M’Cheyne Bible Reading Plan
Malo Amodzi Opembedzera
12 Awa ndi malangizo ndi malamulo amene muyenera kusamalitsanso kuti muwatsatire mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani kuti mutenge pa nthawi yonse imene muti mudzakhale mʼdzikomo. 2 Muwonongeretu kwathunthu malo onse a pamwamba pa mapiri ataliatali ndi pa mapiri angʼonoangʼono ndi pansi pa mtengo uliwonse wotambalala pamene mitundu imene muyilande dzikolo ankapembedzerapo milungu yawo. 3 Mugumule maguwa awo ansembe, ndi kuphwanya miyala yawo yachipembedzo ndipo mutenthe pa moto mafano awo a Asera: mugwetse mafano a milungu yawo ndi kufafaniza mayina awo mʼmalo amenewo.
4 Musapembedze Yehova Mulungu wanu monga mmene amachitira iwowa. 5 Koma inu muzifunafuna kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe pakati pa mafuko anu kuti ayikeko dzina lake ndi kukhalako. Ku malo amenewa muyenera kupitako. 6 Kumeneko muzipititsako zopereka zanu ndi nsembe zanu zopsereza, ndi chakhumi chanu ndi mphatso zapadera zimene munalonjeza kupereka ndi zopereka zanu zaufulu ndi ana oyamba a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. 7 Kumeneko, pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi mabanja anu mudzadya ndi kusangalalako pa china chilichonse chimene mudzakhudza, chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.
8 Musadzachite monga tikuchitira lero lino, aliyense kumachita zimene akuona kuti ndi zoyenera, 9 pakuti simunafike ku malo opumulirako ndi ku cholowa chimene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 10 Koma mudzawoloka Yorodani ndi kukhazikika mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu, ndipo Iye adzakupatsani inu mpumulo ku adani anu okuzungulirani kuti mukhale motchinjirizidwa. 11 Tsono kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti azikhalako muzikabweretsako chilichonse chimene ndikulamulirani inu: zopereka ndi nsembe zanu zopsereza, chakhumi chanu ndi mphatso zapadera, ndi chuma chanu chonse chosankhika chimene munalonjeza kwa Yehova. 12 Ndipo kumeneko inu mukasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamodzi ndi ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi a mʼmidzi yanu, amene alibe gawo kapena cholowa chawochawo. 13 Musamalitse kuti musakaphere nsembe zanu zopsereza paliponse pamene mungafune. 14 Mukaphere pa malo okhawo amene Yehova adzawasankhe mwa limodzi la mafuko anu, ndipo kumeneko mukasunge chilichonse chimene ndikulamulireni.
15 Koma mukhoza kumapha ziweto zanu mʼmizinda iliyonse ndi kudya nyama yake mmene mungafunire, ngati kuti ndi agwape kapena mbawala, monga mwadalitso limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Woyeretsedwa ndi wosayeretsedwa akhoza kuyidya. 16 Koma musamadye magazi. Muziwathira pansi ngati madzi. 17 Musamadyere mʼmizinda yanu chakhumi cha tirigu wanu ndi vinyo watsopano ndi mafuta, kapena za ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu, kapena chilichonse chimene mwalonjeza kuchipereka, nsembe zanu zaufulu, kapena mphatso zapadera, 18 mʼmalo mwake, muzidya pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhira inu, ana anu aamuna ndi aakazi, antchito anu aamuna ndi adzakazi anu, ndi Alevi ochokera mʼmizinda yanu, ndipo mudzasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa chilichonse chimene mudzachikhudza. 19 Muonetsetse kuti musawataye Alevi pa masiku onse amene mukhale mʼdziko lanumo.
20 Yehova Mulungu wanu akadzakulitsa dziko lanu monga anakulonjezerani, ndipo mukapukwa nyama mumanena kuti, “Ndikufuna nyama,” pamenepo mudzadya mmene mungafunire. 21 Ngati malo amene Yehova Mulungu wanu awasankha kuti ayike Dzina lake ali kutali kwambiri ndi inu, mukhoza kupha ziweto pakati pa ngʼombe ndi nkhosa zimene Yehova wakupatsani, monga ndinakulamulani, ndipo mʼmizinda yanuyanu mukhoza kuzidya mmene mungafunire. 22 Muzidye ngati mukudya gwape kapena mbawala. Onse oyeretsedwa monga mwa mwambo ndi osayeretsedwa omwe akhoza kudya. 23 Koma muonetsetse kuti musadye magazi, chifukwa magazi ndi moyo, ndipo musamadye moyo pamodzi ndi nyama. 24 Inu musamadye magazi, muziwathira pansi ngati madzi. 25 Musamadye magazi kuti zikuyendereni bwino inu pamodzi ndi ana anu a pambuyo panu, popeza mudzakhala mukuchita zoyenera pamaso pa Mulungu.
26 Koma mutenge zinthu zanu zoyeretsedwa ndi china chilichonse chimene munalumbira kupereka, ndi kupita kumalo kumene Yehova adzasankhe. 27 Mupereke nsembe zanu zopsereza pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, nyama pamodzi ndi magazi omwe. Magazi a nsembe zanu athiridwe pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyamayo mukhoza kudya. 28 Onetsetsani kuti muzimvera mawu onsewa amene ndikukupatsani kuti zinthu zizikuyenderani bwino nthawi zonse inu ndi ana anu chifukwa mudzakhala mukuchita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
29 Yehova Mulungu wanu adzachotsa pamaso panu mitundu ya anthu amene mukufuna kuwathira nkhondo ndi kuwalanda dzikolo. Koma mukawapirikitsa ndi kukhazikika mʼdziko lawo, 30 ndipo pamene iwo awonongeka pamaso panu, samalirani kuti musakodwe mu msampha pa kufufuza za milungu yawo, nʼkumati, “Kodi anthu a mitunduwa amatumikira bwanji milungu yawo? Ifenso tichita momwemo.” 31 Musapembedze Yehova Mulungu wanu momwe amachitira iwowo, chifukwa popembedza milungu yawoyo amachita zonyansa zamitundumitundu zimene Yehova amadana nazo. Amatentha ngakhale ana awo aamuna ndi aakazi pa moto ngati nsembe za kwa milungu yawo.
32 Onetsetsani kuti mukuchita zimene ndikukulamulirani. Musawonjezerepo kapena kuchotserapo.
97 Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;
magombe akutali akondwere.
2 Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;
chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.
3 Moto umapita patsogolo pake
ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.
4 Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;
dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.
5 Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,
pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.
6 Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,
ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.
7 Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,
iwo amene amanyadira mafano;
mulambireni, inu milungu yonse!
8 Ziyoni akumva ndipo akukondwera,
midzi ya Yuda ikusangalala
chifukwa cha maweruzo anu Yehova.
9 Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;
ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.
10 Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa
pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira
ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
11 Kuwala kumafika pa anthu olungama,
ndi chimwemwe kwa olungama mtima.
12 Kondwerani mwa Yehova Inu olungama
ndipo tamandani dzina lake loyera.
Salimo.
98 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;
dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera
zamuchitira chipulumutso.
2 Yehova waonetsa chipulumutso chake
ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina.
3 Iye wakumbukira chikondi chake
ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;
malekezero onse a dziko lapansi aona
chipulumutso cha Mulungu wathu.
4 Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,
muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera.
5 Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,
ndi zeze ndi mawu a kuyimba,
6 ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna
fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu.
7 Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo.
8 Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,
mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe;
9 izo ziyimbe pamaso pa Yehova,
pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.
Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,
ndi mitundu ya anthu mosakondera.
Mawu a Chitonthozo kwa Anthu a Mulungu
40 Atonthozeni, atonthozeni anthu anga,
akutero Mulungu wanu.
2 Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu
ndipo muwawuzitse
kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha,
tchimo lawo lakhululukidwa.
Ndawalanga mokwanira
chifukwa cha machimo awo onse.
3 Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti,
“Konzani njira ya Yehova
mʼchipululu;
wongolani njira zake;
msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.
4 Chigwa chilichonse achidzaze.
Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse;
Dziko lokumbikakumbika alisalaze,
malo azitundazitunda awasandutse zidikha.
5 Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera,
ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona,
pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”
6 Wina ananena kuti, “Lengeza.”
Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani?
“Pakuti anthu onse ali ngati udzu
ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.
7 Udzu umanyala ndipo maluwa amafota
chifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.”
Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
8 Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,
koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
9 Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,
kwera pa phiri lalitali.
Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,
fuwula kwambiri,
kweza mawu, usachite mantha;
uza mizinda ya ku Yuda kuti,
“Mulungu wanu akubwera!”
10 Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,
ndipo dzanja lake likulamulira,
taonani akubwera ndi mphotho yake
watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
11 Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:
Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake
ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake
ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
12 Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake,
kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake?
Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu,
kapena kuyeza kulemera kwa
mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
13 Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehova
kapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?
14 Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya,
kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru?
Iye anapempha nzeru kwa yani
ndi njira ya kumvetsa zinthu?
15 Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko.
Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo;
mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.
16 Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe,
ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.
17 Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake;
Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu
ndi cha chabechabe.
18 Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani?
Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
19 Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipanga
ndipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golide
naliveka mkanda wasiliva.
20 Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotere
amasankha mtengo umene sudzawola,
nafunafuna mʼmisiri waluso woti
amupangire fano limene silingasunthike.
21 Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe?
Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?
22 Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi,
Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala.
Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga,
nayikunga ngati tenti yokhalamo.
23 Amatsitsa pansi mafumu amphamvu
nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.
24 Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene
kapena kufesedwa chapompano,
ndi kungoyamba kuzika mizu kumene
ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa
ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.
25 Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?
Kapena kodi alipo wofanana nane?”
26 Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.
Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?
Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,
nayitana iliyonse ndi dzina lake.
Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,
palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
27 Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena
ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti,
“Yehova sakudziwa mavuto anga,
Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”
28 Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,
ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.
Iye sadzatopa kapena kufowoka
ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
29 Iye amalimbitsa ofowoka
ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
30 Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,
ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;
31 koma iwo amene amakhulupirira Yehova
adzalandira mphamvu zatsopano.
Adzawuluka ngati chiwombankhanga;
adzathamanga koma sadzalefuka,
adzayenda koma sadzatopa konse.
Mngelo ndi Kabuku
10 Kenaka ndinaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera kumwamba. Anavala mtambo ndipo anali ndi utawaleza pamutu pake. Nkhope yake inali ngati dzuwa, ndipo miyendo yake inali ngati mizati yamoto. 2 Mʼdzanja lake munali kabuku kakangʼono kotsekulidwa. Phazi lake lamanja linaponda mʼnyanja ndipo phazi lake lamanzere linaponda pa mtunda. 3 Mngeloyo anafuwula kwambiri ngati kubangula kwa mkango. Atangofuwula, kunamveka kugunda kwa mabingu asanu ndi awiri. 4 Mabingu asanu ndi awiriwo atangogunda, ine ndinkati ndizilemba; koma ndinamva mawu kuchokera kumwamba kuti, “Zisunge mu mtima zimene mabingu asanu ndi awiriwo anena ndipo usazilembe.”
5 Kenaka mngelo amene ndinamuona ataponda mʼnyanja ndi ku mtunda uja, anakweza dzanja lake lamanja kumwamba. 6 Mngeloyo analumbira mʼdzina la Iye wokhala ndi moyo mpaka muyaya, amene analenga kumwamba ndi zonse zili kumeneko, dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo, nyanja ndi zonse zili mʼmenemo, nati, “Pasakhalenso zochedwa tsopano! 7 Koma patsala pangʼono kuti mngelo wachisanu ndi chiwiri uja awombe lipenga lake, chinsinsi cha Mulungu chidzachitika monga momwe analengezera kwa atumiki ake, aneneri.”
8 Pamenepo mawu amene ndinamva kuchokera kumwamba aja, anandiyankhulanso, anati, “Pita katenge buku lotsekulidwalo mʼdzanja la mngelo amene waponda pa nyanja ndi pa mtundayo.”
9 Choncho ndinapita kwa mngeloyo ndipo ndinamupempha kuti andipatse kabukuko. Iye anati, “Tenga, idya. Mʼmimba mwako kaziwawa koma mʼkamwa mwako kazizuna ngati uchi.” 10 Ndinatenga kabukuko mʼdzanja la mngeloyo ndipo ndinadyadi. Mʼkamwa mwanga kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, mʼmimbamu munkawawa. 11 Ndipo anandiwuza kuti, “Iwe uyenera kulalikiranso za mitundu yambiri ya anthu, za mayiko, ziyankhulo ndi za mafumu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.