M’Cheyne Bible Reading Plan
Paska
9 Yehova anayankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai pa mwezi woyamba wa chaka chachiwiri atatuluka mu Igupto, nati, 2 “Aisraeli azichita Paska pa nthawi yake yoyikika. 3 Muzichita Paska pa nthawi yake yoyikika, madzulo a tsiku la 14 la mwezi uno, potsata malamulo ndi malangizo ake.”
4 Choncho Mose anawuza Aisraeli kuti azichita Paska, 5 ndipo anachitadi Paskayo mʼchipululu cha Sinai madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose.
6 Koma ena a iwo sanathe kuchita nawo Paska pa tsiku limenelo chifukwa anali odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo. Choncho anabwera kwa Mose ndi Aaroni tsiku lomwelo, 7 ndipo anawuza Moseyo kuti, “Ife tadetsedwa chifukwa cha mtembo wa munthu. Nʼchifukwa chiyani taletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena pa nthawi yake?”
8 Mose anawayankha kuti, “Dikirani mpaka nditamva zimene Yehova walamula zokhudza Inu.”
9 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 10 “Uza Aisraeli kuti, ‘Pamene wina mwa inu kapena zidzukulu zanu adetsedwa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala pa ulendo, akhoza kuchita nawo Paska ya Yehova. 11 Azichita chikondwererochi madzulo a pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Azidya mwana wankhosa wamwamuna pamodzi ndi buledi wopanda yisiti ndi ndiwo zowawa zamasamba. 12 Iwo asasiye nyama ina iliyonse mpaka mmawa. Asaswe mafupa aliwonse. Pamene akuchita chikondwerero cha Paska, atsate malangizo onse. 13 Koma ngati munthu wina ali woyeretsedwa ndipo sali pa ulendo koma alephera kuchita Paska, munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu a mtundu wake chifukwa sanabweretse chopereka cha Yehova pa nthawi yake. Munthu ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake.
14 “ ‘Mlendo amene akukhala pakati panu, nafuna kuchita nawo Paska ya Yehova, achite nawo motsata malamulo ndi malangizo ake. Muzikhala ndi malangizo ofanana a Paska; mbadwa kapena mlendo.’ ”
Mtambo Pamwamba pa Chihema
15 Pa tsiku limene anayimika chihema, tenti ya umboni, mtambo unaphimba chihemacho. Kuyambira madzulo mpaka mmawa, mtambo umene unali pamwamba pa chihemacho unkaoneka ngati moto. 16 Zinkachitika motere mosalekeza: mtambo unkakhala pamwamba pa chihema, ndipo usiku unkaoneka ngati moto. 17 Nthawi ina iliyonse mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso, ndipo paliponse pamene mtambo wayima, Aisraeli ankamangapo misasa. 18 Aisraeli ankasamuka pamalopo Yehova akawalamula, ndipo ankamanganso misasa Iyeyo akawalamula. Nthawi yonse imene mtambowo wayima pa chihema, ankakhalabe mʼmisasa yawo. 19 Mtambowo ukakhala pa chihema nthawi yayitali, Aisraeli ankasungabe lamulo la Yehova ndipo iwo sankasamukanso. 20 Nthawi zina mtambowo unkakhala pa chihemapo masiku owerengeka. Aisraeli ankamanga misasa molamulidwa ndi Yehova ndipo ankasamukanso molamulidwa ndi Iyeyo. 21 Nthawi zina mtambo unkakhala kuyambira madzulo mpaka mmawa ndipo unkachoka mmawa mwake, ankasamuka. Kaya ndi masana kapena usiku, pamene mtambo wachoka, ankasamuka. 22 Ngakhale mtambo ukhale pa chihema masiku awiri kapena mwezi kapena chaka, Aisraeli ankakhalabe pa msasa osachoka. Koma ukachoka, ankasamuka. 23 Molamulidwa ndi Yehova ankamanga misasa yawo ndipo ankasamukanso Yehova akawalamula. Ankamvera lamulo la Yehova kudzera mwa Mose.
Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.
45 Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma
pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;
lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
2 Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse
ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,
popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
3 Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu;
mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.
4 Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso
mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo;
dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.
5 Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu,
mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.
6 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
7 Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
10 Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;
iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.
11 Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;
mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.
12 Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,
amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.
13 Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,
chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.
14 Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;
anamwali okhala naye akumutsatira
ndipo abweretsedwa kwa inu.
15 Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;
akulowa mʼnyumba yaufumu.
16 Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;
udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.
17 Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;
choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.
7 Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola
mu nsapato wavalazo!
Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali,
ntchito ya manja ya mmisiri waluso.
2 Mchombo wako uli ngati chikho chowumbika bwino
chimene nthawi zonse ndi chodzaza ndi vinyo.
Chiwuno chako ndi choningʼa ngati mtolo wa tirigu
utazunguliridwa ndi maluwa okongola.
3 Mawere ako akuoneka ngati ana awiri a mbawala,
ngati mphoyo zamapasa.
4 Khosi lako lili see! ngati nsanja ya mnyanga wa njovu.
Maso ako ali ngati mayiwe a ku Hesiboni,
amene ali pafupi ndi chipata cha Bati Rabimu.
Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni,
yoyangʼana ku Damasiko.
5 Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli.
Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu;
mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola.
6 Ndiwe wokongola kwambiri ndiponso wosangalatsa,
iwe wokondedwa, namwali wokondweretsawe!
7 Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa,
ndipo mawere ako ali ngati phava la zipatso.
8 Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa;
ndidzathyola zipatso zake.”
Mawere ako ali ngati maphava a mphesa,
fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi,
9 ndipo pakamwa pako pali ngati vinyo wokoma kwambiri.
Mkazi
Tsono vinyo ameneyu amuthirire wachikondi wanga,
ayenderere bwino pa milomo yake ndi mano ake.
10 Wokondedwayo ine ndine wake,
ndipo chilakolako chake chili pa ine.
11 Bwera wachikondi wanga, tiye tipite ku madera a ku midzi,
tikagone ku midzi.
12 Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa,
tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira,
ngati maluwa ake ayamba kuoneka,
komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa.
Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa.
13 Mitengo ya mankhwala a chisulo ikupereka fungo lake labwino,
ndipo pa khomo pathu pali zipatso zonse zokoma,
zatsopano ndi zakale zomwe,
zimene ndakusungira wokondedwa wanga.
Za Melikizedeki Mkulu wa Ansembe
7 Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku Salemu, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa. 2 Ndipo Abrahamu anamupatsa chakhumi cha zonse anafunkha. Choyamba dzina la Melikizedeki likutanthauza, “Mfumu ya chilungamo,” kenakanso, “Mfumu ya Salemu,” kutanthauza, “Mfumu ya mtendere.” 3 Alibe abambo kapena mayi, alibe chiyambi kapena chitsiriziro cha moyo wake. Iye ali ngati Mwana wa Mulungu ndipo akupitirira kukhala wansembe wamuyaya.
4 Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa chakhumi cha zimene anafunkha. 5 Tsono lamulo likuti, ana a Levi amene amakhala ansembe azilandira chakhumi kuchokera kwa Aisraeli, abale awo ngakhale kuti abale awowo ndi ochokera kwa Abrahamu. 6 Melikizedeki sanali wochokera kwa Levi, komabe analandira chakhumi kuchokera kwa Abrahamu nadalitsa Abrahamuyo amene analandira malonjezo a Mulungu. 7 Mosakayika konse, munthu amene amadalitsa ndi wamkulu kuposa amene akudalitsidwayo. 8 Ansembe amene amalandira chakhumi amafa, choncho Melikizedeki ndi wamkulu kuwaposa iwo chifukwa Malemba amamuchitira umboni kuti ndi wamoyo. 9 Wina angathe kunena kuti Levi, amene amalandira chakhumi, anapereka chakhumicho kudzera mwa Abrahamu, 10 chifukwa pamene Melikizedeki anakumana ndi Abrahamu nʼkuti Levi ali mʼthupi la kholo lake.
Yesu Wofanana ndi Melikizedeki
11 Kukanatheka kukhala wangwiro mwa unsembe wa Levi, pakuti Malamulo anapatsidwa kwa anthu mwa unsembe wa Levi, nʼchifukwa chiyani panafunikanso wansembe wina kuti abwere, wofanana ndi Melikizedeki, osati Aaroni? 12 Pakuti pamene unsembe usintha, malamulonso amayenera kusintha. 13 Ambuye athu Yesu, amene mawuwa akunena za Iye, anali wa fuko lina, ndipo palibe aliyense wochokera fuko lakelo amene anatumikira pa guwa lansembe. 14 Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la Yuda. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe. 15 Ndipo zimene tanenazi zimamveka bwino ngati tiona kuti pafika wansembe wina wofanana ndi Melikizedeki. 16 Yesu sanakhale wansembe chifukwa cha malamulo monga mwa mabadwidwe ake koma mwamphamvu ya moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu anamuchitira umboni kuti,
“Iwe ndi wansembe wamuyaya,
monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.”
18 Choncho lamulo loyamba lachotsedwa chifukwa linali lofowoka ndi lopanda phindu. 19 Tsono Malamulo sangathe kusandutsa chilichonse kukhala changwiro, koma mʼmalo mwake mwalowa chiyembekezo chabwino, chimenechi timayandikira nacho kwa Mulungu.
20 Izi sizinachitiketu wopanda lumbiro. Ena ankakhala ansembe popanda lumbiro. 21 Koma Yesu ankakhala wansembe ndi lumbiro pamene Mulungu anati,
“Ambuye analumbira
ndipo sangasinthe maganizo ake,
‘Iwe ndi wansembe wamuyaya.’ ”
22 Chifukwa cha lumbiroli, Yesu wakhala Nkhoswe ya Pangano lopambana.
23 Tsono ansembe akale aja analipo ambiri, popeza imfa imawalepheretsa kupitiriza ntchitoyi. 24 Koma Yesu popeza ndi wamuyaya, unsembe wake ndi wosatha. 25 Chifukwa chake Iye amapulumutsa kwathunthu amene amabwera kwa Mulungu kudzera mwa Iyeyo. Iye ali ndi moyo nthawi zonse kuti adziwapempherera iwo.
26 Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku. 27 Kusiyana ndi akulu a ansembe ena aja, Yesu sanafunike kupereka nsembe tsiku ndi tsiku poyamba chifukwa cha machimo ake, ndipo kenaka chifukwa cha machimo a anthu ena. Iye anadzipereka nsembe chifukwa cha machimo awo kamodzi kokha pamene anadzipereka yekha. 28 Pakuti lamulo limasankha anthu amene ndi ofowoka kukhala akulu a ansembe; koma lumbiro, lomwe linabwera pambuyo pa lamulo, linasankha Mwana, amene anapangidwa kukhala wangwiro kwamuyaya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.