M’Cheyne Bible Reading Plan
Malamulo Khumi
5 Mose anayitanitsa Aisraeli onse nati:
Tamverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuwuzeni lero. Muwaphunzire ndi kuonetsetsa kuti mukuwatsata. 2 Yehova Mulungu wathu anachita pangano ndi ife ku Horebu. 3 Yehova sanachite pangano ndi makolo athu koma ndi ife, tonse amene tili moyo lero. 4 Yehova anayankhula nanu maso ndi maso kuchokera mʼmoto pa phiri paja. 5 (Pa nthawi imeneyo ine ndinayimirira pakati pa Yehova ndi inu kuti ndikuwuzeni mawu a Yehova, chifukwa inu munkachita mantha ndi moto ndipo simunakwere ku phiri). Ndipo Iye anati:
6 “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.
7 “Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.
8 “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. 9 Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane, 10 koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda ndi kusunga malamulo anga.
11 “Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.
12 “Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika monga momwe Yehova Mulungu wako anakulamulira. 13 Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi, 14 koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi kapena wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu kapena ngʼombe yanu kapena bulu wanu kapena ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu, motero ndiye kuti wantchito wanu wamwamuna ndi wantchito wanu wamkazi adzapumula monga inuyo. 15 Kumbukira kuti unali kapolo ku Igupto ndipo Yehova Mulungu wako anakutulutsa kumeneko ndi dzanja lamphamvu ndi lotambasuka. Choncho Yehova Mulungu wako akukulamula kuti uzisunga tsiku la Sabata.
16 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako monga Yehova Mulungu wako wakulamulira iwe kuti ukhale ndi moyo wautali ndi kuti zikuyendere bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.
17 “Usaphe.
18 “Usachite chigololo.
19 “Usabe.
20 “Usapereke umboni womunamizira mnzako.
21 “Usasirire mkazi wa mnzako. Usasirire nyumba ya mnzako kapena munda wake, wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”
22 Awa ndi malamulo amene Yehova anayankhula ndi mawu okweza kwa gulu lanu lonse pa phiri paja mʼmoto, mtambo ndi mdima woopsa, sanawonjezerepo kanthu. Ndipo anawalemba pa mapale awiri amiyala ndi kundipatsa.
23 Mutamva mawu kuchokera mu mdimawo, phiri lili moto lawilawi, atsogoleri onse a mafuko anu ndi akuluakulu anu anabwera kwa ine. 24 Ndipo munati, “Yehova Mulungu wathu wationetsa ulemerero ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto. Lero taona kuti munthu akhoza kukhala ndi moyo ngakhale Mulungu atayankhula naye. 25 Koma tsopano tife chifukwa chiyani? Moto waukuluwu utinyeketsa, ndipo tifa tikapitirirabe kumva mawu a Yehova Mulungu wathu. 26 Pakuti ndi munthu uti wolengedwa amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo akuyankhula kuchokera mʼmoto, monga tachitiramu, nakhala ndi moyo? 27 Pita pafupi kuti ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akunena. Kenaka udzatiwuze chilichonse chimene Yehova Mulungu wathu akunena ndipo tidzamvera ndi kuchita.”
28 Yehova anakumvani pamene munkayankhula kwa ine ndipo Yehova anati kwa ine, “Ndamva zimene anthuwa anena kwa iwe. Chilichonse chimene anena ndi chabwino. 29 Zikanakhala bwino akanakhala ndi mtima wondiopa ndi kusunga malamulo anga nthawi zonse kuti zinthu ziziwayendera bwino, iwowo pamodzi ndi ana awo kwamuyaya.
30 “Pita uwawuze kuti abwerere ku matenti awo. 31 Koma iwe ukhale kuno ndi ine kuti ndikupatse malamulo, malangizo ndi ziphunzitso zimene azitsatira mʼdziko limene ndiwapatse kuti alitenge.”
32 Choncho samalirani kuchita zimene Yehova Mulungu wanu akukulamulirani inu, musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere. 33 Muyende mʼnjira yonse imene Yehova Mulungu wanu wakulamulirani kuti mukhale ndi moyo ndi kupambana, ndi kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene mudzatengelo.
Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara.
88 Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa,
usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.
2 Pemphero langa lifike pamaso panu;
tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.
3 Pakuti ndili ndi mavuto ambiri
ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda.
4 Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje;
ndine munthu wopanda mphamvu.
5 Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa,
monga ophedwa amene agona mʼmanda,
amene Inu simuwakumbukiranso,
amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.
6 Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni,
mʼmalo akuya a mdima waukulu.
7 Ukali wanu ukundipsinja kwambiri,
mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse.
Sela
8 Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enieni
ndipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo.
Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;
9 maso anga ada ndi chisoni.
Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse;
ndimakweza manja anga kwa Inu.
10 Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa?
Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu?
Sela
11 Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda,
za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?
12 Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima,
kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?
13 Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo;
mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.
14 Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikana
ndi kundibisira nkhope yanu?
15 Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa;
ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.
16 Ukali wanu wandimiza;
zoopsa zanu zandiwononga.
17 Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula;
zandimiza kwathunthu.
18 Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga;
mdima ndiye bwenzi langa lenileni.
Msautso ndi Thandizo
33 Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,
amene sunawonongedwepo!
Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,
iwe amene sunanyengedwepo!
Iwe ukadzaleka kuwononga,
udzawonongedwa,
ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,
ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
2 Inu Yehova, mutikomere mtima ife;
tikulakalaka Inu.
Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,
ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
3 Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;
pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
4 Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.
Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.
5 Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse
adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
6 Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,
adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;
kuopa Yehova ngati madalitso.
7 Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu;
akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
8 Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,
mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.
Mdaniyo ndi wosasunga pangano.
Iye amanyoza mboni.
Palibe kulemekezana.
9 Dziko likulira ndipo likunka likutha.
Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.
Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.
Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
10 Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka
ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga,
ndipo ndidzakwezedwa.
11 Zolingalira zanu nʼzachabechabe
ngati udzu wamanyowa.
Mpweya wamoto udzakupserezani.
12 Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza;
ndi ngati minga yodulidwa.”
13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita;
inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
14 Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha;
anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera:
Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa?
Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
15 Angathe kuti ndi amene amachita zolungama
ndi kuyankhula zoona,
amene amakana phindu lolipeza monyenga
ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu,
amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo
ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
16 Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja,
kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri.
Azidzalandira chakudya chake
ndipo madzi sadzamusowa.
17 Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola
ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
18 Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:
“Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?
Ali kuti wokhometsa misonkho uja?
Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
19 Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,
anthu aja achiyankhulo chosadziwika,
chachilendo ndi chosamveka.
20 Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;
maso anu adzaona Yerusalemu,
mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,
zikhomo zake sizidzazulidwa,
kapena zingwe zake kuduka.
21 Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake
ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.
Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,
sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
22 Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,
Yehova ndiye wotilamulira,
Yehova ndiye mfumu yathu;
ndipo ndiye amene adzatipulumutse.
23 Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka,
sizikutha kulimbitsa mlongoti wake,
matanga ake sakutheka kutambasuka.
Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri
ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
24 Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala”
ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Sarde
3 “Lembera mngelo wampingo wa ku Sarde kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene amasunga mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri. Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zako; umadziwika kuti ndiwe wamoyo koma ndiwe wakufa. 2 Dzuka! Limbitsa zimene zatsalira zomwe zatsala pangʼono kufa, pakuti ndaona kuti ntchito zako nʼzosakwanira pamaso pa Mulungu. 3 Choncho, kumbukira zimene unalandira ndi kumva; uzisunge ndipo ulape. Koma ngati sudzuka, ndidzabwera ngati mbala ndipo sudzadziwa nthawi imene ndidzabwere kwanu.
4 Komabe uli ndi anthu angapo mu Sarde amene sanadetse zovala zawo. Amenewa adzayenda ndi Ine atavala zoyera popeza ndi oyenera kutero. 5 Amene adzapambane adzavala zoyera ngati ena aja. Sindidzafafaniza dzina lake mʼbuku lamoyo, koma ndidzamuchitira umboni pamaso pa Atate anga ndi angelo ake. 6 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Filadefiya
7 “Lembera mngelo wampingo wa ku Filadefiya kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi woyera ndi woonadi, amene ali ndi kiyi ya Davide. Iye akatsekula palibe amene angatseke; ndipo akatseka palibe amene angatsekule. 8 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa ntchito zako. Taona, ndakutsekulira pa khomo ndipo palibe wina amene angatseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa komabe wasunga mawu anga ndipo sunandikane. 9 Amene ndi mpingo wa Satana, amene amadzitcha kuti ndi Ayuda pamene sali choncho, koma ndi onama, ndidzawabweretsa kwa inu ndi kuwagwetsa pansi pa mapazi anu kuti adzazindikire kuti ndimakukondani. 10 Popeza mwasunga mawu anga woti mupirire ndipo mwawugwira mtima, Inenso ndidzakupulumutsani nthawi ya mayesero imene idzabwera pa dziko lonse lapansi kuyesa onse okhala pa dziko lapansi.
11 Ine ndikubwera msanga. Gwiritsitsa chimene uli nacho kuti wina angakulande chipewa chako chaufumu. 12 Iye amene adzapambane ndidzamusandutsa mzati wa mʼNyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso. Pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga ndi dzina la mzinda wa Mulungu wanga, Yerusalemu watsopano, umene ukubwera pansi kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga; ndipo pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano. 13 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.’ ”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Laodikaya
14 “Lembera mngelo wampingo wa ku Laodikaya kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa Ameni, mboni yokhulupirika ndi yoona, gwero la zolengedwa zonse za Mulungu. 15 Ine ndimadziwa ntchito zako, kuti sindiwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha! 16 Tsono popeza ndiwe wofunda chabe, sindiwe wotentha kapena wozizira, ndatsala pangʼono kuti ndikulavule mʼkamwa mwanga. 17 Iwe umati: ‘Ndine wolemera, ndine wachuma ndipo sindisowa kanthu.’ Koma sudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, waumphawi, wosaona ndi wamaliseche. 18 Ndikukulangiza kuti ugule kwa Ine golide woyengedwa ndi moto kuti ukhale wolemera. Ugule zovala zoyera kuti uvale ndi kuphimba umaliseche wako wochititsa manyaziwo. Ndiponso ugule kwa Ine mankhwala a mʼmaso kuti uwone.
19 Amene ndimawakonda ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Choncho chita changu ndipo lapa. 20 Taonani ndayima pa khomo ndikugogoda. Ngati wina amva mawu anga natsekula chitseko, Ine ndidzalowamo ndi kudya naye, Ine ndi iyeyo.
21 Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wokhala nane pamodzi pa mpando wanga waufumu monga mmene Ine ndinapambana ndi kukhala pansi ndi Atate anga pa mpando wawo waufumu. 22 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.