Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 32

Mafuko a ku Tsidya la Yorodani

32 Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo. Choncho Arubeni ndi Agadi anapita kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa atsogoleri a anthu ndi kunena kuti, “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni, Eleali, Sebamu, Nebo ndi Beoni, dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto. Iwo anati, ‘Ngati tapeza ufulu pamaso panu atumiki anufe, mutipatse dziko limeneli kuti likhale lathu. Tisawoloke nanu Yorodani.’ ”

Ndipo Mose anati kwa Agadi ndi Arubeni, “Kodi anthu a mtundu wanu apite ku nkhondo inu mutangokhala kuno? Chifukwa chiyani mukufowoketsa Aisraeli kupita mʼdziko limene Yehova wawapatsa? Izi ndi zimene makolo anu anachita pamene ndinawatuma kuchokera ku Kadesi kukaona dzikolo. Atapita ku chigwa cha Esikolo, ndi kuliona dzikolo, anafowoketsa Aisraeli kuti asalowe mʼdziko limene Yehova anawapatsa. 10 Yehova anakwiya tsiku limenelo ndipo analumbira kuti, 11 ‘Chifukwa sananditsatire ndi mtima wonse, palibe ndi mmodzi yemwe mwa amuna a zaka makumi awiri kapena kuposa pamenepo, amene anachokera ku Igupto, amene adzaone dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 12 Palibe ndi mmodzi yemwe kupatula Kalebe mwana wa Yefune, Mkeni, ndi Yoswa mwana wa Nuni chifukwa anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’ 13 Yehova anakwiyira Aisraeli kwambiri ndipo anawachititsa kuyenda mʼchipululu zaka makumi anayi, mpaka mʼbado wonse wa anthu amene anachita choyipa pamaso pake unatha.

14 “Ndipo onani tsopano, inu mʼbado wochimwa, mwalowa mʼmalo mwa makolo anu ndipo mwachititsa kuti Yehova akwiyire Israeli kwambiri. 15 Ngati muleka kumutsata, Iye adzawasiyiranso anthu onsewa mʼchipululu ndipo mudzawonongetsa anthu onsewa.”

16 Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu. 17 Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli. 18 Sitidzabwerera ku midzi yathu mpaka Mwisraeli aliyense atalandira cholowa chake. 19 Sitidzalandira cholowa chilichonse pamodzi nawo ku tsidya lina la Yorodani, chifukwa cholowa chathu tachipezera ku tsidya lino la kummawa kwa Yorodani.”

20 Tsono Mose anati kwa anthuwo, “Ngati inu mudzachita zimenezi, kutenga zida zankhondo pamaso pa Yehova kuti muchite nkhondo, 21 ndipo ngati nonsenu mudzapita ndi zida kuwoloka Yorodani pamaso pa Yehova mpaka atachotsa adani ake pamaso pake, 22 dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.

23 “Koma mukalephera kuchita izi, mudzakhala mukuchimwira Yehova. Ndipo dziwani kuti tchimo lanu lidzakupezani. 24 Amangireni akazi ndi ana anu mizinda, mangani makola a ziweto zanu, koma chitani zomwe mwalonjeza.”

25 Agadi ndi Arubeni anati kwa Mose, “Ife antchito anu tidzachita monga mbuye wathu mwalamulira. 26 Ana ndi akazi athu, ziweto zathu zina ndi ngʼombe zidzatsala kuno ku mizinda ya Giliyadi, 27 koma antchito anufe, mwamuna aliyense amene ali ndi chida cha nkhondo, adzawoloka kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova monga mbuye wathu wanenera.”

28 Choncho Mose anapereka malamulo awa kwa wansembe Eliezara, kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa akulu a mafuko a Aisraeli. 29 Mose anawawuza kuti, ngati Agadi ndi Arubeni, mwamuna aliyense wokonzekera nkhondo, awoloka Yorodani pamodzi ndi inu pamaso pa Yehova, ndipo dzikolo nʼkugonjetsedwa pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kukhala lawo. 30 Koma ngati sawoloka pamodzi nanu ndi zida zankhondo, ayenera kulandira cholowa chawo pamodzi ndi inu ku Kanaani.

31 Agadi ndi Arubeni anayankha kuti, “Antchito anu adzachita zimene Yehova wanena. 32 Tidzawoloka pamaso pa Yehova ndipo tidzalowa mu Kanaani ndi zida zankhondo, koma cholowa chathu chidzakhala ku tsidya lino la Yorodani.”

33 Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira.

34 Agadi anamanga Diboni, Ataroti, Aroeri, 35 Atiroti-Sofani, Yazeri, Yogibeha, 36 Beti-Nimira ndi Beti-Harani mizinda ya malinga. Anamanganso makola a ziweto zawo. 37 Ndipo Arubeni anamanga Hesiboni, Eleali, Kiriataimu, 38 Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo.

39 Zidzukulu za Makiri mwana wa Manase zinapita ku Giliyadi kulanda mzindawo ndi kuthamangitsira kunja Aamori omwe anali kumeneko. 40 Tsono Mose anapereka Giliyadi kwa Amakiri, ana a Manase, ndipo anakhala kumeneko. 41 Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi. 42 Ndipo Noba analanda Kenati ndi midzi yozungulira ndi kuyitcha Noba, kutengera dzina la iye mwini.

Masalimo 77

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu.

77 Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo;
    ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye;
    usiku ndinatambasula manja mosalekeza
    ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.

Ndinakumbukira Inu Mulungu, ndipo ndinabuwula;
    ndinasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unalefuka.
            Sela
Munagwira zikope zanga kuti ndisagone
    ndipo ndinavutika kwambiri kuti ndiyankhule.
Ndinaganizira za masiku akale,
    zaka zamakedzana;
Ndinakumbukira nyimbo zanga usiku.
    Mtima wanga unasinkhasinkha ndipo mzimu wanga unafunsa kuti,

“Kodi Ambuye adzatikana mpaka muyaya?
    Kodi Iwo sadzaonetsanso kukoma mtima kwawo?
Kodi Chikondi chake chosatha chija chatheratu?
    Kodi malonjezo ake alephera nthawi yonse?
Kodi Mulungu wayiwala kukhala wokoma mtima?
    Kodi mu mkwiyo wake waleka chifundo chake?”

10 Ndipo ndinaganiza, “Pa izi ine ndidzapemphanso:
    zaka za dzanja lamanja la Wammwambamwamba.
11 Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova;
    Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12 Ndidzakumbukira ntchito zanu
    ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”

13 Njira zanu Mulungu ndi zoyera.
    Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14 Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa;
    Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15 Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu,
    zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe.
            Sela

16 Madzi anakuonani Mulungu,
    madzi anakuonani ndipo anachita mantha;
    nyanja yozama inakomoka.
17 Mitambo inakhuthula madzi ake pansi,
    mu mlengalenga munamveka mabingu;
    mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu,
    mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 Njira yanu inadutsa pa nyanja,
    njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu,
    ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.

20 Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa
    mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.

Yesaya 24

Chilango cha Yehova pa Dziko Lapansi

24 Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansi
    ndi kulisandutsa chipululu;
Iye adzasakaza maonekedwe ake
    ndi kumwaza anthu ake onse.
Aliyense zidzamuchitikira mofanana:
    wansembe chimodzimodzi munthu wamba,
    antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna,
    antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi,
    wogula chimodzimodzi wogulitsa,
    wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa,
    okongola chimodzimodzi okongoza.
Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthu
    ndi kusakazikiratu.
            Yehova wanena mawu awa.

Dziko lapansi likulira ndipo likufota,
    dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma,
    anthu omveka a dziko lapansi akuvutika.
Anthu ayipitsa dziko lapansi;
    posamvera malangizo ake;
pophwanya mawu ake
    ndi pangano lake lamuyaya.
Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi;
    anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo,
iwo asakazika
    ndipo atsala ochepa okha.
Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota;
    onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni.
Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha,
    phokoso la anthu osangalala latha,
    zeze wosangalatsa wati zii.
Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo;
    akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo.
10 Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka;
    nyumba iliyonse yatsekedwa.
11 Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo;
    chimwemwe chonse chatheratu,
    palibenso chisangalalo pa dziko lapansi.
12 Mzinda wasanduka bwinja
    zipata zake zagumuka.
13 Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi
    ndiponso pakati pa mitundu ya anthu.
Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa,
    kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.

14 Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe;
    anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.
15 Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova;
    ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.
16 Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda
    “Wolungamayo.”

Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu!
    Tsoka kwa ine!
Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo,
    inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”
17 Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenje
    ndi msampha zikukudikirani.
18 Aliyense wothawa phokoso la zoopsa
    adzagwa mʼdzenje;
ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo
    adzakodwa ndi msampha.

Zitseko zakumwamba zatsekulidwa,
    ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.
19 Dziko lapansi lathyokathyoka,
    ndipo lagawika pakati,
    dziko lapansi lagwedezeka kotheratu.
20 Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera
    likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba;
lalemedwa ndi machimo ake.
    Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.

21 Tsiku limenelo Yehova adzalanga
    amphamvu a kumwamba
    ndiponso mafumu apansi pano.
22 Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi
    ngati amʼndende amene ali mʼdzenje.
Adzawatsekera mʼndende
    ndipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali.
23 Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi;
    pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira;
pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu,
    ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.

1 Yohane 2

Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo. Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi.

Chikondi ndi Chidani

Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake. Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi. Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye. Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala.

Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lakale lomwe lija, limene munali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo la kalelo ndi mawu amene munawamva kale. Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala.

Aliyense amene amati ali mʼkuwunika, koma nʼkumadana ndi mʼbale wake ali mu mdima. 10 Aliyense amene amakonda mʼbale wake amakhalanso mʼkuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. 11 Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake.

12 Inu ana okondedwa, ndikukulemberani
    popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.
13 Inu abambo, ndikukulemberani
    popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
    popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
14 Ana okondedwa, ndikukulemberani
    chifukwa mumawadziwa Atate.
Abambo, ndikukulemberani
    chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
    chifukwa ndinu amphamvu.
    Mawu a Mulungu amakhala mwa inu
    ndipo mumamugonjetsa woyipayo.

Musakonde Dziko Lapansi

15 Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate. 16 Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17 Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.

Anthu Okana Khristu

18 Ana anga, ino ndi nthawi yotsiriza, ndipo monga munamva kale kuti anthu okana Khristu akubwera, ngakhale tsopano okana Khristu ambiri afika kale. Zimenezi zikutisonyeza kuti ino ndi nthawi yotsiriza. 19 Anthu amenewa anachoka pakati pathu, komatu sanali a mʼgulu lathu. Pakuti akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe nafe, koma kuchoka kwawo kunatisonyeza kuti sanali a mʼgulu lathu.

20 Koma inu muli ndi kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo nonsenu mukudziwa choonadi. 21 Sindikukulemberani chifukwa choti simudziwa choonadi ayi, koma chifukwa choti mumadziwa choonadicho, ndipo mukudziwanso kuti bodza silichokera pa choonadi. 22 Wabodzayo ndani? Ndi munthu aliyense amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi. Munthu woteroyo ndi wokana Khristu, ndiponso amakana Atate, ndi Mwana. 23 Aliyense wokana Mwana alibenso Atate. Wovomereza Mwana alinso ndi Atate.

24 Onetsetsani kuti zimene munazimva kuyambira pachiyambi zikhalebe mwa inu. Ngati zikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndiponso mwa Atate. 25 Ndipo chimene anatilonjeza nʼchimenechi: moyo wosatha.

26 Ine ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuwuzeni za amene akufuna kukusocheretsani. 27 Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo.

Ana a Mulungu

28 Tsopano ana okondedwa, khalani mwa Yesu, kuti pamene adzaonekera, ife tidzakhale otsimikizika mu mtima ndi wopanda manyazi pamaso pake akamadzabwera.

29 Popeza mukudziwa kuti Khristu ndi wolungama, choncho mukudziwanso kuti aliyense amene amachita chilungamo ndi mwana wa Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.