Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 33

Malo omwe Aisraeli Anayima pa Ulendo Wawo

33 Malo otsatirawa ndi omwe Aisraeli anayima pa maulendo awo atatuluka mʼdziko la Igupto mʼmagulu awo motsogozedwa ndi Mose ndi Aaroni. Mose analemba malo amene anayambira maulendo awo molamulidwa ndi Yehova. Maulendo awo ndi malo omwe anayambira ndi awa:

Aisraeli ananyamuka kuchokera ku Ramesesi pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, itangotha Paska. Iwo anatuluka nayenda molimba mtima Aigupto onse akuona, pamene ankayika maliro a ana awo oyamba kubadwa, omwe Yehova anawakantha pakati pawo chifukwa Yehova anaweruza milungu yawo.

Aisraeli atachoka ku Ramesesi, anamanga misasa yawo ku Sukoti.

Atachoka ku Sukoti anakamanga misasa yawo ku Etamu, mʼmbali mwa chipululu.

Ndipo atachoka ku Etamu, anabwerera ku Pihahiroti, kummawa kwa Baala-Zefoni, ndipo anamanga misasa yawo pafupi ndi Migidoli.

Atachoka ku Pihahiroti anadutsa mʼkati mwa nyanja kupita ku chipululu ndipo atayenda masiku atatu mʼchipululu cha Etamu, anamanga misasa yawo ku Mara.

Atachoka ku Mara anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe a madzi khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa 70 ndipo anamanga misasa yawo kumeneko.

10 Atachoka ku Elimu anakamanga misasa yawo mʼmbali mwa Nyanja Yofiira.

11 Atachoka ku Nyanja Yofiira anakamanga misasa yawo mʼchipululu cha Sini.

12 Atachoka ku chipululu cha Sini anakamanga ku Dofika.

13 Atachoka ku Dofika anakamanga misasa yawo ku Alusi.

14 Atachoka ku Alusi anakamanga misasa yawo ku Refidimu, kumene kunalibe madzi woti anthu ndi kumwa.

15 Atachoka ku Refidimu anakamanga ku chipululu cha Sinai

16 Atachoka ku chipululu cha Sinai anakamanga misasa yawo ku Kiburoti-Hataava.

17 Atachoka ku Kiburoti-Hataava anakamanga misasa yawo ku Heziroti.

18 Atachoka ku Heziroti anakamanga ku Ritima.

19 Atachoka ku Ritima anakamanga ku Rimoni-Perezi.

20 Atachoka ku Rimoni-Perezi anakamanga ku Libina.

21 Atachoka ku Libina anakamanga ku Risa.

22 Atachoka ku Risa anakamanga ku Kehelata.

23 Atachoka ku Kehelata anakamanga ku phiri la Seferi.

24 Atachoka ku phiri la Seferi anakamanga ku Harada.

25 Atachoka ku Harada anakamanga ku Mekheloti.

26 Atachoka ku Mekheloti anakamanga ku Tahati.

27 Atachoka ku Tahati anakamanga ku Tera.

28 Atachoka ku Tera anakamanga ku Mitika.

29 Atachoka ku Mitika anakamanga ku Hasimona.

30 Atachoka ku Hasimona anakamanga ku Moseroti.

31 Atachoka ku Moseroti anakamanga ku Beni Yaakani.

32 Atachoka ku Beni Yaakani anakamanga ku Hori-Hagidigadi.

33 Atachoka ku Hori-Hagidigadi anakamanga ku Yotibata.

34 Atachoka ku Yotibata anakamanga ku Abirona.

35 Atachoka ku Abirona anakamanga ku Ezioni-Geberi.

36 Atachoka ku Ezioni-Geberi anakamanga ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini chimene ndi Kadesi.

37 Anachoka ku Kadesi ndi kukamanga ku phiri la Hori, mʼmalire mwa dziko la Edomu. 38 Molamulidwa ndi Yehova, wansembe Aaroni anakwera ku phiri la Hori kumene anakamwalirira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu, mʼchaka cha makumi anayi, Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto. 39 Aaroni anamwalira pa phiri la Hori ali ndi zaka 123.

40 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi yomwe inkakhala ku Negevi kummwera kwa Kanaani, inamva kuti Aisraeli akubwera.

41 Atachoka ku phiri la Hori anakamanga ku Zalimoni.

42 Atachoka ku Zalimoni anakamanga ku Punoni.

43 Atachoka ku Punoni anakamanga ku Oboti.

44 Atachoka ku Oboti anakamanga ku Iye-Abarimu.

45 Atachoka ku Iye-Abarimu anakamanga ku Diboni Gadi.

46 Atachoka ku Diboni Gadi anakamanga ku Alimoni-Dibulataimu.

47 Atachoka ku Alimoni-Dibulataimu anakamanga mʼmapiri a Abarimu, pafupi ndi Nebo.

48 Atachoka ku mapiri a Abarimu anakamanga ku zigwa za Mowabu mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko. 49 Ali ku zigwa za Mowabu anamanga mʼmbali mwa Yorodani kuchokera ku Beti-Yesimoti mpaka ku Abeli-Sitimu.

50 Pa zigwa za Mowabu, mʼmbali mwa Yorodani moyangʼanana ndi ku Yeriko, Yehova anawuza Mose kuti, 51 “Nena kwa Aisraeli kuti, ‘Pamene muwoloka Yorodani kulowa mʼdziko la Kanaani, 52 mukathamangitse nzika zonse za mʼdzikomo pamaso panu. Mukawononge mafano awo onse a miyala ndi osula ndi malo awo achipembedzo. 53 Mukalande dzikolo ndi kukhalamo chifukwa ndakupatsani dziko limenelo kuti mukhalemo. 54 Mukagawane dzikolo pochita maere monga mwa mafuko anu. Kwa omwe ali ambiri, cholowa chambiri, ndipo amene ali ocheperapo, chocheperanso. Chilichonse chimene chidzawagwere iwo mwa maere chidzakhala chawo. Mukaligawane monga mwa mafuko a makolo anu.

55 “ ‘Koma ngati simukathamangitsa nzika zimene zili mʼdzikomo, amene mukawalole kukhalamo adzakhala ngati zisonga mʼmaso mwanu ndi ngati minga mʼmbali mwanu. Adzakubweretserani mavuto mʼdziko limene mudzakhalemolo. 56 Ndipo pamenepo ndidzachitira inu zomwe ndinaganiza kuwachitira iwowo.’ ”

Masalimo 78:1-37

Ndakatulo ya Asafu.

78 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa;
    mvetserani mawu a pakamwa panga.
Ndidzatsekula pakamwa panga mʼmafanizo,
    ndidzayankhula zinthu zobisika, zinthu zakalekale
zimene tinazimva ndi kuzidziwa,
    zimene makolo athu anatiwuza.
Sitidzabisira ana awo,
    tidzafotokozera mʼbado wotsatira
ntchito zotamandika za Yehova,
    mphamvu zake, ndi zozizwitsa zimene Iye wachita.
Iye anapereka mawu wodzichitira umboni kwa Yakobo
    ndi kukhazikitsa lamulo mu Israeli,
zimene analamulira makolo athu
    kuphunzitsa ana awo,
kotero kuti mʼbado wotsatira uthe kuzidziwa,
    ngakhale ana amene sanabadwe,
    ndi kuti iwo akafotokozere ana awonso.
Choncho iwo adzakhulupirira Mulungu
    ndipo sadzayiwala ntchito zake
    koma adzasunga malamulo ake.
Iwo asadzakhale monga makolo awo,
    mʼbado wosamvera ndi wowukira,
umene mitima yake inali yosamvera Mulungu,
    umene mizimu yake inali yosakhulupirika kwa Iye.

Anthu a ku Efereimu, ngakhale ananyamula mauta,
    anathawabe pa nthawi ya nkhondo;
10 iwo sanasunge pangano la Mulungu
    ndipo anakana kukhala mʼmoyo wotsatira lamulo lake.
11 Anayiwala zimene Iye anachita,
    zozizwitsa zimene anawaonetsa.
12 Iyeyo anachita zodabwitsa makolo athu akuona,
    mʼdziko la Igupto, mʼchigawo cha Zowani.
13 Anagawa nyanja pakati ndi kudutsitsapo iwowo,
    Iye anachititsa madzi kuyima chilili ngati khoma.
14 Anawatsogolera ndi mtambo masana
    ndi kuwala kwa moto usiku wonse.
15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu
    ndi kuwapatsa madzi ochuluka ngati a mʼnyanja zambiri;
16 Anatulutsa mitsinje kuchokera mʼmingʼalu ya miyala
    ndi kuyenda madzi ngati mitsinje.

17 Komabe iwowo anapitiriza kumuchimwira Iye,
    kuwukira Wammwambamwamba mʼchipululu.
18 Ananyoza Mulungu mwadala
    pomuwumiriza kuti awapatse chakudya chimene anachilakalaka.
19 Iwo anayankhula motsutsana naye ponena kuti,
    “Kodi Mulungu angatipatse chakudya mʼchipululu?
20 Iye atamenya thanthwe
    madzi anatuluka,
    ndipo mitsinje inadzaza ndi madzi.
Koma iye angatipatsenso ife chakudya?
    Kodi angapereke nyama kwa anthu akewa?”
21 Yehova atawamva anakwiya kwambiri;
    moto wake unayaka kutsutsana ndi Yakobo,
    ndipo mkwiyo wake unauka kutsutsana ndi Israeli,
22 pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu
    kapena kudalira chipulumutso chake.
23 Komabe Iye anapereka lamulo kwa mitambo mmwamba
    ndi kutsekula makomo a mayiko akumwamba;
24 anagwetsa mana kuti anthu adye,
    anawapatsa tirigu wakumwamba.
25 Anthu anadya buledi wa angelo,
    Iye anawatumizira chakudya chonse chimene akanatha kudya.
26 Anamasula mphepo ya kummwera kuchokera kumwamba,
    ndi kutsogolera mphepo ya kummwera mwa mphamvu zake.
27 Iye anawagwetsera nyama ngati fumbi,
    mbalame zowuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
28 Anazibweretsa kwa iwo mʼkati mwa misasa yawo,
    kuzungulira matenti awo onse.
29 Iwo anadya mpaka anatsala nazo zochuluka
    pakuti Iye anawapatsa zimene anazilakalaka.
30 Koma iwowo anasiya kudya chakudya anachilakalakacho,
    chakudya chili mʼkamwa mwawobe,
31 mkwiyo wa Mulungu unawayakira;
    Iye anapha amphamvu onse pakati pawo,
    kugwetsa anyamata abwino kwambiri mu Israeli.

32 Ngakhale zinali chomwechi, iwo anapitirira kuchimwa;
    ngakhale anaona zozizwitsa zakezo iwowo sanakhulupirirebe.
33 Kotero Mulungu anachepetsa masiku awo kuti azimirire ngati mpweya.
    Iye anachepetsa zaka zawo kuti zithere mʼmasautso.
34 Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo;
    iwo ankatembenukiranso kwa Iye mwachangu.
35 Ankakumbukira kuti Mulungu ndiye Thanthwe lawo,
    kuti Mulungu Wammwambamwamba ndiye Mpulumutsi wawo.
36 Komabe ankamuthyasika ndi pakamwa pawo,
    kumunamiza ndi malilime awo;
37 Mitima yawo sinali yokhazikika pa Iye,
    iwo sanakhulupirike ku pangano lake.

Yesaya 25

Nyimbo Yotamanda Yehova

25 Yehova ndinu Mulungu wanga;
    ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu,
pakuti mwachita zodabwitsa
    zimene munakonzekeratu kalekale
    mokhulupirika kwambiri.
Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala.
    Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja,
linga la anthu achilendo lero si mzindanso
    ndipo sidzamangidwanso.
Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani;
    mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.
Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka,
    mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake.
Mwakhala ngati pobisalirapo
    pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa.
Pakuti anthu ankhanza
    ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,
    ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma.
Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo.
    Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha,
    inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.

Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera
    anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino.
Phwando la nyama yonona
    ndi vinyo wabwino kwambiri.
Iye adzachotsa kulira
    kumene kwaphimba anthu ngati nsalu.
Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.
    Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya,
Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso
    mwa munthu aliyense;
adzachotsa manyazi a anthu ake
    pa dziko lonse lapansi,
            Yehova wayankhula.

Tsiku limenelo iwo adzati,

“Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu;
    ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa.
Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira;
    tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”

10 Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake;
    ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo,
    ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.
11 Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo,
    ngati mmene amachitira munthu wosambira.
Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo
    ngakhale luso la manja awo.
12 Iye adzagumula malinga awo ataliatali
    ndipo adzawagwetsa
ndi kuwaponya pansi,
    pa fumbi penipeni.

1 Yohane 3

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye. Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.

Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo. Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo. Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.

Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama. Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi. Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu. 10 Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.

Kukondana Wina ndi Mnzake

11 Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake. 12 Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama. 13 Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. 14 Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. 15 Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.

16 Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu. 17 Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? 18 Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi. 19 Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu, 20 nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.

21 Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu. 22 Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa. 23 Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira. 24 Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.