M’Cheyne Bible Reading Plan
Malo a Misasa ya Mafuko Onse a Aisraeli
2 Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni: 2 “Aisraeli azimanga misasa yawo mozungulira tenti ya msonkhano motalikira pangʼono. Munthu aliyense amange pamene pali mbendera ya fuko lake.”
3 Kummawa, kotulukira dzuwa, magulu a msasa wa Yuda amange pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Ayudawo ndi Naasoni mwana wa Aminadabu. 4 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 74,600.
5 Fuko la Isakara lidzamanga pafupi ndi Yuda. Mtsogoleri wa gulu la Isakara ndi Netanieli mwana wa Zuwara. 6 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 54,400.
7 Lotsatira lidzakhala fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa gulu la Zebuloni ndi Eliabu mwana wa Heloni. 8 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 57,400.
9 Anthu onse aamuna mʼmisasa ya Yuda, chiwerengero chawo ndi 186,400 monga mwa magulu awo. Iwowo ndiwo aziyamba kusamuka.
10 Kummwera kudzakhala magulu a msasa wa Rubeni pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa gulu la Rubeni ndi Elizuri mwana wa Sedeuri. 11 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 46,500.
12 Fuko la Simeoni lidzamanga pafupi ndi Rubeni. Mtsogoleri wa gulu la Simeoni ndi Selumieli mwana wa Zurisadai. 13 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 59,300.
14 Lotsatira lidzakhala fuko la Gadi. Mtsogoleri wa gulu la Gadi ndi Eliyasafu mwana wa Deuweli. 15 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 45,650.
16 Anthu onse aamuna mu msasa wa Rubeni, chiwerengero chawo monga mwa magulu awo, ndi 151,450. Iwowo azikhala achiwiri posamuka.
17 Tsono tenti ya msonkhano ndi msasa wa Alevi zidzakhala pakati pa misasayo. Iwo adzasamuka monga momwe anamangira misasa yawo, aliyense pa malo ake pamene pali mbendera yake.
18 Kumadzulo kudzakhala magulu a msasa wa Efereimu pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Aefereimuwo ndi Elisama mwana wa Amihudi. 19 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 40,500.
20 Fuko la Manase lidzakhala pafupi ndi Efereimu. Mtsogoleri wa Amanase ndi Gamalieli mwana wa Pedazuri. 21 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 32,200.
22 Lotsatira lidzakhala fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa Abenjamini ndi Abidani mwana wa Gideoni. 23 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 35,400.
24 Anthu onse aamuna mu msasa wa Efereimu, chiwerengero chawo ndi 108,100 monga mwa magulu awo. Iwowo azikhala achitatu posamuka.
25 Kumpoto kudzakhala msasa wa magulu a Dani pamene pali mbendera yawo. Mtsogoleri wa Adani ndi Ahiyezeri mwana wa Amisadai. 26 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 62,700.
27 Fuko la Aseri lidzamanga pafupi ndi iwowo. Mtsogoleri wa Aaseri ndi Pagieli mwana wa Okirani. 28 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 41,500.
29 Lotsatira lidzakhala fuko la Nafutali. Mtsogoleri wa Anafutali ndi Ahira mwana wa Enani. 30 Chiwerengero cha gulu lake lankhondo ndi 53,400.
31 Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo.
32 Amenewa ndi Aisraeli monga mwa mabanja a makolo awo. Chiwerengero cha Aisraeli onse mʼmisasa chinali 603,550, mwa magulu awo. 33 Koma Alevi sanawawerenge pamodzi ndi Aisraeli enawo monga momwe Yehova analamulira Mose.
34 Choncho Aisraeli anachita zonse zomwe Yehova analamulira Mose. Umo ndi momwe amamangira misasa yawo pamene panali mbendera zawo, ndipo ankasamuka monga mwa mafuko a makolo awo.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.
36 Uthenga uli mu mtima mwanga
wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa:
Mu mtima mwake
mulibe kuopa Mulungu.
2 Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri,
sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.
3 Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo;
iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino.
4 Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa;
iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo
ndipo sakana cholakwa chilichonse.
5 Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,
kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
6 Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,
chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.
Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
7 Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!
Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu
amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;
Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
9 Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;
mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.
10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,
chilungamo chanu kwa olungama mtima.
11 Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane,
kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.
12 Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa,
aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!
12 Uzikumbukira mlengi wako
masiku a unyamata wako,
masiku oyipa asanafike,
nthawi isanafike pamene udzanena kuti,
“Izi sizikundikondweretsa.”
2 Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala,
mwezi ndi nyenyezi zidzada.
Mitambo idzabweranso mvula itagwa.
3 Nthawi imene manja ako adzanjenjemera,
miyendo yako idzafowoka,
pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka,
ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.
4 Makutu ako adzatsekeka,
ndipo sudzamva phokoso lakunja;
sudzamvanso kusinja kwa pa mtondo
kapena kulira kwa mbalame mmawa.
5 Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera,
amaopa kuyenda mʼmisewu;
Mutu umatuwa kuti mbuu,
amayenda modzikoka ngati ziwala
ndipo chilakolako chimatheratu.
Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyaya
ndipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.
6 Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke,
kapena mbale yagolide isanasweke;
mtsuko usanasweke ku kasupe,
kapena mkombero usanathyoke ku chitsime.
7 Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera,
mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.
8 “Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki.
“Zonse ndi zopandapake!”
Mawu Otsiriza
9 Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri. 10 Mlaliki anafufuzafufuza kuti apeze mawu oyenera, ndipo zimene analemba zinali zolondola ndiponso zoona.
11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga, zokamba zawo zimene anasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomera, yoperekedwa ndi mʼbusa mmodzi. 12 Samalira mwana wanga, za kuwonjezera chilichonse pa zimenezi.
Kulemba mabuku ambiri sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.
13 Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa:
uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake,
pakuti umenewu ndiwo udindo
wa anthu onse.
14 Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse,
kuphatikizanso zinthu zonse zobisika,
kaya zabwino kapena zoyipa.
1 Kuchokera kwa Paulo, amene ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu ndi Timoteyo mʼbale wathu.
Kulembera Filemoni, bwenzi lathu lokondedwa ndi mtumiki mnzathu. 2 Kwa Apiya mlongo wathu, Arkipo msilikali mnzathu, ndiponso mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwanu.
3 Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.
Kuyamika ndi Pemphero
4 Ine ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakukumbukira iwe mʼmapemphero anga. 5 Pakuti ndamva za chikondi chako, za chikhulupiriro chako mwa Ambuye Yesu ndiponso za chikondi chako pa oyera mtima onse. 6 Ine ndikupemphera kuti mgwirizano wako ndi ife mʼchikhulupiriro ukhale opindulitsa pozamitsa nzeru zako zozindikira zinthu zilizonse zabwino zimene timagawana chifukwa cha Khristu. 7 Mʼbale, chikondi chako chandipatsa chimwemwe chachikulu ndi chilimbikitso, chifukwa umatsitsimutsa mitima ya anthu a Ambuye.
Paulo Apempha kuti Amuchitire Chifundo Onesimo
8 Tsopano ngakhale kuti mwa Khristu nditha kulimba mtima ndi kulamulira kuti uchite zimene uyenera kuchita, 9 komabe ndikupempha mwachikondi. Ine Paulo, munthu wokalamba, ndipo tsopano ndili mʼndende chifukwa cha Khristu Yesu, 10 ndikukupempha chifukwa cha mwana wanga Onesimo, amene ndamubala ndili mu unyolo. 11 Anali wopanda phindu kwa iwe, koma tsopano wasanduka wa phindu kwa iwe ndi kwa inenso.
12 Ine ndikumutumizanso kwa iwe tsopano, koma potero ndikukhala ngati ndikutumiza mtima wanga weniweni. 13 Ndikanakonda ndikanakhala naye kuno kuti iyeyo azinditumikira mʼmalo mwako pamene ndili mu unyolo chifukwa cha Uthenga Wabwino. 14 Koma sindikufuna kuchita kanthu osakufunsa, nʼcholinga chakuti chilichonse chabwino ungandichitire chikhale mwakufuna kwako osati mokakamiza. 15 Mwina chifukwa chimene unasiyana naye kwa kanthawi ndi chakuti ukhale nayenso nthawi zonse. 16 Osati ngati kapolo, koma woposa kapolo, ngati mʼbale wokondedwa. Iyeyu ndi wokondedwa kwambiri kwa ine koma kwa iweyo ndi wokondedwa koposa, ngati munthu komanso ngati mʼbale mwa Ambuye.
17 Tsono ngati umati ndine mnzako, umulandire iyeyu monga momwe ukanandilandirira ineyo. 18 Ngati anakulakwira kapena kukongola kanthu kalikonse, ndidzalipira ineyo. 19 Ine, Paulo ndikulemba zimenezi ndi dzanja langa. Ine ndidzalipira. Nʼkosafunika kukukumbutsa kuti iweyo ngongole yako kwa ine ndi moyo wakowo. 20 Mʼbale, ndikufuna kuti ndipindule nawe mwa Ambuye; tsono tsitsimutsa mtima wanga mwa Khristu. 21 Ine ndili ndi chitsimikizo cha kumvera kwako pamene ndikukulembera kalatayi. Ndikulemba ndikudziwa kuti udzachita ngakhale kuposa zimene ndakupemphazi.
22 Chinthu chinanso ndi ichi: undikonzere malo, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu adzamvera mapemphero anu ndi kundibwezera kwa inu.
Mawu Otsiriza
23 Epafra, wamʼndende mnzanga chifukwa cha Khristu Yesu akupereka moni. 24 Atumiki anzanga awa, Marko, Aristariko, Dema ndi Luka, akuperekanso moni.
25 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wako.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.