Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Numeri 10

Malipenga Asiliva

10 Yehova anawuza Mose kuti, “Sula malipenga awiri a siliva, ndipo uziwagwiritsa ntchito posonkhanitsa anthu pamodzi ndiponso powasamutsa mʼmisasa. Pamene akuliza malipenga onse awiri, anthu onse asonkhane kwa iwe pa khomo la tenti ya msonkhano. Akaliza limodzi lokha, atsogoleri, akulu a mafuko a Aisraeli, asonkhane kwa iwe. Akaliza lipenga lochenjeza, misasa yomwe ili kummawa iyambe kusamuka. Akaliza lipenga lochenjeza lachiwiri, misasa yakummwera iyambe kusamuka. Kuliza kwa lipenga lochenjeza kudzakhala chizindikiro choyamba ulendo. Pofuna kusonkhanitsa anthu, muziliza malipenga, koma mosiyana ndi mmene malipenga ochenjeza amalizidwira.

“Ana a Aaroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipengawo. Zimenezi zikhale zokhazikika kwa inu ndi ku mibado yanu yonse. Pamene mukupita ku nkhondo mʼdziko lanu lomwe, kulimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipenga ochenjeza ndipo Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndi kukulanditsani mʼmanja mwa adani anu. 10 Komanso pa nthawi yanu ya chisangalalo, pa maphwando anu oyikika ndi maphwando a mwezi watsopano, muziliza malipenga pa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zanu za chiyanjano, ndipo zidzakhala chikumbutso chanu pamaso pa Mulungu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”

Aisraeli Achoka ku Sinai

11 Pa chaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, tsiku la 20, mtambo unachoka pamwamba pa chihema cha umboni. 12 Ndipo Aisraeli ananyamuka kuchoka mʼchipululu cha Sinai ndipo anayenda malo osiyanasiyana mpaka pamene mtambo unayima mʼchipululu cha Parani. 13 Kameneka kanali koyamba kuti Aisraeli anyamuke monga momwe Yehova analamulira Mose.

14 Magulu a msasa wa Yuda ndiwo anayamba kunyamuka potsata mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu lawo anali Naasoni mwana wa Aminadabu. 15 Mtsogoleri wa gulu la fuko la Isakara anali Netanieli mwana wa Zuwara, 16 Eliabu mwana wa Heloni ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Zebuloni. 17 Kenaka anagwetsa chihema, ndipo Ageresoni ndi Amerari amene ananyamula chihemacho, ananyamuka.

18 Kenaka magulu a msasa wa fuko la Rubeni ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Elizuri mwana wa Sedeuri. 19 Mtsogoleri wa fuko la Simeoni anali Selumieli mwana wa Zurisadai, 20 ndipo Eliyasafu mwana wa Deuweli ndiye ankatsogolera fuko la Gadi. 21 Kenaka Akohati ananyamuka atanyamula zinthu zopatulika. Chihema chinkayenera kuyimikidwa iwo asanafike.

22 Magulu a msasa wa Aefereimu anatsatira potsatira mbendera yawo. Elisama mwana wa Amihudi ndiye anali mtsogoleri wawo. 23 Gamalieli mwana wa Pedazuri ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Manase. 24 Abidani mwana wa Gideoni ndiye anali mtsogoleri wa mtundu wa Benjamini.

25 Pambuyo pa magulu onse panali magulu a msasa wa Dani, omwe ankateteza magulu onsewa ndipo ananyamuka potsatira mbendera yawo. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri mwana wa Amisadai. 26 Pagieli mwana wa Okirani ndiye anali mtsogoleri wa fuko la Aseri, 27 ndipo mtsogoleri wa mtundu wa Nafutali anali Ahira mwana wa Enani. 28 Umenewu ndiwo unali mndandanda wa kayendedwe ka magulu a Aisraeli pamene ankanyamuka ulendo wawo mʼmagulumagulu.

29 Ndipo Mose anawuza Hobabu mwana wa Reueli Mmidiyani, mpongozi wa Mose kuti, “Tikunyamuka kupita ku malo amene Yehova anati, ‘Ndidzakupatsani.’ Tiye upite nafe ndipo tidzakusamalira bwino, pakuti Yehova analonjeza zinthu zabwino kwa Israeli.”

30 Hobabu anayankha kuti, “Ayi, sindipita nanu, ndibwerera ku dziko la kwathu ndi kwa abale anga.”

31 Ndipo Mose anati, “Pepa usatisiye popeza ukudziwa kumene tingamange misasa mʼchipululu muno ndipo udzakhala maso athu. 32 Iweyo ukapita nafe, tidzagawana nawe zinthu zabwino zomwe Yehova adzatipatsa.”

33 Motero ananyamuka ku Phiri la Yehova nayenda ulendo wa masiku atatu. Bokosi la Chipangano cha Yehova linkayenda patsogolo pawo pa masiku atatuwo kuti apeze malo woti apumulepo. 34 Mtambo wa Yehova unkawaphimba masana pamene ankasamuka pa misasa yawo.

35 Nthawi iliyonse imene Bokosi la Chipangano likunyamuka, Mose ankanena kuti,

“Dzukani, Inu Yehova!
    Adani anu abalalike;
    Odana nanu athawe pamaso panu.

36 “Pamene likupumula, ankanena kuti,

“Bwererani, Inu Yehova,
    ku chinamtindi cha Aisraeli.”

Masalimo 46-47

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.

46 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
    thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
    ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
    ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,
    malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;
    Mulungu adzawuthandiza mmawa.
Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;
    Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,
    chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;
    Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;
    amatentha zishango ndi moto.
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;
    ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;
    ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”

11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
    fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
    Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
    anayika anthu pansi pa mapazi athu.
Iye anatisankhira cholowa chathu,
    chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
            Sela

Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
    Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
    imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.

Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
    imbirani Iye salimo la matamando.
Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
    Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
    monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
    Iye wakwezedwa kwakukulu.

Nyimbo ya Solomoni 8

Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga,
    amene anayamwa mawere a amayi anga!
Ndikanakumana nawe pa njira,
    ndikanakupsompsona,
    ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza.
Ndikanakutenga
    ndi kukulowetsa mʼnyumba ya amayi anga,
    amayi amene anandiphunzitsa,
ndikanakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe,
    zotsekemera za makangadza.
Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere
    ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani:
    musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa
    mpaka pamene chifunire ichocho.

Abwenzi

Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo,
    atatsamira wokondedwa wakeyo?

Mkazi

Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi,
    pamenepo ndi pamene amayi anachirira,
    pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo.
Undiyike pamtima pako ngati chidindo,
    ngati chidindo cha pa dzanja lako;
pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa,
    nsanje ndiyaliwuma ngati manda.
Chikondi chimachita kuti lawilawi
    ngati malawi a moto wamphamvu.
Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi,
    mitsinje singachikokolole chikondicho.
Ngati wina apereka chuma chonse
    cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi,
    adzangonyozeka nazo kotheratu.

Abwenzi

Ife tili naye mlongo wathu wamngʼono,
    koma alibe mawere,
kodi tidzamuchitira chiyani mlongo wathuyu
    pa tsiku limene adzamufunsire?
Ngati iye ndi khoma,
    tidzamumangira nsanja ya siliva.
Ngati iye ndi chitseko,
    tidzamutchinga ndi matabwa a mkungudza.

Mkazi

10 Ine ndili ngati khoma,
    ndipo mawere anga ndi nsanja zake.
Tsono mʼmaso mwa bwenzi langa
    ndine wobweretsa mtendere.
11 Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni;
    iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi,
aliyense mwa iwo ankayenera kupereka
    ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake.
12 Koma munda wanga wampesa ndi wangawanga ndiponso wa ine ndekha.
    Iwe Solomoni, khala nazo ndalama zasiliva 1,000
    ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za amene akusamalira mundawo.

Mwamuna

13 Iwe amene umakhala mʼminda
    uli pamodzi ndi anzako,
    ndilole kuti ndimve liwu lako!

Mkazi

14 Fulumira wokondedwa wanga,
    ndipo ukhale ngati gwape
kapena mwana wa mbawala
    wothamanga mʼmapiri mʼmene mumamera mbewu zokometsera chakudya.

Ahebri 8

Mkulu wa Ansembe wa Pangano Latsopano

Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu Waulemerero kumwamba. Ndipo akutumikira mʼmalo opatulika, mu Tenti yeniyeni yoyikidwa ndi Ambuye, osati ndi munthu.

Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu, ndipo kunali koyenera kuti wansembe wathunso akhale nʼkanthu kopereka. Ngati iye akanakhala pa dziko lapansi, sakanakhala wansembe pakuti alipo kale anthu amene amapereka mphatso zolembedwa mʼMalamulo. Iwo amatumikira pamalo opatulika amene ndi chithunzi ndi chifanizo cha zimene zili kumwamba. Ichi ndi chifukwa chake Mose anachenjezedwa pamene anali pafupi kumanga Tenti: “Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” Koma Yesu analandira utumiki wopambana kuposa wawo monga Iyenso ali Nkhoswe ya pangano lopambana kuposa lakale lija, chifukwa pangano latsopano lakhazikika pa malonjezano opambana kwambiri.

Ngati pangano loyamba lija likanakhala langwiro, sipakanafunikanso lina mʼmalo mwake. Koma Mulungu anapeza zolakwika pakati pa anthu ndipo anati,

“Masiku akubwera,” akutero Yehova,
    “pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
    ndiponso nyumba ya Yuda.
Silidzakhala ngati pangano
    limene ndinachita ndi makolo awo,
pamene ndinawagwira padzanja
    nʼkuwatulutsa ku Igupto
chifukwa iwo sanasunge pangano langa lija
    ndipo Ine sindinawasamalire,
            akutero Ambuye.
10 Tsono ili ndi pangano ndidzapangane ndi nyumba ya Israeli:
    Atapita masiku amenewa, akutero Ambuye,
Ine ndidzayika malamulo anga mʼmaganizo mwawo,
    ndi kulemba mʼmitima mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo,
    ndipo iwo adzakhala anthu anga.
11 Sipadzafunikanso wina kuti aphunzitse mnzake,
    kapena munthu kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, udziwe Ambuye
chifukwa onse adzandidziwa,
    kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu.
12 Pakuti Ine ndidzawakhululukira zoyipa zawo,
    ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

13 Ponena kuti, pangano “latsopano” Mulungu wapanga pangano loyamba lija kukhala lotha ntchito, ndipo chilichonse chimene chayamba kutha ntchito ndi kukalamba, chili pafupi kuchokeratu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.