Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 18

Kugonana Koletsedwa

18 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Musamachite zomwe amachita anthu a ku Igupto kumene munkakhala kuja, ndiponso musamachite zomwe amachita anthu a ku Kanaani kumene ndikukupititsani. Musatsatire miyambo yawo. Inu muzimvera malamulo anga ndipo muzisamalitsa kutsatira malangizo anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Choncho sungani malangizo ndi malamulo anga, popeza munthu amene amvera zimenezi adzakhala ndi moyo. Ine ndine Yehova.

“ ‘Munthu aliyense asagonane ndi wachibale wake. Ine ndine Yehova.

“ ‘Usachititse manyazi abambo ako pogonana ndi amayi ako. Iwo ndi amayi ako. Usagonane nawo.

“ ‘Usagonane ndi mkazi wa abambo ako (osakhala amayi okubala). Ukatero ukuchititsa manyazi abambo ako.

“ ‘Usagonane ndi mlongo wako, mwana wamkazi wa abambo ako, kapena mwana wamkazi wa amayi ako, kaya anabadwira mʼnyumba mwanu kapena kwina.

10 “ ‘Usagonane ndi mdzukulu wako: mwana wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wa mwana wako wamkazi. Kutero nʼkudzichotsa ulemu.

11 “ ‘Usagonane ndi mwana wamkazi wa mkazi wa abambo ako, amene abambo akowo anabereka; popeza ameneyo ndi mlongo wako.

12 “ ‘Usagonane ndi mlongo wa abambo ako; popeza ameneyo ndi thupi limodzi ndi abambo ako.

13 “ ‘Usagonane ndi mchemwali wa amayi ako chifukwa ameneyo ndi thupi limodzi ndi amayi ako.

14 “ ‘Usachititse manyazi mchimwene wa abambo ako pogonana ndi mkazi wake popeza amenewo ndi azakhali ako.

15 “ ‘Usagonane ndi mpongozi wako popeza ameneyo ndi mkazi wa mwana wako. Choncho usamuchititse manyazi.

16 “ ‘Usagonane ndi mkazi wa mchimwene wako popeza potero ukuchititsa manyazi mʼbale wakoyo.

17 “ ‘Usagonane ndi mkazi ndiponso mwana wake wamkazi. Usagonane ndi mwana wamkazi wa mwana wake wamwamuna, kapena mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi. Amenewo ndi thupi limodzi ndi mkaziyo. Kutero ndikuchita chinthu choyipa kwambiri.

18 “ ‘Usakwatire mchemwali wa mkazi wako ndi kumagonana naye mkazi wakoyo ali moyo ngati wopikisana naye.

19 “ ‘Usamuyandikire mkazi kuti ugonane naye pa nthawi yake yosamba.

20 “ ‘Usagonane ndi mkazi wa mnzako ndi kudziyipitsa naye.

21 “ ‘Usapereke mwana wako aliyense kuti akhale nsembe yamoto kwa Moleki ndi kuyipitsa dzina la Yehova. Ine ndine Yehova.

22 “ ‘Usagonane ndi mwamuna ngati mkazi; chimenecho ndi chinthu chonyansa.

23 “ ‘Usagonane ndi nyama ndi kudziyipitsa nayo. Mkazi asadzipereke kwa nyama kuti agonane nayo. Chimenecho ndi chisokonezo.

24 “ ‘Musadzidetse ndi zinthu zimenezi chifukwa umo ndi mmene mitundu ina imene ndikuyithamangitsa pamaso panu inadzidetsera. 25 Choncho dziko linayipa ndipo ndinalilanga chifukwa cha tchimo lake. Motero dzikolo linasanza anthu ake okhalamo. 26 Koma inu mukasunge malangizo ndi malamulo anga. Mbadwa ndiponso alendo amene akukhala pakati panu asakachite china chilichonse cha zinthu zonyansazi, 27 pakuti zinthu zonsezi ndi zomwe ankachita anthu amene ankakhala mʼdzikomo inu musanafike, ndipo dziko linayipitsidwa. 28 Koma inu musachite zimenezi kuti dziko lingakusanzeni mutaliyipitsa monga linasanzira mitundu imene imakhalamo inu musanafike.

29 “ ‘Aliyense wochita zinthu zonyansa zimenezi achotsedwe pakati pa anthu anzake. 30 Choncho mverani malangizo anga oletsa kuchita miyambo yonyansayi imene ankatsatira anthu amene analipo inu musanafike ndi kudziyipitsa nayo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

Masalimo 22

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide.

22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya?
    Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe?
    Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
Inu Mulungu wanga, ine ndimalira masana, koma simuyankha,
    usikunso, ndipo sindikhala chete.

Inu ndinu Woyera, wokhala pa mpando waufumu;
    ndinu matamando a Israeli.
Pa inu makolo athu anadalira;
    iwo anadalira ndipo Inu munawapulumutsa.
Analirira kwa inu ndipo munawapulumutsa.
    Iwo anakhulupirira Inu ndipo simunawakhumudwitse.

Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,
    wosekedwa ndi wonyozedwa ndi anthu onse.
Onse amene amandiona amandiseka;
    amandiyankhulira mawu achipongwe akupukusa mitu yawo kunena kuti
“Iyeyu amadalira Yehova,
    musiyeni Yehovayo amulanditse.
Musiyeni Yehova amupulumutse
    popeza amakondwera mwa Yehovayo.”

Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga.
    Munachititsa kuti ndizikudalirani
    ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
10 Chibadwire ine ndinaperekedwa kwa Inu;
    kuchokera mʼmimba mwa amayi anga Inu mwakhala muli Mulungu wanga.
11 Musakhale kutali ndi ine,
    pakuti mavuto ali pafupi
    ndipo palibe wina wondipulumutsa.

12 Ngʼombe zazimuna zandizungulira;
    ngʼombe zazimuna zamphamvu za ku Basani zandizinga.
13 Mikango yobangula pokadzula nyama,
    yatsekula kwambiri pakamwa pawo kulimbana nane.
14 Ine ndatayika pansi ngati madzi
    ndipo mafupa anga onse achoka mʼmalo mwake.
Mtima wanga wasanduka phula;
    wasungunuka mʼkati mwanga.
15 Mphamvu zanga zauma ngati phale,
    ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada;
    mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
16 Agalu andizungulira;
    gulu la anthu oyipa landizinga.
    Alasa manja ndi mapazi anga.
17 Ine nditha kuwerenga mafupa anga onse;
    anthu amandiyangʼanitsitsa ndi kundidzuma.
18 Iwo agawana zovala zanga pakati pawo
    ndi kuchita maere pa zovala zangazo.

19 Koma Inu Yehova, musakhale kutali;
    Inu mphamvu yanga, bwerani msanga kuti mudzandithandize.
20 Pulumutsani moyo wanga ku lupanga,
    moyo wanga wopambanawu ku mphamvu ya agalu.
21 Ndilanditseni mʼkamwa mwa mikango;
    pulumutseni ku nyanga za njati.

22 Ine ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga;
    ndidzakutamandani mu msonkhano.
23 Inu amene mumaopa Yehova mutamandeni!
    Inu zidzukulu zonse za Yakobo, mulemekezeni!
    Muopeni mwaulemu, inu zidzukulu zonse za Israeli!
24 Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza
    kuvutika kwa wosautsidwayo;
Iye sanabise nkhope yake kwa iye.
    Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.

25 Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira.
    Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
26 Osauka adzadya ndipo adzakhuta;
    iwo amene amafunafuna Yehova adzamutamanda.
    Mitima yanu ikhale ndi moyo mpaka muyaya!
27 Malekezero onse a dziko lapansi
    adzakumbukira Yehova ndi kutembenukira kwa Iye,
ndipo mabanja a mitundu ya anthu
    adzawerama pamaso pake,
28 pakuti ulamuliro ndi wake wa Yehova
    ndipo Iye amalamulira anthu a mitundu yonse.

29 Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira;
    onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake;
    iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
30 Zidzukulu zamʼtsogolo zidzamutumikira Iye;
    mibado ya mʼtsogolo idzawuzidwa za Ambuye.
31 Iwo adzalengeza za chilungamo chake
    kwa anthu amene pano sanabadwe
    pakuti Iye wachita zimenezi.

Mlaliki 1

Zapansipano Nʼzopandapake

Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu:

“Zopandapake! Zopandapake!”
    atero Mlaliki.
“Zopandapake kotheratu!
    Zopandapake.”

Kodi munthu amapindulanji pa ntchito zake zonse
    zimene amasautsidwa nazo pansi pano?
Mibado imabwera ndipo mibado imapita,
    koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse.
Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa
    ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira.
Mphepo imawombera cha kummwera
    ndi kukhotera cha kumpoto;
imawomba mozungulirazungulira,
    kumangobwererabwerera komwe yachokera.
Mitsinje yonse imakathira ku nyanja,
    koma nyanjayo sidzaza;
kumene madziwo amachokera,
    amabwereranso komweko.
Zinthu zonse ndi zotopetsa,
    kutopetsa kwake ndi kosaneneka.
Maso satopa ndi kuona
    kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva.
Zomwe zinalipo kale zidzakhalaponso,
    zomwe zinachitika kale zidzachitikanso.
    Ndiye kuti chatsopano palibiretu pansi pano.
10 Kodi chilipo chinthu chimene wina anganene kuti,
    “Taona! Ichi ndiye chatsopano?”
Chinalipo kale, kalekale;
    chinalipo ife kulibe.
11 Anthu akale sakumbukiridwa,
    ngakhale amene adzabwera mʼtsogolomu
sadzakumbukiridwa ndi iwo
    amene adzabwere pambuyo pawo.

Nzeru Nʼzopandapake

12 Ine, Mlalikine, ndinali mfumu ya Israeli mu Yerusalemu. 13 Ndinayika mtima wanga pophunzira ndi kufunafuna mwa nzeru zinthu zonse zimene zimachitika pansi pa thambo. Ndi ntchito yolemetsa ndithu imene Mulungu anayipereka kwa anthu! 14 Ine ndaona zinthu zonse zochitika pansi pano; zinthu zonsezo ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.

15 Chinthu chokhota sichingathe kuwongoledwa;
    chimene palibe sichingathe kuwerengedwa.

16 Ine ndinaganiza mu mtima mwanga, “Taona, ine ndakula ndi kukhala wa nzeru zochuluka kupambana aliyense amene analamulirapo Yerusalemu ndisanabadwe; ndaphunzira nzeru zochuluka ndi luntha.” 17 Ndipo ndinadzipereka kuti ndithe kumvetsa kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani, uchitsiru nʼchiyani, koma ndinazindikira ichi, kuti kuteronso nʼkungodzivuta chabe.

18 Pakuti nzeru zochuluka zimabweretsa chisoni chochulukanso:
    chidziwitso chochuluka, zowawa zochulukanso.

1 Timoteyo 3

Zowayenereza Oyangʼanira ndi Atumiki

Mawu woona ndi awa: Ngati munthu akufunitsitsa atakhala woyangʼanira, ndiye kuti akufuna ntchito yabwino. Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandewu, koma wofatsa, asakhale wokonda mikangano, kapena wokonda ndalama. Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni. (Ngati munthu sadziwa kusamala banja lake lomwe, angathe bwanji kusamala mpingo wa Mulungu?) Asakhale wongotembenuka mtima kumene kuopa kuti angadzitukumule napezeka pa chilango monga Satana. Ayeneranso kukhala munthu wambiri yabwino ndi akunja, kuti anthu asamutonze nagwa mu msampha wa Satana.

Momwemonso atumiki, akhale anthu oyenera ulemu, woona mtima, osakhala okonda zoledzeretsa, osakonda kupeza zinthu mwachinyengo. Ayenera kugwiritsa mozama choonadi cha chikhulupiriro ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino. 10 Ayambe ayesedwa kaye, ndipo ngati palibe kanthu kowatsutsa, aloleni akhale atumiki.

11 Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse.

12 Mtumiki akhale wokhulupirika kwa mkazi wake ndipo ayenera kukhala wosamalira bwino ana ake ndi onse a pa khomo pake. 13 Iwo amene atumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndipo amakhala chitsimikizo chachikulu cha chikhulupiriro chawo mwa Khristu Yesu.

Cholinga cha Malangizo a Paulo

14 Ngakhale ndili ndi chiyembekezo choti ndifika komweko posachedwapa, ndikukulemberani malangizo awa. 15 Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi. 16 Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu:

Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu,
    Mzimu anamuchitira umboni,
angelo anamuona,
    analalikidwa pakati pa mitundu yonse,
dziko lapansi linamukhulupirira,
    anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.