M’Cheyne Bible Reading Plan
Za Mnaziri
6 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi afuna kuchita lonjezo lapadera, lonjezo lodzipatula yekha kwa Yehova ngati Mnaziri, 3 sayenera kumwa vinyo kapena zakumwa zosasa ndipo asamamwe chakumwa chilichonse cha mphesa. Asamamwe madzi a mphesa kapena kudya mphesa zaziwisi kapena zowuma. 4 Pa nthawi yonse imene ali Mnaziri, asamadye chilichonse chopangidwa kuchokera ku mphesa ngakhale mbewu zake kapena makungu ake.’
5 “ ‘Pa nthawi yonse ya lonjezo lodzipatula yekhalo, asamete kumutu kwake ndi lumo. Akhale wopatulika mpaka nthawi yake yonse ya kudzipatula yekha kwa Yehova itatha. Alileke tsitsi la pamutu pake kuti likule.’ 6 Pa nthawi yonse imene munthuyo wadzipatula yekha kwa Yehova asayandikire mtembo. 7 Ngakhale abambo ake kapena amayi ake kapena mchimwene wake kaya mchemwali wake atamwalira, asadzidetse pokhudza mitembo yawo chifukwa kulumbira kwake kwa kudzipatula yekha kwa Yehova kuli pamutu pake. 8 Munthuyo ndi wopatulika masiku onse odzipereka kwake kwa Yehova.
9 “Ngati munthu wina afa mwadzidzidzi pafupi naye ndi kudetsa tsitsi lake loperekedwalo, amete mutu wake pa tsiku lodziyeretsa, tsiku lachisanu ndi chiwiri. 10 Tsono pa tsiku lachisanu ndi chitatu abweretse nkhunda ziwiri kapena mawunda awiri anjiwa kwa wansembe pa khomo lolowera ku tenti ya msonkhano. 11 Wansembe apereke imodzi kuti ikhale nsembe yauchimo ndi ina nsembe yopsereza yotetezera tchimo chifukwa anachimwa popezeka pafupi ndi mtembo. Ndipo tsiku lomwelo apatulenso tsitsi la pamutu pake. 12 Adzipereke kwa Yehova pa nthawi yodzipatula ndipo abweretse nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi ngati nsembe yopepesera. Masiku akale sawerengedwanso chifukwa anadzidetsa pa nthawi yodzipatulira kwake.
13 “Tsono ili ndi lamulo la Mnaziri pamene nthawi yodzipatula kwake yatha: Abwere naye pa khomo la tenti ya msonkhano. 14 Pamenepo apereke chopereka chake kwa Yehova: Nkhosa yayimuna ya chaka chimodzi yopanda chilema kuti ikhale nsembe yopsereza, mwana wankhosa wamkazi mmodzi wopanda chilema kuti ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa imodzi yayikulu yayimuna kuti ikhale nsembe yachiyanjano, 15 ndipo abwere pamodzi ndi nsembe yachakudya ndi nsembe yachakumwa ndi dengu la buledi wopanda yisiti, makeke opangidwa ndi ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda ta buledi topakidwa mafuta.
16 “Wansembe apereke zimenezi pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe ya uchimo ndi nsembe yopsereza. 17 Apereke dengu la buledi wopanda yisiti ndiponso nsembe yachiyanjano kwa Yehova ya nkhosa yayimuna, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi chopereka cha chakumwa.
18 “Mnaziriyo amete tsitsi limene analipereka lija pa khomo la tenti ya msonkhano. Atenge tsitsilo ndi kuliyika pa moto umene uli pansi pa nsembe yachiyanjano.
19 “Mnaziriyo atatha kumeta tsitsi analiperekalo, wansembe ayike mʼmanja mwake mwendo wa mmwamba wankhosa yayimuna umene waphikidwa ndipo atengenso keke ndi kamtanda ka buledi, zonse zopanda yisiti zomwe zili mʼdengu lija. 20 Wansembe aziweyule pamaso pa Yehova ngati nsembe yoweyula. Zimenezi ndi zopatulika ndipo ndi za wansembe pamodzi ndi chidale chimene anachiweyula ndi ntchafu yomwe anayipereka ija. Zitatha izi, Mnaziri akhoza kumwa vinyo.
21 “Ili ndi lamulo la Mnaziri yemwe walonjeza kudzipereka kwa Yehova podzipatula yekha kuphatikiza pa zomwe angathe kukwaniritsa. Ayenera kukwaniritsa lonjezo lomwe wachitalo potsata lamulo la Mnaziri.”
Kupereka Mdalitso
22 Yehova anawuza Mose kuti, 23 “Uza Aaroni ndi ana ake aamuna kuti, ‘Umu ndi mmene muzidalitsira Aisraeli. Muzinena kuti,
24 “ ‘Yehova akudalitse
ndi kukusunga;
25 Yehova awalitse nkhope yake pa iwe,
nakuchitira chisomo;
26 Yehova akweze nkhope yake pa iwe,
nakupatse mtendere.’ ”
27 Choncho akadzatchula dzina langa podalitsa Aisraeli, Ine ndidzawadalitsadi.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
40 Mofatsa ndinadikira Yehova
Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
2 Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,
mʼthope ndi mʼchithaphwi;
Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe
ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
3 Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,
nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.
Ambiri adzaona,
nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.
4 Ndi wodala munthu
amakhulupirira Yehova;
amene sayembekezera kwa odzikuza,
kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
5 Zambiri, Yehova Mulungu wanga,
ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.
Zinthu zimene munazikonzera ife
palibe amene angathe kukuwerengerani.
Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,
zidzakhala zambiri kuzifotokoza.
6 Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,
koma makutu anga mwawatsekula;
zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo
Inu simunazipemphe.
7 Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.
Mʼbuku mwalembedwa za ine.
8 Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;
lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”
9 Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;
sinditseka milomo yanga
monga mukudziwa Inu Yehova.
10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;
ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.
Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu
pa msonkhano waukulu.
11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.
12 Pakuti mavuto osawerengeka andizungulira;
machimo anga andigonjetsa, ndipo sindingathe kuona.
Alipo ambiri kuposa tsitsi la mʼmutu mwanga,
ndipo mtima wanga ukufowoka mʼkati mwanga.
13 Pulumutseni Yehova;
Bwerani msanga Yehova kudzandithandiza.
14 Onse amene akufunafuna kuchotsa moyo wanga
achititsidwe manyazi ndi kusokonezedwa;
onse amene amakhumba chiwonongeko changa
abwezedwe mwamanyazi.
15 Iwo amene amanena kwa ine kuti, “Hee! Hee!”
abwerere akuchita manyazi.
16 Koma iwo amene amafunafuna Inu
akondwere ndi kusangalala mwa Inu;
iwo amene amakonda chipulumutso chanu
nthawi zonse anene kuti, “Yehova akwezeke!”
17 Komabe Ine ndine wosauka ndi wosowa;
Ambuye andiganizire.
Inu ndinu thandizo langa ndi wondiwombola wanga;
Inu Mulungu wanga, musachedwe.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
41 Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka;
Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.
2 Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake;
Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko
ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.
3 Yehova adzamuthandiza pamene akudwala
ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.
4 Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo;
chiritseni pakuti ndakuchimwirani.”
5 Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti,
“Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?”
6 Pamene wina abwera kudzandiona,
amayankhula mwachinyengo, pomwe mtima wake ukusonkhanitsa zachipongwe;
kenaka iye amatuluka ndi kukalengeza kunja.
7 Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane,
iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti,
8 “Matenda owopsa amugwira;
sadzaukapo pamalo pamene wagona.”
9 Ngakhale bwenzi langa la pamtima amene ndinamudalira,
iye amene amadya pamodzi ndi ine
watukula chidendene chake kulimbana nane.
10 Koma Yehova mundichititre chifundo,
dzutseni kuti ndiwabwezere.
11 Ine ndikudziwa kuti mukukondwera nane,
pakuti mdani wanga sandigonjetsa.
12 Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga
ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.
13 Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli
kuchokera muyaya mpaka muyaya.
Ameni ndi Ameni.
Mwamuna
4 Ndiwe wokongoladi wokondedwa wanga!
Ndithudi, ndiwe wokongola!
Maso ako ali ngati nkhunda kumbuyo kwa nsalu yophimba kumutu.
Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi
zikutsetsereka kuchokera ku Giliyadi.
2 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe zangometedwa kumene,
zochokera kozisambitsa kumene.
Iliyonse ili ndi ana amapasa;
palibe imene ili yokha.
3 Milomo yako ili ngati mbota yofiira;
pakamwa pako ndi pokongola kwambiri.
Kukhalira kumbuyo kwa nsalu yako yophimba
kumutuyo, masaya ako akuoneka ngati mabandu a makangadza.
4 Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide,
yomangidwa bwino ndi yosalala;
pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000,
zishango zonsezo za anthu ankhondo.
5 Mawere ako ali ngati tiana tiwiri ta nswala,
ngati ana amapasa a nswala
amene akudya pakati pa maluwa okongola.
6 Kamphepo kamadzulo kakayamba kuwuzira
ndipo mithunzi ikayamba kuthawa,
ndidzapita ku phiri la mure
ndi ku chitunda cha lubani.
7 Ndiwe wokongola kwambiri wokondedwa wanga;
palibe chilema pa iwe.
8 Tiye tichoke ku Lebanoni iwe mkwatibwi wanga,
tiye tichoke ku Lebanoni,
utsikepo pa msonga ya Amana,
kuchoka pa msonga ya phiri la Seniri, pamwamba penipeni pa Herimoni,
kuchoka ku mapanga a mikango
ndiponso kumapiri kumene akambuku amavutitsa.
9 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, wanditenga mtima,
iwe wanditenga mtima
ndi kapenyedwe ka maso ako,
ndiponso ndi umodzi mwa mikanda ya mʼkhosi mwako.
10 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, chikondi chako nʼchosangalatsa!
Chikondi chako nʼchosangalatsa kwambiri kupambana vinyo,
ndiponso fungo la mafuta ako ndi lopambana zonunkhiritsa zonse!
11 Iwe mkwatibwi wanga, milomo yako ikuchucha uchi ngati chisa cha njuchi;
pansi pa lilime lako pali mkaka ndi uchi.
Fungo lonunkhira la zovala zako likumveka ngati fungo la ku Lebanoni.
12 Iwe mlongo wanga, mkwatibwi wanga, ndiwe munda wopiringidzidwa;
ndiwe kasupe wotchingidwa, chitsime chotetezedwa.
13 Zomera zako ndi munda wa zipatso za makangadza;
muli zipatso zokoma kwambiri,
muli hena ndi nadi,
14 nadi ndi safiro,
kalamusi ndi sinamoni,
komanso mtengo uliwonse wonunkhira bwino.
Mulinso mure ndi aloe
ndi zonunkhiritsa zonse zabwino kwambiri.
15 Iwe ndiwe kasupe wa mʼmunda,
chitsime cha madzi oyenda,
mtsinje wa madzi ochokera ku Lebanoni.
Mkazi
16 Dzuka, iwe mphepo yakumpoto,
ndipo bwera, iwe mphepo yakummwera!
Uzira pa munda wanga,
kuti fungo lake lonunkhira lifalikire ponseponse.
Bwenzi langa alowe mʼmunda mwake
ndi kudya zipatso zake zabwino kwambiri.
Mpumulo wa Anthu a Mulungu
4 Popeza lonjezo lakuti tidzalowe mu mpumulo umene anatilonjeza lilipobe, tiyeni tisamale kuti pasakhale wina aliyense mwa inu wodzalephera kulowamo. 2 Pakuti Uthenga Wabwino unalalikidwa kwa ife, monganso iwo aja; koma iwo sanapindule nawo uthengawo chifukwa anangomva koma osakhulupirira. 3 Tsono ife amene takhulupirira talowa mu mpumulo, monga momwe Mulungu akunenera kuti,
“Ndili wokwiya ndinalumbira kuti,
‘Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.’ ”
Ananena zimenezi ngakhale anali atatsiriza kale ntchito yolenga dziko lapansi. 4 Pena pake wayankhula za tsiku lachisanu ndi chiwiri mʼmawu awa: “Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, Mulungu anapumula ku ntchito zake zonse.” 5 Pa ndime inonso akunena za zomwezo pamene akuti, “Iwo sadzalowa konse mu mpumulo wanga.”
6 Popeza kwatsalabe kuti ena adzalowe mu mpumulowo, koma aja anayamba kumva Uthenga Wabwino sanalowe chifukwa cha kusamvera kwawo. 7 Nʼchifukwa chake Mulungu anayikanso tsiku lina limene analitcha “Lero.” Patapita nthawi yayitali Iye anayankhula za tsiku lomweli kudzera mwa Davide, monga ndinanena kale kuti,
“Lero mukamva mawu ake,
musawumitse mitima yanu.”
8 Ngati Yoswa akanalowetsa anthu mu mpumulo, Mulungu sakananena pambuyo pake za tsiku lina. 9 Kotero tsono kwatsala mpumulo wa Sabata kwa anthu a Mulungu; 10 Pakuti aliyense amene analowa mu mpumulo wa Mulungu anapuma pa ntchito zake, monga momwe Mulungu anachitira. 11 Tiyeni tsono tiyesetse kulowa mu mpumulo, kuti pasapezeke wina aliyense wolephera potsatira chitsanzo chawo cha kusamvera.
12 Paja Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amalowa mpaka molumikizirana moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana fundo ndi mafuta a mʼmafupa. Amaweruza malingaliro ndi zokhumba za mʼmitima. 13 Palibe kanthu kobisika pamaso pa Mulungu. Zinthu zonse zili poyera ndi zovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
Yesu Mkulu wa Ansembe Wopambana
14 Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene timavomereza. 15 Pakuti sitili ndi Mkulu wa ansembe amene sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofowoka zathu. Koma tili naye amene anayesedwa mʼnjira zonse monga ife, koma sanachimwe. 16 Tiyeni tsono tiyandikire ku mpando waufumu, wachisomo mopanda mantha, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo chotithandiza pa nthawi yeniyeni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.