M’Cheyne Bible Reading Plan
Malamulo a Nthenda za pa Khungu Zopatsirana
13 Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 2 “Munthu akakhala ndi chithupsa, kapena mʼbuko, kapena chikanga pa thupi lake chimene chitha kusanduka nthenda ya khate, abwere naye munthuyo kwa Aaroni wansembe kapena kwa mmodzi mwa ana ake amene ndi ansembe. 3 Tsono wansembe ayangʼanitsitse nthendayo pa khungupo, ndipo ngati ubweya wa pamalo pamene pali nthendapo wasanduka woyera, komanso kuti nthendayo yazama mʼkati kupitirira khungu, ndiye kuti nthendayo ndi khate. Wansembe akamuonetsetsa alengeze kuti ndi wodetsedwa. 4 Ngati chikanga cha pa khungulo chikuoneka choyera, ndipo kuya kwake sikukuonekera kuti kwapitirira khungu ndi ubweya wake pamalopo sunasanduke woyera, wansembe amuyike wodwalayo padera kwa masiku asanu ndi awiri. 5 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso bwino wodwalayo. Ndipo ngati waona kuti nthendayo sinasinthe ndipo sinafalikire pa khungu, amuyikenso wodwalayo padera kwa masiku ena asanu ndi awiri. 6 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembeyo amuonenso bwino munthuyo, ndipo ngati nthendayo yazima ndi kusafalikira pa khungu, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi woyera. Umenewo unali mʼbuko chabe. Choncho munthuyo achape zovala zake ndipo adzakhala woyera. 7 Koma ngati mʼbukowo ufalikira pakhungu atakadzionetsa kale kwa wansembe ndipo wansembeyo nʼkulengeza kuti munthuyo ndi woyeretsedwa, ndiye kuti apitenso kukadzionetsa kwa wansembeyo. 8 Wansembe amuonetsetsenso munthuyo, ndipo ngati mʼbukowo wafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa ndi kuti nthendayo ndi khate.
9 “Ngati munthu aliyense ali ndi nthenda ya pakhungu yoyipitsa thupi, wodwalayo abwere naye kwa wansembe. 10 Wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati ali ndi chithupsa chamaonekedwe woyera pa khungupo chimene chasandutsa ubweya wa pamalopo kukhala woyera, ndipo ngati pali zilonda pa chotupacho, 11 limenelo ndi khate lachikhalire la pa khungu, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Asamutsekere munthu woteroyo pakuti ndi wodetsedwa kale.
12 “Ndipo ngati, mʼkuona kwa wansembe, khate lija lafalikira pa khungu lonse moti lamugwira thupi lonse kuyambira kumutu mpaka kumapazi, 13 wansembe amuonetsetse munthuyo, ndipo ngati khatero lagwira thupi lake lonse, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Popeza kuti thupi lonse lasanduka loyera, munthuyo ndi woyeretsedwa. 14 Koma pa tsiku limene zilonda zidzaoneka pa iye, munthuyo adzakhala wodetsedwa. 15 Wansembe aonetsetse zilondazo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zilondazo ndi zodetsedwa ndipo ili ndi khate. 16 Koma zilondazo zikasinthika ndi kusanduka zoyera, munthuyo ayenera kupita kwa wansembe. 17 Wansembe amuonetsetse ndipo ngati zilondazo zasanduka zoyera, wansembe amutchule wodwalayo kuti ndi woyera ndipo adzakhala woyera ndithu.
18 “Ngati pa khungu la munthu wodwalayo pali chithupsa chimene chinapola kale, 19 ndipo pamalo pamene panali chithupsacho pakatuluka chotupa choyera kapena banga loyera mofiirira, munthuyo ayenera kukadzionetsa kwa wansembe. 20 Wansembe aonetsetse bwino ndipo ngati chikuoneka kuti chazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka woyera, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Imeneyo ndi nthenda ya khate imene yatuluka mʼchithupsacho. 21 Koma ngati wansembe waonetsetsa napeza kuti palibe ubweya woyera ndipo chithupsacho sichinazame, koma chazimirira, wansembeyo amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri. 22 Ngati nthendayo ikufalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limeneli ndi khate. 23 Koma bangalo likakhala malo amodzi, wosafalikira, chimenecho ndi chipsera cha chithupsacho, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera.
24 “Munthu akakhala ndi bala lamoto pa khungu lake, ndipo chilonda cha balalo chikasanduka banga loyera mofiirira kapena loyera, 25 wansembe aonetsetse bangalo, ndipo ngati ubweya wa pa bangapo usanduka woyera, ndipo balalo lioneka kuti ndi lozama, limenelo ndi khate lomwe latuluka pa balalo. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate la pa khungu. 26 Koma ngati wansembe waonetsetsa balalo ndipo palibe ubweya woyera, ndipo ngati balalo silinazame ndi kuti lazirala, wansembe amuyike padera wodwalayo kwa masiku asanu ndi awiri. 27 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso wodwalayo, ndipo ngati bangalo lafalikira pa khungu, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Limenelo ndi khate. 28 Koma ngati bangalo likhala pa malo amodzi wosafalikira pa khungu, ndipo lazimirira, limenelo ndi thuza la bala lamoto, ndipo wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Chimenecho ndi chipsera chamoto.
29 “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi nthenda kumutu kapena ku chibwano, 30 wansembe aonetsetse balalo ndipo likaoneka kuti lazama, ndipo ubweya wa pamalopo wasanduka wachikasu ndi wonyololoka, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa. Zimenezo ndi mfundu zonyerenyetsa, khate lakumutu kapena ku chibwano. 31 Koma wansembe akaonetsetsa mfundu zonyerenyetsazo, ndipo zikaoneka kuti sizinazame ndi kuti palibe ubweya wakuda, wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku asanu ndi awiri. 32 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo, ndipo ngati sizinafalikire ndipo palibe ubweya wachikasu pamalopo ndiponso sizinazame, 33 wodwalayo ametedwe, koma pamene pali mfunduyo pasametedwe. Wansembe amuyike padera munthuyo kwa masiku enanso asanu ndi awiri. 34 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aonetsetsenso mfundu zonyerenyetsazo ndipo ngati sizinafalikire pa khungu ndi kuti sizinazame, wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyera. Tsono achape zovala zake, ndipo adzakhala woyera. 35 Koma mfundu zonyerenyetsazo zikafalikira pa khungu, wansembe atalengeza kuti ndi woyera, 36 wansembe amuonetsetsenso wodwalayo ndipo ngati mfunduzo zafalikira pa khungu, iye asalabadirenso zoyangʼana ngati ubweya uli wachikasu. Munthuyo ndi wodetsedwa. 37 Koma ngati wansembe waonetsetsa kuti mfunduzo sizinasinthe ndipo ubweya wakuda wamera pa mfundupo, ndiye kuti wodwalayo wachira. Tsono wansembe alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa.
38 “Mwamuna kapena mkazi akakhala ndi mawanga woyera pa khungu, 39 wansembe aonetsetse mawangawo, ndipo ngati ali otuwa, ndiye kuti ndi mibuko chabe yotuluka pa khungu. Munthuyo ndi woyera.
40 “Tsitsi la munthu likayoyoka kumutu ndiye kuti ndi dazi limenelo koma munthuyo ndi woyeretsedwa. 41 Ngati tsitsi lake layoyoka chapamphumi ndiye kuti ndi dazi la pa chipumi limenelo koma munthuyo ndi woyera. 42 Koma ngati pa dazi la pamutu kapena la pa chipumi pakhala chithupsa choyera mofiirira, ndiye kuti ndi khate limenelo lochokera mu dazi la pamutu lija kapena pa chipumi lija. 43 Tsono wansembe amuonetsetse wodwalayo ndipo ngati chithupsa cha pa dazi lapankhongo kapena pa dazi lapachipumicho ndi choyera mofiirira monga nthenda ya khate imaonekera, 44 ndiye kuti munthuyo ali ndi khate, motero ndi wodetsedwa. Wansembe alengeze kuti munthuyo ndi wodetsedwa chifukwa cha chithupsa cha pamutu pakepo.
45 “Munthu wa khate lotere avale sanza, tsitsi lake alilekerere, aphimbe mlomo wake wapamwamba ndipo azifuwula kuti, ‘Ndine wodetsedwa, ndine wodetsedwa!’ 46 Munthu wodwalayo adzakhala wodetsedwa kwa nthawi yonse imene ali ndi nthendayo. Iye ayenera kumakhala payekha kunja kwa msasa.
Malamulo a Nguwi ya pa Zovala
47 “Nsalu iliyonse ikakhala ndi nguwi, 48 kaya ndi chovala chopangidwa ndi nsalu yathonje kapena yaubweya, yoluka ndi thonje kapena ubweya, yachikopa kapena yopangidwa ndi chikopa, 49 ndipo ngati pamalo pamene pachita nguwiyo pali ndi maonekedwe obiriwira kapena ofiirira imeneyo ndi nguwi yoyipitsa chovala ndipo chovalacho chikaonetsedwe kwa wansembe. 50 Wansembeyo ayionetsetse nguwiyo ndipo chovalacho achiyike padera kwa masiku asanu ndi awiri. 51 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri ayionetsetsenso nguwiyo ndipo ngati nguwiyo yafalikira pa chovalacho, chathonje kapena chaubweya, kapena pa chikopacho, kaya ndi cha ntchito ya mtundu wanji, imeneyo ndi nguwi yoopsa ndipo chovalacho ndi chodetsedwa. 52 Wansembe atenthe chovala chathonje kapena chaubweya chija, ngakhalenso chinthu chachikopa chija popeza nguwiyo yachidetsa. Nguwiyo ndi yoopsa choncho chinthucho achitenthe.
53 “Koma ngati wansembe akayangʼanitsitsa nguwiyo apeza kuti sinafalikire pa chovalacho kapena pa chinthu chilichonse chachikopa, 54 iye alamulire kuti chinthu choyipitsidwacho achichape. Akatero achiyike padera kwa masiku enanso asanu ndi awiri. 55 Chovalacho chitachapidwa, wansembe achionenso ndipo ngati nguwiyo sinasinthe maonekedwe ake, ngakhale kuti sinafalikire, chovalacho ndi chodetsedwa ndithu. Muchitenthe, ngakhale kuti nguwiyo ili kumbuyo kapena kumaso kwa chinthucho. 56 Koma ngati wansembe aonetsetsa nʼkupeza kuti nguwi ija yathimbirira pa chovala chija kapena pa chinthu chachikopa chija atachichapa, ndiye angʼambeko chinthucho pa banga la nguwiyo. 57 Koma ngati nguwiyo iwonekanso pa chovala chathonje kapena chaubweya ndiye kuti nguwiyo ikufalikira. Chilichonse chimene chili ndi nguwi chiyenera kutenthedwa. 58 Chovala chathonje kapena chaubweya, ngakhale chinthu china chilichonse chopangidwa ndi chikopa, mukachichapa nguwi yake nʼkuchoka muchichapenso kawiri ndipo chidzakhala choyeretsedwa.”
59 Amenewa ndiwo malamulo a nguwi yokhala pa chovala chaubweya kapena pa chovala chathonje, kapenanso pa chinthu chilichonse chopangidwa ndi chikopa kuti muzitha kulekanitsa choyeretsedwa ndi chodetsedwa.
Salimo la Davide.
15 Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?
Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?
2 Munthu wa makhalidwe abwino,
amene amachita zolungama,
woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
3 ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,
amene sachitira choyipa mnansi wake
kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
4 amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.
Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,
amene amakwaniritsa zomwe walonjeza
ngakhale pamene zikumupweteka,
5 amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja
ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa.
Iye amene amachita zinthu zimenezi
sadzagwedezeka konse.
Mikitamu ya Davide.
16 Ndisungeni Inu Mulungu,
pakuti ine ndimathawira kwa Inu.
2 Ndinati kwa Yehova, “Inu ndinu Ambuye anga;
popanda Inu, ine ndilibe chinthu chinanso chabwino.”
3 Kunena za oyera mtima amene ali pa dziko,
amenewa ndi olemekezeka, amene ndimakondwera nawo.
4 Anthu amene amathamangira kwa milungu ina
mavuto awo adzachulukadi.
Ine sindidzathira nawo nsembe zawo zamagazi
kapena kutchula mayina awo ndi pakamwa panga.
5 Yehova, Inu mwandipatsa cholowa changa ndi chikho changa;
mwateteza kolimba gawo langa.
6 Malire a malo anga akhala pabwino;
ndithudi, ine ndili cholowa chokondweretsa kwambiri.
7 Ine ndidzatamanda Yehova amene amandipatsa uphungu;
ngakhale usiku mtima wanga umandilangiza.
8 Ndayika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.
Popeza Iyeyo ali kudzanja langa lamanja,
sindidzagwedezeka.
9 Choncho mtima wanga ndi wosangalala ndipo pakamwa panga pakukondwera;
thupi langanso lidzakhala pabwino,
10 chifukwa Inu simudzandisiya ku manda,
simudzalola kuti woyera wanu avunde.
11 Inu mwandidziwitsa njira ya moyo;
mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu,
ndidzasangalala mpaka muyaya pa dzanja lanu lamanja.
27 Usamanyadire za mawa,
pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.
2 Munthu wina akutamande, koma osati wekha;
mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.
3 Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri,
koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.
4 Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa.
Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.
5 Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino
kuposa chikondi chobisika.
6 Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino,
koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.
7 Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi,
koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.
8 Munthu amene wasochera ku nyumba kwake,
ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.
9 Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima,
ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.
10 Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako,
ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto;
mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.
11 Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga;
pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.
12 Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,
koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.
13 Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;
ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.
14 Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri,
anthu adzamuyesa kuti akutemberera.
15 Mkazi wolongolola ali ngati
mvula yamvumbi.
16 Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo
kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.
17 Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake,
chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.
18 Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake,
ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.
19 Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi,
chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.
20 Manda sakhuta,
nawonso maso a munthu sakhuta.
21 Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo,
chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.
22 Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo
ndi musi ngati chimanga,
uchitsiru wakewo sudzachoka.
23 Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili.
Kodi usamalire bwino ziweto zako?
24 Paja chuma sichikhala mpaka muyaya,
ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.
25 Pamene udzu watha, msipu nʼkumera;
ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,
26 ana ankhosa adzakupatsani chovala
ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.
27 Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri
kuti muzidya inuyo ndi banja lanu
ndi kudyetsa antchito anu aakazi.
1 Paulo, Silivano ndi Timoteyo.
Kulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
2 Chisomo ndi mtendere kwa inu kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.
Kuyamika ndi Pemphero
3 Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe. 4 Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo.
5 Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira. 6 Mulungu ndi wolungama ndipo adzalanga amene amakusautsaniwo 7 ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. 8 Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. 9 Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake 10 pa tsiku limene iye adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ndi kuyamikidwa ndi onse amene anakhulupirira. Inu mudzakhala nawo mʼgulumo chifukwa munakhulupirira umboni wathu.
11 Nʼchifukwa chake timakupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera mayitanidwe ake, ndi kuti mwa mphamvu zake akwaniritse cholinga chanu chilichonse chabwino ndi chilichonse chochitika mwachikhulupiriro. 12 Ife timapempherera zimenezi kuti dzina la Ambuye athu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mulemekezedwe mwa Iyeyo. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.