Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 9

Osati Chifukwa cha Kulungama kwa Israeli

Mvera Israeli. Watsala pangʼono kuwoloka Yorodani ndi kukathamangitsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iweyo, imene mizinda yake ndi ikuluikulu yokhala ndi makoma ofika mpaka kumwamba. Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?” Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera.

Yehova Mulungu wako akadzawapirikitsa pamaso pako, usadzanene mu mtima mwako kuti, “Yehova wandibweretsa kuno kudzalanda dziko lino chifukwa cha kulungama kwanga.” Ayi, koma ndi chifukwa cha kuyipa kwa anthu amene Yehova ati awapirikitse pamaso pako. Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Tsono zindikira kuti si chifukwa cha kulungama kwako kuti Yehova Mulungu wako akukupatsa dziko labwinoli kuti ulitenge popeza ndiwe wokanika.

Mwana Wangʼombe Wagolide

Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova. Ku Horebu munaputa mkwiyo wa Yehova, kotero kuti anakwiya kwambiri nafuna kukuwonongani. Nditakwera ku phiri kuti ndikalandire miyala iwiri ya malamulo, ya pangano limene Yehova anachita ndi inu, ndinakhala ku phiriko kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana, sindinadye buledi kapena kumwa madzi. 10 Yehova anandipatsa miyala iwiri yolembedwa ndi chala chake. Pa miyalapo panali malamulo onse amene Yehova analengeza kwa inu pa phiri kuchokera mʼmoto pa tsiku la msonkhano.

11 Pakutha pa masiku makumi anayi usiku ndi usana, Yehova anandipatsa miyala iwiri, miyala ya pangano. 12 Tsono Yehova anandiwuza, “Tsikako kuno msanga, chifukwa anthu ako aja unawatulutsa ku Iguptowa adziyipitsa. Iwo apatukapo mofulumira pa zimene ndinawalamulira ndipo adzipangira fano lachitsulo.”

13 Ndipo Yehova anati kwa ine, “Anthu awa ndawaona ndipo ndi anthu okanikadi! 14 Ndilekeni ndiwawononge ndi kufafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi wochuluka kuposa iwo.”

15 Choncho ndinatembenuka ndi kutsika phiri moto ukanayakabe. Ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga. 16 Ine poyangʼana ndinaona kuti inu munachimwira Yehova Mulungu wanu. Munadzipangira fano lowumbidwa ngati mwana wangʼombe. Inuyo munapatuka msanga kuchoka pa njira imene Yehova anakulamulirani. 17 Motero ine ndinaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwanga, ndi kuyiphwanya inu mukuona.

18 Tsono nthawi yomweyo ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana. Sindinadye buledi kapena kumwa madzi chifukwa cha machimo onse amene munawachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kumukwiyitsa kwambiri. 19 Ine ndinachita mantha ndi mkwiyo ndi ukali wa Yehova chifukwa anakwiya nanu kokwanira kukuwonongani. Koma Yehova anandimveranso. 20 Ndipo Yehova anakwiya ndi Aaroni ndipo akanamuwononga, koma ine ndinamupemphereranso Aaroniyo. 21 Ndiponso ndinatenga chinthu chanu choyipacho, mwana wangʼombe amene munapangayo, ndi kumuwotcha pa moto. Kenaka ndinamuphwanya ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi ndipo ndinawaza fumbilo mu mtsinje umene unkayenda kuchokera mʼphiri.

22 Inu munamukwiyitsanso Yehova ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibiroti Hatava.

23 Ndipo Yehova atakutulutsani ku Kadesi Barinea anati, “Pitani mukatenge dziko limene ndakupatsani.” Koma munawukira ulamuliro wa Yehova Mulungu wanu. Inu simunamukhulupirire kapena kumumvera. 24 Kuyambira pamene ndinakudziwani, mwakhala owukira Yehova.

25 Ine ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku chifukwa Yehova ananena kuti akuwonongani. 26 Ndinapemphera kwa Ambuye ndi kuti, “Haa Yehova Wamkulukulu, musawawononge anthu anu, chuma chanuchanu chimene munachipulumutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ku Igupto ndi dzanja lanu la mphamvu. 27 Kumbukirani atumiki anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Musatengere kupulupudza, kuyipa ndi kuchimwa kwawo anthuwa. 28 Kupanda kutero, ndiye kuti anthu a ku dziko lija munatitulutsaku adzati, ‘Yehova anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu popeza sanathe kukawalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza ndipo anadana nawo.’ 29 Koma iwowa ndi anthu anu, chuma chanu chimene munachitulutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ndi mkono wanu wotambasuka.”

Masalimo 92-93

Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata.

92 Nʼkwabwino kutamanda Yehova
    ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba,
Kulengeza chikondi chanu mmawa,
    ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku,
kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi
    ndi mayimbidwe abwino a zeze.

Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova;
    Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu.
Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova,
    maganizo anu ndi ozamadi!
Munthu wopanda nzeru sadziwa,
    zitsiru sizizindikira,
kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu
    ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula,
adzawonongedwa kwamuyaya.

Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya.

Zoonadi adani anu Yehova,
    zoonadi adani anu adzawonongeka;
    onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa.
10 Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati;
    mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga.
11 Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane,
    makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa.

12 Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa,
    adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
13 odzalidwa mʼnyumba ya Yehova,
    adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.
14 Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo,
    adzakhala anthete ndi obiriwira,
15 kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama;
    Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.”
93 Yehova akulamulira, wavala ulemerero;
    Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,
    dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;
    Inu ndinu wamuyaya.

Nyanja zakweza Inu Yehova,
    nyanja zakweza mawu ake;
    nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,
    ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,
    Yehova mmwamba ndi wamphamvu.

Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;
    chiyero chimakongoletsa nyumba yanu
    mpaka muyaya.

Yesaya 37

Hezekiya Apempha Thandizo kwa Yehova

37 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. Iye anatuma Eliyakimu woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’ Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a kazembe amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.”

Akuluakulu a mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”

Kazembe wa ankhondo uja atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.

Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya ku Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11 Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka? 12 Makolo anga anawononga mizinda ya Gozani, Harani, Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu inayi ija anawapulumutsa anthu a mizindayi? 13 Kodi mafumu a ku Hamati, Aripadi, Safaravaimu, Hena ndi Iva ali kuti?”

Pemphero la Hezekiya

14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova: 16 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 17 Inu Yehova tcherani khutu ndipo mumve. Inu Yehova, tsekulani maso anu ndipo muone. Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza, kunyoza Mulungu wamoyo.

18 “Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu yonse ya anthu ndi mayiko awo. 19 Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu. 20 Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”

Yehova Ayankha Pemphero la Hezekiya

21 Tsono Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga wochokera kwa Yehova kwa Hezekiya poyankha pemphero lake lokhudza Senakeribu mfumu ya ku Asiriya. 22 Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa:

“Mwana wamkazi wa Ziyoni
    akukunyoza ndi kukuseka.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu,
    akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.
23 Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani?
    Kodi iwe wafuwulira
ndi kumuyangʼana monyada ndani?
    Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!
24 Kudzera mwa amithenga ako
    iwe wanyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
    ‘Ndi magaleta anga ochuluka
ndafika pamwamba pa mapiri,
    pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni.
Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri,
    ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini.
Ndafika pa msonga pake penipeni,
    nkhalango yake yowirira kwambiri.
25 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
    ndi kumva madzi akumeneko
ndi mapazi anga
    ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’

26 “Kodi sunamvepo
    kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale?
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
    tsopano ndazichitadi,
kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa
    kukhala milu ya miyala.
27 Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu,
    ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi.
Anali ngati mbewu za mʼmunda,
    ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu omera pa denga,
    umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.

28 “Koma Ine ndimadziwa zonse za iwe;
    ndimadziwa pamene ukuyima ndi pamene ukukhala; ndimadziwa pamene ukutuluka ndi pamene ukulowa,
    ndiponso momwe umandikwiyira Ine.
29 Chifukwa umandikwiyira Ine
    ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
    ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa
    njira yomwe unadzera pobwera.

30 “Iwe Hezekiya, chizindikiro chako cha zimene zidzachitike ndi ichi:

“Chaka chino mudzadya zimene zamera zokha,
    ndipo chaka chachiwiri zimene zaphukira pa zomera zokha,
koma chaka chachitatu mudzafesa ndi kukolola,
    mudzawoka mitengo yamphesa ndi kudya zipatso zake.
31 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsalire
    adzazika mizu yawo pansi ndipo adzabereka zipatso poyera.
32 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
    ndi ku phiri la Ziyoni gulu la anthu opulumuka.
Changu cha Yehova Wamphamvuzonse
    chidzachita zimenezi.

33 “Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya:

“Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
    kapena kuponyamo muvi uliwonse.
Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango
    kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.
34 Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera;
    sadzalowa mu mzinda umenewu,”
            akutero Yehova.
35 “Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu,
    chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!”

36 Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse! 37 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anasasula misasa nʼkuchoka kubwerera kukakhala ku Ninive.

38 Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.

Chivumbulutso 7

Anthu 144,000

Zitatha izi ndinaona angelo anayi atayima pa mbali zinayi za dziko lapansi, atagwira mphepo zinayi za dziko lapansi kuletsa kuti mphepo iliyonse isawombe pa dziko kapena pa nyanja kapena pa mtengo uliwonse. Kenaka ndinaona mngelo wina akuchokera kummawa, ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuwulira angelo anayi aja amene anapatsidwa mphamvu yowononga dziko ndi nyanja kuti, “Musawononge dziko, nyanja ndi mitengo kufikira titalemba chizindikiro pa mphumi za atumiki a Mulungu wathu.” Choncho ndinamva chiwerengero cha amene ankayenera kulembedwa chizindikiro aja. Analipo okwanira 144,000 kuchokera ku mafuko onse a Israeli.

Ochokera fuko la Yuda analipo 12,000 amene analembedwa chizindikiro.

Ochokera fuko la Rubeni analipo 12,000;

ochokera fuko la Gadi analipo 12,000;

ochokera fuko la Aseri analipo 12,000;

ochokera fuko la Nafutali analipo 12,000;

ochokera fuko la Manase analipo 12,000;

ochokera fuko la Simeoni analipo 12,000;

ochokera fuko la Levi analipo 12,000;

ochokera fuko la Isakara analipo 12,000;

ochokera fuko la Zebuloni analipo 12,000;

ochokera fuko la Yosefe analipo 12,000;

ochokera fuko la Benjamini analipo 12,000.

Gulu Lalikulu la Anthu Ovala Zoyera

Zitatha izi ndinayangʼana patsogolo panga ndipo ndinaona gulu lalikulu la anthu loti munthu sangathe kuliwerenga lochokera dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu wa anthu uliwonse ndi chiyankhulo chilichonse, atayima patsogolo pa mpando waufumu, pamaso pa Mwana Wankhosa. Iwo anali atavala mikanjo yoyera ndi kunyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo. 10 Ndipo ankafuwula mokweza kuti:

“Chipulumutso chimachokera kwa Mulungu wathu,
wokhala pa mpando waufumu
ndi kwa Mwana Wankhosa.”

11 “Angelo onse anayimirira kuzungulira mpando waufumu uja, kuzunguliranso akuluakulu aja ndi zamoyo zinayi zija. Angelo aja anadzigwetsa pansi chafufumimba patsogolo pa mpando waufumu napembedza Mulungu. 12 Iwo anati,

“Ameni!
Matamando ndi ulemerero,
nzeru, mayamiko, ulemu,
ulamuliro ndi mphamvu
zikhale kwa Mulungu wathu kunthawi zanthawi,
Ameni!”

13 Pamenepo mmodzi wa akuluakulu aja anandifunsa kuti, “Kodi avala mikanjo yoyerawa ndani ndipo akuchokera kuti?”

14 Ine ndinayankha kuti, “Mbuye wanga mukudziwa ndinu.”

Tsono iye anandiwuza kuti, “Amenewa ndi amene anatuluka mʼmazunzo aakulu aja. Anachapa mikanjo yawo naziyeretsa mʼmagazi a Mwana Wankhosa. 15 Nʼchifukwa chake,

“iwowa ali patsogolo pa mpando waufumu wa Mulungu
    ndipo akutumikira usana ndi usiku mʼNyumba ya Mulungu;
ndipo Iye wokhala pa mpando waufumu
    adzawaphimba ndi tenti yake.
16 ‘Iwowa sadzamvanso njala,
    sadzamvanso ludzu,
dzuwa kapena kutentha kulikonse
    sikudzawawotcha.’
17 Pakuti Mwana Wankhosa amene ali pakati pa mpando waufumu
    adzakhala mʼbusa wawo.
‘Iye adzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo.’
    ‘Ndipo Mulungu adzawapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.’ ”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.