M’Cheyne Bible Reading Plan
Kora, Datani ndi Abiramu Awukira Mose
16 Kora mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliabu, pamodzi ndi Oni mwana wa Perezi, ana a Rubeni, anayamba kudzikuza, 2 ndipo anawukira Mose. Mʼgulu mwawo munali atsogoleri a Aisraeli 250, anthu otchuka amene anasankhidwa ndi anthu pa msonkhano. 3 Iwo anasonkhana kudzatsutsana ndi Mose ndi Aaroni nawawuza kuti, “Mwawonjeza! Anthu onsewa ndi oyera, aliyense wa iwo, ndipo Yehova ali pakati pawo. Chifukwa chiyani mukudzikuza pakati pa gulu lonse la Yehova?”
4 Mose atamva izi, anagwa chafufumimba. 5 Ndipo iye anawuza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti, “Yehova mawa mmawa adzasonyeza yemwe ndi wake ndiponso amene ndi woyera mtima. Munthuyo adzabwera pafupi ndi Iye. Munthu amene adzamusankheyo adzamusendeza pafupi. 6 Iwe Kora pamodzi ndi onse amene akukutsatira chitani izi: Tengani zofukizira 7 ndipo mawa muyikemo moto ndi lubani pamaso pa Yehova. Munthu amene Yehova amusankhe ndiye amene ali woyera. Alevi inu mwawonjeza kwambiri!”
8 Mose anawuzanso Kora kuti, “Inu Alevi, tsopano tamverani! 9 Kodi sizinakukwanireni kuti Mulungu wa Israeli anakupatulani pakati pa gulu lonse la Aisraeli ndi kukubweretsani pafupi ndi Iye, kuti muzigwira ntchito ku nyumba ya Yehova ndi kumayima pamaso pa gulu, kumatumikira? 10 Wakubweretsa iwe pamodzi ndi Alevi anzako kufupi ndi Iye mwini. Koma tsopano ukufuna kutenganso unsembe. 11 Nʼkulakwira Yehova kuti iwe ndi gulu lako lonseli mwasonkhana kuti mutsutsane ndi Yehova. Kodi Aaroni ndani kuti muzikangana naye?”
12 Kenaka Mose anayitana Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu koma iwo anati, “Sitibwera! 13 Kodi sikukwanira kuti unatitulutsa, kutichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphe mʼchipululu muno? Kodi tsopano ukufunanso kutilemetsa? 14 Kuwonjezera apo, sunatilowetse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kapena kutipatsa malo wolima ndi minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuchotsa maso a anthuwa? Ayi, sitibwera!”
15 Pamenepo Mose anakwiya kwambiri ndipo anati kwa Yehova, “Musalandire chopereka chawo. Sindinatenge kalikonse kwa iwo ngakhale bulu, ndiponso sindinalakwire wina aliyense wa iwo.”
16 Mose anati kwa Kora, “Iwe ndi okutsatira onse mudzaonekere pamaso pa Yehova mawa, iweyo ndi iwowo pamodzi ndi Aaroni. 17 Munthu aliyense akatenge chofukizira ndi kuyikamo lubani, zofukizira 250 zonse pamodzi ndi kuzibweretsa pamaso pa Yehova. Iwe ndi Aaroni mudzabweretsenso zofukizira zanu.” 18 Choncho munthu aliyense anatenga chofukizira chake nayikamo moto ndi lubani, ndipo anayima pamodzi ndi Mose ndi Aaroni pa khomo la tenti ya msonkhano. 19 Kora atasonkhanitsa omutsatira ake onse amene amatsutsa nawo pa khomo la tenti ya msonkhano, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa gulu lonselo. 20 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 21 “Chokani pakati pa gulu ili kuti ndithetse mkanganowu kamodzinʼkamodzi.”
22 Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa chafufumimba ndipo analira mokweza, “Chonde Mulungu, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, kodi mudzakwiyira gulu lonse pamene munthu mmodzi yekha ndiye amene wachimwa?”
23 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, 24 “Uza gulu lonse kuti, ‘Khalani kutali ndi matenti a Kora, Datani ndi Abiramu.’ ”
25 Mose anayimirira napita kwa Datani, Abiramu ndi kwa akuluakulu a Israeli amene ankamutsatira. 26 Anachenjeza gulu lonse kuti, “Khalani kutali ndi matenti a anthu oyipawa! Musakhudze kanthu kawo kalikonse, mukatero mudzawonongedwa limodzi nawo chifukwa cha machimo awo.” 27 Choncho anthuwo anachokadi ku matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali atatuluka nayima pamodzi ndi akazi awo, ana awo ndi makanda awo pa makomo a matenti awo.
28 Tsono Mose anati, “Umu ndi mmene mudzadziwire kuti Yehova ndiye amene anandituma kuti ndichite zinthu zonsezi ndipo kuti si maganizo anga. 29 Ngati anthu awa afa ndi imfa ya chilengedwe ndi kuwachitikira zomwe zimachitikira munthu aliyense, ndiye kuti Yehova sananditume. 30 Koma Yehova akachita china chake chachilendo, nthaka nitsekula pakamwa pake ndi kuwameza iwo pamodzi ndi zonse zimene ali nazo, iwowa nʼkulowa mʼmanda ali moyo, pamenepo mudzazindikira kuti anthu amenewa ananyoza Yehova.”
31 Atangotsiriza kuyankhula zimenezi, nthaka ya pamene anayimapo inagawikana 32 ndipo dziko linatsekula pakamwa pake ndi kuwameza pamodzi ndi nyumba zawo ndi anthu onse a Kora ndi katundu wawo yense. 33 Analowa mʼmanda amoyo pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. Nthaka inawatsekera ndi kuwawononga ndipo sanaonekenso. 34 Atamva kulira kwawo, Aisraeli onse amene anali pafupi ndi anthuwo anathawa akufuwula kuti, “Nthaka imezanso ife!”
35 Ndipo moto wochokera kwa Yehova unabwera nʼkunyeketsa anthu 250 amene ankapereka nsembe yofukiza aja.
36 Yehova anawuza Mose kuti, 37 “Uza Eliezara mwana wa Aaroni, wansembe kuti atenge zofukizirazo pakati pa mitembo yopsererayo ndipo amwazire makalawo kutali chifukwa zofukizirazo nʼzopatulika. 38 Izi ndi zofukizira za anthu omwe anafa chifukwa cha uchimo wawo. Musule zofukizirazo kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, chifukwa zinaperekedwa kwa Yehova ndipo ndi zopatulika. Zimenezi zikhale chizindikiro kwa Aisraeli.”
39 Choncho Eliezara, wansembe, anasonkhanitsa zofukizira zamkuwa zija zomwe anthu opsererawo anabwera nazo ndipo anazisula kuti zikhale zophimbira pa guwa lansembe, 40 monga momwe Yehova anamulangizira kudzera mwa Mose. Chimenechi chinali chikumbutso kwa Aisraeli kuti munthu wina aliyense, kupatula zidzukulu za Aaroni, sayenera kupsereza lubani pamaso pa Yehova, kuopa kuti munthu woteroyo angakhale ngati Kora ndi omutsatira ake.
41 Tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisraeli linatsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Iwo anati, “Inu mwapha anthu a Yehova.”
42 Koma pamene anthuwo anasonkhana kuti atsutsane ndi Mose ndi Aaroni, atatembenuka kuyangʼana ku tenti ya msonkhano, mwadzidzidzi mtambo unaphimba tentiyo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera. 43 Pamenepo Mose ndi Aaroni anapita patsogolo pa tenti ya msonkhano ija 44 ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 45 “Chokani pakati pa gulu la anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.” Ndipo iwo anagwa pansi chafufumimba.
46 Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Tenga chofukizira chako ndipo ikamo lubani pamodzi ndi moto wochokera pa guwa lansembe, fulumira, pita pa gulu la anthuwo ndipo ukachite nsembe yopepesera machimo awo popeza mkwiyo wa Yehova wafika, mliri wayamba.” 47 Ndipo Aaroni anachita monga ananenera Mose, nathamangira mʼkatikati mwa gulu la anthuwo. Pamenepo nʼkuti mliri utayamba kale pakati pa anthu aja ndipo Aaroni anafukiza lubani ndi kupereka nsembe yopepesera machimo awo. 48 Iye anayimirira pakati pa anthu amoyo ndi akufa ndipo mliri unaleka. 49 Komabe anthu 14, 700 anafa ndi mliriwo, kuwonjezera pa aja amene anafa chifukwa cha Kora. 50 Ndipo Aaroni anabwerera kwa Mose ku khomo la tenti ya msonkhano, chifukwa mliriwo unali utatha.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, ndakatulo ya Davide; pamene Doegi Mwedomu anapita kwa Sauli ndi kunena kuti “Davide wapita ku nyumba ya Ahimeleki.”
52 Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira ndi zoyipa, iwe munthu wamphamvu?
Nʼchifukwa chiyani ukudzitamandira tsiku lonse,
iwe munthu wochititsa manyazi pamaso pa Mulungu?
2 Tsiku lonse umakhalira kuganizira za kuwononga ena;
lilime lako lili ngati lumo lakuthwa,
ntchito yako nʼkunyenga.
3 Iwe umakonda choyipa mʼmalo mwa kuyankhula choonadi.
Umakonda kunama kupambana kuyankhula zoona.
Sela
4 Umakonda mawu onse opweteka,
iwe lilime lachinyengo!
5 Zoonadi Mulungu adzakutsitsa kupita ku chiwonongeko chamuyaya:
iye adzakukwatula ndi kukuchotsa mʼtenti yako;
iye adzakuzula kuchoka mʼdziko la amoyo.
6 Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha;
adzamuseka nʼkumanena kuti,
7 “Pano tsopano pali munthu
amene sanayese Mulungu linga lake,
koma anakhulupirira chuma chake chambiri
nalimbika kuchita zoyipa!”
8 Koma ine ndili ngati mtengo wa olivi
wobiriwira bwino mʼnyumba ya Mulungu;
ndimadalira chikondi chosatha cha Mulungu
kwa nthawi za nthawi.
9 Ine ndidzakutamandani kwamuyaya chifukwa cha zimene mwachita;
chifukwa cha zimene mwachita; mʼdzina lanu ndidzayembekezera
pakuti dzina lanulo ndi labwino. Ndidzakutamandani pamaso pa oyera mtima anu.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide.
53 Chitsiru chimati mu mtima mwake,
“Kulibe Mulungu.”
Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa;
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino.
2 Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano
pa ana a anthu
kuti aone ngati alipo wina wanzeru,
wofunafuna Mulungu.
3 Aliyense wabwerera,
iwo onse pamodzi akhala oyipa;
palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino,
ngakhale mmodzi.
4 Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi;
anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi,
ndipo sapemphera kwa Mulungu?
5 Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu
pamene panalibe kanthu kochititsa mantha.
Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo;
inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza.
6 Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni!
Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake,
lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Ndakatulo ya Davide. Pamene anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ndipo anati, “Kodi Davide sakubisala pakati pathu.”
54 Pulumutseni Inu Mulungu, mwa dzina lanu;
onetsani kuti ndine wosalakwa mwamphamvu yanu.
2 Imvani pemphero langa, Inu Mulungu
mvetserani mawu a pakamwa panga.
3 Alendo akundithira nkhondo;
anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga,
anthu amene salabadira za Mulungu.
4 Zoonadi Mulungu ndi thandizo langa;
Ambuye ndiye amene amandichirikiza ine.
5 Lolani kuti choyipa chifike pa iwo amene amandichita chipongwe;
mwa kukhulupirika kwanu awonongeni.
6 Ine ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu;
ndidzatamanda dzina lanu, Inu Yehova,
pakuti ndi labwino.
7 Pakuti Iyeyo wandipulumutsa ku masautso anga onse,
ndipo maso anga apenya kupambana kwa pa adani anga.
Masomphenya a Yesaya
6 Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. 2 Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. 3 Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti
“Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse.
Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
4 Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.
5 Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”
6 Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe. 7 Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
8 Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?”
Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”
9 Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa:
“ ‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa;
kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’
10 Tsono anthu amenewa uwaphe mtima;
uwagonthetse makutu,
ndipo uwatseke mʼmaso.
Mwina angaone ndi maso awo,
angamve ndi makutu awo,
angamvetse ndi mitima yawo,
kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
11 Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?”
Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti,
“Mpaka mizinda itasanduka mabwinja
nʼkusowa wokhalamo,
mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo,
mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,
12 mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali,
dziko nʼkusiyidwa kwathunthu.
13 Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko,
nachonso chidzawonongedwa.
Koma monga momwe mitengo ya muwanga ndi thundu
imasiyira chitsa pamene ayidula,
chonchonso mbewu yoyera idzatsalira ngati chitsa chotsala mʼdziko.”
Mawu Achilimbikitso Otsiriza
13 Pitirizani kukondana monga abale. 2 Musayiwale kusamalira alendo, pakuti pochita zimenezi anthu ena anasamalira angelo amene samawadziwa. 3 Muzikumbukira amene ali mʼndende ngati kuti inunso ndi omangidwa, ndiponso amene akusautsidwa ngati inunso mukuvutika.
4 Ukwati muziwulemekeza nonse, ndipo mwamuna ndi mkazi azikhala wokhulupirika, pakuti anthu adama ndi achigololo Mulungu adzawalanga. 5 Mtima wanu usakonde ndalama koma mukhutitsidwe ndi zimene muli nazo, chifukwa Mulungu anati,
“Sadzakusiyani,
kapena kukutayani konse.”
6 Kotero ife tikunena molimba mtima kuti,
“Ambuye ndiye mthandizi wanga;
sindidzachita mantha. Munthu angandichitenji ine?”
7 Muzikumbukira atsogoleri anu, amene amakulalikirani Mawu a Mulungu. Ganizirani zamoyo wawo ndipo tsatirani chikhulupiriro chawo. 8 Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse.
9 Musasocheretsedwe ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo. Nʼkwabwino kuti mitima yathu ilimbikitsidwe ndi chisomo osati ndi chakudya, chimene sichipindulitsa iwo amene amachidya. 10 Ife tili ndi guwa lansembe, ndipo ansembe otumikira mʼtenti cha Ayuda, saloledwa kudya zochokera pamenepo.
11 Mkulu wa ansembe amatenga magazi kukapereka nsembe chifukwa cha machimo, koma nyamayo imawotchedwa kunja kwa msasa. 12 Nʼchifukwa chakenso Yesu anafera kunja kwa mzinda kuti ayeretse anthu ake kudzera mʼmagazi ake. 13 Tiyeni tsono, tipite kwa iye kunja kwa msasa, titasenza chitonzo chake. 14 Pakuti ife tilibe mzinda wokhazikika koma tikudikira mzinda umene ukubwera.
15 Tsono, tiyeni kudzera mwa Yesu tipereke nsembe zachiyamiko kwa Mulungu osalekeza, chipatso cha milomo imene imavomereza dzina lake. 16 Ndipo musayiwale kumachita zabwino ndi kuthandiza ena, pakuti Mulungu amakondwera ndi nsembe zotere. 17 Muzimvera atsogoleri anu ndi kugonjera ulamuliro wawo, iwo amakuyangʼanirani monga anthu amene adzayenera kufotokoza za ntchito yawo pamaso pa Mulungu. Muziwamvera kuti agwire ntchito yawo ndi chimwemwe osati molemedwa pakuti izi sizingakupindulireni.
18 Mutipempherere ifenso. Pakuti tikutsimikiza kuti tili ndi chikumbumtima changwiro ndipo timafuna kuchita zinthu zonse mwaulemu. 19 Ine ndikukupemphani kuti mundipempherere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga.
20 Mulungu wamtendere, amene kudzera mʼmagazi a pangano lamuyaya anaukitsa Ambuye athu Yesu kwa akufa, amene ndi Mʼbusa wamkulu, 21 akupatseni chilichonse chabwino kuti muchite chifuniro chake ndipo Mulungu achite mwa ife, chimene chingamukomere kudzera mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ku nthawi zanthawi, Ameni.
22 Ndikukupemphani abale kuti mulandire mawu anga achilimbikitso, pakuti ndakulemberani mwachidule.
23 Ine ndikufuna kuti inu mudziwe kuti mʼbale wathu Timoteyo wamasulidwa. Ngati iye angafike msanga ndibwera naye kudzakuonani.
24 Mupereke moni kwa atsogoleri anu onse ndiponso kwa anthu onse a Mulungu. Abale ochokera ku Italiya akupereka moni.
25 Chisomo chikhale ndi inu nonse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.