M’Cheyne Bible Reading Plan
Tsiku la Mwambo Wopepesera Machimo
16 Atafa ana awiri a Aaroni amene anaphedwa atapita pamaso pa Yehova mosayenera, Yehova anayankhula ndi Mose. 2 Yehova anawuza Mose kuti, “Uza mchimwene wako Aaroni kuti asamalowe ku Malo Wopatulika, kuseri kwa katani, pamaso pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano nthawi iliyonse imene akufuna kuopa kuti angadzafe, pakuti Ine ndimaoneka mu mtambo umene uli pamwamba pa chivundikiro cha Bokosi la Chipangano.
3 “Aaroni azilowa Malo Wopatulika Kwambiri motere: azitenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. 4 Azivala mwinjiro wopatulika wa nsalu yosalala, azivalanso kabudula wa mʼkati wa nsalu yosalala, azimanga lamba wa nsalu yosalala, ndipo avalenso nduwira ya nsalu yosalala kumutu. Zimenezi ndi nsalu zopatulika ndipo atasamba thupi lonse azivala zimenezi. 5 Kuchokera pa gulu la Aisraeli, Aaroni azitenga mbuzi zazimuna ziwiri kuti zikhale nsembe yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza.
6 “Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale yopepesera machimo a iye mwini kuti achite mwambo wopepesera machimo ake pamodzi ndi a banja lake. 7 Kenaka atenge mbuzi ziwiri zija ndipo aziyimike pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. 8 Aaroni ndiye achite maere pa mbuzi ziwirizo kuti imodzi ikhale ya Yehova, ndipo inayo ikhale ya Azazele. 9 Aaroni abwere ndi mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi ya Yehova, ndipo apereke kuti ikhale nsembe yopereka chifukwa cha tchimo. 10 Koma mbuzi imene maere aonetsa kuti ndi yosenza machimo, apereke ya moyo pamaso pa Yehova, kuti achite mwambo wopepesera machimo pa mbuziyo poyitumiza ku chipululu kuti ikhale ya Azazele.
11 “Aaroni apereke ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo ake. Ndiye achite mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake pamodzi ndi banja lake. Pambuyo pake aphe ngʼombe yopepesera machimo ake aja. 12 Kenaka iye atenge chofukizira chodzaza ndi makala a moto ochokera pa guwa lansembe pamaso pa Yehova. Atengenso lubani wonunkhira ndi woperapera wokwanira manja awiri, ndipo alowe naye kuseri kwa katani. 13 Athire lubani pa moto pamaso pa Yehova kuti utsi wa lubaniyo uphimbe chivundikiro chimene chili pamwamba pa Bokosi la Chipangano, kuti Aaroniyo asafe. 14 Ndipo atenge magazi ena a ngʼombeyo, awawaze ndi chala chake pa chivundikiro cha kummawa; kenaka awaze magaziwo ndi chala chake kasanu ndi kawiri patsogolo pa chivundikirocho.
15 “Kenaka Aaroni aphe mbuzi ya nsembe yopepesera machimo a anthu, ndipo magazi ake alowe nawo kuseri kwa katani ndi kuchita chimodzimodzi monga anachitira ndi magazi a ngʼombe aja: Aaroni awaze magaziwo pa chivundikiro chija ndi patsogolo pa chivundikirocho. 16 Pamenepo ndiye kuti wansembeyo wachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika chifukwa cha kudetsedwa ndi kuwukira kwa Aisraeli pa machimo ena aliwonse amene achita. Achite chimodzimodzi ndi tenti ya msonkhano imenenso ili yodetsedwa chifukwa cha machimo awo. 17 Mu tenti ya msonkhano musakhale munthu ndi mmodzi yemwe nthawi imene Aaroni akupita kukachita mwambo wopepesera ku Malo Wopatulika mpaka atatulukako. Musakhale munthu mu tenti ya msonkhano mpaka atachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake, banja lake ndi gulu lonse la Aisraeli.
18 “Kenaka, Aaroniyo akatuluka apite ku guwa limene lili pamaso pa Yehova ndi kulichitira mwambo wolipepesera. Atengeko magazi a ngʼombe yayimuna ndiponso magazi a mbuzi ndi kuwapaka pa nyanga zonse za guwa lansembe. 19 Magazi ena awawaze pa guwalo ndi chala chake kasanu ndi kawiri kuliyeretsa ndi kulipatula kuchotsa zodetsa za Aisraeli.
20 “Aaroni akatsiriza mwambo wopepesera Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa, azibwera ndi mbuzi yamoyo kudzayipereka nsembe. 21 Aaroni asanjike manja ake pa mutu wa mbuziyo ndipo awulule pa mbuziyo zoyipa zonse ndi zowukira zonse za Aisraeli, kutanthauza machimo awo onse. Machimowo awayike pa mutu wa mbuziyo. Kenaka munthu amene anasankhidwa athamangitsire mbuziyo ku chipululu. 22 Mbuziyo isenze machimo awo onse ndi kupita nawo kutali ndipo munthuyo aleke mbuziyo kuti ipite ku chipululuko.
23 “Pambuyo pake Aaroni alowe mu tenti ya msonkhano ndi kuvula zovala zosalala zija zimene anavala polowa ku Malo Wopatulika ndi kuzisiya komweko. 24 Asambe thupi lonse ku Malo Wopatulika ndi kuvala zovala zake za nthawi zonse. Kenaka atuluke ndi kukapereka nsembe yopsereza ya iye mwini, ndiponso nsembe yopsereza yoperekera anthu. Akatero ndiye kuti wachita mwambo wopepesera machimo a iye mwini wake ndi a anthu. 25 Mafuta a nyama yopepesera machimo awatenthe pa guwa lansembe.
26 “Tsono munthu amene anaperekeza mbuzi yosenza machimo ija achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe ku msasa. 27 Ngʼombe ndi mbuzi zoperekera nsembe yopepesera machimo zimene magazi ake anabwera nawo kuti achitire mwambo wopepesera Malo Wopatulika, azitulutsire kunja kwa msasa. Koma zikopa zake, nyama yake ndi matumbo ake azitenthe. 28 Munthu amene azitenthe achape zovala zake ndi kusamba. Pambuyo pake alowe mu msasa.
29 “Ili likhale lamulo lanu lamuyaya: Mwezi wachisanu ndi chiwiri, pa tsiku la khumi la mwezi, mugonje pamaso pa Yehova. Musamagwire ntchito iliyonse, kaya ndinu mbadwa kapena mlendo amene akukhala pakati panu, 30 chifukwa tsiku limeneli kudzachitika mwambo wopepesera machimo anu, kukuyeretsani kuti mukhale oyeretsedwa ku machimo anu pamaso pa Yehova. 31 Limeneli ndi tsiku lanu la Sabata lopumula, ndipo muzigonja pamaso pa Yehova. Limeneli ndi lamulo lanu la muyaya. 32 Wansembe amene wadzozedwa ndi kupatulidwa kuti akhale wansembe kulowa mʼmalo mwa abambo ake ndiye azichita mwambo wopepesera machimo atavala zovala zake zosalala ndi zopatulika. 33 Adzachite mwambo wopepesera machimo Malo Wopatulika, tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Adzachitenso mwambo wopepesera anzake ndi gulu lonse la anthu.
34 “Ili likhale lamulo lanu lamuyaya. Mwambo wopepesera machimo uzichitika kamodzi pa chaka chifukwa cha machimo a anthu onse.”
Ndipo Mose anachita monga momwe Yehova analamulira.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
thambo limalalikira ntchito za manja ake.
2 Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
3 Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
liwu lawo silimveka.
4 Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
5 Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
6 Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.
7 Lamulo la Yehova ndi langwiro,
kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
8 Malangizo a Yehova ndi olungama,
amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
amapereka kuwala.
9 Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
powasunga pali mphotho yayikulu.
12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.
14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
zikhale zokondweretsa pamaso panu,
Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.
Mawu a Aguri
30 Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake wa ku Masa:
Munthuyo anati kwa Itieli, “Inu Mulungu, ine ndatopa.
Inu Mulungu, ine ndatopa. Ndalefukiratu.
2 “Ine ndine munthu wopusa kuposa anthu onse;
ndilibe nzeru zomvetsa zinthu zonga za munthu.
3 Sindinaphunzire nzeru,
ndipo Woyerayo sindimudziwa.
4 Kodi ndani anakwera kumwamba ndi kutsikako?
Ndani anafumbatapo mphepo mʼmanja mwake?
Ndani anamanga madzi mʼchovala chake?
Ndani anakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi?
Dzina lake ndani? Ndiwuze ngati ukudziwa!
Ndipo mwana wake dzina lake ndani?
5 “Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika;
Iye ndi chishango kwa amene amathawira kwa Iye.
6 Usawonjezepo kanthu pa mawu ake,
kuopa kuti Iye angadzakudzudzule ndi kukupeza kuti ndiwe wabodza.”
7 “Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri
musandimane zimenezo ndisanafe:
8 Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo.
Chachiwiri, ndisakhale mʼmphawi kapena munthu wachuma.
Koma muzindidyetsa chakudya chondikwanira tsiku ndi tsiku
9 kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani,
nʼkumanena kuti, ‘Yehova ndiye yaninso?’
Kuopanso kuti ndikakhala wosauka ndingayambe kuba,
potero nʼkuyipitsa dzina la Mulungu wanga.”
10 “Usamusinjirire wantchito kwa mbuye wake
kuopa kuti angakutemberere ndipo iweyo nʼkupezeka wolakwa.”
11 “Alipo ena amene amatemberera abambo awo,
ndipo sadalitsa amayi awo.
12 Pali ena amene amadziyesa okha oyera mtima
komatu sanachotse zoyipa zawo.
13 Pali ena ndi odzitukumula kwambiri,
amene amakweza zikope modzitukumula.
14 Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga
ndipo zibwano zawo zili ngati mipeni
moti amadya amphawi ndi kuwachotsa pa dziko lapansi.
Amachotsanso anthu osauka pakati pa anzawo.”
15 “Msundu uli ndi ana aakazi awiri
iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ”
“Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta,
zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’
16 Manda, mkazi wosabala,
nthaka yosakhuta madzi
ndiponso moto womangoyakirayakira!”
17 Aliyense amene amanyoza abambo ake,
ndi kunyozera kumvera amayi ake,
makwangwala a ku chigwa adzamukolowola maso
ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
18 Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa,
zinthu zinayi zimene ine sindizimvetsetsa.
19 Ndipo ndi izi: mmene chiwulukira chiwombankhanga mlengalenga;
mmene iyendera njoka pa thanthwe;
mmene chiyendera chombo pa nyanja;
ndiponso mmene mwamuna achitira akakhala ndi namwali.
20 Umu ndi mʼmene mkazi amachitira atachita chigololo:
Atatha kudya ndi kupukuta pakamwa pake
iye amanena kuti “Sindinachite kalikonse kolakwa.”
21 Pali zinthu zitatu zimene zimanjenjemeretsa dziko lapansi,
pali zinthu zinayi zimene dziko lapansi silingathe kuzipirira:
22 Kapolo amene wasanduka mfumu,
chitsiru chimene chakhuta,
23 mkazi wonyozeka akakwatiwa
ndiponso wantchito wamkazi akalanda mwamuna wa mbuye wake.
24 Pali zinthu zinayi zingʼonozingʼono pa dziko lapansi,
komatu ndi zochenjera kwambiri:
25 Nyerere zili ngati anthu opanda mphamvu,
komatu zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe;
26 mbira zili ngati anthu opanda mphamvu
komatu zimakonza pokhalapo pawo mʼmiyala;
27 dzombe lilibe mfumu,
komatu lonse limakhala mʼmagulumagulu poyenda.
28 Buluzi ungathe kumugwira mʼmanja
komatu amapezeka mʼnyumba za mafumu.
29 “Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya,
pali zinthu zinayi zimene zimayenda monyadira:
30 Mkango umene uli wamphamvu kuposa nyama zonse,
ndipo suthawa kanthu kalikonse.
31 Tambala woyenda chinyachinya, mbuzi yayimuna,
ndiponso mfumu yoyenda pakati pa anthu ake.
32 “Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza wekha,
kapena ngati wakhala ukukonzekera zoyipa,
ndiye khala kaye chete, uganizire bwino!
33 Paja pakutha mkaka mafuta amapangidwa,
ndipo ukapsinya mphuno, magazi amatuluka,
ndipo mikangano imakhalapo ukalimbikira kukwiya.”
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu.
2 Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro.
Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe.
Kutsutsa Aphunzitsi Onyenga
3 Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga, 4 kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro. 5 Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona. 6 Anthu ena anapatuka pa zimenezi ndipo anatsata nkhani zopanda tanthauzo. 7 Iwo amafuna kukhala aphunzitsi amalamulo, koma sadziwa zimene akunena, kapena zimene akufuna kutsimikiza.
8 Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. 9 Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. 10 Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. 11 Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa.
Chisomo cha Ambuye kwa Paulo
12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake. 13 Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro. 14 Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu.
15 Mawu odalirika ndi woyenera kuwavomereza kwathunthu ndi awa: Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwitsitsa. 16 Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha. 17 Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.
Ntchito ya Timoteyo
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo 19 utagwiritsitsa chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. Ena anazikana zimenezi motero chikhulupiriro chawo chinawonongeka. 20 Ena mwa amenewa ndi Humenayo ndi Alekisandro, amene ndinawapereka kwa Satana kuti aphunzire kusachita chipongwe Mulungu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.