M’Cheyne Bible Reading Plan
Ana Aakazi a Zelofehadi
27 Kenaka ana aakazi a Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wamwamuna wa Manase, a mʼmabanja a Manase, mwana wa Yosefe anabwera. Mayina a ana aakaziwo anali awa: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anakayima 2 pa chipata cha tenti ya msonkhano pamaso pa Mose, wansembe Eliezara, atsogoleri ndi anthu onse, ndipo anati, 3 “Abambo athu anafera mʼchipululu koma sanali nawo mʼgulu la anthu otsatira Kora, omwe anasonkhana pamodzi kutsutsana ndi Yehova. Abambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo ndipo sanasiye ana aamuna. 4 Nʼchifukwa chiyani dzina la abambo athu lasowa pakati pa fuko lawo, kodi popeza analibe mwana wamwamuna? Tipatseni cholowa chathu pakati pa abale a abambo athu.”
5 Tsono Mose anabweretsa nkhani yawo pamaso pa Yehova 6 ndipo Yehova anati kwa iye, 7 “Zimene ana aakazi a Zelofehadi akunena ndi zoona. Uyenera kuwapatsadi cholowa chawo pakati pa abale a abambo awo ndipo uwapatse cholowa cha abambo awowo.
8 “Uza Aisraeli kuti, ‘Ngati munthu afa wosasiya mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. 9 Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chakecho kwa abale ake. 10 Ngati alibe abale muzipereka cholowa chake kwa abale a abambo ake. 11 Ngati abambo ake analibe mʼbale, muzipereka cholowa chakecho kwa mnansi wake wa mʼbanja lake kuti chikhale chake. Ili likhale lamulo kwa Aisraeli, monga momwe Yehova analamulira Mose.’ ”
Yoswa Alowa Mʼmalo mwa Mose
12 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kwera phiri la Abarimu kuti ukaone dziko limene ndalipereka kwa Aisraeli. 13 Ukakaliona udzamwalira ngati Aaroni mʼbale wako, 14 chifukwa pamene anthu anawukira ku madzi a Meriba mʼchipululu cha Zini, inu nonse simunamvere lamulo londilemekeza Ine ngati Woyera pamaso pawo.” (Awa anali madzi a ku Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini).
15 Mose anati kwa Yehova, 16 “Ngati nʼkotheka Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, sankhani munthu woti ayangʼanire gulu ili kuti 17 alitsogolere potuluka ndi polowa, kuti anthu a Yehova asakhale ngati nkhosa zopanda mʼbusa.”
18 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene ali ndi mzimu wa utsogoleri, ndipo umusanjike dzanja lako. 19 Umuyimiritse pamaso pa wansembe Eliezara ndi pamaso pa gulu lonse ndipo umupatse mphamvu zolamulira, anthuwo akuona. 20 Umupatse gawo lina la ulemerero wako kuti Aisraeli onse azimumvera. 21 Ayime pamaso pa wansembe Eliezara, amene adzamudziwitse zimene Yehova akufuna pogwiritsa ntchito Urimu. Iye akalamula, Aisraeli onse azituluka ndipo akalamulanso, Aisraeliwo azibwereranso.”
22 Mose anachita monga Yehova anamulamulira. Anatenga Yoswa ndi kumuyimiritsa pamaso pa Eliezara wansembe ndi pamaso pa gulu lonse. 23 Ndipo anamusanjika manja ndi kumupatsa mphamvu, monga Yehova ananenera kudzera mwa Mose.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pempho.
70 Fulumirani Mulungu kundipulumutsa;
Yehova bwerani msanga kudzandithandiza.
2 Iwo amene akufunafuna moyo wanga
achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene akukhumba chiwonongeko changa
abwezedwe mopanda ulemu.
3 Onse amene akunena kwa ine kuti, “Aha, aha,”
abwerere chifukwa cha manyazi awo.
4 Koma onse amene akufunafuna Inu
akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
nthawi zonse anene kuti, “Mulungu akuzike!”
5 Koma ine ndine wosauka ndi wosowa;
bwerani msanga kwa ine Inu Mulungu.
Inu ndinu thandizo langa ndi momboli wanga;
Inu Yehova musachedwe.
71 Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;
musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
2 Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,
mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
3 Mukhale thanthwe langa lothawirapo,
kumene ine nditha kupita nthawi zonse;
lamulani kuti ndipulumuke,
pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
4 Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,
kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.
5 Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
6 Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;
Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,
ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
7 Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri
koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.
8 Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,
kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.
9 Musanditaye pamene ndakalamba;
musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.
10 Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane;
iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.
11 Iwo amati, “Mulungu wamusiya;
mutsatireni ndi kumugwira,
pakuti palibe amene adzamupulumutse.”
12 Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu,
bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.
13 Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi,
iwo amene akufuna kundipweteka
avale chitonzo ndi manyazi.
14 Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse,
ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.
15 Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu,
za chipulumutso chanu tsiku lonse,
ngakhale sindikudziwa muyeso wake.
16 Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.
17 Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa,
ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa
18 Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu
musanditaye Inu Mulungu,
mpaka nditalengeza mphamvu zanu
kwa mibado yonse yakutsogolo.
19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba.
Ndani wofanana nanu Inu Mulungu,
amene mwachita zazikulu?
20 Ngakhale mwandionetsa mavuto
ambiri owawa,
mudzabwezeretsanso moyo wanga;
kuchokera kunsi kwa dziko lapansi,
mudzandiukitsanso.
21 Inu mudzachulukitsa ulemu wanga
ndi kunditonthozanso.
22 Ndidzakutamandani ndi zeze
chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu,
ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe,
Inu Woyera wa Israeli.
23 Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe
pamene ndidzayimba matamando kwa Inu
amene mwandiwombola.
24 Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo
tsiku lonse,
pakuti iwo amene amafuna kundipweteka
achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.
Uthenga Wotsutsa Damasiko
17 Uthenga wonena za Damasiko:
“Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda,
koma udzasanduka bwinja.
2 Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu
ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi
popanda wina woziopseza.
3 Ku Efereimu sikudzakhalanso linga,
ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu;
Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu
monga anthu a ku Israeli,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
4 “Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira;
ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
5 Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu
umene anatsiriza kukolola.
Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu
anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
6 Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale
monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni
kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi
mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,”
akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
7 Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo
ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
8 Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe,
ntchito ya manja awo,
ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera,
ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
9 Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
10 Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu;
simunakumbukire Thanthwe, linga lanu.
Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino,
ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
11 nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo
ndi kuphukira maluwa mmawa mwake,
komabe zimenezi sizidzakupindulirani
pa tsiku la mavuto.
12 Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri,
akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja!
Aa, phokoso la anthu a mitundu ina,
akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
13 Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri,
koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula.
Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri,
ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
14 Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika,
ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa.
Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu,
gawo la amene amatibera zinthu zathu.
Za Kulangidwa kwa Kusi
18 Tsoka kwa anthu a ku Kusi.
Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko a dzombe.
2 Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo,
mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi,
ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro,
kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala,
ndi woopedwa ndi anthu.
Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena.
Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”
3 Inu nonse anthu a pa dziko lonse,
inu amene mumakhala pa dziko lapansi,
pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri
yangʼanani,
ndipo pamene lipenga lilira
mumvere.
4 Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti,
“Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana,
monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha,
monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”
5 Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka
ndiponso mphesa zitayamba kupsa,
Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira,
ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.
6 Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama
ndiponso zirombo zakuthengo;
mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe,
ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.
7 Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse,
zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala,
kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe,
mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo,
anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.
Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.
Akulu Ampingo ndi Anyamata mu Mpingo
5 Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. 2 Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. 3 Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo. 4 Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.
5 Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,
“Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,
koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”
6 Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. 7 Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
8 Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. 9 Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
10 Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba. 11 Kwa Iye kukhale mphamvu mpaka muyaya, Ameni.
Mawu Otsiriza
12 Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu. 13 Imani mwamphamvu mʼchisomochi. Mlongo wanu amene ali ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi nanu akupereka moni, nayenso Marko, mwana wanga, akupereka moni. 14 Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.