Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 15

Zopereka Zapadera

15 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo, ndipo mukamadzapereka kwa Yehova, nsembe yotentha pa moto ya ngʼombe kapena nkhosa monga fungo lokoma kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena nsembe zina, nsembe yapadera chifukwa cha lumbiro kapena nsembe yoperekedwa mwaufulu kapenanso yoperekedwa pa chikondwerero, munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi. Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ”

“Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka, ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova.

“ ‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova, pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri. 10 Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 11 Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere. 12 Ngakhale zingachuluke chotani, chitani izi kwa iliyonse ya nyamazo.

13 “ ‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova. 14 Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira. 15 Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. 16 Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’ ”

17 Yehova anawuza Mose kuti, 18 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko 19 ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka. 20 Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu. 21 Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka.

Chopereka Chopepesera Machimo Ochita Mosadziwa

22 “ ‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose, 23 lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo, 24 ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa. 25 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo. 26 Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa.

27 “ ‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. 28 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa. 29 Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo.

30 “ ‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake. 31 Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’ ”

Wosasunga Sabata Aphedwa

32 Aisraeli ali mʼchipululu, munthu wina anapezeka akutola nkhuni tsiku la Sabata. 33 Amene anamupeza akutola nkhunizo anabwera naye kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa gulu lonse 34 ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye. 35 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.” 36 Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Mphonje pa Zovala

37 Yehova anawuza Mose kuti, 38 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira. 39 Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu. 40 Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu. 41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

Masalimo 51

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

51 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
    molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
molingana ndi chifundo chanu chachikulu
    mufafanize mphulupulu zanga.
Munditsuke zolakwa zanga zonse
    ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,
    ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa
    ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,
Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama
    pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,
    wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;
    mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,
    munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,
    mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
Mufulatire machimo anga
    ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

10 Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
    ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 Musandichotse pamaso panu
    kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu
    ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

13 Pamenepo ndidzaphunzitsa anthu amphulupulu njira zanu
    kuti ochimwa adzabwerere kwa inu.
14 Mundipulumutse ku tchimo lokhetsa magazi, Inu Mulungu,
    Mulungu wa chipulumutso changa,
    ndipo lilime langa lidzayimba zachilungamo chanu.
15 Inu Ambuye tsekulani milomo yanga,
    ndipo pakamwa panga padzalengeza matamando anu.
16 Inu simusangalatsidwa ndi nsembe wamba.
    Ndikanapereka nsembe yopsereza, Inu simukondwera nayo.
17 Nsembe za Mulungu ndi mzimu wosweka;
    mtima wosweka ndi wachisoni
    Inu Mulungu simudzawunyoza.

18 Mwa kukoma mtima kwanu mupange Ziyoni kuti alemere;
    mumange makoma a Yerusalemu.
19 Kotero kudzakhala nsembe zachilungamo,
    nsembe yonse yopsereza yokondweretsa Inu;
    ndipo ngʼombe zazimuna zidzaperekedwa pa guwa lanu la nsembe.

Yesaya 5

Nyimbo ya Munda Wamphesa

Ndidzamuyimbira bwenzi langa
    nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa:
Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa
    pa phiri la nthaka yachonde.
Anatipula nachotsa miyala yonse
    ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri.
Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo
    ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo.
Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,
    koma ayi, unabala mphesa zosadya.

“Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,
    weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa
    kupambana chomwe ndawuchitira kale?
Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino,
    bwanji unabala mphesa zosadya?
Tsopano ndikuwuzani
    chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa:
ndidzachotsa mpanda wake,
    ndipo mundawo udzawonongeka;
ndidzagwetsa khoma lake,
    ndipo nyama zidzapondapondamo.
Ndidzawusandutsa tsala,
    udzakhala wosatengulira ndi wosalimira
    ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.
Ndidzalamula mitambo
    kuti isagwetse mvula pa mundapo.”

Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse
    ndi Aisraeli,
ndipo anthu a ku Yuda ndiwo
    minda yake yomukondweretsa.
Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;
    mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.

Tsoka ndi Chiweruzo

Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba,
    ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda,
mpaka mutalanda malo onse
    kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.

Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti,

“Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja,
    nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
10 Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi,
    kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”

11 Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa
    nathamangira chakumwa choledzeretsa,
amene amamwa mpaka usiku
    kufikira ataledzera kotheratu.
12 Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe,
    matambolini, zitoliro ndi vinyo,
ndipo sasamala ntchito za Yehova,
    salemekeza ntchito za manja ake.
13 Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo
    chifukwa cha kusamvetsa zinthu;
atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala,
    ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
14 Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta
    ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake;
mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka;
    adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko.
15 Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa,
    anthu onse adzachepetsedwa,
    anthu odzikuza adzachita manyazi.
16 Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama.
    Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
17 Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo;
    ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.

18 Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo,
    ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,
19 amene amanena kuti, “Yehova afulumire,
    agwire ntchito yake mwamsanga
    kuti ntchitoyo tiyione.
Ntchito zionekere,
    zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita,
    zichitike kuti tizione.”

20 Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino
    ndipo zabwino amaziyesa zoyipa,
amene mdima amawuyesa kuwala
    ndipo kuwala amakuyesa mdima,
amene zowawasa amaziyesa zotsekemera
    ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.

21 Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru
    ndipo amadziyesa ochenjera.

22 Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo
    ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
23 amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu
    koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
24 Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu
    ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto,
momwemonso mizu yawo idzawola
    ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi;
chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse,
    ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
25 Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake;
    watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha
Mapiri akugwedezeka,
    ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala.

Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke,
    dzanja lake likanali chitambasulire;

26 Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali,
    akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.
Awo akubwera,
    akubweradi mofulumira kwambiri!
27 Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa,
    palibe amene akusinza kapena kugona;
palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka,
    palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.
28 Mivi yawo ndi yakuthwa,
    mauta awo onse ndi okoka,
ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi,
    magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
29 Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango,
    amabangula ngati misona ya mkango;
imadzuma pamene ikugwira nyama
    ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
30 Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula
    ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja.
Ndipo wina akakayangʼana dzikolo
    adzangoona mdima ndi zovuta;
    ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.

Ahebri 12

Yesu Chitsanzo Chathu

12 Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu. Muzilingalira za Iye amene anapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafowoke ndi kutaya mtima. Polimbana ndi uchimo, simunafike mpaka pokhetsa magazi.

Mulungu Amalanga Ana ake

Kodi mwayiwala mawu olimbitsa mtima aja, amene Mulungu anayankhula kwa inu ngati ana ake? Mawuwo ndi awa:

“Mwana wanga, usapeputse kulanga kwa Ambuye
    ndipo usataye mtima pamene akukudzudzula.
Chifukwa Ambuye amadzudzula amene amawakonda
    ndipo amalanga aliyense amene amamulandira.”

Pamene mukupirira masautso monga chilango, Mulungu achitira inu monga ana ake. Kodi ndi mwana wotani amene abambo ake samulanga? Ngati inu simulangidwa, komatu aliyense amalangidwa, ndiye kuti sindinu ana enieni koma amʼchigololo. Komanso, tonsefe tinali ndi abambo athu otibala amene amatilanga ndipo timawapatsa ulemu. Nanga kodi sitidzagonjera Atate a mizimu yathu kuti tikhale ndi moyo? 10 Abambo athu ankatilanga kwa kanthawi kochepa monga amaonera kufunika kwake, koma Mulungu amatilanga kuti tipindule, kuti tikhale oyera mtima. 11 Palibe chilango chimene chimaoneka kuti ndi chabwino pa nthawiyo, komatu chowawa. Koma pambuyo pake, chimabweretsa chipatso chachilungamo ndi mtendere kwa iwo amene aleredwa mwa njira imeneyi.

12 Nʼchifukwa chake limbitsani manja anu otopa ndi mawondo anu ogowoka. 13 Muziyenda mʼnjira zowongoka, kuti iwo amene akukutsatirani ngakhale ndi olumala ndi ofowoka asapunthwe ndi kugwa koma adzilimbikitsidwa.

Chenjezo kwa Okana Mulungu

14 Yesetsani kukhala pa mtendere ndi anthu onse ndi kukhala oyera mtima, pakuti popanda chiyero palibe ndi mmodzi yemwe adzaona Ambuye. 15 Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri. 16 Yangʼanitsitsani kuti pasakhale wina wachigololo. Kapena wosapembedza ngati Esau, amene chifukwa cha chakudya cha kamodzi kokha anagulitsa ukulu wake. 17 Monga inu mukudziwa, pambuyo pake pamene anafuna kuti adalitsidwe anakanidwa. Sanapezenso mpata woti asinthe maganizo, ngakhale anafuna madalitsowo ndi misozi.

18 Inu simunafike ku phiri limene mungathe kulikhudza, loyaka moto wa mdima bii, la mphepo yamkuntho; 19 limene pali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mawu. Anthu amene amamva mawuwo anapempha kuti asawayankhulenso mawu ena. 20 Iwo anachita mantha ndi lamulo lija lakuti, “Ngakhale nyama ikangokhudza phirilo, iphedwe ndi miyala.” 21 Maonekedwenso a Mose anali woopsa kwambiri, ngakhale Mose yemwe anati, “Ine ndinachita mantha ndi kunjenjemera.”

22 Koma inu mwafika ku Phiri la Ziyoni, ku mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba. Mwafika mu msonkhano wa angelo osangalala osawerengeka. 23 Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro. 24 Kwa Yesu mʼkhalapakati wa pangano latsopano, ndiponso mwafika ku magazi owazidwa amene amayankhula mawu abwino kuposa magazi a Abele.

25 Chenjerani kuti musakane kumvera amene akuyankhula nanu. Anthu amene anakana kumvera iye amene anawachenjeza uja pa dziko lapansi pano, sanapulumuke ku chilango ayi, nanga tsono ife tidzapulumuka bwanji ngati tikufulatira wotichenjeza wochokera kumwamba? 26 Pa nthawiyo mawu ake anagwedeza dziko lapansi, koma tsopano Iye walonjeza kuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza osati dziko lapansi lokha komanso thambo.” 27 Mawu akuti, “Kamodzi kenanso,” akuonetsa kuchotsedwa kwa zimene zitha kugwedezeka, zonse zolengedwa, kotero kuti zimene sizingatheke kugwedezeka zitsale.

28 Popeza tikulandira ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhale oyamika ndi kupembedza Mulungu movomerezeka ndi mwaulemu ndi mantha. 29 Pakuti Mulungu wathu ndi moto wonyeketsa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.