Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 24

Mafuta ndi Buledi wa Pamaso pa Yehova

24 Yehova anawuza Mose kuti, “Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale, a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse. Kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, mʼchihema cha msonkhano, Aaroni azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa, nthawi zonse. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pa mibado yonse. Aaroni ayatse nyale zimene zili pa choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri kuti zikhale zoyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova.

“Mutenge ufa wosalala ndipo muphike makeke khumi ndi awiri ndipo keke iliyonse ikhale ya ufa wa makilogalamu awiri. Muwayike pa tebulo la golide wabwino kwambiri pamaso pa Yehova mʼmizere iwiri. Mzere uliwonse ukhale wa makeke asanu ndi imodzi. Pa mzere uliwonse muyikepo lubani wafungo lokoma kuti pamodzi ndi bulediyo akhale wachikumbutso cha nsembe yopsereza yopereka kwa Yehova. Sabata ndi sabata nthawi zonse Aaroni aziyika makeke amenewa pamaso pa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti akhale pangano lamuyaya. Chakudyacho ndi cha Aaroni ndi ana ake ndipo azidyera ku malo wopatulika chifukwa kwa iye chakudyacho ndi chopatulika kwambiri chochokera pa chopereka chopsereza cha Yehova.”

Woyankhula Monyoza Mulungu Aphedwa ndi Miyala

10 Tsiku lina munthu wina wamwamuna amene amayi ake anali Mwisraeli koma abambo ake anali Mwigupto anapita kwa Aisraeli ndipo anakangana ndi Mwisraeli wina ku msasa. 11 Munthu uja ananyoza dzina la Yehova ndi kulitemberera. Choncho anabwera naye kwa Mose. Dzina la amayi ake linali Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani. 12 Anamuyika mʼndende mpaka atadziwa bwino chofuna cha Yehova.

13 Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, 14 “Pita naye kunja kwa msasa munthu wotembererayo. Onse amene anamumva akutemberera asanjike manja awo pamutu pake ndipo gulu lonse la anthu limugende miyala. 15 Choncho uza Aisraeli kuti, ‘Aliyense wotemberera Mulungu wake alangidwe. 16 Aliyense wonyoza dzina la Yehova, mlendo ngakhale mbadwa, aphedwe. Gulu lonse la anthu limuponye miyala.

17 “ ‘Ngati munthu wina aliyense achotsa moyo wa munthu mnzake, munthuyo ayenera kuphedwa. 18 Aliyense wopha chiweto cha mnzake ayenera kulipira china. Moyo kulipa moyo. 19 Ngati munthu avulaza mnzake, nayenso amuchite zomwe wachitira mnzakeyo: 20 kuthyola fupa kulipira kuthyola fupa, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino. Monga momwe anavulazira mnzake, amuvulaze chimodzimodzinso. 21 Aliyense wopha chiweto cha mnzake, alipire chiweto china, koma aliyense wopha munthu ayenera kuphedwa. 22 Lamulo la mlendo ndi mbadwa ndi limodzi lomweli. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

23 Pamenepo Mose anawuza Aisraeli zimenezi, ndipo iwo anatulutsira munthu wotembererayo kunja kwa msasa ndi kumugenda miyala. Aisraeli anachita zimene Yehova analamula Mose.

Masalimo 31

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

31 Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;
    musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;
    mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.
Tcherani khutu lanu kwa ine,
    bwerani msanga kudzandilanditsa;
mukhale thanthwe langa lothawirapo,
    linga lolimba kundipulumutsa ine.
Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,
    chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.
Ndimasuleni mu msampha umene anditchera
    pakuti ndinu pothawirapo panga.
Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga;
    womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.

Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe;
    ine ndimadalira Yehova.
Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu
    popeza Inu munaona masautso anga
    ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.
Inu simunandipereke kwa mdani
    koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.

Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;
    maso anga akulefuka ndi chisoni,
    mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10 Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima
    ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;
mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,
    ndipo mafupa anga akulefuka.
11 Chifukwa cha adani anga onse,
    ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;
ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.
    Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12 Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;
    ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;
    zoopsa zandizungulira mbali zonse;
iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,
    kuti atenge moyo wanga.

14 Koma ndikudalira Inu Yehova;
    ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
    ndipulumutseni kwa adani anga
    ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
    pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.
17 Yehova musalole kuti ndichite manyazi,
    pakuti ndalirira kwa Inu;
koma oyipa achititsidwe manyazi
    ndipo agone chete mʼmanda.
18 Milomo yawo yabodzayo ikhale chete,
    pakuti chifukwa cha kunyada
    ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.

19 Ndi waukulu ubwino wanu
    umene mwawasungira amene amakuopani,
umene mumapereka anthu akuona
    kwa iwo amene amathawira kwa Inu.
20 Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa,
    kuwateteza ku ziwembu za anthu;
mʼmalo anu okhalamo mumawateteza
    kwa anthu owatsutsa.

21 Matamando akhale kwa Yehova,
    pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine
    pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.
22 Ndili mʼnkhawa zanga ndinati,
    “Ine ndachotsedwa pamaso panu!”
Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga
    pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.

23 Kondani Yehova oyera mtima ake onse!
    Yehova amasunga wokhulupirika
    koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.
24 Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,
    inu nonse amene mumayembekezera Yehova.

Mlaliki 7

Nzeru

Mbiri yabwino ndi yopambana mafuta onunkhira bwino,
    ndipo tsiku lomwalira ndi lopambana tsiku lobadwa.
Kuli bwino kupita ku nyumba yamaliro
    kusiyana ndi kupita ku nyumba yamadyerero:
Pakuti imfa ndiye mathero a munthu aliyense;
    anthu amoyo azichisunga chimenechi mʼmitima mwawo.
Chisoni nʼchabwino kusiyana ndi kuseka,
    pakuti nkhope yakugwa ndi yabwino chifukwa imakonza mtima.
Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa,
    koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.
Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru
    kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru.
Kuseka kwa zitsiru kuli ngati
    kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika,
    izinso ndi zopandapake.

Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru,
    ndipo chiphuphu chimawononga mtima.

Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake,
    ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza.
Usamafulumire kukwiya mu mtima mwako,
    pakuti mkwiyo ndi bwenzi la zitsiru.

10 Usamafunse kuti, “Nʼchifukwa chiyani masiku amakedzana anali abwino kupambana masiku ano?”
    pakuti si chinthu chanzeru kufunsa mafunso oterewa.

11 Nzeru ngati cholowa, ndi chinthu chabwino
    ndipo imapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano.
12 Nzeru ndi chitetezo,
    monganso ndalama zili chitetezo,
koma phindu la chidziwitso ndi ili:
    kuti nzeru zimasunga moyo wa munthu amene ali nazo nzeruzo.

13 Taganizirani zimene Mulungu wazichita:

ndani angathe kuwongola chinthu
    chimene Iye anachipanga chokhota?
14 Pamene zinthu zili bwino, sangalala;
    koma pamene zinthu sizili bwino, ganizira bwino:
Mulungu ndiye anapanga nthawi yabwinoyo,
    ndiponso nthawi imene si yabwinoyo.
Choncho munthu sangathe kuzindikira
    chilichonse cha mʼtsogolo mwake.

15 Pa moyo wanga wopanda phinduwu ndaona zinthu ziwiri izi:

munthu wolungama akuwonongeka mʼchilungamo chake,
    ndipo munthu woyipa akukhala moyo wautali mʼzoyipa zake.
16 Usakhale wolungama kwambiri
    kapena wanzeru kwambiri,
    udziwonongerenji wekha?
17 Usakhale woyipa kwambiri,
    ndipo usakhale chitsiru,
    uferenji nthawi yako isanakwane?
18 Nʼkwabwino kuti utsate njira imodzi,
    ndipo usataye njira inayo.
    Munthu amene amaopa Mulungu adzapewa zinthu ziwiri zonsezi.

19 Nzeru zimapereka mphamvu zambiri kwa munthu wanzeru
    kupambana olamulira khumi a mu mzinda.

20 Palibe munthu wolungama pa dziko lapansi
    amene amachita zabwino zokhazokha ndipo sachimwa.

21 Usamamvetsere mawu onse amene anthu amayankhula,
    mwina udzamva wantchito wako akukutukwana,
22 pakuti iwe ukudziwa mu mtima mwako
    kuti nthawi zambiri iwenso unatukwanapo ena.

23 Zonsezi ndinaziyesa ndi nzeru zanga ndipo ndinati,

“Ine ndatsimikiza mu mtima mwanga kuti ndikhale wanzeru,”
    koma nzeruyo inanditalikira.
24 Nzeru zimene zilipo,
    zili kutali ndipo ndi zozama kwambiri,
    ndani angathe kuzidziwa?
25 Kotero ndinayikapo mtima wanga kuti ndidziwe,
    ndifufuze ndi kumafunafuna nzeru ndi mmene zinthu zimakhalira
ndipo ndinafunanso kudziwa kuyipa kwa uchitsiru
    ndiponso kupusa kwake kwa misala.

26 Ndinapeza kanthu kowawa kupambana imfa,
    mkazi amene ali ngati khoka,
amene mtima wake uli ngati khwekhwe,
    ndipo manja ake ali ngati maunyolo.
Munthu amene amakondweretsa Mulungu adzathawa mkaziyo,
    koma mkaziyo adzakola munthu wochimwa.

27 Mlaliki akunena kuti, “Taonani, chimene ndinachipeza ndi ichi:

“Kuwonjezera chinthu china pa china kuti ndidziwe mmene zinthu zimachitikira,
28     pamene ine ndinali kufufuzabe
    koma osapeza kanthu,
ndinapeza munthu mmodzi wolungama pakati pa anthu 1,000,
    koma pakati pawo panalibepo mkazi mmodzi wolungama.
29 Chokhacho chimene ndinachipeza ndi ichi:
    Mulungu analenga munthu, anamupatsa mtima wolungama,
    koma anthu anatsatira njira zawozawo zambirimbiri.”

2 Timoteyo 3

Zoopsa za Mʼmasiku Otsiriza

Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.

Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu, amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi. Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa. Koma sadzapita nazo patali kwambiri zimenezi, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwawo monga anachitira Yanesi ndi Yambere.

Paulo Alimbikitsa Timoteyo

10 Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga, 11 mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi. 12 Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, 13 pomwe anthu oyipa ndi onyenga adzanka nayipirayipira, kunamiza ena, iwo nʼkumanamizidwanso. 14 Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi. 15 Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu. 16 Malemba onse anawalembetsa ndi Mulungu, ndipo othandiza pophunzitsa, podzudzula, pokonza cholakwika ndi polangiza za chilungamo 17 kuti munthu wa Mulungu akonzekere bwino lomwe kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.