M’Cheyne Bible Reading Plan
Malire a Dziko la Kanaani
34 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa:
3 “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere. 4 Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, 5 kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu.
6 “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo.
7 “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori 8 ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi, 9 ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto.
10 “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. 11 Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti. 12 Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere.
“ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ”
13 Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka, 14 chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo. 15 Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.”
16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni. 18 Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. 19 Mayina awo ndi awa:
Kalebe mwana wa Yefune,
wochokera ku fuko la Yuda,
20 Semueli mwana wa Amihudi,
wochokera ku fuko la Simeoni;
21 Elidadi mwana wa Kisiloni,
wochokera ku fuko la Benjamini;
22 Buki mwana wa Yogili,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani;
23 Hanieli mwana wa Efodi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe;
24 Kemueli mwana wa Sifitani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe.
25 Elizafani mwana wa Parinaki,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni;
26 Palitieli mwana wa Azani,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara,
27 Ahihudi mwana wa Selomi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri;
28 Pedaheli mwana wa Amihudi,
mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.”
29 Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani.
38 Komabe Iye anali wachifundo;
anakhululukira mphulupulu zawo
ndipo sanawawononge.
Nthawi ndi nthawi Iye anabweza mkwiyo wake
ndipo sanawutse ukali wake wonse.
39 Iye anakumbukira kuti iwo anali anthu chabe,
mphepo yopita imene sibwereranso.
40 Nthawi zambiri iwo ankamuwukira Iye mʼchipululu
ndi kumumvetsa chisoni mʼdziko lopanda kanthu!
41 Kawirikawiri iwo ankamuyesa Mulungu;
ankamuputa Woyera wa Israeli.
42 Sanakumbukire mphamvu zake,
tsiku limene Iye anawawombola kwa ozunza,
43 tsiku limene Iyeyo anaonetsa poyera zizindikiro zozizwitsa zake mu Igupto,
zozizwitsa zake mʼchigawo cha Zowani.
44 Iye anasandutsa mitsinje yawo kukhala magazi;
Iwo sanathe kumwa madzi ochokera mʼmitsinje yawo.
45 Iye anawatumizira magulu a ntchentche zimene zinawawononga,
ndiponso achule amene anawasakaza.
46 Iye anapereka mbewu zawo kwa ziwala,
zokolola zawo kwa dzombe.
47 Iye anawononga mphesa zawo ndi matalala
ndiponso mitengo yawo yankhuyu ndi chisanu.
48 Iye anapereka ngʼombe zawo ku matalala,
zoweta zawo ku zingʼaningʼani.
49 Anakhuthula moto wa ukali wake pa iwo,
anawapsera mtima nawakwiyira nʼkuwabweretsera masautso.
Zimenezi zinali ngati gulu la angelo osakaza.
50 Analolera kukwiya,
sanawapulumutse ku imfa
koma anawapereka ku mliri.
51 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
zipatso zoyamba kucha za mphamvu zawo mʼmatenti a Hamu
52 Koma Iye anatulutsa anthu ake ngati ziweto;
anawatsogolera ngati nkhosa kudutsa mʼchipululu.
53 Anawatsogolera bwinobwino kotero kuti analibe mantha
koma nyanja inamiza adani awo.
54 Kotero anawafikitsa ku malire a dziko lake loyera,
ku dziko lamapiri limene dzanja lake lamanja linawatengera.
55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu patsogolo pawo
ndipo anapereka mayiko awo kwa Aisraeli kuti akhale awo;
Iye anakhazikitsa mafuko a Israeli mʼnyumba zawo.
56 Koma iwo anayesa Mulungu
ndi kuwukira Wammwambamwamba;
sanasunge malamulo ake.
57 Anakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo awo,
anapotoka monga uta wosakhulupirika.
58 Anakwiyitsa Iyeyo ndi malo awo opembedzera mafano;
anawutsa nsanje yake ndi mafano awo.
59 Pamene Mulungu anamva zimenezi, anakwiya kwambiri;
Iye anakana Israeli kwathunthu.
60 Anasiya nyumba ya ku Silo,
tenti imene Iyeyo anayimanga pakati pa anthu.
61 Anatumiza mphamvu zake ku ukapolo,
ulemerero wake mʼmanja mwa adani.
62 Anapereka anthu ake ku lupanga;
anakwiya kwambiri ndi cholowa chake.
63 Moto unanyeketsa anyamata awo,
ndipo anamwali awo analibe nyimbo za ukwati;
64 ansembe awo anaphedwa ndi lupanga,
ndipo amayi awo amasiye sanathe kulira.
65 Kenaka Ambuye anakhala ngati akudzuka kutulo,
ngati munthu wamphamvu wofuwula chifukwa cha vinyo.
66 Iye anathamangitsa adani ake;
anawachititsa manyazi ku nthawi zonse.
67 Kenaka Iye anakana matenti a Yosefe,
sanasankhe fuko la Efereimu;
68 Koma anasankha fuko la Yuda,
phiri la Ziyoni limene analikonda.
69 Iye anamanga malo ake opatulika ngati zitunda,
dziko limene analikhazikitsa kwamuyaya.
70 Anasankha Davide mtumiki wake
ndi kumuchotsa pakati pa makola ankhosa;
71 kuchokera koyangʼanira nkhosa anamubweretsa
kuti akhale mʼbusa wa anthu ake, Yakobo,
wa Israeli cholowa chake.
72 Ndipo Davide anawaweta ndi mtima wolungama;
ndi manja aluso anawatsogolera.
Nyimbo ya Matamando
26 Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi.
Tili ndi mzinda wolimba.
Mulungu amawuteteza ndi zipupa
ndi malinga.
2 Tsekulani zipata za mzinda
kuti mtundu wolungama
ndi wokhulupirika ulowemo.
3 Inu mudzamupatsa munthu
wa mtima wokhazikika
mtendere weniweni.
4 Mudalireni Yehova mpaka muyaya,
chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.
5 Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba,
iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula,
amagumula makoma ake
ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.
6 Mapazi a anthu akuwupondereza,
mapazi a anthu oponderezedwa,
mapazi anthu osauka.
7 Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza,
Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.
8 Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,
ife timayembekezera Inu;
mitima yathu imakhumba kukumbukira
ndi kulemekeza dzina lanu.
9 Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;
nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.
Pamene muweruza dziko lapansi
anthu amaphunzira kuchita chilungamo.
10 Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa,
saphunzira chilungamo.
Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo,
ndipo sazindikira ululu wa Yehova.
11 Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange,
koma iwo sakuliona dzanjalo.
Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu;
ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
12 Yehova, mumatipatsa mtendere;
ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.
13 Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu,
koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.
14 Iwo tsopano sadzadzukanso;
mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa
pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga;
palibenso amene amawakumbukira.
15 Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu;
mwauchulukitsa ndithu
ndipo mwalandirapo ulemu;
mwaukuza mbali zonse za dziko.
16 Yehova, anthu anu anabwera kwa Inu pamene anali mʼmasautso;
pamene munawalanga,
iwo anapemphera kwa Inu.
17 Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikira
amamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu,
ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.
18 Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana,
koma sitinapindulepo kanthu,
kapena kupulumutsa dziko lapansi;
sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.
19 Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo;
matupi awo adzadzuka.
Iwo amene ali ku fumbi tsopano
adzadzuka ndi kuyimba mosangalala.
Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera,
momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.
20 Abale anga, pitani mukalowe mʼnyumba zanu
ndipo mukadzitsekere;
mukabisale kwa kanthawi kochepa
mpaka ukali wake utatha.
21 Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala;
akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo.
Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo;
dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.
Kuyesa Mizimu
4 Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi. 2 Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu, 3 koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.
4 Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi. 5 Aneneri onyengawa ndi ochokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake amayankhula za dziko lapansi, ndipo dziko lapansi limawamvera. 6 Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.
Mulungu ndiye Chikondi
7 Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu. 8 Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi. 9 Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo. 10 Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu. 11 Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake. 12 Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.
13 Ife tikudziwa kuti timakhala mwa Iye ndipo Iyeyo amakhala mwa ife chifukwa anatipatsa Mzimu wake. 14 Ndipo taona ndipo tikuchitira umboni, kuti Atate anatuma Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi. 15 Ngati aliyense avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye ndipo iyeyo amakhala mwa Mulungu. 16 Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife.
Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye. 17 Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu. 18 Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro.
19 Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda. 20 Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone. 21 Ndipo Iye anatipatsa lamulo lakuti: Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso mʼbale wake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.