalamo alambire chirombo choyamba chija, chimene bala lake losati nʼkupola linali litapola. 13 Ndipo chinachita zizindikiro zazikulu zodabwitsa, mpaka kumagwetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba anthu akuona. 14 Chifukwa cha zizindikiro zimene chinaloledwa kuchita mʼmalo mwa chirombo choyamba chija, chimene bala lake linapola, chinanyenga anthu okhala pa dziko lapansi. Chinalamula anthu kuti apange fano mopereka ulemu kwa chirombo chimene chinavulazidwa ndi lupanga, koma nʼkukhalabe ndi moyo. 15 Chirombo cha chiwirichi chinapatsidwa mphamvu zakupereka mpweya kwa fano la chirombo choyamba chija kuti liyankhule ndi kuphetsa aliyense wokana kupembedza fanolo. 16 Chinakakamiza aliyense, wamngʼono, wamkulu, wolemera, wosauka, mfulu ndi kapolo kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. 17 Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, chimene ndi dzina la chirombocho kapena nambala yotanthauza dzina lake.
18 Pano pafunika nzeru. Munthu amene ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chirombocho, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.