M’Cheyne Bible Reading Plan
Cholowa cha Ana Aakazi a Zelofehadi
36 Atsogoleri a mabanja a fuko la Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase omwe anali ochokera ku fuko la ana a Yosefe anabwera ndi kuyankhula ndi Mose, atsogoleri ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli. 2 Iwo anati, “Pamene Yehova analamula mbuye wanga kuti apereke dziko ngati cholowa kwa Aisraeli mwa maere, anakulamulani inu kupereka cholowa cha mʼbale wathu Zelofehadi kwa ana ake aakazi. 3 Tsopano ngati akwatiwa ndi aamuna ochokera ku mafuko ena a mitundu ya Aisraeli, cholowa chawo chidzatengedwa kuchoka pa cholowa cha makolo athu ndipo adzachiwonjezera ku fuko limene akwatiwakolo. Ndipo gawo lina la cholowacho, lopatsidwa kwa ife lidzatengedwa. 4 Pamene chaka cha chikondwerero cha zaka makumi asanu, cha Aisraeli chafika, cholowa chawo chidzawonjezeredwa ku fuko limene iwo akwatiwako. Ndipo katundu wawo adzachotsedwa pa cholowa cha fuko la makolo athu.”
5 Tsono mwa lamulo la Yehova, Mose anapereka lamulo ili kwa Aisraeli: “Zimene ana a Yosefe akunena ndi zoona. 6 Izi ndi zimene Yehova akulamula kwa ana aakazi a Zelofehadi: Atha kukwatiwa ndi aliyense amene angakondweretsedwe naye koma zingakhale bwino atakwatiwa mʼfuko la abambo awo 7 kuti cholowa cha Israeli chisapite ku fuko lina, pakuti Mwisraeli aliyense ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. 8 Mwana wamkazi aliyense amene adzalandira cholowa cha dziko la fuko lililonse la Israeli ayenera kukwatiwa ndi munthu wa fuko la abambo ake. 9 Cholowa chilichonse mu Israeli sichiyenera kupita ku fuko lina, popeza fuko lililonse la Israeli liyenera kusunga cholowa chimene linalandira.”
10 Choncho ana aakazi a Zelofehadi anachita monga Yehova analamulira Mose. 11 Ana aakazi a Zelofehadi amene ndi Mahila, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, anakwatiwa ndi asuweni awo a ku mbali ya abambo awo. 12 Anakwatiwa mʼmafuko a zidzukulu za Manase mwana wa Yosefe, ndipo cholowa chawo chinakhalabe mʼfuko la abambo awo.
13 Awa ndi malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kupyolera mwa Mose ku chigwa cha Mowabu mʼmbali mwa Yorodani, ku Yeriko.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.
80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
2 kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
bwerani ndi kutipulumutsa.
3 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
4 Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
5 Mwawadyetsa buledi wa misozi;
mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
6 Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
ndipo adani athu akutinyoza.
7 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
8 Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto;
munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.
9 Munawulimira munda wamphesawo,
ndipo unamera ndi kudzaza dziko.
10 Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake,
mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.
11 Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja,
mphukira zake mpaka ku mtsinje.
12 Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake
kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?
13 Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga
ndipo zirombo za mthengo zimawudya.
14 Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse!
Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone!
Uyangʼanireni mpesa umenewu,
15 muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala,
mwana amene inu munamukuza nokha.
16 Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto;
pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.
17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.
19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
Tsoka kwa Efereimu
28 Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu.
Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa
limene lili pa mutu pa anthu
oledzera a mʼchigwa chachonde.
2 Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga.
Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga,
ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho;
ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.
3 Ulamuliro wa atsogoleri oledzera
a ku Efereimu adzawuthetsa.
4 Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa
lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja,
udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa
imene munthu akangoyiona amayithyola
nthawi yokolola isanakwane.
5 Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse
adzakhala ngati nkhata yaufumu,
chipewa chokongola
kwa anthu ake otsala.
6 Iye adzapereka mtima
wachilungamo kwa oweruza,
adzakhala chilimbikitso kwa
amene amabweza adani pa zipata za mzinda.
7 Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo
ndipo akusochera chifukwa cha mowa:
ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa
ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo;
akusochera chifukwa cha mowa,
akudzandira pamene akuona masomphenya,
kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
8 Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha
ndipo palibenso malo wopanda zonyansa.
9 Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani?
Uthengawu akufuna kufotokozera yani?
Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa,
kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
10 Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono
lemba ndi lemba, mzere ndi mzere,
phunziro ndi phunziro.
Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.”
11 Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino.
Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene
12 anakuwuzani kuti,
“Malo opumulira ndi ano,
otopa apumule, malo owusira ndi ano.”
Koma inu simunamvere.
13 Choncho Yehova adzakuphunzitsani
pangʼonopangʼono lemba ndi lemba,
mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro.
Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo,
adzapweteka ndi kukodwa mu msampha
ndipo adzakutengani ku ukapolo.
14 Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova,
inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.
15 Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa,
ife tachita mgwirizano ndi manda.
Pamene mliri woopsa ukadzafika
sudzatikhudza ife,
chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu
ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.”
16 Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi:
“Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri
ngati maziko mu Ziyoni,
mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu;
munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
17 Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake,
ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere;
matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza,
ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
18 Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa;
mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa.
Pakuti mliri woopsa udzafika,
ndipo udzakugonjetsani.
19 Ndipo ukadzangofika udzakutengani.
Udzafika mmawa uliwonse,
usiku ndi usana.”
Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu
adzaopsedwa kwambiri.
20 Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo;
ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.
21 Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu
adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni;
adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo,
ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
22 Tsopano lekani kunyoza,
mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri;
Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti,
“Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.”
23 Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga;
mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena.
24 Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha?
Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha?
25 Pamene iye wasalaza mundawo,
kodi samafesa mawere ndi chitowe?
Kodi suja samadzala tirigu
ndi barele mʼmizere yake,
nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?
26 Mulungu wake amamulangiza
ndi kumuphunzitsa njira yabwino.
27 Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero,
kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta;
mawere amapuntha ndi ndodo
ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.
28 Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi,
komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke.
Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta,
koma akavalo ake satekedza tiriguyo.
29 Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,
wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.
1 Ndine mkulu wampingo, kulembera:
Mayi wosankhidwa ndi Mulungu ndi kwa ana ake amene ndimawakonda mʼchoonadi. Ndipo sindine ndekha amene ndimawakonda, komanso onse odziwa choonadi. 2 Timakukondani chifukwa cha choonadi chimene chimakhala mwa ife ndipo chidzakhala mwa ife mpaka muyaya.
3 Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Yesu Khristu, Mwana wa Atate, zikhale ndi ife mʼchoonadi ndi mʼchikondi.
Choonadi ndi Chikondi
4 Ndinakondwera kwambiri nditapeza ana anu ena akuyenda mʼchoonadi, monga Atate anatilamulira. 5 Ndipo tsopano, amayi wokondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lomwe lija takhala nalo kuyambira pachiyambi. Ine ndikukupemphani kuti tidzikondana wina ndi mnzake. 6 Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.
7 Ndikunena zimenezi chifukwa anthu ambiri onyenga, amene savomereza kuti Yesu Khristu anabwera monga munthu, akuyenda mʼdziko lapansi. Munthu aliyense otere ndi wonyenga ndiponso wokana Khristu. 8 Chenjerani kuti mungataye chimene mwagwirira ntchito, koma chitani khama kuti mukalandire mphotho yanu yonse. 9 Aliyense amene sasunga chiphunzitso cha Khristu, alibe Mulungu. Koma amene amasunga chiphunzitsochi, ameneyo alinso ndi Atate ndi Mwana. 10 Ngati wina aliyense abwera kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamulandire mʼnyumba mwanu kapena kumupatsa moni. 11 Aliyense wolandira munthu wotere ndiye kuti akuvomerezana nazo ntchito zake zoyipa.
12 Ndili nazo zambiri zoti ndikulembereni, koma sindikufuna kuzilemba mʼkalata. Mʼmalo mwake, ndikuyembekeza kufika kwanuko kuti tidzakambirane nanu pamaso ndi pamaso, potero chimwemwe chathu chidzakhala chathunthu.
13 Ana a mlongo wanu wosankhidwa ndi Mulungu akupereka moni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.