Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 19

Malamulo Osiyanasiyana

19 Yehova anawuza Mose kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Khalani oyera mtima chifukwa Ine, Yehova Mulungu wanu, ndine Woyera.

“ ‘Aliyense mwa inu azilemekeza abambo ake ndi amayi ake. Ndipo muzisunga masabata anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

“ ‘Musatembenukire ku mafano kapena kudzipangira nokha milungu ya zitsulo zosungunula. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

“ ‘Pamene mukupereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova, muyipereke mwanjira yoti ilandiridwe. Nsembe izidyedwa tsiku lomwe mwayiperekalo kapena mmawa mwake. Chilichonse chotsala mpaka tsiku lachitatu chiyenera kutenthedwa. Ngati mudya choperekacho tsiku lachitatu, ndiye kuti mwachita chonyansa ndipo chakudyacho sichidzalandiridwa. Munthu aliyense amene adya chakudyacho adzasenza machimo ake chifukwa wayipitsa chinthu chimene ndi choyera kwa Yehova. Munthu ameneyo achotsedwe pakati pa anthu anzake.

“ ‘Pamene mukolola zinthu mʼmunda mwanu musakolole mpaka mʼmphepete mwa munda, ndipo musatole khunkha lake. 10 Musakolole mphesa zonse mʼmunda wanu wa mpesa kapena kutola mphesa zakugwa mʼmundamo. Zimenezi muzisiyire anthu osauka ndi alendo. Ine ndine Yehova Mulungu wako.

11 “ ‘Musabe.

“ ‘Musamanamizane.

“ ‘Musachitirane zinthu mwachinyengo.

12 “ ‘Musalumbire mʼdzina langa monyenga popeza kutero ndi kuyipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

13 “ ‘Musapsinje mnzanu kapena kumulanda zinthu zake.

“ ‘Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka mmawa.

14 “ ‘Musatemberere wosamva kapena kuyikira munthu wosaona chinthu choti apunthwe nacho patsogolo pake, koma muziopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

15 “ ‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musachite tsankho pakati pa osauka ndi olemera, koma muweruze mlandu wa mnzanu mwachilungamo.

16 “ ‘Musamapite uku ndi uku kunena bodza pakati pa anthu anu.

“ ‘Musachite kanthu kalikonse kamene kangadzetse imfa kwa mnzanu. Ine ndine Yehova.

17 “ ‘Musamude mʼbale wanu mu mtima mwanu. Koma mudzudzuleni mnzanu moona mtima kuti musakhale wolakwa.

18 “ ‘Musamubwezere mnzanu choyipa kapena kumusungira kanthu kunkhosi, koma konda mnansi wako monga iwe mwini. Ine ndine Yehova.

19 “ ‘Muzisunga malangizo anga.

“ ‘Tsono musamalole kuti ngʼombe zanu zikwerane ndi chiweto cha mtundu wina.

“ ‘Ndiponso musamadzale mbewu za mitundu iwiri mʼmunda umodzi.

“ ‘Musavale chovala chopangidwa ndi nsalu za mitundu iwiri.

20 “ ‘Ngati munthu agonana ndi kapolo wamkazi amene wafunsidwa mbeta ndi munthu wina, koma sanawomboledwe kapenanso kulandira ufulu wake, alangidwe. Koma onsewa asaphedwe, chifukwa mkaziyo anali asanalandire ufulu wake. 21 Koma mwamunayo abwere ndi nsembe yopepesera kupalamula kwa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna 22 ndipo wansembe achite nayo mwambo wopepesera chifukwa cha kupalamula kumene anachita pamaso pa Yehova. Akatero tchimo lake lidzakhululukidwa.

23 “ ‘Mukadzalowa mʼdzikomo ndi kudzala mtengo wa mtundu uliwonse wa zipatso, zipatso zakezo mudzaziyese ngati zodetsedwa. Ndiye kuti kwa zaka zitatu zidzakhale zoletsedwa kwa inu. Musadzazidye nthawi imeneyi. 24 Chaka chachinayi, zipatso zake zonse zidzakhala zopatulika, ndipo zidzakhala chopereka cha matamando kwa Yehova. 25 Koma chaka chachisanu, mudzatha kudya zipatso zake kuti mitengoyo idzakubalireni zochuluka. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

26 “ ‘Musadye nyama ya magazi.

“ ‘Musamawombeze kapena kuchita zamatsenga.

27 “ ‘Musamamete mduliro kapena kumeta mʼmphepete mwa ndevu zanu.

28 “ ‘Musadzichekecheke pathupi panu chifukwa cha munthu wakufa kapena kudzitema mphini pa thupi lanu. Ine ndine Yehova.

29 “ ‘Musamuyipitse mwana wanu wamkazi pomusandutsa mkazi wachiwerewere. Mukatero dziko lidzasanduka la anthu achiwerewere ndi lodzaza ndi zoyipa.

30 “ ‘Muzisunga Masabata anga ndipo muzilemekeza malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.

31 “ ‘Musamapite kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena kwa owombeza. Musamawafunefune kuti angakuyipitseni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

32 “ ‘Muzikhala mwa ulemu pamaso pa munthu wachikulire, ndipo muzichitira ulemu munthu wokalamba. Kumeneko ndiye kuopa Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.

33 “ ‘Pamene mlendo akhala nanu mʼdziko mwanu, musamuzunze. 34 Mlendo amene akhala nanu akhale ngati mmodzi mwa mbadwa zanu. Mumukonde monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Paja inu munali alendo mʼdziko la Igupto. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

35 “ ‘Musamachite za chinyengo poweruza mlandu, kapena poyeza utali, kulemera ngakhalenso kuchuluka kwa zinthu. 36 Miyeso ya sikelo, miyeso yoyezera kulemera kwa zinthu, miyeso yotchedwa efa ndi miyeso yotchedwa hini zikhale zolungama. Ine ndine Yehova, Mulungu wanu amene ndinakutulutsani ku dziko la Igupto.

37 “ ‘Choncho muzisunga malangizo ndi malamulo angawa ndi kuwatsatira. Ine ndine Yehova.’ ”

Masalimo 23-24

Salimo la Davide.

23 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu.
    Amandigoneka pa msipu wobiriwira,
amanditsogolera ku madzi akumwa abwino,
    amatsitsimutsa moyo wanga.
Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo
    chifukwa cha dzina lake.
Ngakhale ndiyende
    mʼchigwa cha mdima wakuda bii,
sindidzaopa choyipa,
    pakuti Inu muli ndi ine;
chibonga chanu ndi ndodo yanu
    zimanditonthoza.

Mumandikonzera chakudya
    adani anga akuona.
Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;
    chikho changa chimasefukira.
Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata
    masiku onse a moyo wanga,
ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova
    kwamuyaya.

Salimo la Davide.

24 Dziko lapansi ndi la Yehova ndi zonse zimene zili mʼmenemo,
    dziko ndi onse amene amakhala mʼmenemo;
pakuti Iye ndiye anayika maziko ake pa nyanja
    ndi kulikhazika pamwamba pa madzi.

Ndani angakwere phiri la Yehova?
    Ndani angathe kuyima pa malo ake opatulika?
Iye amene ali ndi mʼmanja moyera ndi mtima woyera,
    amene sapereka moyo wake kwa fano
    kapena kulumbira mwachinyengo.
Iyeyo adzalandira madalitso kwa Yehova
    ndipo Mulungu mpulumutsi wake adzagamula kuti alibe mlandu.
Umenewo ndiwo mʼbado wa amene amafunafuna Yehova;
    amene amafunafuna nkhope yanu, Inu Mulungu wa Yakobo.
            Sela

Tukulani mitu yanu inu zipata;
    tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
    kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
    Yehova Wamphamvuzonse,
    Yehova ndiye wamphamvu pa nkhondo.
Tukulani mitu yanu, inu zipata;
    tsekukani, inu zitseko zakalekalenu,
    kuti Mfumu yaulemerero ilowe.
10 Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani?
    Yehova Wamphamvuzonse,
    Iye ndiye Mfumu yaulemerero.
            Sela

Mlaliki 2

Zosangalatsa Nʼzopandapake

Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Tsopano ndiyese zosangalatsa kuti ndipeze zomwe ndi zabwino.” Koma izi zinaonekanso kuti ndi zopandapake. “Kuseka,” ndinati, “imeneyo ndi misala. Ndipo kodi chisangalalo chimabweretsa phindu lanji?” Ndinayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewu unali uchitsiru, pamenepo nʼkuti maganizo anga akutsogozedwa ndi nzeru. Ine ndinkati mwina kapena njira yotero nʼkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku owerengeka a moyo wawo.

Ndinagwira ntchito zikuluzikulu: Ndinadzimangira nyumba ndi kuwoka mipesa. Ndinalima madimba ndi minda yamitengo; ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso za mitundu yonse. Ndinakumba mayiwe osungiramo madzi woti ndizithirira minda ya mitengo yodzalidwa ija. Ndinagula akapolo aamuna ndi akapolo aakazi, ndiponso ndinali ndi akapolo ena omwe anabadwira mʼnyumba mwanga. Ndinalinso ndi ngʼombe ndi nkhosa zambiri kupambana aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Ndinadzikundikira siliva ndi golide, ndiponso chuma chochokera kwa mafumu ndi madera awo. Ndinali ndi amuna ndi akazi oyimba ndiponso azikazi; zinthu zokondweretsa mtima wa munthu. Ndinali munthu wotchuka kupambana wina aliyense mu Yerusalemu amene analipo ndisanabadwe. Mu zonsezi nzeru zanga zinali nane.

10 Sindinadzimane chilichonse chimene maso anga anachifuna;
    mtima wanga sindinawumane zokondweretsa.
Mtima wanga unakondwera ndi ntchito yanga yonse,
    ndipo iyi ndiyo inali mphotho ya ntchito zanga zonse zolemetsa.
11 Koma pamene ndinayamba kuyangʼanayangʼana zonse zimene ndinachita ndi manja anga,
    ndi zimene ndinazivutikira kuti ndizipeze,
zonsezi zinali zopandapake; kungodzivuta chabe,
    palibe chomwe ndinapindula pansi pano.

Nzeru ndi Uchitsiru Nʼzopandapake

12 Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani,
    komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani.
Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani
    choposa chimene chinachitidwa kale?
13 Ndinaona kuti nzeru ndi yopambana uchitsiru,
    monga momwe kuwala kumapambanira mdima.
14 Munthu wanzeru amayenda maso ali patsogolo,
    pamene chitsiru chimayenda mʼchimbulimbuli;
koma ndinazindikira kuti chomwe
    chimawachitikira onsewo ndi chimodzi.

15 Pamenepo ndinalingalira mu mtima mwanga,

“Zochitikira chitsiru zidzandichitikiranso ine.
    Nanga tsono phindu langa nʼchiyani pakukhala wanzeru?”
Ndinati mu mtima mwanga,
    “Ichinso ndi chopandapake.”
16 Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali;
    mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika.
Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru!

Kugwira Ntchito Nʼkopandapake

17 Kotero ndinadana nawo moyo chifukwa ntchito zimene zimagwiridwa pansi pano ndi zosautsa kwa ine. Ntchito zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe. 18 Ine ndinadana nazo ntchito zonse zimene ndinazigwira pansi pano, chifukwa ndinayenera kudzazisiyira wina amene adzalowa mʼmalo mwanga. 19 Ndipo ndani amadziwa kuti munthu ameneyo adzakhala wanzeru kapena chitsiru? Komabe munthuyo adzakhala wolamulira zonse zimene ndinazichita pansi pano mwa nzeru zanga. Izinso ndi zopandapake. 20 Motero ndinayamba kutaya mtima chifukwa cha ntchito zonse zimene ndinazivutikira pansi pano. 21 Pakuti munthu atha kugwira ntchito yake mwanzeru, chidziwitso ndi luntha, ndipo kenaka nʼkusiyira wina amene sanakhetserepo thukuta. Izinso ndi zopandapake ndiponso tsoka lalikulu. 22 Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zonse zolemetsa ndi zodetsa nkhawa zimene amazichita pansi pano? 23 Masiku ake onse amakhala achisoni, ntchito yake imakhala yovuta; ngakhale usiku womwe, mtima wake supumula. Izinso ndi zopandapake.

24 Kwa munthu palibe chabwino china kuposa kudya, kumwa ndi kukondwerera ntchito zake. Izinso ndaona kuti ndi zochokera kwa Mulungu, 25 pakuti popanda Iye, ndani angadye ndi kupeza chisangalalo? 26 Munthu amene amakondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamusandutsa wanzeru, wozindikira ndi wachisangalalo, koma wochimwa, Mulungu amamupatsa ntchito yosonkhanitsa ndi kusunga chuma kuti adzachipereke kwa amene Mulunguyo amakondwera naye. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

1 Timoteyo 4

Malangizo kwa Timoteyo

Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda. Ziphunzitso zimenezi zimachokera ku chinyengo cha anthu onama, amene chikumbumtima chawo chinamatidwa ndi chitsulo cha moto. Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika. Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.

Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata. Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu. Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo.

Amenewa ndi mawu odalirika ndi oyenera kuwalandira kwathunthu. 10 Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira.

11 Lamulira ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi. 12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. 13 Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa. 14 Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja.

15 Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. 16 Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.