Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 19

Phulusa ndi Madzi Oyeretsera

19 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: “Lamulo limene Yehova wapereka ndi ili: Uzani Aisraeli kuti abweretse ngʼombe yayikazi yofiira yopanda chilema chilichonse imenenso sinakhalepo pa goli. Muyipereke kwa Eliezara, wansembe ndipo apite nayo kunja kwa msasa. Iphedwe iye ali pomwepo. Ndipo Eliezara wansembe atengeko ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake ndi kuwaza kasanu nʼkawiri ku tsogolo kwa tenti ya msonkhano. Wansembeyo akuona, ngʼombeyo ayiwotche chikopa chake, mnofu wake, magazi ake ndi zamʼkati zake. Wansembe atenge mtengo wamkungudza, hisope ndi kansalu kofiira ndipo aponye zimenezo pakati pa moto umene akuwotchera ngʼombeyo. Zitatha izi, wansembeyo ayenera kuchapa zovala zake ndiponso asambe ndi madzi. Iye angathe kupita ku msasa, komabe adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Munthu amene amawotcha ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.

“Munthu amene ndi woyeretsedwa achotse phulusa la ngʼombeyo ndi kuliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa msasa. Aisraeli adzasunge phulusalo kuti azikaligwiritsa ntchito polithira mʼmadzi woyeretsera ndi wochotsera tchimo. 10 Munthu wochotsa phulusa la ngʼombeyo ayeneranso kuchapa zovala zake. Iyenso adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo.

11 “Aliyense wokhudza mtembo wa munthu wina aliyense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri. 12 Adziyeretse yekha ndi madzi pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ndipo adzayeretsedwa. Koma ngati sadziyeretsa yekha pa tsiku la chitatu ndi lachisanu ndi chiwiri sadzakhala woyeretsedwa. 13 Aliyense amene akhudza mtembo wa munthu nʼkulephera kudziyeretsa yekha, ndiye kuti wadetsa Nyumba ya Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraeli. Iye ndi wodetsedwa chifukwa sanamuwaze madzi oyeretsa; kudetsedwa kwake kukhalabe pa iyeyo.

14 “Pamene munthu wamwalira mu tenti, lamulo lomwe ligwire ntchito ndi ili: Aliyense wolowa mu tentimo ndi amene anali momwemo adzakhala odetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri, 15 ndiponso chiwiya chilichonse chopanda chivundikiro chidzakhala chodetsedwa.

16 “Aliyense wokhudza munthu amene waphedwera kunja ndi lupanga kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe, kapena aliyense wokhudza fupa la munthu kapena manda, munthu ameneyo adzakhala wodetsedwa kwa masiku asanu ndi awiri.

17 “Za munthu wodetsedwayo: ikani phulusa lochokera ku nsembe ya chiyeretso mu mtsuko ndi kuthiramo madzi abwino. 18 Tsono munthu woyeretsedwa atenge hisope, amuviyike mʼmadzi ndi kuwaza tentiyo ndi zipangizo zonse, pamodzi ndi anthu anali mʼmenemo. Ayenera kuwazanso aliyense wakhudza fupa kapena, munthu wochita kuphedwa, kapena amene wafa ndi imfa ya chilengedwe kapenanso amene wakhudza manda. 19 Munthu woyeretsedwa ndiye awaze munthu wodetsedwayo pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amuyeretse. Munthu amene akuyeretsedwayo ayenera kuchapa zovala zake ndi kusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyeretsedwa. 20 Koma ngati munthu wodetsedwayo sadziyeretsa yekha, ndiye kuti ayenera kuchotsedwa pakati pa gulu chifukwa anadetsa malo wopatulika a Yehova, popeza sanawazidwe madzi oyeretsa ndiye kuti ndi wodetsedwa. 21 Ili ndi lamulo lokhazikika kwa iwo.

“Munthu amene amawaza madzi oyeretsawo ayenera kuchapa zovala zake ndipo yense wokhudza madzi oyeretserawo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Chilichonse chimene munthu wodetsedwayo achikhudze chidzakhala chodetsedwa ndiponso aliyense wochikhudza adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.”

Masalimo 56-57

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati.

56 Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri;
    tsiku lonse akundithira nkhondo.
Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse,
    ambiri akumenyana nane monyada.

Ndikachita mantha
    ndimadalira Inu.
Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda,
    mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha.
    Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?

Tsiku lonse amatembenuza mawu anga;
    nthawi zonse amakonza zondivulaza.
Iwo amakambirana, amandibisalira,
    amayangʼanitsitsa mayendedwe anga
    ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.

Musalole konse kuti athawe;
    mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu.
Mulembe za kulira kwanga,
    mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu.
    Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?

Adani anga adzabwerera mʼmbuyo
    pamene ndidzalirira kwa Inu.
    Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.
10 Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda,
    mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda,
11 mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha.
    Kodi munthu angandichite chiyani?

12 Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu;
    ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu.
13 Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa
    ndi mapazi anga kuti ndingagwe,
kuti ndiyende pamaso pa Mulungu
    mʼkuwala kwa moyo.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga.

57 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo,
    pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo.
Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu
    mpaka chiwonongeko chitapita.

Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba,
    kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.
Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa,
    kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri.
    Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.

Ine ndili pakati pa mikango,
    ndagona pakati pa zirombo zolusa;
anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi,
    malilime awo ndi malupanga akuthwa.

Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba;
    mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

Iwo anatchera mapazi anga ukonde
    ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa.
Anakumba dzenje mʼnjira yanga
    koma agweramo okha mʼmenemo.

Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu
    mtima wanga ndi wokhazikika.
    Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.
Dzuka moyo wanga!
    Dzukani zeze ndi pangwe!
    Ndidzadzuka mʼbandakucha.

Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu,
    ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.
10 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba;
    kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.

11 Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba,
    mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

Yesaya 8:1-9:7

Asiriya, Chida cha Yehova

Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira. Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”

Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’ Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”

Yehova anayankhulanso ndi Ine;

“Popeza anthu a dziko ili akana
    madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu,
ndipo akukondwerera Rezini
    ndi mwana wa Remaliya,
nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa
    madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo;
    mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo.
Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse
    ndi mʼmagombe ake onse.
Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira,
    adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi.
Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse,
    iwe Imanueli!”

Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere!
    Tamverani, inu mayiko onse akutali.
Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
    Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
10 Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu,
    kambiranani zochita, koma zidzalephereka,
pakuti Mulungu ali nafe.

Yehova Achenjeza Mneneri

11 Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:

12 “Usamanene kuti ndi chiwembu,
    chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu
usamaope zimene anthuwa amaziopa,
    ndipo usamachite nazo mantha.
13 Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera,
    ndiye amene uyenera kumuopa,
    ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
14 ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika;
    koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala
mwala wopunthwitsa,
    mwala umene umapunthwitsa anthu,
thanthwe limene limagwetsa anthu.
    Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
15 Anthu ambiri adzapunthwapo
    adzagwa ndi kuthyokathyoka,
    adzakodwa ndi kugwidwa.”

16 Manga umboniwu
    ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
17 Ndidzayembekezera Yehova,
    amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo.
Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.

18 Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.

19 Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo, 20 kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala. 21 Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo. 22 Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.

Ufumu wa Mesiya

Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.

Anthu oyenda mu mdima
    awona kuwala kwakukulu;
kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani
    kuwunika kwawafikira.
Inu mwauchulukitsa mtundu wanu
    ndipo mwawonjezera chimwemwe chawo.
Iwo akukondwa pamaso panu,
    ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola,
ngatinso mmene anthu amakondwera
    pamene akugawana zolanda ku nkhondo.
Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani,
    inu mwathyola goli
limene limawalemera,
    ndodo zimene amamenyera mapewa awo,
    ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.
Nsapato iliyonse ya munthu wankhondo,
    ndiponso chovala chilichonse chodonthekera magazi
zidzatenthedwa pa moto
    ngati nkhuni.
Chifukwa mwana watibadwira,
    mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife,
    ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.
Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti
    Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,
    Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
Ulamuliro ndi mtendere wake
    zidzakhala zopanda malire.
Iye adzalamulira ufumu wake ali pa
    mpando waufumu wa Davide,
ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza
    mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo
    kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya.
Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse
    watsimikiza kuchita zimenezi.

Yakobo 2

Kuchita Tsankho Nʼkosaloledwa

Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?

Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?

Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. 10 Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse. 11 Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo.

12 Muziyankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene mudzaweruzidwe ndi lamulo limene limapereka ufulu, 13 chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.

Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino

14 Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? 15 Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. 16 Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? 17 Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

18 Koma wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino.”

Onetsani chikhulupiriro chanu chopanda ntchito zabwino ndipo ineyo ndidzakuonetsani chikhulupiriro changa pochita ntchito zabwino. 19 Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.

20 Munthu wopusa iwe, kodi ukufuna umboni woti chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino nʼchakufa? 21 Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe? 22 Tsono mukuona kuti chikhulupiriro chake ndi ntchito zabwino zinkachitika pamodzi, ndipo chikhulupiriro chake chinasanduka chenicheni chifukwa cha ntchito zake zabwino. 23 Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. 24 Tsono mukuona kuti munthu amasanduka wolungama ndi ntchito zabwino osati ndi chikhulupiriro chokha ayi.

25 Nʼchimodzimodzinso, kodi wadama uja, Rahabe, sanasanduke wolungama chifukwa cha zomwe anachita pamene anapereka malo ogona kwa azondi aja ndi kuwathawitsira mbali ina? 26 Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.