Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Levitiko 9

Ansembe Ayamba Kutumikira

Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Mose anayitana Aaroni, ana ake ndi akuluakulu a Aisraeli. Ndipo anawuza Aaroni kuti, “Tenga mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yako yopepesera machimo ndi nkhosa yayimuna kuti ikhale nsembe yopsereza. Zonsezi zikhale zopanda chilema ndipo uzipereke pamaso pa Yehova. Kenaka uwawuze Aisraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. Mutengenso mwana wangʼombe ndi mwana wankhosa. Zonsezi zikhale za chaka chimodzi ndi zopanda chilema kuti zikhale nsembe yopsereza. Mutengenso ngʼombe yayimuna ndi nkhosa yayimuna kuti zikhale nsembe yachiyanjano zoti ziperekedwe pamaso pa Yehova. Pamodzi ndi izi mubwerenso ndi nsembe yachakudya yosakaniza ndi mafuta pakuti lero Yehova akuonekerani.’ ”

Anthu anatenga zonse zimene Mose analamula nabwera nazo pa khomo la tenti ya msonkhano. Gululo linasendera pafupi ndi kuyima pamaso pa Yehova. Tsono Mose anati, “Izi ndi zimene Yehova walamula kuti muchite kuti ulemerero wa Yehova ukuonekereni.”

Pambuyo pake Mose anawuza Aaroni kuti, “Sendera pafupi ndi guwa ndipo upereka nsembe yako yopepesera machimo ndi nsembe yako yopsereza ndikuchita mwambo wopepesera machimo ako ndi machimo a anthu. Anthuwa apereke nsembe zawo zopepesera machimo monga momwe Yehova walamulira.”

Choncho Aaroni anasendera pafupi ndi guwa, napha mwana wangʼombe uja kukhala nsembe yake yopepesera machimo. Ana a Aaroni anabwera ndi magazi kwa Aaroni ndipo iye anaviyika chala chake mʼmagaziwo, nawapaka pa nyanga za guwa. Magazi wotsalawo anawathira pa tsinde la guwalo. 10 Kenaka anatentha paguwapo, mafuta, impsyo pamodzi ndi mafuta amene amakuta chiwindi ngati nsembe yopepesera machimoyo, monga momwe Yehova analamulira Mose. 11 Koma nyama ndi chikopa anazitenthera kunja kwa msasa.

12 Kenaka anapha nsembe yopsereza. Ana a Aaroni atabwera ndi magazi kwa iye, Aaroniyo anawawaza mbali zonse za guwa. 13 Ana akewo anamupatsa nyama yoduladula ya nsembe yopsereza ija pamodzi ndi mutu ndipo anazitentha pa guwa. 14 Aaroni anatsuka matumbo ndi miyendo nazitentha pa guwa pamodzi ndi nsembe yopsereza ija.

15 Kenaka Aaroni anapereka zopereka za anthuwo. Anatenga mbuzi yopepesera machimo a anthuwo, yopereka chifukwa cha tchimo, nayipha ndi kuyipereka kuti ikhale yopepesera machimo monga anachitira ndi nsembe yoyamba ija.

16 Anabwera ndi nsembe yopsereza, nayipereka potsata mwambo wake. 17 Anabweranso ndi chopereka cha chakudya. Anatapa ufa dzanja limodzi ndi kutentha pa guwa, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mmawa ija.

18 Tsono Aaroni anapha ngʼombe ndi nkhosa yayimuna monga nsembe yachiyanjano ya anthu. Ana ake anamupatsira magazi ndipo anawawaza mbali zonse za guwa. 19 Anamupatsiranso mafuta a ngʼombeyo ndi nkhosa yayimunayo: mchira wamafuta, mafuta wokuta matumbo, impsyo ndi mafuta wokuta chiwindi. 20 Ana a Aaroni anayika mafutawo pa zidale. Pambuyo pake Aaroni anatentha mafutawo pa guwa lansembe. 21 Koma zidale ndi ntchafu ya kumanja Aaroni anaziweyula ngati chopereka choweyula pamaso pa Yehova.

22 Kenaka Aaroni anakweza manja ake pa anthuwo nawadalitsa. Ndipo atatha kupereka nsembe yopepesera machimo, nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano, anatsika pa guwapo.

23 Ndipo Mose pamodzi ndi Aaroni analowa mu tenti ya msonkhano. Atatulukamo anadalitsa anthuwo ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse. 24 Pomwepo moto unatuluka pamaso pa Yehova niwutentha nsembe zopsereza ndi mafuta zimene zinali pa guwa. Anthu onse ataona zimenezi anafuwula mwachimwemwe ndipo anaweramitsa nkhope zawo pansi.

Masalimo 10

10 Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali?
    Chifukwa chiyani mukudzibisa nokha pa nthawi ya mavuto?

Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka,
    amene akodwa mʼnjira zimene iye wakonza.
Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake;
    amadalitsa aumbombo ndi kuchitira chipongwe Yehova.
Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu;
    mʼmaganizo ake wonse mulibe malo a Mulungu.
Zinthu zake zimamuyendera bwino;
    iye ndi wamwano ndipo malamulo anu ali nawo kutali;
    amanyogodola adani ake onse.
Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze.
    Ndidzakhala wokondwa nthawi zonse ndipo sindidzakhala pa mavuto.”
Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza;
    zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.
Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi,
    kuchokera pobisalapo amapha anthu osalakwa,
    amayangʼanayangʼana mwachinsinsi anthu oti awawononge.
Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba.
    Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu;
    amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.
10 Anthuwo amawapondaponda ndipo amakomoka;
    amakhala pansi pa mphamvu zake.
11 Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala,
    wabisa nkhope yake ndipo sakuonanso.”

12 Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu.
    Musayiwale anthu opanda mphamvu.
13 Nʼchifukwa chiyani munthu woyipa amachitira chipongwe Mulungu?
    Chifukwa chiyani amati mu mtima mwake,
    “Iye sandiyimba mlandu?”
14 Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa,
    mumaganizira zochitapo kanthu.
Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti
    Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.
15 Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa;
    muzengeni mlandu chifukwa cha zoyipa zake
    zimene sizikanadziwika.

16 Yehova ndi Mfumu kwamuyaya;
    mitundu ya anthu idzawonongeka kuchoka mʼdziko lake.
17 Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa;
    mumawalimbikitsa ndipo mumamva kulira kwawo.
18 Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa,
    ndi cholinga chakuti munthu amene ali wa dziko lapansi asaopsenso.

Miyambo 24

24 Usachitire nsanje anthu oyipa,
    usalakalake kuti uzikhala nawo,
pakuti mitima yawo imalingalira chiwawa,
    ndipo pakamwa pawo pamayankhula zoyambitsa mavuto.

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru,
    ndipo imakhazikika ndi anthu odziwa zinthu;
Munthu wodziwa zinthu angathe kudzaza zipinda zake
    ndi chuma chamtengowapatali ndiponso chabwino.

Munthu wodziwa zinthu ali ndi mphamvu yayikulu kuposa munthu wanyonga zambiri,
    ndipo munthu wachidziwitso amaposa munthu wamphamvu.
Pafunika malangizo kuti ukamenye nkhondo.
    Pakakhala aphungu ambiri kupambana kumakhalapo.

Nzeru ndi chinthu chapatali kwambiri kwa chitsiru;
    chilibe choti chiyankhule pabwalo la milandu pa chipata.

Amene amakonzekera kuchita zoyipa
    adzatchedwa mvundulamadzi.
Kukonzekera kuchita za uchitsiru ndi tchimo,
    ndipo munthu wonyoza amanyansa anthu.

10 Ngati utaya mtima nthawi ya mavuto ndiye kuti
    mphamvu yako ndi yochepadi!

11 Uwapulumutse amene akutengedwa kuti akaphedwe;
    uwalanditse amene akuyenda movutika kupita kokaphedwa.
12 Ukanena kuti, “Koma ife sitinadziwe kanthu za izi,”
    kodi Iye amene amasanthula mtima sazindikira zimenezi?
Kodi Iye amene amateteza moyo wako sazidziwa zimenezi?
    Kodi Iye sadzalipira munthu malingana ndi ntchito zake?

13 Mwana wanga, uzidya uchi popeza ndi wabwino;
    uchi wochokera mʼchisa cha njuchi ndi wokoma ukawulawa.
14 Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako;
    ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo,
    ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.

15 Usachite zachifwamba nyumba ya munthu wolungama ngati munthu woyipa.
    Usachite nayo nkhondo nyumba yake;
16 paja munthu wolungama akagwa kasanu nʼkawiri amadzukiriranso.
    Koma woyipa adzathedwa tsoka likadzawafikira.

17 Usamakondwera ndi kugwa kwa mdani wako.
    Mtima wako usamasangalale iye akapunthwa.
18 Kuopa kuti Yehova ataziona zimenezi nayipidwa nazo,
    angaleke kukwiyira mdaniyo.

19 Usavutike mtima chifukwa cha anthu ochita zoyipa
    kapena kuchitira nsanje anthu oyipa,
20 paja munthu woyipa alibe tsogolo.
    Moyo wa anthu oyipa adzawuzimitsa ngati nyale.

21 Mwana wanga, uziopa Yehova ndi mfumu,
    ndipo usamagwirizana ndi anthu owachitira mwano,
22 awiri amenewa amagwetsa tsoka mwadzidzidzi.
    Ndani angadziwe mavuto amene angagwetse?

Malangizo Enanso a Anthu Anzeru

23 Malangizo enanso a anthu anzeru ndi awa:

Kukondera poweruza mlandu si chinthu chabwino:
24 Aliyense amene amawuza munthu wolakwa kuti, “Iwe ndi munthu wosalakwa,”
    anthu a mitundu yonse adzamutemberera, ndi mitundu ya anthu idzayipidwa naye.
25 Koma olanga anthu oyipa zinthu zidzawayendera bwino
    ndipo madalitso ochuluka adzakhala pa iwo.

26 Woyankhula mawu owona
    ndiye amaonetsa chibwenzi chenicheni.

27 Ugwiriretu ntchito zako zonse,
    makamaka za ku munda
    ndipo pambuyo pake uyambe kumanga nyumba.

28 Usakhale mboni yotsutsa mnzako popanda chifukwa,
    kapena kugwiritsa ntchito pakamwa pako kunena zachinyengo.
29 Usanene kuti, “Ine ndidzamuchitira iye monga momwe wandichitira ine;
    ndidzamubwezera munthu ameneyo zimene anandichitira.”

30 Ndinkayenda mʼmbali mwa munda wa munthu waulesi
    ndinadutsa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru.
31 Ndinapeza kuti paliponse mʼmundamo munali mutamera minga,
    mʼnthaka imeneyo munali mutamera khwisa,
    ndipo mpanda wake wamiyala unali utawonongeka.
32 Tsono nditaona ndinayamba kuganizira mu mtima mwanga
    ndipo ndinatolapo phunziro ili:
33 Ukati, “Bwanji ndigone pangʼono,” kapena “Ndiwodzereko pangʼono,”
    kapenanso “Ndipinde manja pangʼono kuti ndipumule,”
34 umphawi udzafika pa iwe ngati mbala
    ndipo usiwa udzakupeza ngati munthu wachifwamba.

1 Atesalonika 3

Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene. Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu, ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi. Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi. Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.

Nkhani Yolimbikitsa Kuchokera kwa Timoteyo

Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo. Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa. Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye. Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10 Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.

11 Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. 12 Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. 13 Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.