Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 11

Moto Wochokera kwa Yehova

11 Anthu atadandaula kwa Yehova chifukwa cha mavuto awo, Yehovayo anamva ndipo anakwiya kwambiri. Kenaka moto wa Yehova unayaka pakati pawo ndi kutentha zigawo zina za kunja kwa msasa. Anthuwo analira kwa Mose ndipo Moseyo atapemphera kwa Yehova, motowo unazima. Motero malowo anawatcha Tabera, chifukwa moto wa Yehova unayaka pakati pawo.

Zinziri Zochokera kwa Yehova

Anthu ena osokoneza amene anali pakati pa Aisraeli anayamba kukhumba chakudya cha ku Igupto ndipo Aisraeli nawonso anayamba kufuwula kwambiri nʼkumati, “Tikanangopeza nyama yoti nʼkudya! Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Igupto komanso nkhaka, mavwende, anyezi wamitundumitundu ndi adyo. Koma tsopano chilakolako chathu chatha. Sitikuona kanthu kena kakudya koma mana basi!”

Mana ankafanana ndi mbewu zamapira ndipo maonekedwe ake anali ngati ulimbo wowuma. Anthu ankapita kukatola manawo, nʼkumasinja mu mtondo kapena kupera. Ankawaphika mu mʼphika kapena kupanga makeke. Ndipo ankakoma ngati makeke ophikira mafuta a olivi. Mame akamagwa pa msasawo usiku ankagwera kumodzi ndi manawo.

10 Mose anamva anthu a banja lililonse akufuwula, banja lililonse pa khomo la tenti yake. Yehova anakwiya kwambiri ndipo Mose anavutikanso mu mtima. 11 Mose anafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani mwabweretsa mavuto otere pa mtumiki wanune? Nʼchiyani chimene ndachita choti sichinakusangalatseni mpaka kundisenzetsa katundu wa anthu onsewa? 12 Kodi Ndine amene ndinatenga pathupi pa anthu onsewa? Kodi ndinawabala ndine? Bwanji mukundiwuza kuti ndiwanyamule mʼmanja mwanga, monga momwe mlezi amanyamulira kamwana, kupita nawo ku malo omwe munalonjeza ndi lumbiro kwa makolo awo? 13 Ndingayipeze kuti nyama yoti anthu onsewa adye? Iwowa akulirira ine kuti, ‘Tipatse nyama tidye!’ 14 Sindingathe kusamala anthu onsewa ndekha. Katundu ameneyu ndi wolemera kwambiri kwa ine. 15 Ngati umu ndi mmene muzichitira nane, chonde ingondiphani pompano. Koma ngati mwandikomera mtima ndiye ndisaonenso mavutowa.”

16 Yehova anawuza Mose kuti, “Undibweretsere anthu 70 ochokera pakati pa akuluakulu a Aisraeli, amene umawadziwa kuti ndiwo atsogoleri komanso akuluakulu a mabanja. Abwere ku tenti ya msonkhano kuti ayime kumeneko pamodzi ndi iwe. 17 Ndidzatsika ndi kuyankhula nawe kumeneko, ndipo ndidzatenga mzimu umene uli pa iwe ndi kuyika pa iwowo. Adzakuthandiza kusenza nkhawa za anthuwa ndipo sudzasenzanso wekha.”

18 “Uwawuze anthuwo kuti, ‘Mudziyeretse, kukonzekera mawa, pamene mudzadya nyama.’ Yehova anakumvani pamene munkalira kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanapeza nyama yoti tidye! Tinkakhala bwino ku Igupto!’ Tsopano Yehova adzakupatsani nyama ndipo mudzayidyadi. 19 Simudzadya tsiku limodzi lokha, kapena masiku awiri, kapena asanu, khumi kapena masiku makumi awiri, 20 koma mwezi wonse, mpaka itakukolani ndi kutopa nayo chifukwa mwakana Yehova yemwe ali pakati panu ndipo mwalira pamaso pake kuti, ‘Bwanji tinachoka ku Igupto?’ ”

21 Koma Mose anati, “Taonani pano ndili pakati pa anthu 600,000 amene ndi kuyenda nawo ndipo Inuyo mukuti, ‘Ndidzawapatsa nyama kuti adye mwezi wathunthu!’ 22 Kodi ngakhale titapha nkhosa ndi ngʼombe, zingawakwanire? Ngakhale titagwira nsomba zonse za mʼnyanja, kodi zingawakwanire iwowa?”

23 Yehova anayankha Mose kuti, “Kodi dzanja langa ndi lalifupi? Uwona tsopano ngati zimene ndanenazo zichitike kapena ayi.”

24 Choncho Mose anatuluka nakawuza anthu zomwe Yehova ananena. Anasonkhanitsa pamodzi akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja ndi kuwayimiritsa mozungulira Chihema. 25 Ndipo Yehova anatsika mʼmitambo ndi kuyankhula naye ndipo anatengako mzimu womwe unali pa Mose ndi kuwuyika pa akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja. Pamene mzimuwo unakhazikika pa akuluakuluwo, anayamba kunenera koma sanapitirize.

26 Koma anthu ena awiri omwe mayina awo anali Elidadi ndi Medadi, anatsalira mu msasa. Anali nawo mʼgulu la olembedwa aja, koma sanapite nawo ku Chihema. Komabe mzimu unakhala pa iwo ndipo ananenera ali mu msasa. 27 Mnyamata wina anathamanga kudzawuza Mose kuti, “Elidadi ndi Medadi akunenera mu msasa.”

28 Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha kuti, “Mbuye wanga Mose, aletseni!”

29 Koma Mose anati, “Kodi ukuchita nsanje chifukwa cha ine? Ndikanakonda kuti anthu onse a Yehova akhale aneneri ndi kuti Yehova ayike mzimu wake pa iwo!” 30 Mose ndi akuluakulu a Israeli aja anabwerera ku msasa.

31 Pamenepo Yehova anawutsa mphepo yochokera ku nyanja imene inabweretsa zinziri. Zinzirizo zinagwera pansi kuzungulira msasa, mtunda wa kilomita imodzi mbali zonse ndipo msinkhu wake unali mita imodzi. 32 Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse. 33 Koma pamene anthuwo ankadya nyamayo, asanayimeze nʼkomwe, ukali wa Yehova unafika pa iwo ndipo Iye anawakantha ndi mliri woopsa. 34 Nʼchifukwa chake malowo anawatcha Kibiroti Hatava chifukwa pamenepo anakwirirapo anthu osusuka aja.

35 Kuchoka pa Kibiroti Hatava anthuwo anayenda kupita ku Heziroti ndipo anakhala kumeneko kwa kanthawi.

Masalimo 48

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
    mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
Lokongola mu utali mwake,
    chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
    mzinda wa Mfumu yayikulu.
Mulungu ali mu malinga ake;
    Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
    pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
    anathawa ndi mantha aakulu.
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
    ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
    zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.

Monga momwe tinamvera,
    kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
    mu mzinda wa Mulungu wathu.
    Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
    ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
    matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
    dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
    midzi ya Yuda ndi yosangalala
    chifukwa cha maweruzo anu.

12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
    werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
    penyetsetsani malinga ake,
    kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
    Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

Yesaya 1

Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.

Anthu Owukira

Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi!
    Pakuti Yehova wanena kuti,
“Ndinabala ana ndi kuwalera,
    koma anawo andiwukira Ine.
Ngʼombe imadziwa mwini wake,
    bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake,
koma Israeli sadziwa,
    anthu anga samvetsa konse.”

Haa, mtundu wochimwa,
    anthu olemedwa ndi machimo,
obadwa kwa anthu ochita zoyipa,
    ana odzipereka ku zoyipa!
Iwo asiya Yehova;
    anyoza Woyerayo wa Israeli
    ndipo afulatira Iyeyo.

Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe?
    Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira?
Mutu wanu wonse uli ndi mabala,
    mtima wanu wonse wafowokeratu.
Kuchokera ku phazi mpaka ku mutu
    palibe pabwino,
paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda,
    mabala ali magazi chuchuchu,
mabala ake ngosatsuka, ngosamanga
    ndiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.

Dziko lanu lasanduka bwinja,
    mizinda yanu yatenthedwa ndi moto;
minda yanu ikukololedwa ndi alendo
    inu muli pomwepo,
    dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha
    ngati nsanja mʼmunda wampesa,
ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka,
    ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
Yehova Wamphamvuzonse akanapanda
    kutisiyira opulumuka,
tikanawonongeka ngati Sodomu,
    tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.

10 Imvani mawu a Yehova,
    inu olamulira Sodomu;
mverani lamulo la Mulungu wathu,
    inu anthu a ku Gomora!
11 Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani
    nsembe zanu zochuluka?”
“Zandikola nsembe zanu zopsereza
    za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa;
sindikusangalatsidwanso
    ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
12 Ndani anakulamulirani kuti
    mubwere nazo pamaso panga?
    Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
13 Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo!
    Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine.
Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa,
    kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
14 Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika
    ndimadana nazo.
Zasanduka katundu wondilemera;
    ndatopa kuzinyamula.
15 Mukamatambasula manja anu popemphera,
    Ine sindidzakuyangʼanani;
ngakhale muchulukitse mapemphero anu,
    sindidzakumverani.
Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
16     sambani, dziyeretseni.
Chotsani pamaso panu
    ntchito zanu zoyipa!
Lekani kuchita zoyipa,
17     phunzirani kuchita zabwino!
Funafunani chilungamo,
    thandizani oponderezedwa.
Tetezani ana amasiye,
    muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”

18 Yehova akuti,
    “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu.
Ngakhale machimo anu ali ofiira,
    adzayera ngati thonje.
Ngakhale ali ofiira ngati kapezi,
    adzayera ngati ubweya wankhosa.
19 Ngati muli okonzeka kundimvera
    mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
20 koma mukakana ndi kuwukira
    mudzaphedwa ndi lupanga.”
            Pakuti Yehova wayankhula.

21 Taonani momwe mzinda wokhulupirika
    wasandukira wadama!
Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama;
    mu mzindamo munali chilungamo,
    koma tsopano muli anthu opha anzawo!
22 Siliva wako wasanduka wachabechabe,
    vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.
23 Atsogoleri ako ndi owukira,
    anthu ogwirizana ndi mbala;
onse amakonda ziphuphu
    ndipo amathamangira mphatso.
Iwo sateteza ana amasiye;
    ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.
24 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu,
    Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti,
“Haa, odana nane ndidzawatha,
    ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
25 Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe;
    ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa,
    monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
26 Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana,
    aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja.
Kenaka iweyo udzatchedwa
    mzinda wolungama,
    mzinda wokhulupirika.”

27 Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama,
    anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.
28 Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi,
    ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.

29 “Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu
    imene inkakusangalatsani;
mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda
    imene munayipatula.
30 Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota,
    mudzakhala ngati munda wopanda madzi.
31 Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma,
    ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali;
motero zonse zidzayakira limodzi,
    popanda woti azimitse motowo.”

Ahebri 9

Kupembedza mʼTenti ya Dziko Lapansi

Pangano loyamba lija linali ndi malamulo okhudza chipembedzo, ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu. Anthu ankamanga chihema. Mʼchipinda choyamba munali choyikapo nyale, tebulo ndi buledi woperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa Malo Opatulika. Kuseri kwa chinsalu chotchinga chachiwiri kunkatchedwa Malo Opatulika kwambiri. Mʼmenemo munali guwa lansembe lagolide lofukizirapo lubani. Munalinso Bokosi la Chipangano lokutidwa ndi golide. Mʼbokosimo munali mʼphika wagolide mʼmene ankasungiramo mana ndi ndodo ya Aaroni imene inaphuka ija, ndiponso miyala ya pangano. Pamwamba pa bokosilo panali zifanizo za angelo otchedwa akerubi aulemerero, ataphimba chivundikiro cha bokosilo chimene chinali malo okhululukirapo machimo. Koma nʼzosatheka tsopano kufotokoza zinthu mwatsatanetsatane.

Zinthu zonsezi zitakonzedwa, ansembe ankalowamo mʼchipinda choyamba chija nthawi ndi nthawi kumatumikiramo. Koma Mkulu wa ansembe yekha ndiye ankalowa chipinda chachiwiri chija kamodzi kokha pa chaka. Iye sankalowamo wopanda magazi. Magaziwo ankapereka nsembe kwa Mulungu chifukwa cha iye mwini ndiponso chifukwa cha machimo a anthu amene ankachita mosazindikira. Mwa njira imeneyi Mzimu Woyera ankaonetsa kuti njira yolowera ku malo opatulika inali isanaonetsedwe pamene Chihema choyamba chinali chilipo. Zimenezi nʼzofanizira chabe, ndipo zinkalozera nthawi ino, kusonyeza kuti mphatso ndi nsembe zimene zinkaperekedwa sizinkachotsa chikumbumtima cha wopembedzayo. 10 Inali nkhani ya zakudya, ya zakumwa ndi ya miyambo yosiyanasiyana ya masambidwe. Anali malamulo akunja kokha mpaka pa nthawi imene anakonzanso zonse mwatsopano.

Magazi a Yesu

11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano. 12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. 13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi, 14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.

15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija.

16 Ngati munthu alemba pangano losiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba panganolo wamwaliradi, 17 chifukwa pangano lotere limakhala ndi mphamvu ngati wolembayo wamwalira. Siligwira ntchito pamene wolembayo ali ndi moyo. 18 Nʼchifukwa chake pangano loyamba lija silinachitike popanda kukhetsa magazi. 19 Mose atawawuza anthu onse malamulo, anatenga magazi a ana angʼombe amphongo ndi ambuzi yayimuna pamodzi ndi madzi, ubweya wofiira ndiponso chitsamba chotchedwa hisope, ndi kuwaza pa buku ndi anthu onse. 20 Iye anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulirani kuti mulisunge.” 21 Momwemonso Mose anawaza magazi pa Chihema chija ndiponso pa zipangizo zonse zogwiritsa ntchito pa chipembedzo. 22 Monga mwa malamulo titha kunena kuti, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi ndipo popanda kukhetsa magazi palibe kukhululukidwa machimo.

23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo. 24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. 25 Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake. 26 Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. 27 Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa, 28 momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.