M’Cheyne Bible Reading Plan
Anthu Awukira
14 Usiku umenewo gulu lonse la Aisraeli linalira mofuwula kwambiri. 2 Ndipo Aisraeli onse anayankhula motsutsana ndi Mose ndi Aaroni. Gulu lonse linanena kwa iwo kuti, “Kunali bwino tikanafera ku Igupto kapena mʼchipululu muno! 3 Nʼchifukwa chiyani Yehova akutilowetsa mʼdziko limenelo? Kodi kuti tikaphedwe ndi lupanga? Kuti akazi ndi ana athu akatengedwe ngati katundu wolanda ku nkhondo? Kodi sikungakhale bwino kuti tibwerere ku Igupto?” 4 Ndipo anawuzana wina ndi mnzake kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri ndipo tibwerere ku Igupto.”
5 Koma Mose ndi Aaroni anadzigwetsa pansi chafufumimba pamaso pa Aisraeli onse omwe anasonkhana pamenepo. 6 Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, omwe anali amodzi mwa amene anakazonda nawo dziko, anangʼamba zovala zawo 7 ndipo anati kwa gulu lonse la Aisraeli, “Dziko limene tinakayendamo ndi kuliona ndi labwino kwambiri zedi. 8 Ngati Yehova akukondwera nafe, adzatitsogolera kulowa mʼdziko limenelo. Dziko loyenda mkaka ndi uchi adzalipereka kwa ife, 9 koma musawukire Yehova. Komanso musaope anthu a mʼdzikomo, pakuti tidzawagonjetsa. Chitetezo chawachokera, koma ife Yehova ali nafe. Musawaope.”
10 Koma gulu lonse linayankhula zofuna kuwagenda miyala. Pamenepo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisraeli onse ku tenti ya msonkhano. 11 Yehova anawuza Mose kuti, “Anthu awa adzandinyoza mpaka liti? Sadzandikhulupirira mpaka liti, ngakhale ndachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi pakati pawo? 12 Ndidzawakantha ndi mliri ndi kuwawononga. Koma ndidzakusandutsa iwe mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwo.”
13 Mose anati kwa Yehova, “Aigupto adzamva zimenezi! Mwa mphamvu yanu munawatulutsa anthu amenewa pakati pawo. 14 Ndipo iwowo adzawuza anthu okhala mʼdziko lino zimenezi. Anthuwa amva kale kuti Inu Yehova mumakhala pakati pa anthu amenewa ndi kuti Inuyo Yehova mwawaonekera maso ndi maso. Mtambo wanu umakhala pamwamba pawo ndiponso mumayenda nawo mu mtambo woyima, masana ndi moto woyima, usiku. 15 Tsono mukawapha anthu onsewa nthawi imodzi, mayiko amene anamva za Inu adzati, 16 ‘Yehova walephera kuwalowetsa anthuwo mʼdziko lomwe anawalonjeza molumbira, ndipo wawapha mʼchipululu.’
17 “Chonde Ambuye wonetsani mphamvu yanu monga munalonjezera kuti, 18 ‘Yehova sakwiya msanga, ndipo ndi wodzaza ndi chikondi chosasinthika, wokhululukira tchimo ndi kuwukira. Koma Iye sadzaleka kulanga ochimwa. Iyeyo amalanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo kufikira mʼbado wachitatu ndi wachinayi.’ 19 Chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, akhululukireni anthuwa tchimo lawo monga mwakhala mukuwakhululukira kuchokera pa nthawi imene anachoka ku Igupto mpaka tsopano.”
20 Yehova anayankha kuti, “Ndawakhululukira monga wapemphera. 21 Komabe, ndikunenetsa kuti pali Ine, ndiponso pamene dziko lapansi ladzaza ndi ulemerero wa Yehova, 22 palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinazichita ku Igupto ndi mʼchipululu muno, koma osandimvera ndi kundiyesa kokwanira kakhumi, 23 palibe ndi mmodzi yemwe wa anthu amenewa amene adzaone dziko limene ndinalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo. Aliyense amene anandinyoza sadzaliona dzikolo. 24 Koma mtumiki wanga Kalebe, pakuti ali ndi mtima wosiyana ndi ena ndiponso amanditsatira ndi mtima wonse, ndidzamulowetsa mʼdziko limene anapitamolo ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo ngati cholowa chawo. 25 Ndipo popeza kuti Aamaleki ndi Akanaani akukhala ku chigwa, mawa mubwerere ndipo mupite ku chipululu podzera ku Nyanja Yofiira.”
26 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 27 “Kodi anthu oyipawa adzangʼungʼudza ndi kutsutsana nane mpaka liti? Ndamva madandawulo a Aisraeli ongʼungʼudzawa. 28 Tsono awuze kuti, ‘Ndikulumbira pali Ine,’ akutero Yehova, ‘Ndidzakuchitirani zinthu zonse zimene ndamva inu mukunena: 29 Mitembo yanu idzakhala ili ngundangunda mʼchipululu muno; mtembo wa munthu aliyense pakati panu amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo, amene anawerengedwa pa chiwerengero chija ndipo anangʼungʼudza motsutsana nane. 30 Palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene adzalowe mʼdziko lomwe ndinalumbira mokweza manja kuti likhale lanu, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni. 31 Koma ana anu amene mukunena kuti adzatengedwa ngati katundu wolanda ku nkhondo, Ine ndidzawalowetsa kuti akasangalale mʼdziko limene munalikana. 32 Koma inu mitembo yanu idzakhala ngundangunda mʼchipululu muno. 33 Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu muno zaka makumi anayi, kuvutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka munthu womaliza mwa inu atafa mʼchipululu muno. 34 Mudzavutika chifukwa cha machimo anu kwa zaka makumi anayi Chaka chimodzi chikuyimira tsiku limodzi la masiku makumi anayi amene munakazonda dziko lija ndipo mudzadziwa kuyipa kwake kwa kukangana ndi Ine.’ 35 Ine Yehova, ndanena, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oyipawa, amene agwirizana kunditsutsa. Adzathera mʼchipululu momwe muno, adzafera muno basi.”
36 Ndipo anthu amene Mose anawatuma kukazonda dziko aja anachoka pamaso pake nachititsa gulu lonse la anthu kuwukira Moseyo chifukwa chofalitsa mbiri yoyipa ya dzikolo. 37 Anthu amene ankafalitsa mbiri yoyipa ya dzikolo anakanthidwa ndi mliri ndipo anafa pamaso pa Yehova. 38 Mwa anthu amene anakaona dzikolo, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune ndi okhawo amene anapulumuka.
39 Mose atafotokoza izi kwa Aisraeli onse, anthuwo analira kwambiri. 40 Mmamawa tsiku linalo anapita mbali ya ku dziko la mapiri. Iwo anati, “Tachimwa, tipita ku dziko limene Yehova anatilonjeza.”
41 Koma Mose anati, “Chifukwa chiyani simukumvera lamulo la Yehova? Zimenezi sizitheka! 42 Musapite chifukwa Yehova sali pakati panu. Mudzagonjetsedwa ndi adani anu 43 chifukwa kumeneko mukakumana ndi Aamaleki ndi Akanaani. Popeza mwaleka kutsata Yehova, Iyeyo sadzakhala nanu ndipo mudzaphedwa ndi lupanga.”
44 Komabe mwa maganizo awo anapita molunjika dziko la mapiri ngakhale kuti Mose sanachoke ndi Bokosi la Chipangano la Yehova pa msasa. 45 Koma Aamaleki ndi Akanaani amene ankakhala ku dziko lamapirilo anatsika ndi kumenyana nawo ndipo anawakantha mʼnjira yonse mpaka ku Horima.
Salimo la Asafu.
50 Wamphamvuyo, Yehova Mulungu,
akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi
kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
2 Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri
Mulungu akuwala.
3 Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete;
moto ukunyeketsa patsogolo pake,
ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
4 Iye akuyitanitsa zamumlengalenga
ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
5 Mundisonkhanitsire okhulupirika anga,
amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
6 Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake,
pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.
7 Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula,
iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa;
ndine Mulungu, Mulungu wako.
8 Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako,
kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.
9 Ine sindikufuna ngʼombe yayimuna kuchokera mʼkhola lako
kapena mbuzi za mʼkhola lako,
10 pakuti nyama iliyonse yakunkhalango ndi yanga
ndiponso ngʼombe za ku mapiri ochuluka.
11 Ine ndimadziwa mbalame iliyonse mʼmapiri
ndiponso zolengedwa zonse zakutchire ndi zanga.
12 Ndikanakhala ndi njala sindikanakuwuzani,
pakuti dziko lonse ndi zonse zimene zili mʼmenemo ndi zanga.
13 Kodi ndimadya nyama ya ngʼombe zazimuna
kapena kumwa magazi a mbuzi?
14 “Pereka nsembe zachiyamiko kwa Mulungu,
kwaniritsa malonjezo ako kwa Wammwambamwamba.
15 Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso;
Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”
16 Koma kwa woyipa, Mulungu akuti,
“Kodi uli ndi mphamvu yanji kuti uzinena malamulo anga
kapena kutenga pangano langa pa milomo yako?
17 Iwe umadana ndi malangizo anga
ndipo umaponyera kumbuyo kwako mawu anga.
18 Ukaona wakuba umamutsatira,
umachita maere ako pamodzi ndi achigololo
19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako pa zinthu zoyipa
ndipo umakonza lilime lako kuchita chinyengo.
20 Nthawi zonse umayankhula motsutsana ndi mʼbale wako
ndipo umasinjirira mwana wa amayi ako enieni.
21 Wachita zimenezi ndipo Ine ndinali chete;
umaganiza kuti ndine wofanana nawe
koma ndidzakudzudzula
ndipo ndidzakutsutsa pamaso pako.
22 “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu
kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
23 Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza,
ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse
chipulumutso cha Mulungu.”
Chiweruzo pa Yerusalemu ndi Yuda
3 Taonani tsopano, Ambuye
Yehova Wamphamvuzonse,
ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda
zinthu pamodzi ndi thandizo;
adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
2 anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,
oweruza ndi aneneri,
anthu olosera ndi akuluakulu,
3 atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,
aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
4 Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo;
ana akhanda ndiwo adzawalamulire.
5 Anthu adzazunzana,
munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake.
Anthu wamba adzanyoza
akuluakulu.
6 Munthu adzagwira mʼbale wake
mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati,
“Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu;
lamulira malo opasuka ano!”
7 Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti,
“Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake.
Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga;
musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
8 Yerusalemu akudzandira,
Yuda akugwa;
zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova,
sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
9 Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa;
amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu;
salibisa tchimo lawolo.
Tsoka kwa iwo
odziputira okha mavuto.
10 Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino,
pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.
11 Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo!
Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
12 Achinyamata akupondereza anthu anga,
ndipo amene akuwalamulira ndi akazi.
Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani;
akukuchotsani pa njira yanu.
13 Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu;
wakonzeka kuti aweruze anthu ake.
14 Yehova akuwazenga milandu
akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:
“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;
nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
15 Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga,
nʼkudyera masuku pamutu amphawi?”
Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
16 Yehova akunena kuti,
“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,
akuyenda atakweza makosi awo,
akukopa amuna ndi maso awo
akuyenda monyangʼama
akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
17 Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;
Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
18 Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi, 19 ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope, 20 maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa, 21 mphete ndi zipini, 22 zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama, 23 magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
24 Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,
mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;
mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;
mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;
mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
25 Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,
asilikali ako adzafera ku nkhondo.
26 Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;
Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.
4 Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri
adzagwira mwamuna mmodzi,
nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu,
ndi kuvala zovala zathu;
inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu.
Tichotseni manyazi aumbeta!”
Nthambi ya Yehova
2 Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli. 3 Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu. 4 Ambuye adzasambitsa akazi a Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zawo. Adzatsuka magazi amene anakhetsedwa mu Yerusalemu ndi mzimu wachiweruzo ndiponso mzimu wamoto. 5 Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova. 6 Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothawiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi owusiramo mvula.
Za Chikhulupiriro cha anthu Akale
11 Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu. 2 Ndi chikhulupiriro chimenechi makolo athu akale anayamikidwa.
3 Ndi chikhulupiriro timazindikira kuti dziko lapansi ndi la mmwamba zinapangidwa ndi Mawu a Mulungu, ndikuti zinthu zoonekazi zinachokera ku zinthu zosaoneka. 4 Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa imene Kaini anapereka. Ndi chikhulupiriro anatchedwa munthu wolungama Mulungu atayamikira zopereka zake. Ngakhale iye anafa, akuyankhulabe chifukwa cha chikhulupiriro chakecho.
5 Ndi chikhulupiriro Enoki anatengedwa wamoyo, motero iye sanalawe imfa; sanapezeke chifukwa Mulungu anamutenga. Pakuti asanatengedwe anayamikiridwa kuti ankakondweretsa Mulungu. 6 Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka mphotho kwa amene akumufunitsitsa.
7 Ndi chikhulupiriro, Nowa atachenjezedwa za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anachita mantha napanga chombo kuti apulumutsire banja lake. Ndi chikhulupiriro chake anatsutsa dziko lapansi ndipo analandira chilungamo chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.
8 Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita. 9 Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso. 10 Pakuti amadikira mudzi wokhala ndi maziko, umene mmisiri ndi womanga wake ndi Mulungu.
11 Ndi chikhulupiriro Sara analandira mphamvu zokhala ndi pakati ngakhale kuti zaka zake zobala mwana zinali zitapita kale, popeza anamutenga amene analonjeza kukhala wokhulupirika. 12 Nʼchifukwa chake mwa munthu mmodzi, amene anali ngati wakufa, munatuluka mibado yochuluka ngati nyenyezi ndi yosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
13 Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi. 14 Anthu amene amanena zinthu zotere amaonekeratu kuti akufuna dziko lawo lenileni. 15 Akanakhala kuti akuganizira za dziko limene analisiya akanapeza mpata obwerera kwawo. 16 Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.
17 Ndi chikhulupiriro Abrahamu, Mulungu atamuyesa, anapereka Isake ngati nsembe. Ngakhale anali munthu woti Mulungu anamulonjeza, anakhala wokonzeka kupereka nsembe mwana wake mmodzi yekhayo. 18 Za mwana ameneyu Mulungu anamuwuza iye kuti, “Zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake.” 19 Abrahamu amazindikira kuti Mulungu angathe kuukitsa akufa, ndipo tingathe kunena mofanizira kuti iye analandiranso Isake ngati wouka kwa akufa.
20 Ndi chikhulupiriro Isake anadalitsa Yakobo ndi Esau pa zatsogolo lawo.
21 Ndi chikhulupiriro, pamene Yakobo ankamwalira anadalitsa ana awiri a Yosefe, ndipo anapembedza Mulungu atatsamira ndodo yake.
22 Ndi chikhulupiriro Yosefe ali pafupi kumwalira anayankhula za kutuluka kwa Aisraeli mu Igupto ndipo anawawuza zoti adzachite ndi mafupa ake.
23 Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.
24 Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao. 25 Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. 26 Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo. 27 Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo. 28 Ndi chikhulupiriro anachita Paska ndi kuwaza magazi, kuti mngelo wowononga ana oyamba kubadwa asaphe ana oyamba kubadwa a Aisraeli.
29 Ndi chikhulupiriro Aisraeli anawoloka Nyanja Yofiira ngati pa mtunda powuma, koma Aigupto atayesa kutero anamizidwa.
30 Ndi chikhulupiriro mpanda wa Yeriko unagwa, Aisraeli atawuzungulira kasanu ndi kawiri.
31 Ndi chikhulupiriro Rahabe, mkazi wadama sanaphedwe pamodzi ndi osamvera aja chifukwa analandira bwino ozonda aja ku nyumba kwake.
32 Kodi ndinenenso chiyani? Nthawi yandichepera yoti ndinene za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, Samueli ndi aneneri, 33 amene ndi chikhulupiriro anagonjetsa mafumu, anakhazikitsa chilungamo ndi kulandira zimene zinalonjezedwa. Anatseka pakamwa pa mikango, 34 anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo. 35 Amayi ena analandira anthu awo amene anafa, ataukitsidwanso. Enanso anazunzidwa ndipo anakana kumasulidwa, kuti adzaukenso ndi moyo wabwino. 36 Ena anawaseka ndi kuwakwapula, pamenenso ena anamangidwa ndi kupita ku ndende. 37 Anagendedwa miyala; anachekedwa pakati; ena anaphedwa ndi lupanga. Iwo anayendayenda atavala zikopa zankhosa ndi zikopa zambuzi, umphawi okhaokha, ozunzidwa ndi kuvutitsidwa. 38 Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje.
39 Onsewa anayamikidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, komabe palibe wa iwo amene analandira zimene analonjezedwa. 40 Mulungu anatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.