M’Cheyne Bible Reading Plan
Aisraeli Agonjetsa Amidiyani
31 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Uwabwezere zoyipa Amidiyani chifukwa cha zimene anachitira Aisraeli. Ukatha kuchita zimenezi, iwe udzamwalira.”
3 Ndipo Mose anati kwa Aisraeli, “Perekani zida kwa ena mwa anthu anu kuti akamenyane ndi Amidiyani ndi kuwabwezera choyipa mʼmalo mwa Yehova. 4 Mutumize ku nkhondoko amuna 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli.” 5 Choncho amuna okwana 12,000 anatenga zida kukonzekera nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse la Aisraeli. 6 Mose anawatumiza ku nkhondo, anthu 1,000 kuchokera ku fuko lililonse pamodzi ndi Finehasi mwana wa Eliezara wansembe amene ananyamula zipangizo zochokera ku malo wopatulika ndi malipenga okaliza.
7 Iwo anamenyana ndi Amidiyani monga momwe Yehova analamulira Mose ndipo anapha mwamuna aliyense. 8 Mwa anthu ophedwawo munali Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani. Ndipo anaphanso ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori. 9 Aisraeli anagwira ukapolo amayi a Chimidiyani ndi ana awo ndipo analandanso ngʼombe, ziweto zawo zina zonse ndi katundu wawo yense. 10 Anawotcha mizinda yonse imene Amidiyani ankakhalamo pamodzi ndi misasa yawo yonse. 11 Anatenga zonse zimene analanda ku nkhondoko, anthu ndi zoweta zomwe. 12 Ndipo anabwera nawo akapolowo ndi zolanda ku nkhondozo kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa gulu lonse la Aisraeli ku misasa yawo ku chigwa cha Mowabu, mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko.
13 Mose, wansembe Eliezara ndi atsogoleri onse a gululo anapita kukakumana nawo kunja kwa misasa. 14 Mose anakwiya nawo akuluakulu a magulu a ankhondowo: olamulira 1,000 ndi olamulira 100, amene ankachokera ku nkhondo.
15 Iye anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mwawaleka amoyo amayi onsewa?” 16 Paja iwo ndi amene ankatsatira uphungu wa Balaamu ndiponso ndi amene anachititsa Aisraeli kuti asiye Yehova pa zimene zinachitika ku Peori, kotero mliri unagwera anthu a Yehova. 17 Tsopano iphani munthu wamwamuna aliyense. Ndiponso iphani mayi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna, 18 koma sungani mtsikana aliyense amene sanagonepo ndi mwamuna.
19 “Inu nonse amene mwaphapo wina wake, kapena kukhudza aliyense amene anaphedwa mukhale kunja kwa msasa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku lachitatu mudziyeretse nokha pamodzi ndi akapolo anu. 20 Muyeretsenso zovala zanu ndi china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, ubweya wa mbuzi kapenanso ndi mtengo.”
21 Tsono wansembe Eliezara anati kwa asilikali amene anapita ku nkhondo aja, “Lamulo limene Yehova anapereka kwa Mose ndi ili: 22 Golide, siliva, mkuwa, chitsulo, chiwaya, mtovu 23 ndi china chilichonse chimene sichingapse ndi moto muchidutsitse pa moto, ndipo chidzayeretsedwa. Komanso chiyeretsedwe ndi madzi oyeretsa. Ndipo chilichonse chimene chingapse ndi moto muchidutsitse mʼmadzimo. 24 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muchape zovala zanu ndipo mudzayera. Mukatero mutha kulowa mu msasa.”
Kugawana Zolanda ku Nkhondo
25 Yehova anawuza Mose kuti, 26 “Iwe ndi wansembe Eliezara ndiponso akuluakulu a mabanja a anthuwa, muwerenge anthu onse ndi ziweto zomwe zinagwidwa ku nkhondo. 27 Mugawe zolanda ku nkhondozo magawo awiri, lina la ankhondo amene anapita ku nkhondo, lina la anthu onse. 28 Pa gawo la ankhondowo, mutengeko gawo la Yehova, pa zofunkha 500 zilizonse mutengeko chimodzi, pa akapolo, ngʼombe, bulu ndi nkhosa. 29 Utenge zimenezo pa theka la gawo la ankhondowo ndipo upereke kwa wansembe Eliezara kuti zikhale zopereka zanu kwa Yehova. 30 Kuchokera pa theka la gawo la Aisraeli, utengeko cholanda chimodzi pa makumi asanu aliwonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa, mbuzi kapena zoweta zina. Uzipereke kwa Alevi amene ntchito yawo ndi yosamalira tenti ya Yehova.” 31 Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara anachita monga Yehova analamulira Mose.
32 Zotsala pa zolanda ku nkhondo zimene ankhondowo anatenga zinali nkhosa 675,000, 33 Ngʼombe 72,000, 34 abulu 61,000, 35 ndi atsikana omwe sanagonepo ndi mwamuna 32,000.
36 Gawo la ankhondo amene anapita ku nkhondo linali:
nkhosa 337,500, 37 mwa zimenezi gawo la Yehova linali 675;
38 ngʼombe zinalipo 36,000 ndipo gawo la Yehova linali 72;
39 abulu analipo 30,500 ndipo gawo la Yehova linali 61;
40 anthu analipo 16,000 ndipo gawo la Yehova linali 32.
41 Mose anapereka kwa wansembe Eliezara gawo limene linali loyenera kupereka kwa Yehova monga momwe Yehova analamulira Mose.
42 Pa gawo la Aisraeli, Mose anapatula theka limodzi kuchotsa pa zolanda ku nkhondo zonse zimene zinabwera ndi ankhondo aja. 43 Tsono gawo la Aisraeli linali ili: nkhosa 337,500, 44 ngʼombe 36,000, 45 abulu 30,500, 46 anthu 16,000. 47 Kuchoka pa gawo la Aisraelilo, Mose anatengapo chimodzi pa zolanda ku nkhondo makumi asanu aliwonse, anthu ndi nyama, ndipo anazipereka kwa Alevi amene ankayangʼanira tenti ya Yehova monga Yehova analamulira Mose.
48 Pamenepo omwe ankayangʼanira magulu a ankhondo olamulira 1,000 ndi olamulira 100 anabwera kwa Mose, 49 iwo anati kwa iye, “Ife anthu anu tawerenga ankhondo amene timawalamulira. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene wasowa. 50 Ndipo tabweretsa zopereka kwa Yehova zimene munthu aliyense anapeza: ziwiya zagolide, zibangiri, zigwinjiri, mphete zosindikizira, ndolo ndi mikanda kuti tichitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova.”
51 Ndipo Mose ndi wansembe Eliezara analandira kuchokera kwa atsogoleriwo golide pamodzi ndi zipangizo zonse zosula. 52 Golide yense wochokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 zomwe Mose ndi Eliezara anapereka ngati mphatso kwa Yehova zinali zolemera makilogalamu 200. 53 Wankhondo aliyense anatenga zomwe analanda yekha ku nkhondo. 54 Mose ndi Eliezara wansembe analandira golide kuchokera kwa atsogoleri a 1,000 ndi atsogoleri a 100 ndi kukamuyika mu tenti ya msonkhano ngati chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo.
75 Tikuthokoza Inu Mulungu,
tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,
anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
2 Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera,
ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,
ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.
Sela
4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’
ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;
musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”
6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo
kapena ku chipululu.
7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza:
Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho
chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;
Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi
amamwa ndi senga zake zonse.
9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;
ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa
koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu.
76 Mulungu amadziwika mu Yuda;
dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.
2 Tenti yake ili mu Salemu,
malo ake okhalamo mu Ziyoni.
3 Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka,
zishango ndi malupanga, zida zankhondo.
Sela
4 Wolemekezeka ndinu,
wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.
5 Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma,
Iwowo amagona tulo tawo totsiriza;
palibe mmodzi wamphamvu
amene angatukule manja ake.
6 Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo,
kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.
7 Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa.
Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?
8 Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo,
ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,
9 pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze,
kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko.
Sela
10 Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando
ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.
11 Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse;
anthu onse omuzungulira abweretse mphatso
kwa Iye amene ayenera kuopedwa.
12 Iye amaswa mzimu wa olamulira;
amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.
Za Chilango cha Turo
23 Uthenga wonena za Turo:
Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi:
pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa
ndipo mulibe nyumba kapena dooko.
Zimenezi anazimva
pochokera ku Kitimu.
2 Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja,
inu amalonda a ku Sidoni,
iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.
3 Pa nyanja zazikulu
panabwera tirigu wa ku Sihori;
zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malonda
ndi anthu a mitundu ina.
4 Chita manyazi, iwe Sidimu
pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti,
“Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana;
sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”
5 Mawuwa akadzamveka ku Igupto,
iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.
6 Wolokerani ku Tarisisi,
lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.
7 Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja,
mzinda wakalekale,
umene anthu ake ankapita
kukakhala ku mayiko akutali?
8 Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina,
mzinda umene amalonda ake ndi akalonga
ndi otchuka
pa dziko lapansi?
9 Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezi
kuti athetse kunyada kwawo
ndi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.
10 Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo
inu anthu a ku Tarisisi,
pakuti mulibenso chokutetezani.
11 Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanja
ndipo wagwedeza maufumu ake.
Iye walamula kuti Kanaani
agwetse malinga ake.
12 Iye anati, “Simudzakondwanso konse,
inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa!
“Ngakhale muwolokere ku Kitimu,
kumeneko simukapezako mpumulo.”
13 Onani dziko la Ababuloni,
anthu amenewa tsopano atheratu!
Asiriya asandutsa Turo kukhala
malo a zirombo za ku chipululu;
anamanga nsanja zawo za nkhondo,
anagumula malinga ake
ndipo anawasandutsa bwinja.
14 Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi;
chifukwa malinga ako agwetsedwa!
15 Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:
16 “Tenga zeze wako uzungulire mzinda,
iwe mkazi wachiwerewere woyiwalika;
imba zeze mokometsera, imba nyimbo zambiri,
kuti anthu akukumbukire.”
17 Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi. 18 Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.
Mawu a Moyo
1 Tikukulalikirani za Mawu a moyo amene analipo kuyambira pachiyambi, amene tinawamva, amene tinawaona ndi maso athu, amene tinawapenyetsetsa, ndipo tinawakhudza ndi manja athu. 2 Moyowo unaoneka, tinawuona ndipo tikuchitira umboni. Tikukulalikirani za moyo wosatha umene unali ndi Atate ndipo unaonekera kwa ife. 3 Tikukulalikirani chimene tinachiona ndi kumva, kuti inuyo muyanjane nafe. Kuyanjana kwathu, tikuyanjana ndi Atate ndiponso ndi Mwana wawo, Yesu Khristu. 4 Tikukulemberani zimenezi kuti chimwemwe chathu chikhale chathunthu.
Kuyenda mu Kuwunika
5 Uthenga umene tinamva kwa Iye ndipo tikuwulalikira kwa inu ndi uwu: Mulungu ndiye kuwunika ndipo mwa Iye mulibe mdima konse. 6 Tikanena kuti timayanjana naye, koma nʼkumayendabe mu mdima, tikunama ndipo sitikuchita choonadi. 7 Koma tikamayenda mʼkuwunika, monga Iye ali mʼkuwunika, pamenepo timayanjana wina ndi mnzake, ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Kuwulula Machimo ndi Kukhululukidwa
8 Tikanena kuti tilibe tchimo, tikudzinyenga tokha ndipo mwa ife mulibe choonadi. 9 Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera chosalungama chilichonse. 10 Ife tikanena kuti sitinachimwe, tikumutenga Mulungu kukhala wonama, ndipo Mawu ake sali mwa ife.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.