M’Cheyne Bible Reading Plan
Za Kulumbira
30 Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi: 2 Munthu wamwamuna ngati walonjeza kwa Yehova kapena kulumbira kuti adzachita zimene walumbirazo, asaphwanye mawuwo koma ayenera kuchita chilichonse chimene wanena.
3 “Pamene munthu wamkazi amene akukhalabe mʼnyumba ya abambo ake alumbira kwa Yehova kuti adzachita zimene walonjeza pa ubwana wake, 4 abambo ake namva kulumbira kwakeko kapena kulonjeza kwake kuti adzachitadi, ndipo abambo akewo wosayankhula kanthu, mkaziyo achitedi zomwe analumbirazo. Ayenera kudzachita zonse zimene walonjeza zija. 5 Koma ngati abambo akewo amva kulumbira kwake ndi kumukaniza, palibe lamulo lomukakamiza mkaziyo kuchita zimene walonjeza. Yehova adzamukhululukira chifukwa abambo ake anamukaniza.
6 “Ngati akwatiwa atalumbira kale kapena ngati alonjeza mofulumira ndi pakamwa pake, 7 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma wosanenapo kanthu, mkaziyo achitedi zomwe walumbirazo. Achite ndithu zomwe walonjeza zija. 8 Koma ngati mwamuna wake amuletsa atamva kulumbira kwakeko, pamenepo amumasula mayiyo ku zimene analumbira komanso ku zimene analonjeza mosaganiza bwinozo ndipo Yehova adzamukhululukira.
9 “Mayi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi.
10 “Koma ngati mayi wokwatiwa alumbira nalonjeza kuti adzachitadi zimene walonjeza, 11 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma osayankhulapo kanthu, osamuletsa, ayenera kuchitadi zonse zimene walumbira ndi zonse zimene walonjeza. 12 Koma ngati mwamuna wake amva ndi kumuletsa kuti asachite zomwe walumbirazo, palibe lamulo lomukakamiza mayiyo kuchita zomwe walumbirazo kapenanso zimene walonjeza. Popeza mwamuna wake wamuletsa, Yehova adzamukhululukira mayiyo. 13 Mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana zimene mayiyo walumbira kapena zimene walonjeza zokhudza kudzilanga yekha. 14 Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira. 15 Koma ngati mwamunayo amukaniza patapita kanthawi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa mʼmalo mwa mayiyo.”
16 Awa ndiwo malamulo amene Yehova analamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso abambo ndi mwana wawo wamkazi amene akanali mtsikana wokhalabe mʼnyumba ya abambo akewo.
Ndakatulo ya Asafu.
74 Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu?
Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu?
2 Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale,
fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola,
phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala.
3 Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya
chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika.
4 Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe;
anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso.
5 Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo
kuti adule mitengo mʼnkhalango.
6 Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo
zonse zimene tinapachika.
7 Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi;
anadetsa malo okhalamo dzina lanu.
8 Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.”
Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo.
9 Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa;
palibe aneneri amene atsala
ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji.
10 Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu?
Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya?
11 Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja?
Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge!
12 Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale;
Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi.
13 Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu;
munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi.
14 Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani
ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu.
15 Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje,
munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse.
16 Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso;
Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi.
17 Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi;
munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja.
18 Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova,
momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.
19 Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo;
nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa.
20 Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko
asanduka mochitira zachiwawa zochuluka.
21 Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi;
osauka ndi osowa atamande dzina lanu.
22 Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu;
kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse.
23 Musalekerere phokoso la otsutsana nanu,
chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza.
Za Chilango cha Yerusalemu
22 Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya:
Kodi chachitika nʼchiyani,
kuti nonsenu mukwere pa madenga?
2 Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,
iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?
Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,
kapena kufera pa nkhondo.
3 Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi;
koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe.
Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo,
ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
4 Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;
ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.
Musayesere kunditonthoza
chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
5 Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione
mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo
mʼChigwa cha Masomphenya.
Malinga agumuka,
komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
6 Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta
ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.
Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
7 Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,
ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
8 zonse zoteteza Yuda zachotsedwa.
Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana
zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
9 inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide
anali ndi malo ambiri ogumuka;
munasunga madzi
mu chidziwe chakumunsi.
10 Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu
ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
11 Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime
chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,
koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,
kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
12 Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi;
kumeta mutu wanu mpala
ndi kuvala ziguduli.
13 Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;
munapha ngʼombe ndi nkhosa;
munadya nyama ndi kumwa vinyo.
Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa
pakuti mawa tifa!”
14 Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
15 Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,
amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16 Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo
kuti udzikumbire manda kuno,
kudzikumbira manda pa phiri
ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
17 “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba
ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
18 Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira
ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.
Kumeneko ndiko ukafere
ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.
Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
19 Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako
ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
20 “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. 21 Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. 22 Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. 23 Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. 24 Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
25 “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
Kubwera kwa Ambuye
3 Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera. 2 Ndikufuna kuti mukumbukire mawu amene anayankhulidwa kale ndi aneneri oyera mtima ndiponso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu analipereka kudzera mwa atumwi.
3 Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa. 4 Iwo adzati, “Kodi suja Ambuye analonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nʼkale anamwalira makolo athu, koma zinthu zonse zili monga anazilengera poyamba paja.” 5 Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi. 6 Ndi madzinso achigumula, dziko lapansi la masiku amenewo linawonongedwa. 7 Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu.
8 Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! 9 Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape.
10 Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa.
11 Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu 12 pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. 13 Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo.
14 Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye. 15 Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. 16 Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha.
17 Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. 18 Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.