M’Cheyne Bible Reading Plan
Balaki Ayitana Balaamu
22 Aisraeli anayenda kupita ku zigwa za Mowabu nakamanga misasa yawo tsidya lina la Yorodani moyangʼanana ndi Yeriko.
2 Tsono Balaki mwana wa Zipori anaona zonse zimene Aisraeli anachitira Aamori, 3 ndipo Amowabu anaopa anthuwo chifukwa analipo ambiri. Amowabuwo anachita mantha kwambiri mpaka ananjenjemera chifukwa cha Aisraeli.
4 Iwo anati kwa akuluakulu a ku Midiyani, “Gulu ili lidzabudula zonse zimene zatizungulira monga momwe ngʼombe yothena imathera udzu wa ku tchire.”
Tsono Balaki mwana wa Zipori, yemwe anali mfumu ya Mowabu pa nthawi imeneyo, 5 anatumiza amithenga kwa Balaamu mwana wa Beori, yemwe anali ku Petori, pafupi ndi mtsinje, mʼdziko la kwawo kuti akamuyitane. Balaki anati:
“Taonani, anthu ochokera ku Igupto abwera, adzaza dziko lonse ndipo akufuna kuchita nane nkhondo. 6 Tsopano bwera, utemberere anthu amenewa chifukwa ndi amphamvu kwambiri kuposa ine. Mwina ndingadzawagonjetse ndi kuwatulutsira kunja kwa dzikoli chifukwa ndikudziwa kuti amene umawadalitsa amadalitsika, ndipo amene umawatemberera amatembereredwa.”
7 Akuluakulu a Mowabu ndi akuluakulu a Midiyani ananyamuka atatenga ndalama zokalipirira mawula. Atafika kwa Balaamu, anamuwuza zomwe Balaki ananena.
8 Balaamu anawawuza kuti, “Mugone konkuno usiku uno, ndipo ndikuyankhani zomwe Yehova andiwuze.” Choncho akuluakulu a Amowabu anagona kwa Balaamu.
9 Mulungu anabwera kwa Balaamu namufunsa kuti, “Kodi anthu ali ndi iwewa ndani?”
10 Balaamu anayankha Mulungu kuti, “Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, ananditumizira uthenga uwu: 11 ‘Taonani, anthu amene achokera ku dziko la Igupto adzaza dziko lonse. Tsopano bwera udzawatemberere mʼmalo mwanga. Mwina ndidzatha kumenyana nawo ndi kuwatulutsa.’ ”
12 Koma Mulungu anawuza Balaamu kuti, “Usapite nawo. Usawatemberere anthu amenewo chifukwa ndi odalitsika.”
13 Mmawa mwake Balaamu anadzuka ndi kuwuza akuluakulu a Balaki aja kuti, “Bwererani ku dziko la kwanu chifukwa Yehova sanandilole kuti ndipite nanu.”
14 Kotero akuluakulu a Mowabu anabwerera kwa Balaki ndi kukanena kuti, “Balaamu wakana kubwera nafe.”
15 Kenaka Balaki anatumanso akuluakulu ena ambiri ndi olemekezeka kwambiri kuposa oyamba aja ndipo 16 anafika kwa Balaamu nati;
“Zomwe Balaki mwana wa Zipori akunena ndi izi: ‘Usalole kuti china chilichonse chikulepheretse kubwera kwa ine, 17 chifukwa ndidzakulipira bwino kwambiri ndipo ndidzakuchitira chilichonse chimene unganene. Bwera ndipo uwatemberere anthu amenewa mʼmalo mwanga.’ ”
18 Koma Balaamu anayankha atumiki a Balaki kuti, “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingachite chilichonse chachikulu kapena chachingʼono kuposa kuchita lamulo la Yehova Mulungu wanga. 19 Tsopano mukhale kuno usiku uno monga ena anachitira, ndidzaona chimene Yehova adzandiwuza.”
20 Usiku umenewo Mulungu anabwera kwa Balaamu ndipo anati, “Popeza anthu awa abwera kudzakuyitana, nyamuka, pita nawo koma ukachite zokhazo zimene ndikuwuze.”
Bulu Ayankhula
21 Balaamu anadzuka mmawa, namanga bulu wake wamkazi ndipo anapita ndi akuluakulu a Mowabu. 22 Koma Mulungu anakwiya kwambiri pamene ankapita ndipo mngelo wa Yehova anayima pa njira kutsutsana naye. Balaamu anakwera bulu wake wamkazi ndipo antchito ake awiri anali naye. 23 Pamene buluyo anaona mngelo wa Yehova atayima pa njira ndi lupanga mʼmanja mwake, anapatukira kumbali kwa msewu napita kutchire. Balaamu anamumenya kuti abwerere mu msewu.
24 Kenaka mngelo wa Yehova anayima mʼkanjira kakangʼono pakati pa minda iwiri ya mpesa yokhala ndi makoma mbali zonse 25 Bulu uja ataona mngelo wa Yehova anadzipanikiza ku khoma, kukhukhuza phazi la Balaamu kukhomako. Ndipo pomwepo Balaamu anamenya buluyo kachiwiri.
26 Kenaka mngelo wa Yehova anapita patsogolo ndi kuyima pamalo opanikizika pomwe panalibe poti nʼkutembenukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere. 27 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anagona pansi Balaamu ali pa msana, ndipo iye anakwiya ndi kumumenya ndi ndodo yake. 28 Pamenepo Yehova anayankhulitsa bulu uja, ndipo buluyo anati kwa Balaamu, “Ndakuchitirani chiyani kuti mundimenye katatuka?”
29 Balaamu anati kwa buluyo, “Wandipusitsa, ndikanakhala ndi lupanga mʼmanja mwanga, ndikanakupha pomwe pano.”
30 Buluyo anati kwa Balaamu, “Kodi sindine bulu wanu, amene mumakwera nthawi zonse kufikira lero? Kodi ndinakuchitiranipo zoterezi?”
Iye anati “Ayi.”
31 Pomwepo Yehova anatsekula maso Balaamu ndipo anaona mngelo wa Yehovayo ali chiyimire pa njira ndi lupanga losolola. Tsono iye anawerama nalambira pamaso pake.
32 Mngelo wa Yehova anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani wamenya bulu wako katatu? Taona, Ine ndabwera kudzakutsutsa chifukwa ulendo wakowu ndi woyipa pamaso panga. 33 Buluyu anandiona ndi kupatuka katatu aka. Akanakhala kuti sanapatuke, ndikanakupha tsopano, koma buluyu nʼkanamusiya ndi moyo.”
34 Balaamu anati kwa mngelo wa Yehova uja, “Ndachimwa. Sindinadziwe kuti munayima pa njira kunditsutsa. Tsopano ngati Inu simunakondwe, ineyo ndibwerera.”
35 Mngelo wa Yehova anati kwa Balaamu, “Pita ndi anthuwa koma ukayankhule zokhazo zimene ndikakuwuze.” Choncho Balaamu anapita ndi akuluakulu a Balaki.
36 Balaki atamva kuti Balaamu akubwera, anapita kukakumana naye ku mzinda wa Mowabu umene unali mʼmalire a Arinoni, mʼmphepete mwa dziko lake. 37 Balaki anati kwa Balaamu, “Kodi sindinakutumizire uthenga woti ubwere msanga? Chifukwa chiyani sunabwere kwa ine? Kodi sindingathe kukulipira mokwanira?”
38 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Taonani, ndabwera kwa inu lero, kodi ine ndili ndi mphamvu zoti nʼkuyankhula chilichonse? Inetu ndiyenera kuyankhula zokhazo zimene Mulungu wandiwuza.”
39 Pamenepo Balaamu anapita pamodzi ndi Balaki ku Kiriati-Huzoti. 40 Balaki anapereka nsembe ngʼombe ndi nkhosa, ndipo anapereka zina kwa Balaamu ndi kwa akuluakulu omwe anali naye. 41 Mmawa mwake Balaki anatenga Balaamu napita limodzi ku Bamoti Baala, ndipo kumeneko anakaonako gulu lina la Aisraeliwo.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Kutsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Davide.
62 Moyo wanga umapeza mpumulo mwa Mulungu yekha;
chipulumutso changa chimachokera kwa Iye.
2 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iye ndi linga langa, choncho sindidzagwedezeka.
3 Kodi nonsenu mudzalimbana naye munthu mpaka liti?
Kodi mudzamugwetsa pansi ngati khoma losalimba,
ngati mpanda wogwedezeka?
4 Iwo akufunitsitsa kumugwetsa
kuti achoke pa malo ake apamwamba.
Iwo amakondweretsedwa ndi mabodza.
Ndi pakamwa pawo amadalitsa
koma mʼmitima yawo amatemberera.
5 Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;
chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
7 Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:
Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
8 Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;
khuthulani mitima yanu kwa Iye,
pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.
Sela
9 Anthu wamba ndi mpweya chabe;
anthu apamwamba ndi bodza chabe;
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;
iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
10 Musadalire kulanda mwachinyengo
kapena katundu wobedwa;
ngakhale chuma chanu chichuluke,
musayike mtima wanu pa icho.
11 Mulungu wayankhula kamodzi,
ine ndamvapo zinthu ziwiri;
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
12 komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu
molingana ndi ntchito zake.
Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda.
63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga,
moona mtima ine ndimakufunafunani;
moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu,
thupi langa likulakalaka inu,
mʼdziko lowuma ndi lotopetsa
kumene kulibe madzi.
2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika
ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
3 Chifukwa chikondi chanu
ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani.
4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga,
ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga.
5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona.
Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya.
6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu;
ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku.
7 Chifukwa ndinu thandizo langa,
ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Moyo wanga umakangamira Inu;
dzanja lanu lamanja limandigwiriziza.
9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa;
adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi.
10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga
ndi kukhala chakudya cha ankhandwe.
11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu;
onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo,
koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.
Za Ufumu Wamtendere wa Mesiya
11 Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese
ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.
2 Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye
Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu,
Mzimu wauphungu ndi wamphamvu,
Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.
3 Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa.
Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso,
kapena kugamula mlandu potsata zakumva;
4 koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo,
adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi.
Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake;
atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
5 Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake
ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.
6 Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa,
kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi,
mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi
ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
7 Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi,
ana awo adzagona pamodzi,
ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.
8 Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba,
ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.
9 Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga
pa phiri lopatulika la Yehova,
pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova
monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.
10 Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero. 11 Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.
12 Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera,
ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli;
Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yuda
kuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.
13 Nsanje ya Efereimu idzatha,
ndipo adani a Yuda adzatha;
Efereimu sadzachitira nsanje Yuda,
ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.
14 Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo;
ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa.
Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu,
ndipo Aamoni adzawagonjera.
15 Yehova adzaphwetsa
mwendo wa nyanja ya Igupto;
adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha
pa mtsinje wa Yufurate.
Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri
kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.
16 Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira
amene anatsalira ku Asiriya,
monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli
pamene amachokera ku Igupto.
Nyimbo za Mayamiko
12 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:
“Ndikukuyamikani, Inu Yehova;
chifukwa ngakhale munandipsera mtima,
mkwiyo wanu wachoka,
ndipo mwanditonthoza.
2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;
ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.”
3 Mudzakondwera popeza Yehova
ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.
4 Tsiku limenelo mudzati:
“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;
mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;
zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.
6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;
pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”
Chenjezo kwa Achuma Opondereza Anzawo
5 Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni. 2 Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu. 3 Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza. 4 Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse. 5 Mwakhala pa dziko lapansi pano moyo ofewa ndipo mwalidyera dziko lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lokaphedwa. 6 Mwaweruza kuti ndi wolakwa ndipo mwapha munthu wosalakwa, amene sakutsutsana nanu.
Kupirira Mʼmasautso
7 Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza. 8 Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera. 9 Abale, musamanenezane zoyipa kuopa kuti mungadzaweruzidwe. Woweruza ali pa khomo!
10 Abale, tengerani chitsanzo cha aneneri amene anayankhula mʼdzina la Ambuye. Iwowo anakumana ndi zovuta koma anapirira. 11 Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.
12 Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa.
Pemphero la Chikhulupiriro
13 Kodi alipo wina mwa inu amene ali pa mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Ayimbe nyimbo zolemekeza. 14 Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. 15 Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa. 16 Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.
17 Eliya anali munthu ngati ife. Iye anapemphera mwamphamvu kuti mvula isagwe ndipo sinagwedi kwa zaka zitatu ndi theka. 18 Kenaka anapempheranso, ndipo kumwamba kunagwetsa mvula, ndipo dziko lapansi linatulutsa zomera zake. 19 Abale anga, ngati mmodzi wa inu apatuka pa choonadi ndipo wina wake ndi kumubweza, 20 kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.