Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 21

Kuwonongedwa kwa Aradi

21 Mfumu ya Akanaani ya ku Aradi, imene inkakhala ku Negevi, itamva kuti Aisraeli akubwera kudzera msewu wopita ku Atarimu, inachita nkhondo ndi Aisraeli nigwira ena mwa iwo. Ndipo Israeli anachita lonjezo ili kwa Yehova: “Mukapereka anthu awa mʼdzanja lathu ife tidzawonongeratu mizinda yawo.” Yehova anamva pempho la Aisraeli ndipo anapereka Akanaaniwo kwa iwo. Anawawononga pamodzi ndi mizinda yawo. Kotero malowo anatchedwa Horima.

Njoka Yamkuwa

Aisraeli anayenda kuchokera ku phiri la Hori kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira kuzungulira dziko la Edomu. Koma anthu anataya mtima mʼnjiramo ndipo anayankhula motsutsana ndi Mulungu ndi Mose, nati, “Chifukwa chiyani munatitulutsa kuchoka mʼdziko la Igupto kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya, kulibe madzi ndipo chakudya cha chabechabechi tatopa nacho.”

Choncho Yehova anatumiza njoka zaululu pakati pawo. Zinaluma anthu ndipo Aisraeli ambiri anafa. Anthuwo anabwera kwa Mose ndi kunena kuti, “Tachimwa chifukwa tayankhula motsutsana ndi Yehova komanso inu. Pempherani kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Tsono Mose anapempherera anthuwo.

Yehova anati kwa Mose, “Upange njoka yaululu ndipo uyipachike pa mtengo. Aliyense amene walumidwa akangoyangʼana njokayo adzakhala ndi moyo.” Pamenepo Mose anapanga njoka yamkuwa ndi kuyipachika pa mtengo. Ndipo aliyense wolumidwa akayangʼana njoka yamkuwayo ankakhala ndi moyo.

Ulendo wa ku Mowabu

10 Aisraeli anayendabe nakamanga misasa yawo ku Oboti. 11 Kenaka anasamuka ku Oboti nakamanga misasa yawo ku Iye-Abarimu, mʼchipululu chimene chili kummawa kwa Mowabu, kotulukira dzuwa. 12 Kuchoka kumeneko anayendabe nakamanga misasa yawo mʼchigwa cha Zeredi. 13 Anasamukanso kumeneko nakamanga moyandikana ndi Arinoni mʼdera limene lili mʼchipululu chimene chimafika mʼdziko la Aamori. Arinoni ndiwo malire a Mowabu ndi Aamori. 14 Nʼchifukwa chake Buku la Nkhondo za Yehova limati,

“Mzinda wa Wahebu uli mu Sufa,
mu zigwa za Arinoni, 15     ku matsitso a zigwa
amene afika mpaka ku Ari
    nakhudza malire a dziko la Mowabu.”

16 Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Beeri, pa chitsime chomwe Yehova anawuza Mose kuti, “Sonkhanitsa anthu pamodzi ndipo ndidzawapatsa madzi.”

17 Pamenepo Aisraeli anayimba nyimbo iyi:

“Tulutsa madzi, chitsime iwe!
    Chiyimbireni nyimbo,
18 chitsime chomwe anakumba mafumu,
    chomwe anakumba anthu omveka,
    ndi ndodo zawo zaufumu ndi ndodo zawo zoyendera.”

Kenaka anachoka ku chipululu ndi kupita ku Matana. 19 Kuchoka ku Matana anapita ku Nahalieli, kuchoka ku Nahalieli anapita ku Bamoti, 20 ndipo atachoka ku Bamoti anapita ku chigwa cha dziko la Mowabu kudzera njira ya pamwamba pa phiri la Pisiga, moyangʼanana ndi Yesimoni.

Kugonjetsedwa kwa Sihoni ndi Ogi

21 Aisraeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, kuti,

22 “Tiloleni kuti tidutse mʼdziko mwanu. Sitidzapatukira mʼminda mwanu kapena mu mpesa wanu kapena kumwa madzi mʼchitsime chili chonse. Tidzayenda mu msewu waukulu wa mfumu mpaka titadutsa malire a dziko lanu.”

23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisraeli adutse mʼdziko mwake. Iye anasonkhanitsa pamodzi ankhondo ake onse kuti akamenyane ndi Aisraeli mʼchipululu. Atafika pa Yahazi anamenyana ndi Aisraeli. 24 Koma Aisraeli anamupha ndi kulanda dziko lake kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki, kulekezera mʼmalire a dziko la Aamoni, chifukwa malire a dziko la Aamoni anali otetezedwa. 25 Ndipo Aisraeli analanda mizinda yonse ya Aamori, nakhalamo kuphatikizapo Hesiboni ndi midzi yake yozungulira. 26 Hesiboni unali mzinda wa Sihoni mfumu ya Aamori, yemwe anamenyana ndi mfumu yakale ya dziko la Mowabu. Lonselo linakhala dziko lake mpaka ku Arinoni.

27 Nʼchifukwa chake alakatuli amati:

“Bwerani ku Hesiboni, mzindawo umangidwenso;
    mzinda wa Sihoni ukhazikike.

28 “Moto unabuka ku Hesiboni,
    malawi a moto kuchokera mu mzinda wa Sihoni.
Unanyeketsa Ari mzinda wa ku Mowabu,
    nzika za ku malo okwera a Arinoni.
29 Tsoka kwa iwe Mowabu!
    Mwawonongedwa inu anthu a ku Kemosi!
Ana ake aamuna wawasandutsa ngati anthu othawathawa
    ndipo ana ake aakazi ngati akapolo,
    akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori.

30 “Koma ife tawagonjetsa;
    Hesiboni wawonongedwa mʼnjira monse mpaka kufika ku Diboni.
Tawaphwasula mpaka ku mzinda wa Nofa,
    mzinda womwe umafika ku Medeba.

31 “Choncho Aisraeli anakhala mʼdziko la Aamori.”

32 Mose atatumiza azondi ku Yazeri, Aisraeliwo analanda midzi yozungulira ndi kuthamangitsa Aamori omwe ankakhala kumeneko. 33 Kenaka anabwerera, nadzera njira ya ku Basani. Choncho Ogi mfumu ya ku Basani ndi gulu lake lonse lankhondo anatuluka kukakumana nawo ndipo anamenyana nawo ku Ederi.

34 Yehova anati kwa Mose, “Usachite naye mantha pakuti ndamupereka mʼmanja mwako pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo ndi dziko lake lomwe. Ndipo uchite kwa iye zimene unachita Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamulira ku Hesiboni.”

35 Choncho Aisraeli anapha Ogi pamodzi ndi ana ake aamuna ndi gulu lake lonse la nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala wamoyo, ndipo analanda dziko lakelo.

Masalimo 60-61

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere.

60 Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza.
    Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba,
    konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto;
    inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.

Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera
    kuti tisonkhanireko pothawa uta.

Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja,
    kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:
    “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu
    ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.
Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;
    Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,
    Yuda ndi ndodo yanga yaufumu
Mowabu ndi mbale yanga yosambira,
    pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga,
    pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”

Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa?
    Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
10 Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife
    ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.
11 Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu,
    pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.
12 Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano
    ndipo tidzapondaponda adani athu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Loyimbidwa ndi zipangizo za zingwe.

61 Imvani kulira kwanga, Inu Mulungu;
    mvetserani pemphero langa.

Kuchokera ku malekezero a dziko lapansi ine ndimayitana Inu
    ndimayitana pomwe mtima wanga ukufowoka;
    tsogolereni ku thanthwe lalitali kuposa ineyo.
Pakuti Inu mwakhala pothawirapo panga,
    nsanja yolimba polimbana ndi adani anga.

Ine ndikulakalaka kukhala mʼtenti yanu kwamuyaya
    ndi kupeza chitetezo mu mthunzi wa mapiko anu.
Pakuti Inu Mulungu mwamva malumbiro anga;
    mwandipatsa cholowa cha iwo amene amaopa dzina lanu.

Wonjezerani masiku a moyo wa mfumu,
    zaka zake kwa mibado yochuluka.
Iye akhale pa mpando waufumu pamaso pa Mulungu kwamuyaya;
    ikani chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu kuti zimuteteze.

Kotero ndidzayimba matamando kwamuyaya pa dzina lanu
    ndi kukwaniritsa malumbiro anga tsiku ndi tsiku.

Yesaya 10:5-34

Chiweruzo cha Mulungu pa Asiriya

“Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga,
    iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!
Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu,
    ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine,
kukafunkha ndi kulanda chuma,
    ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.
Koma izi si zimene akufuna kukachita,
    izi si zimene zili mʼmaganizo mwake;
cholinga chake ndi kukawononga,
    kukapulula mitundu yambiri ya anthu.
Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’
    ‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi?
Kodi Hamati sali ngati Aripadi,
    nanga Samariya sali ngati Damasiko?
10 Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano,
    mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;
11 nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake
    monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’ ”

12 Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake. 13 Pakuti mfumuyo ikuti,

“ ‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa,
    ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu.
Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu,
    ndinafunkha chuma chawo;
    ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.
14 Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu
    ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame,
ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa,
    motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse;
palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake,
    kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”

15 Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito,
    kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito?
Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula,
    kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!
16 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
    adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu;
kunyada kwa mfumuyo kudzapsa
    ndi moto wosazima.
17 Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto,
    Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto.
Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza
    ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
18 Ankhondo ake adzawonongedwa
    ngati nkhalango yayikulu
    ndi ngati nthaka yachonde.
19 Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri,
    yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.

Aisraeli Otsala

20 Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli,
    opulumuka a nyumba ya Yakobo,
sadzadaliranso anthu
    amene anawakantha,
koma adzadalira Yehova,
    Woyerayo wa Israeli.
21 Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo
    adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.
22 Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja,
    otsala okha ndiwo adzabwerere.
Chiwonongeko chalamulidwa,
    chidzaonetsa chilungamo chosefukira.
23 Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse
    monga momwe analamulira.

24 Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti,

“Inu anthu anga okhala mu Ziyoni,
    musawaope Asiriya,
amene amakukanthani ndi ndodo
    nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
25 Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu
    ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”

26 Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu,
    monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu;
ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi
    ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
27 Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu,
    goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu;
golilo lidzathyoka
    chifukwa cha kunenepa kwambiri.

28 Adani alowa mu Ayati
    apyola ku Migironi;
    asunga katundu wawo ku Mikimasi.
29 Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti,
    “Tikagona ku Geba”
Rama akunjenjemera;
    Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.
30 Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu!
    Tchera khutu, iwe Laisa!
    Iwe Anatoti wosauka!
31 Anthu a ku Madimena akuthawa;
    anthu a ku Gebimu bisalani.
32 Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu;
    adzagwedeza mikono yawo,
kuopseza anthu a ku Ziyoni,
    pa phiri la Yerusalemu.

33 Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,
    adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo,
mitengo yodzikweza idzadulidwa,
    mitengo yayitali idzagwetsedwa.
34 Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira;
    Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.

Yakobo 4

Kugonjera Mulungu

Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu? Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.

Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu. Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife? Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati,

“Mulungu amatsutsa odzikuza,
    koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”

Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani. Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira. Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. 10 Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.

11 Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza. 12 Pali mmodzi yekha Wopereka Malamulo ndi Woweruza. Ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga. Kodi ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?

Kunyadira za Mawa

13 Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.” 14 Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. 15 Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.” 16 Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa. 17 Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.