Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 13-14

Kupembedza Milungu Ina

13 Ngati mneneri kapena wina aliyense amene amanena zamʼtsogolo mwa maloto atuluka pakati panu, nalengeza za chizindikiro chozizwitsa kapena chodabwitsa, chinthu nʼkuchitikadi, tsono iyeyo nʼkunena kuti, “Tiyeni titsatire milungu ina, tiyeni tiyipembedze,” (kunena milungu imene simunayidziwe), musamumvere mneneriyo kapena wolotayo. Yehova Mulungu wanu afuna akuyeseni kuti aone ngati mumamukonda ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Muyenera kutsatira Yehova Mulungu wanu, ndipo ndi Iyeyo amene muyenera kumuopa. Muzisunga malamulo ake ndi kumamumvera, muzimutumikira ndipo kumukangamira Iyeyo. Mneneri kapena wolotayo ayenera kuphedwa, popeza analalikira zopandukira Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani ku Igupto ndi kukupulumutsani ku dziko la ukapolo. Wolalikirayo anafuna kukupatutsani pa njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani kuti muyitsatire. Muzichotsa choyipa pakati panu.

Ngati mʼbale wanu weniweni kapena mwana wanu wamwamuna kapena wamkazi, kapena mkazi wanu wokondedwa, kapena mnzanu wapamtima akukakamizani mwachinsinsi, nʼkumati, “Tiyeni tipite tikapembedze milungu ina” (milungu imene inuyo kapena makolo anu sanayidziwe, milungu ya anthu okuzungulirani, kaya ndi apafupi kapena akutali, kuchokera kumapeto mpaka kumapeto kwina kwa dziko lapansi), musamugonjere kapena kumumvera. Musamumvere chisoni. Musamuleke kapena kumutchinjiriza. Mumuphe ndithu. Dzanja lanu likhale loyambirira kumupha, kenaka manja a anthu ena onse. 10 Mumuponye miyala mpaka kumupha, chifukwa anafuna kukupatutsani pa njira ya Yehova Mulungu amene anakutulutsani ku Igupto, dziko la ukapolo. 11 Tsono Aisraeli onse adzamva nachita mantha, ndipo palibe mmodzi pakati panu amene adzachitenso choyipa chotere.

12 Ngati mumvetsedwa kuti ku umodzi mwa mizinda imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mukhalemo, 13 kwapezeka anthu ena oyipa pakati panu ndipo asocheretsa anthu ambiri mʼmizinda yanu, pomanena kuti, “Tiyeni tikapembedze milungu ina” (milungu imene simunayidziwe), 14 mukuyenera kufunsa, kulondola ndi kufufuza bwino nkhaniyo. Ndipo ngati zitatsimikizikadi kuti ndi zoona kuti chinthu chonyansa chotere chachitikadi pakati panu, 15 muyenera kuwapha onse okhala mu mzinda umenewo. Muwonongeretu kwathunthu mzindawo, anthu ake ndi ziweto zake zomwe. 16 Katundu yense wa anthu mu mzindawo mumuwunjike pamodzi pakatikati pa bwalo losonkhanako ndipo mutenthe mzindawo pamodzi ndi katundu wake yense monga nsembe yathunthu yopsereza ya kwa Yehova Mulungu wanu. Mzinda umenewo ukhale bwinja mpaka muyaya, usadzamangidwenso. 17 Musapezeke ndi kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa kuti Yehova abweze mkwiyo wake wochititsa manthawu. Adzakuchitirani chifundo ndi kukumverani chisoni, ndipo adzakuchulukitsani monga analonjeza mwa lumbiro kwa makolo anu, 18 chifukwa mumamvera Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino ndi kuchita zoyenera pamaso pake.

Zoletsedwa pa Maliro

14 Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu. Osamadzichekacheka kapena kudzimeta pamphumi chifukwa cha abale anu amene amwalira, pakuti ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu. Pakati pa anthu onse pa dziko lonse lapansi, Yehova wasankha inu kuti chikhale chuma chake chamtengo wapatali.

Musamadye chinthu chilichonse chonyansa. Nyama zomwe mukhoza kudya ndi izi: ngʼombe, nkhosa, mbuzi, mbawala, gwape, mphoyo, mphalapala, ngoma, nyumbu ndi mbalale. Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya. Komabe pakati pa nyama zimene zimabzikula kapena zogawikana zipondero, zimene simukuyenera kudya ndi ngamira, kalulu ndi mbira. Zimenezi ngakhale zimabzikula, zipondero zake sizogawikana, choncho ndi zodetsedwa, musadye. Nkhumba simabzikula ndi yodetsedwanso ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa.

Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi, mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10 Koma chilichonse chimene chilibe minga ya pa msana ndi mamba musadye pakuti nʼchodetsedwa.

11 Mukhoza kudya mbalame iliyonse yoyenera kudya. 12 Koma simukuyenera kudya izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 13 nankapakapa, akamtema, akhungubwi a mitundu yonse, ndi mtundu uliwonse wa miphamba, 14 mtundu uliwonse wa khwangwala, 15 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo, mtundu uliwonse wa akabawi, 16 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 17 tsekwe, vuwo, dembo, 18 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.

19 Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. Musamadye zimenezi. 20 Koma chowuluka chilichonse choyenera kudya mukhoza kudya.

21 Musamadye chilichonse chimene mwachipeza chofaifa. Mukhoza kupatsa mlendo amene akukhala mu mzinda wina uliwonse wa mizinda yanu. Iyeyo akhoza kudya kapena mukhoza kugulitsa kwa wina aliyense amene sali wa mtundu wanu. Koma inu ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu.

Musamaphike mwana wambuzi mu mkaka wa mayi wake.

Za Chakhumi

22 Muzionetsetsa kuti mukupatula chakhumi pa zokolola zanu chaka chilichonse. 23 Muzidyera chakhumi cha tirigu wanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta, ndi ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene adzasankhe ngati kokhalako dzina lake, kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu. 24 Koma ngati malo amenewa ali kutali kwambiri ndipo kuti inu mwadalitsidwa ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo simungathe kunyamula chakhumi chanu (chifukwa chakuti malo amene Yehova adzasankha kukayikako dzina lake ali kutali kwambiri), 25 ndiye musinthitse chakhumi chanucho ndi siliva, ndipo mutenge silivayo ndi kupita naye kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. 26 Gwiritsani ntchito silivayo kugula chilichonse chimene muchifuna monga ngʼombe, nkhosa, vinyo kapena zakumwa zina zosasitsa, kapena china chilichonse chimene muchifuna. Ndipo inu ndi anthu a pa banja panu mudzazidyera komweko pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kukondwera. 27 Alevi okhala mʼmizinda yanu musaleke kuwathandiza popeza alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo.

28 Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzibweretsa zakhumi zonse pa zokolola za chaka chimenecho ndi kuzisunga mʼmidzi yanu, 29 kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse.

Masalimo 99-101

99 Yehova akulamulira,
    mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
    dziko lapansi ligwedezeke.
Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
    Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
    Iye ndi woyera.

Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
    Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mulambireni pa mapazi ake;
    Iye ndi woyera.

Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
    Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
    ndipo Iyeyo anawayankha.
Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
    iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.

Inu Yehova Mulungu wathu,
    munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
    ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
    pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.

Salimo. Nyimbo yothokoza.

100 Fuwulani kwa Yehova mwachimwemwe, inu dziko lonse lapansi.
    Mulambireni Yehova mosangalala;
    bwerani pamaso pake ndi nyimbo zachikondwerero.
Dziwani kuti Yehova ndi Mulungu.
    Iye ndiye amene anatipanga ndipo ife ndife ake;
    ndife anthu ake, nkhosa za pabusa pake.

Lowani ku zipata zake ndi chiyamiko
    ndi ku mabwalo ake ndi matamando;
    muyamikeni ndi kutamanda dzina lake.
Pakuti Yehova ndi wabwino ndipo chikondi chake ndi chamuyaya;
    kukhulupirika kwake nʼkokhazikika pa mibado ndi mibado.

Salimo la Davide.

101 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;
    kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
Ndidzatsata njira yolungama;
    nanga mudzabwera liti kwa ine?

Ndidzayenda mʼnyumba mwanga
    ndi mtima wosalakwa.
Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa
    pamaso panga.

Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;
    iwo sadzadziphatika kwa ine.
Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;
    ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.

Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri
    ameneyo ndidzamuletsa;
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,
    ameneyo sindidzamulekerera.

Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,
    kuti akhale pamodzi ndi ine;
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa
    adzanditumikira.

Aliyense wochita chinyengo
    sadzakhala mʼnyumba mwanga.
Aliyense woyankhula mwachinyengo
    sadzayima pamaso panga.

Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu
    onse oyipa mʼdziko;
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa
    mu mzinda wa Yehova.

Yesaya 41

Mulungu Thandizo la Israeli

41 “Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja!
    Alekeni ayandikire ndi kuyankhula;
tiyeni tikhale pamodzi
    kuti atiweruze.

“Ndani anadzutsa wochokera kummawa
    uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita?
Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake
    ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa
ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi
    nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
Amawalondola namayenda mosavutika,
    mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.
Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza,
    si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu?
Ine Yehova, ndine chiyambi
    ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”

Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa;
    anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera.
Akuyandikira pafupi, akubwera;
    aliyense akuthandiza mnzake
    ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide,
    ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo
    amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala.
Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.”
    Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.

“Koma Iwe Israeli mtumiki wanga,
    Yakobo amene ndakusankha,
    Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi,
    ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi.
Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’
    Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
10 Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;
    usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.
Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,
    ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

11 “Onse amene akupsera mtima
    adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa;
onse amene akukangana nawe
    sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
12 Udzafunafuna adani ako,
    koma sadzapezeka.
Iwo amene akuchita nawe nkhondo
    sadzakhalanso kanthu.
13 Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,
    amene ndikukugwira dzanja lako lamanja
ndipo ndikuti, usaope;
    ndidzakuthandiza.
14 Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,
    iwe wochepa mphamvu Israeli,
chifukwa Ine ndidzakuthandiza,”
    akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
15 “Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu
    chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri.
Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya,
    ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
16 Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso
    adzamwazika ndi kamvuluvulu.
Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako,
    ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:

17 “Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi,
    koma sakuwapeza;
    ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu.
Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo;
    Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
18 Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma,
    ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa.
Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi
    ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
19 Mʼchipululu ndidzameretsa
    mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi.
Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo
    ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
20 kuti anthu aone ndi kudziwa;
    inde, alingalire ndi kumvetsa,
kuti Yehova ndiye wachita zimenezi;
    kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.

21 “Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’
    Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’
22 Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze
    zomwe zidzachitike mʼtsogolo.
Tifotokozereni zinthu zamakedzana
    tiziganizire
    ndi kudziwa zotsatira zake.
Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,
23     tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani,
    ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu.
Chitani chinthu chabwino kapena choyipa,
    ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
24 Koma inu sindinu kanthu
    ndipo zochita zanu nʼzopandapake;
    amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.

25 “Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera,
    munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana.
Amapondaponda olamulira ngati matope,
    ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
26 Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe,
    kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’
Palibe amene ananena,
    palibe analengeza zimenezi,
    palibe anamva mawu anu.
27 Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’
    Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.
28 Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe,
    palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu,
    palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.
29 Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo!
    Zochita zawo si kanthu konse;
    mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.

Chivumbulutso 11

Mboni Ziwiri

11 Ndinapatsidwa bango longa ndodo yoyezera ndipo ndinawuzidwa kuti, “Pita, kayeze Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukawerenge anthu opembedza mʼNyumbamo. Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42. Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.” Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi. Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo. Mbonizo zili ndi mphamvu yomanga mvula kuti isagwe pa nthawi imene akulalikirayo; ndipo zili ndi mphamvu yosanduliza madzi kukhala magazi ndi yokantha dziko lapansi ndi miliri ya mitundumitundu nthawi iliyonse imene zingafune.

Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha. Mitembo yawo idzakhala ili gone pabwalo la mu mzinda waukulu umene mozimbayitsa umatchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwako. Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira. 10 Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi.

11 Koma patapita masiku atatu ndi theka aja, mpweya wopatsa moyo wochoka kwa Mulungu unalowa mwa aneneriwo, ndipo anayimirira, ndipo amene anawaona anachita mantha aakulu. 12 Kenaka aneneri aja anamva mawu ofuwula ochokera kumwamba owawuza kuti, “Bwerani kuno.” Ndipo anapitadi kumwamba mu mtambo adani awo aja akuwaona.

13 Nthawi yomweyo panachitika chivomerezi choopsa mwakuti chigawo chimodzi cha magawo khumi a mzinda chinagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomerezicho, ndipo opulumukawo anachita mantha kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wakumwamba.

14 Tsoka lachiwiri lapita; koma tsoka lachitatu likubwera posachedwapa.

Lipenga Lachisanu ndi Chiwiri

15 Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati,

“Ufumu wa dziko lapansi uli
    mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja,
    ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”

16 Ndipo akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yawo yaufumu pamaso pa Mulungu, anadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu 17 Iwo anati,

“Ife tikuyamika Inu Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse,
    amene mulipo ndipo munalipo,
chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yayikulu,
    ndipo mwayamba kulamulira.
18 A mitundu ina anapsa mtima;
    koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo.
Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa,
    yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri,
anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu,
    wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe.
Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.”

19 Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.